Chimwemwe cha Yehova Ndicho Linga Lathu
“Lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho [linga lanu, NW].”—NEHEMIYA 8:10.
1, 2. (a) Kodi linga nchiyani? (b) Kodi ndimotani mmene Davide anasonyezera kuti anathaŵira mwa Yehova?
YEHOVA ndi linga losayerekezereka. Ndipo kodi linga nchiyani? Ndilo malo otchingidwa, otetezera kapena opulumukiramo. Davide wa m’Israyeli wakale anaona Mulungu kukhala linga lake. Mwachitsanzo, talingalirani za nyimbo imene Davide anaimbira Wam’mwambamwamba “mmene Yehova anamlanditsa m’dzanja la adani ake onse, ndi m’dzanja la Sauli,” mfumu ya Israyeli.—Salmo 18, timawu tapamwamba.
2 Davide anayamba nyimbo yokhudza mtima imeneyo ndi mawu akuti: “Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga. Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.” (Salmo 18:1, 2) Atachotseredwa chitetezo cha lamulo mopanda chilungamo ndi kulondalondedwa ndi Mfumu Sauli, Davide wolungamayo anathaŵira mwa Yehova, mongadi mmene munthu angathaŵire m’malo otchingidwa kuti apulumuke tsoka.
3. Kodi nchifukwa ninji Ayuda a m’tsiku la Ezara anakhala ndi “kusekerera kwakukulu”?
3 Chimwemwe chimene Yehova amapereka ndicho linga losalephera kwa awo oyenda m’njira zake monga osunga umphumphu. (Miyambo 2:6-8; 10:29) Ndithudi, kuti anthu akhale ndi chimwemwe chopatsidwa ndi Mulungu, ayenera kuchita chifuniro chake. Pazimenezi, talingalirani zimene zidachitika mu Yerusalemu mu 468 B.C.E. Mlembi Ezara limodzinso ndi ena anazindikiritsa Chilamulo mwa kuchiŵerenga momvekera bwino. Ndiyeno anthuwo analimbikitsidwa kuti: “Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeratu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho [linga lanu, NW].” “Kusekerera kwakukulu” kunakhalapo pamene Ayuda anagwiritsira ntchito chidziŵitso chimene anapeza ndipo anachita Madyerero a Misasa achisangalalo. (Nehemiya 8:1-12) Awo amene anali ndi ‘chimwemwe cha Yehova monga linga lawo’ anapeza nyonga ya kulambira ndi kumtumikira. Popeza kuti chimwemwe cha Yehova chinali linga lawo, tiyenera kuyembekezera anthu a Mulungu lerolino kukhalanso achimwemwe. Pamenepa, kodi ndi zifukwa zina zotani zamakono zokhalira achimwemwe?
“Nimukondwere Monsemo”
4. Kodi ndi chifukwa chapadera chotani chimene chimapatsa chimwemwe anthu a Yehova?
4 Chifukwa china chapadera ndicho makonzedwe amene Yehova wapanga a kusonkhana pamodzi. Misonkhano yadera ndi yachigawo ya Mboni za Yehova imawapatsa chimwemwe lerolino, monga momwe madyerero apachaka ochitidwa ndi Aisrayeli anadzetsera chimwemwe m’mitima yawo. Anthu a Israyeli anauzidwa kuti: “Masiku asanu ndi aŵiri muchitire Yehova Mulungu wanu madyerero m’malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m’zipatso zanu zonse, ndi m’ntchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.” (Deuteronomo 16:13-15) Inde, Mulungu anafuna kuti iwo ‘akondwere monsemo.’ Zilinso motero kwa Akristu oona, popeza mtumwi Paulo anasonkhezera okhulupirira anzake kuti: “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.”—Afilipi 4:4.
5. (a) Kodi chimwemwe nchiyani, ndipo Akristu amachipeza motani? (b) Kodi ndimotani mmene tingakhalire ndi chimwemwe mosasamala kanthu za mayesero?
