Odzipatulira—Kwa Yani?
“Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.” —EKSODO 24:7.
1, 2. (a) Kodi anthu ena ngodzipereka ku chiyani? (b) Kodi kudzipatulira kuli chabe kwa awo amene ali ndi chipembedzo?
MU February 1945, oyendetsa ndege za Zero-fighter a gulu la asilikali la Yatabe Flying Corps la Japan anasonkhana m’holo. Aliyense anapatsidwa kapepala kolembapo ngati iye akadzipereka kukhala chiŵalo cha gulu loukira la kamikaze. “Ndinaganiza kuti chinali chiitano changa cha kudzipereka nsembe panthaŵi imene dziko lathu linali patsoka,” anatero ofesala wina amene analipo panthaŵiyo. “Posonkhezeredwa ndi mtima wanga kuti ndikatumikire, ndinadzipereka kaamba ka ntchitoyo.” Iye anaphunzitsidwa kuyendetsa Ohka (ndege ya roketi yokafa nayo) ndi mmene akanaiwombanitsira ku sitima yapamadzi ya nkhondo ya adani. Komabe, nkhondoyo inatha iye asanakhale ndi mpata wa kuchita zimenezo ndi kufera dziko lake ndi mfumu yake. Pamene Japan anagonja pa nkhondoyo, chikhulupiriro chake mwa mfumu chinagwiritsidwa mwala.
2 Panthaŵi ina, anthu ambiri ku Japan anali odzipereka kwa mfumu, imene anaona kukhala mulungu wamoyo. Kumaiko ena, kunali ndipo kudakali zinthu zina zimene zimapembedzedwa. Anthu miyandamiyanda ngodzipereka kwa Mariya, Buddha, kapena milungu ina—yoimiridwa kaŵirikaŵiri ndi mafano. Posonkhezeredwa ndi mawu okopa, ena amapatsa alaliki a pa TV ndalama zopezedwa movutikira kupereka chichirikizo cha mtima wonse chimene chimalingana ndi kudzipereka. Pambuyo pa nkhondo, Ajapani ogwiritsidwa mwala anafuna chinthu china chatsopano chimene akapatulirako miyoyo yawo. Kwa ena, ntchito inakhala chinthu chimenecho. Kummaŵa kapena Kumadzulo, ambiri amadzipereka pa kukundika chuma. Achichepere amasumika miyoyo yawo pa oimba, ndipo amatsanzira moyo wawo. Lerolino anthu ambiri akhala odzilambira, akumapanga zikhumbo zawo kukhala chinthu chosonyezako kudzipereka kwawo. (Afilipi 3:19; 2 Timoteo 3:2) Koma kodi zinthuzo kapena anthu otero alidi oyenerera kusonyezedwa kudzipereka kwamtima wonse kwa munthu?
3. Kodi ndimotani mmene zinthu zimene anthu amadziperekako zakhalira zopanda pake?
3 Atayang’anizana ndi zenizeni, olambira mafano kaŵirikaŵiri amagwiritsidwa mwala. Kudzipereka ku mafano kumawagwiritsa mwala pamene olambirawo azindikira kuti mafano awo ali chabe “ntchito za manja a anthu.” (Salmo 115:4) Pamene mbiri yoipa yonena za alaliki omveka ivumbuluka, anthu oona mtima amathedwa nzeru. Pamene chuma “chosatsimikizirika” chinalephera, antchito anapsinjika maganizo pamene anapeza kuti anali pa ndandanda ya awo amene anali kuchotsedwa ntchito. Kutsika kwa chuma kwaposachedwapa kunaloŵetsa olambira Chuma m’mavuto aakulu. Ngongole zimene zinatengedwa pofuna kupanga ndalama zambiri zinakhala mtolo popanda chiyembekezo chenicheni cha kuzibwezera. (Mateyu 6:24) Pamene akatswiri a rock ndi osangulutsa ena amwalira kapena kuzimiririka, olambira awo amatsala okha. Ndipo awo amene akhala ndi moyo wodzikhutiritsa kaŵirikaŵiri amatuta zipatso zoipa.—Agalatiya 6:7.
4. Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera anthu kupatulira miyoyo yawo ku zinthu zopanda pake?
4 Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera anthu kudzipatulira ku zinthu zopanda pake zoterozo? Makamaka, uli mzimu wa dziko lolamuliridwa ndi Satana Mdyerekezi. (Aefeso 2:2, 3) Chiyambukiro cha mzimu umenewu chimaonekera m’njira zosiyanasiyana. Munthu angalamuliridwe ndi miyambo ya makolo imene anailandira kwa iwo. Maphunziro ndi maleredwe angayambukire kwambiri kalingaliridwe. Mkhalidwe wa kuntchito ungasonkhezere “antchito omenya nkhondo” kukhala omwerekera ndi ntchito, kumene kungaike moyo wawo pachiswe. Chikhumbo chofuna zowonjezereka chimakulitsidwa ndi mkhalidwe wa dzikoli wokondetsa zinthu zakuthupi. Ambiri mitima yawo njoipitsidwa, ikumawasonkhezera kudzipereka iwo eni ku zikhumbo zawo zadyera. Amalephera kupenda kuti aone ngati zinthu zimenezo ziyenerera kudzipereka kwawo.
Mtundu Wodzipatulira
5. Kodi ndi kudzipatulira kwa Yehova kotani kumene kunachitidwa zaka zoposa 3,500 zapitazo?
5 Zoposa zaka 3,500 zapitazo, mtundu wina wa anthu unapeza munthu woyenerera kwambiri kudzipereka kwawo. Iwo anadzipatulira kwa Mulungu mfumuyo, Yehova. Monga gulu, mtundu wa Israyeli unalengeza kudzipatulira kwake kwa Mulungu m’chipululu cha Sinai.
6. Kodi tanthauzo la dzina la Mulungu linali kudzakhala lotani kwa Aisrayeli?
6 Kodi chinasonkhezera Aisrayeli kuchita mwanjira imeneyi nchiyani? Pamene anali muukapolo mu Igupto, Yehova anatuma Mose kukawamasula. Mose anafunsa mmene akadziŵikitsira Mulungu amene anamtuma, ndipo Mulungu anadzidziŵikitsa iye mwini kukhala “ndidzatsimikizira kukhala amene ndidzatsimikizira kukhala.” Anauza Mose kukauza ana a Israyeli kuti: “Ndidzatsimikizira kukhala wandituma kwa inu.” (Eksodo 3:13, 14, NW) Mawu ameneŵa anasonyeza kuti Yehova amakhala chilichonse chimene afunikira kuti achite zifuno zake. Akadzidziŵikitsa iye mwini kukhala Wokwaniritsa malonjezo mwa njira imene makolo a Aisrayeli sanadziŵe.—Eksodo 6:2, 3.
7, 8. Kodi Aisrayeli anali ndi maumboni otani akuti Yehova anali Mulungu woyenerera kudzipereka kwawo?
7 Aisrayeli anaona dziko la Igupto ndi anthu ake akukanthidwa ndi Miliri Khumi. (Salmo 78:44-51) Ndiyeno, mwinamwake oposa mamiliyoni atatu, kuphatikizapo akazi ndi ana, anamanga katundu wawo natuluka m’dziko la Goseni usiku womwewo, chimene chinali chinthu chodabwitsa. (Eksodo 12:37, 38) Ndiyeno, pa Nyanja Yofiira, Yehova anadzionetsera kukhala “wankhondo” pamene anapulumutsa anthu ake ku magulu a nkhondo a Farao mwa kugaŵa nyanjayo kuti Aisrayeli awoloke ndiyeno pambuyo pake mwa kuitseka kumiza Aaigupto olondolawo. Chotero, “Israyeli anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aaigupto, ndipo anthuwo anawopa Yehova; nakhulupirira Yehova.”—Eksodo 14:31; 15:3; Salmo 136:10-15.
8 Monga ngati kuti anali kusoŵabe umboni wa tanthauzo la dzina la Mulungu, Aisrayeli anang’ung’udzira Yehova ndi womuimira wake Mose ponena za kusoŵa kwa chakudya ndi madzi. Yehova anatumiza zinziri, anagwetsa mana, ndi kutulutsa madzi m’thanthwe ku Meriba. (Eksodo 16:2-5, 12-15, 31; 17:2-7) Yehova anapulumutsanso Aisrayeli pa kuukira kwa Amaleki. (Eksodo 17:8-13) Panalibe mmene Aisrayeli akanakanira zimene Yehova analengeza kwa Mose pambuyo pake kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.” (Eksodo 34:6, 7) Indedi, Yehova anadzionetsera kukhala munthu woyenerera kudzipereka kwawo.
9. Kodi nchifukwa ninji Yehova anapatsa Aisrayeli mpata wa kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa kumtumikira, ndipo iwo anayankha motani?
9 Ngakhale kuti Yehova anali ndi umwini pa Aisrayeli pokhala atawaombola ku Igupto, iye, monga Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, anawapatsa mwaŵi wa kusonyeza mwaufulu chikhumbo chawo cha kumtumikira. (Deuteronomo 7:7, 8; 30:15-20) Analongosolanso zofunika za pangano lake ndi Aisrayeli. (Eksodo 19:3-8; 20:1–23:33) Pamene zofunika zimenezi zinafotokozedwa ndi Mose, Aisrayeli analengeza kuti: “Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.” (Eksodo 24:3-7) Mwa kudzisankhira okha, iwo anakhala mtundu wodzipatulira kwa Ambuye Mfumu Yehova.
Chiyamikiro Chimatsogolera ku Kudzipatulira
10. Kodi kudzipatulira kwathu kwa Yehova kuyenera kuzikidwa pa chiyani?
10 Yehova, Mlengiyo, akupitirizabe kukhala woyenerera kudzipereka kwathu kwamtima wonse. (Malaki 3:6; Mateyu 22:37; Chivumbulutso 4:11) Komabe, kudzipatulira kwathu sikuyenera kuzikidwa pa kungokhulupirira kamodzinkamodzi, kutengeka maganizo, kapena kukakamizidwa ndi ena—ngakhale makolo. Kuyenera kuzikidwa pa chidziŵitso cholongosoka cha choonadi chonena za Yehova ndi chiyamikiro cha zimene Yehova watichitira. (Aroma 10:2; Akolose 1:9, 10; 1 Timoteo 2:4) Monga momwedi Yehova anapatsira Aisrayeli mwaŵi wa kusonyeza mwaufulu kudzipatulira kwawo, amatipatsanso mpata wa kudzipatulira ife eni mwaufulu ndi kusonyeza poyera kudzipatulirako.—1 Petro 3:21.
11. Kodi kuphunzira kwathu Baibulo kwavumbula chiyani ponena za Yehova?
11 Mwa kuphunzira Baibulo, timamdziŵa Mulungu monga munthu. Mawu ake amatithandiza kuzindikira mikhalidwe yake yosonyezedwa ndi chilengedwe. (Salmo 19:1-4) Titha kuona m’Mawu ake kuti sali Utatu wachinsinsi amene sangamveke bwino konse. Salephera nkhondo, choncho samakana Umulungu wake. (Eksodo 5:11; 1 Akorinto 8:5, 6; Chivumbulutso 11:17, 18) Popeza wakwaniritsa malonjezo ake, timakumbutsidwa zimene dzina lake labwinolo, Yehova, limaimira. Iye ali Wachifuno Wamkulu. (Genesis 2:4, NW, mawu amtsinde; Salmo 83:18; Yesaya 46:9-11) Mwa kuphunzira Baibulo, timazindikira bwino lomwe mmene iye alili wokhulupirika ndi wodalirika.—Deuteronomo 7:9; Salmo 19:7, 9; 111:7.