5 Popeza kuti Yehova amafuna kuti tikhale achimwemwe, iye amatipatsa chimwemwe monga chimodzi cha zipatso za mzimu woyera. (Agalatiya 5:22, 23) Ndipo kodi chimwemwe nchiyani? Ndicho chisangalalo cha mtima chochititsidwa ndi chiyembekezo kapena kupeza chinthu chabwino. Chimwemwe ndicho mkhalidwe wa chisangalalo chenicheni, kusekereradi. Chipatso cha mzimu wa Mulungu chimenechi chimatichirikiza pachiyeso. “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, [Yesu] anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Ahebri 12:2) Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.” Koma bwanji ngati sitidziŵa chochita ndi chiyeso? Pamenepo tikhoza mwachidaliro kupempherera nzeru ya mmene tingachitire nacho. Kuchita mogwirizana ndi nzeru yakumwamba kumatikhozetsa kuthetsa mavuto kapena kupirira ziyeso zopitirizabe popanda kutaya chimwemwe cha Yehova.—Yakobo 1:2-8.
6. Kodi ndi zifukwa zina ziti zopatsa chimwemwe zimene tsopano tidzakambitsirana?
6 Chimwemwe chimene Yehova amapatsa chimatilimbitsa kuti tichirikize kulambira koona. Ndi zimene zinachitikanso m’masiku a Nehemiya ndi Ezara. Ayuda a panthaŵi imeneyo amene anali ndi chimwemwe cha Yehova monga linga lawo analimbitsidwa kuti achirikize kulambira koona. Ndipo pamene anachirikiza kulambira Yehova, chimwemwe chawo chinawonjezeka. Zilinso motero lerolino. Monga alambiri a Yehova, tili ndi maziko okhalira ndi chimwemwe chachikulu. Tsopano tiyeni tipende zingapo za zifukwa zathu zambiri zokhalira achimwemwe.
Unansi ndi Mulungu Kupyolera mwa Kristu
7. Ponena za Yehova, kodi ndi chifukwa chiti chimene Akristu ali nacho chokhalira achimwemwe?
7 Unansi wathu woyandikana ndi Yehova umatipangitsa kukhala anthu osangalala koposa padziko lapansi. Tisanakhale Akristu, tinali mbali ya chitaganya cha anthu osalungama ‘okhala mumdima wamaganizo ndi alendo pa moyo wochokera kwa Mulungu.’ (Aefeso 4:18) Ha, tili okondwa chotani nanga kuti sitilinso otalikirana ndi Yehova! Ndithudi, kukhalabe m’chiyanjo chake kumafuna kuyesayesa. Tiyenera ‘kukhalabe m’chikhulupiriro, ochirimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha uthenga wabwino.’ (Akolose 1:21-23) Tiyenera kukondwera poona kuti Yehova anatikokera kwa Mwana wake mogwirizana ndi mawu a Yesu mwiniyo akuti: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye.” (Yohane 6:44) Ngati tiyamikiradi unansi wathu wa mtengo wapatali ndi Mulungu kupyolera mwa Kristu, tidzapeŵa chilichonse chimene chingauwononge.
8. Kodi ndimotani mmene Yesu wawonjezerera pa mkhalidwe wathu wachimwemwe?
8 Kukhululukidwa kwa machimo kupyolera m’nsembe ya dipo ya Yesu kuli chifukwa chachikulu chokhalira achimwemwe chifukwa chakuti ndiko kumene kumatheketsa unansi wathu ndi Mulungu. Mwa kachitidwe ka kuchimwira dala, kholo lathu loyamba Adamu linadzetsa imfa pa mtundu wonse wa anthu. Komabe, mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” Paulo analembanso kuti: “Monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse. Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.” (Aroma 5:8, 18, 19) Tiyenera kukhala achimwemwe chotani nanga kuti Yehova Mulungu ali wofunitsitsa kuwombola mbadwa za Adamu zimene zimagwiritsira ntchito makonzedwe achikondi amenewo!
Kumasuka ku Chipembedzo ndi Kutseguka Maso
9. Kodi nchifukwa ninji tili achimwemwe ponena za chipembedzo?
9 Kumasuka ku Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, ndiko chifukwa china chokhalira achimwemwe. Choonadi cha Mulungu nchimene chatimasula. (Yohane 8:32) Ndipo chimasuko ku mkazi wachigololo wachipembedzo ameneyu chimatanthauza kuti sitikugaŵana m’machimo ake, kukanthidwa ndi miliri yake, kapena kuloŵa m’chiwonongeko limodzi naye. (Chivumbulutso 18:1-8) Palibe chomvetsa chisoni chilichonse pa kuthaŵa zonsezo!
10. Kodi ndi kutseguka maso kotani kumene tikukhala nako monga anthu a Yehova?
10 Kuzindikira ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu m’moyo ndiko zifukwa zinanso zokhalira ndi chimwemwe chachikulu. Pokhala omasuka ku chisonkhezero cha chipembedzo chonyenga, tikusangalala ndi chidziŵitso chauzimu chomvekera bwino nthaŵi zonse choperekedwa ndi Atate wathu wakumwamba kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Pakati pa anthu onse okhala padziko lapansi, awo okha odzipereka kotheratu kwa Yehova ndiwo ali ndi mzimu woyera ndi dalitso la kumvetsetsa Mawu ake ndi chifuniro chake. Zili monga momwe Paulo ananenera kuti: “Zimene zili zonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye. Koma kwa ife Mulungu anatiwonetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.” (1 Akorinto 2:9, 10) Tiyenera kukhala oyamikira ndi achimwemwenso kuti tikusangalala ndi kuzindikira kopita patsogolo kosonyezedwa m’mawu a Miyambo 4:18 kuti: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.”
Chiyembekezo cha Ufumu ndi Moyo Wamuyaya
11. Kodi ndimotani mmene chiyembekezo chachimwemwe cha Ufumu chagaŵidwira kwa ena?
11 Chiyembekezo chathu cha Ufumu nachonso chimatipatsa chimwemwe. (Mateyu 6:9, 10) Monga Mboni za Yehova, talengeza kwanthaŵi yaitali kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha mtundu wonse wa anthu. Mwachitsanzo, talingalirani za chaka cha 1931, pamene tinatenga dzina lakuti Mboni za Yehova mwa chigamulo chovomerezedwa mwachimwemwe pa misonkhano yaikulu yokwanira 51 kuzungulira dziko lonse. (Yesaya 43:10-12) Chigamulo chimenecho ndi nkhani yapadera yokambidwa ndi J. F. Rutherford (pulezidenti wapanthaŵiyo wa Watch Tower Society) zinafalitsidwa m’kabuku kakuti The Kingdom, the Hope of the World. Mmenemo munaphatikizidwanso chigamulo china chopangidwa pa msonkhano umenewo, cha kutsutsa Dziko Lachikristu kaamba ka mpatuko wake ndi kuchitira Mboni za Yehova mwachipongwe. Icho chinalengezanso kuti: “Chiyembekezo cha dziko ndicho ufumu wa Mulungu, ndipo palibenso chiyembekezo china.” Pamiyezi yoŵerengeka, Mboni za Yehova zinagaŵira makope oposa mamiliyoni asanu a kabuku kameneka m’mbali zonse za dziko lapansi. Kuyambira pamenepo kaŵirikaŵiri tatsimikiziritsa kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu.
12. Kodi ndi ziyembekezo za moyo zosangalatsa zotani zimene zaikidwa pamaso pa awo otumikira Yehova?
12 Tikusangalalanso ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya mu ulamuliro wa Ufumuwo. “Kagulu ka nkhosa” ka Akristu odzozedwa kali ndi chiyembekezo cha kumwamba chosangalatsa. “Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu,” analemba motero mtumwi Petro, “iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu; kuti tilandire choloŵa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’mwamba inu.” (Luka 12:32; 1 Petro 1:3, 4) Lerolino, unyinji wa Mboni za Yehova ukuyembekezera moyo wosatha m’Paradaiso wokhala mu ulamuliro wa Ufumuwo. (Luka 23:43; Yohane 17:3) Palibe anthu ena padziko lapansi amene ali ndi ziyembekezo zachimwemwe zimene zingayerekezeredwe ndi zathu. Tiyenera kuzisamalira bwino chotani nanga!
Ubale Wodalitsidwa
13. Kodi ndimotani mmene tiyenera kuonera ubale wathu wa mitundu yonse?
13 Kukhala mbali ya ubale wa mitundu yonse wokhawo wovomerezedwa ndi Mulungu kulinso kodzetsa chimwemwe chachikulu. Mokondweretsa, tili ndi mabwenzi ofunika koposa padziko lapansi. Yehova Mulungu iye mwini anasonya ku tsiku lathuli ndipo anati: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.” (Hagai 2:7) Zoona, Akristu onse ali opanda ungwiro. Komabe, Yehova wakokera anthu oterowo kwa iye mwini kupyolera mwa Yesu Kristu. (Yohane 14:6) Popeza kuti Yehova wakokera kwa iye mwini anthu amene amawalingalira kukhala ofunika, chimwemwe chathu chidzachuluka ngati tiwasonyeza chikondi chaubale, kuwalemekeza kwambiri, kugwirizana nawo m’zochita zaumulungu, kuwalimbikitsa m’mayesero awo, ndi kuwapempherera.
14. Kodi ndi chilimbikitso chotani chimene tingapeze pa 1 Petro 5:5-11?
14 Zonsezi zidzawonjezera chimwemwe chathu. Ndithudi, chimwemwe cha Yehova ndichodi linga la ubale wathu wauzimu kuzungulira dziko lonse lapansi. Inde, tonsefe timakumana ndi mazunzo ndi zovuta zina. Koma zimenezi ziyenera kutikokera pamodzi ndi kutipatsa lingaliro la umodzi monga mbali ya gulu limodzi loona la Mulungu pa dziko lapansi. Monga momwe Petro ananenera, tiyenera kudzichepetsa pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, tikumatayira nkhaŵa zathu zonse pa iye ndi kuzindikira kuti iye amatisamalira. Tifunikira kukhala maso chifukwa chakuti Mdyerekezi akufuna kutilikwira, koma sitili tokha m’zimenezi, pakuti Petro akuwonjezera kuti: “Mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.” Ndipo ubale wachimwemwe wa mitundu yonse umenewu sudzagwa konse, pakuti tili ndi chitsimikiziritso chakuti ‘titamva zoŵaŵa kanthaŵi, Mulungu adzatifikitsa, ndipo adzatikhazikitsa ndi kutilimbikitsa.’ (1 Petro 5:5-11) Tangolingalirani zimenezo. Ubale wathu wachimwemwe udzakhala kunthaŵi zomka muyaya!
Moyo wa Chifuno
15. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Mboni za Yehova zili ndi moyo wachifuno?
15 Ife tili ndi chimwemwe m’dziko lino lodzala ndi mavuto chifukwa chakuti tili ndi moyo wa chifuno. Taikiziridwa utumiki umene umadzetsa chimwemwe kwa ife ndi kwa ena. (Aroma 10:10) Ulidi mwaŵi wodzetsa chimwemwe kukhala antchito anzake a Mulungu. Pa zimenezi, Paulo anati: “Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa. Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha. Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.”—1 Akorinto 3:5-9.
16, 17. Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zingatchulidwe zotsimikizira kuti anthu a Yehova ali ndi miyoyo ya chifuno ndi yachimwemwe?
16 Zitsanzo zambiri zingaperekedwe zosonyeza kuti kutumikira Yehova mokhulupirika kumachititsa moyo wa chifuno umene umatidzaza ndi chimwemwe. Nachi chitsanzo chenicheni: “Ndinaunguza m’Nyumba Yaufumu yodzala ndi anthu [patsiku la programu ya kuipatulira] ndipo ndinaona kuti ziŵalo zisanu ndi zitatu za banja langa zinalipo, kuphatikizapo ineyo ndi mkazi wanga, ndi atatu a ana athu ndi anzawo a muukwati. . . . Mkazi wanga ndi ine takhaladi ndi moyo wachimwemwe ndi chifuno mu utumiki wa Mulungu.”
17 Kulinso kosangalatsa mtima kudziŵa kuti pausinkhu uliwonse munthu akhoza kuyamba moyo wachimwemwe wokhala ndi chifuno chenicheni mu utumiki wa Yehova. Mwachitsanzo, mkazi wina amene anaphunzira choonadi cha Baibulo panyumba yosamalira okalamba anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova pausinkhu wa zaka 102. Motero iye anamaliza moyo wake ndi chifuno chosangalatsa, ‘kuwopa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake.’—Mlaliki 12:13.
Linga Losalephera
18. Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuti tilake kutaya mtima ndi kuti tiwonjezere chimwemwe chathu?
18 Chimwemwe cha Yehova ndicho linga losalephera kwa okhulupirika. Komabe, kukhala ndi chimwemwe chimenechi sikutanthauza kuti sitidzakhala ndi nthaŵi zachisoni monga zimene zinasonkhezera Yesu m’Getsemane kunena kuti: “Moyo wanga uli ndi chisoni chambiri, kufikira imfa.” (Marko 14:32-34) Tinene kuti kulondola zinthu zadyera kwachititsa kutaya mtima. Pamenepo tiyenera kusintha njira yathu ya moyo. Ngati chimwemwe chathu chazilala chifukwa cha kusenza mopanda dyera mtolo wolemera wa mathayo a Malemba, mwinamwake tiyenera kupanga masinthidwe amene adzatichotsera chipsinjo ndi kubwezeretsa mzimu wathu wachimwemwe. Ndiponso, Yehova adzatidalitsa ndi chimwemwe ngati tiyesayesa kumkondweretsa mwa kukaniza mwamphamvu thupi lochimwa, dziko loipa, ndi Mdyerekezi.—Agalatiya 5:24; 6:14; Yakobo 4:7.
19. Kodi ndimotani mmene tiyenera kuonera thayo lililonse limene tili nalo m’gulu la Mulungu?
19 Pa zifukwa zimene talongosolazi, ndi pa zifukwa zinanso zambiri, tili ndi chisangalalo chachikulu. Kaya tili ofalitsa a mpingo kapena tikuchita mtundu wina wa utumiki wanthaŵi yonse, tonsefe tingakhale ndi zambiri zochita m’ntchito ya Ambuye, ndipo zimenezi zidzawonjezeradi chimwemwe chathu. (1 Akorinto 15:58) Mosasamala kanthu za mwaŵi uliwonse umene tingakhale nawo m’gulu la Yehova, tiyeni tiuyamikire ndi kupitirizabe mwachimwemwe kupereka utumiki wopatulika kwa Mulungu wathu wachikondi ndi wachimwemwe.—1 Timoteo 1:11.
20. Kodi thayo lathu lalikulu koposa nlotani, ndipo kodi tiyenera kukhala otsimikizira ponena za chiyani?
20 Makamaka tili ndi chifukwa chokhalira achimwemwe ndi thayo lathu la kunyamula dzina lalikulu la Yehova monga Mboni zake. Inde, tili opanda ungwiro ndipo timayang’anizana ndi mayesero ambiri, koma monga Mboni za Yehova, tiyeni tikumbukire madalitso athu abwino koposa. Ndipo kumbukirani kuti, Atate wathu wakumwamba wachikondiyo sadzalephera konse. Tikhale otsimikizira kuti nthaŵi zonse tidzadalitsidwa ngati chimwemwe cha Yehova chili linga lathu.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi “chimwemwe cha Yehova” nchiyani?
◻ Kodi ndimotani mmene Akristu amapezera chimwemwe chenicheni?
◻ Kodi ndi zifukwa zina ziti zimene Mboni za Yehova zilili zachimwemwe?
◻ Kodi nchifukwa ninji chimwemwe cha Yehova chili linga losalephera?