12. (a) Kodi nchiyani chimene chimatikopera kwa Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene zochitika zenizeni m’moyo zolembedwa m’Baibulo zimasonkhezera munthu kufuna kutumikira Yehova? (c) Kodi mumamva bwanji ponena za kutumikira Yehova?
12 Chimene chimatikopera kwa Yehova makamaka ndicho umunthu wake wachikondi. Baibulo limasonyeza mmene alili wachikondi, wokhululuka, ndi wachifundo pochita ndi anthu. Talingalirani mmene analemeretsera Yobu pamene Yobu anasunga umphumphu mokhulupirika. Zimene zinachitikira Yobu zimasonyeza kuti “Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11; Yobu 42:12-17) Talingalirani za mmene Yehova anachitira ndi Davide pamene anachita chigololo ndi mbanda. Inde, Yehova ali wokonzekera kukhululukira ngakhale machimo aakulu pamene wochimwayo afika kwa iye ndi “mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:3-11, 17) Talingalirani njira imene Yehova anachitira ndi Saulo wa ku Tariso, amene poyamba anali wozunza anthu a Mulungu wotsimikiza mtima. Zitsanzo zimenezi zimasonyeza chifundo cha Mulungu ndi kufunitsitsa kwake kugwiritsira ntchito anthu olapa. (1 Akorinto 15:9; 1 Timoteo 1:15, 16) Paulo analingalira kuti akakhoza kuika moyo wake weniweniwo pa kutumikira Mulungu wachikondi ameneyu. (Aroma 14:8) Kodi mumalingalira zofananazo?
13. Kodi ndi chisonyezero chachikulu chiti cha chikondi cha Yehova chimene chimasonkhezera oongoka mtima kudzipatulira kwa iye?
13 Kwa Aisrayeli, Yehova anapereka chipulumutso kuwachotsa muukapolo m’Igupto, ndipo wakonza njira yotipulumutsira ku ukapolo wa uchimo ndi imfa—nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. (Yohane 3:16) Paulo akuti: “Mulungu anatsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Kakonzedwe kachikondi kameneka kamasonkhezera a mitima yoongoka kudzipatulira iwo eni kwa Yehova kudzera mwa Yesu Kristu. “Pakuti chikondi cha Kristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa; ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.”—2 Akorinto 5:14, 15; Aroma 8:35-39.
14. Kodi chidziŵitso chokha cha zochita za Yehova chili chokwanira kutisonkhezera kupatulira miyoyo yathu kwa iye? Fotokozani.
14 Chikhalirechobe, kukhala ndi chidziŵitso cha umunthu wa Yehova ndi zochita zake ndi mtundu wa anthu sikuli kokwanira. Kuyamikira Yehova kwaumwini kuyenera kukulitsidwa. Kodi zimenezo zingachitidwe motani? Mwa kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu m’miyoyo yathu ndi kudzionera tokha kuti malamulo opezekamo amagwiradi ntchito. (Yesaya 48:17) Tiyenera kumva kuti Yehova watipulumutsa ku mavuto a dziko loipa ili lolamuliridwa ndi Satana. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 6:11.) M’nkhondo yathu ya kuchita chimene chili chabwino, timaphunzira kudalira Yehova, ndipo timadzionera tokha kuti Yehova ali Mulungu wamoyo, “Wakumva pemphero.” (Salmo 62:8; 65:2) Posapita nthaŵi timamva kukhala oyandikana naye kwambiri ndipo timakhala okhoza kumuululira zakukhosi kwathu. Chikondi chachikulu kaamba ka Yehova chimakula mwa ife. Mosakayikira chimenechi chidzatitsogolera ku kupatulira miyoyo yathu kwa iye.
15. Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera mwamuna wina, amene kale anali wodzipatulira ku ntchito, kutumikira Yehova?
15 Ambiri afikira pa kudziŵa Mulungu wachikondi ameneyu, Yehova, ndipo apatulira moyo wawo kwa iye kumtumikira. Mwachitsanzo, talingalirani za wokonza magetsi wina amene anali ndi bizinesi yachipambano. Nthaŵi zina anali kuyamba ntchito mmaŵa ndi kugwira ntchitoyo tsiku lonse mpaka usiku, akumafika panyumba ndi 5 koloko mmaŵa tsiku lotsatira. Atapuma pafupifupi ola limodzi, ankapita kukagwira ntchito yotsatira. “Ndinali wodzipatulira ku ntchito yanga,” iye anakumbukira. Pamene mkazi wake anayamba kuphunzira Baibulo, anagwirizana naye. Iye akuti: “Milungu yonse imene ndinali kudziŵa panthaŵiyo inali kungoyembekezera kutumikiridwa, yosachita kalikonse kutithandiza. Koma Yehova anayamba kuchitapo kanthu natumiza Mwana wake wobadwa yekha pa dziko lapansi mwa kudzimana kwakukulu.” (1 Yohane 4:10, 19) M’miyezi khumi, mwamuna ameneyu anadzipatulira kwa Yehova. Pambuyo pake, anasumika maganizo ake pa kutumikira Mulungu wamoyo. Anayamba utumiki wanthaŵi yonse nasamuka kukatumikira kumene kusoŵa kunali kokulira. Iye, mofanana ndi atumwi, ‘anasiya zonse ndi kutsata Yesu.’ (Mateyu 19:27) Pambuyo pa miyezi iŵiri, iye ndi mkazi wake anaitanidwa kukatumikira panthambi ya Watch Tower Bible and Tract Society m’dziko limene anali kukhalamo, kuti akathandize pantchito ya magetsi. Kwa zaka zoposa 20 wakhala akugwira ntchito panthambi, akumachita ntchito imene amakonda—osati kaamba ka iye mwini koma kaamba ka Yehova.
Sonyezani Poyera Kudzipatulira Kwanu
16. Kodi ndi zinthu ziti zimene munthu ayenera kuchita podzipatulira kwa Yehova?
16 Pambuyo pophunzira Baibulo kwa nthaŵi yakutiyakuti, achichepere ndi achikulire omwe moyamikira amazindikira Yehova ndi zimene wawachitira. Zimenezi ziyenera kuwasonkhezera kudzipereka iwo eni kwa Mulungu. Inu mwina mungakhale mmodzi wa ameneŵa. Kodi mungadzipatulire motani kwa Yehova? Mutapeza chidziŵitso cholongosoka m’Baibulo, muyenera kuchita mogwirizana ndi chidziŵitsocho ndi kusonyeza chikhulupiriro mwa Yehova ndi Yesu Kristu. (Yohane 17:3) Lapani ndi kutembenuka pa njira iliyonse yakale yauchimo. (Machitidwe 3:19) Ndiyeno mudzafika pa kudzipatulira, mukumakutchula m’mawu olingaliridwa bwino m’pemphero kwa Yehova. Mosakayikira pemphero limenelo lidzakhomerezeka kwachikhalire m’maganizo mwanu, pakuti lidzakhala chiyambi cha unansi watsopano ndi Yehova.
17. (a) Kodi nchifukwa ninji akulu amapenda mafunso okonzedwa limodzi ndi odzipatulira atsopano? (b) Kodi nchinthu chofunika chiti chimene chiyenera kuchitidwa munthu atangodzipatulira, ndipo nchifukwa ninji?
17 Monga momwedi Mose anafotokozerera kwa Aisrayeli zofunika zoloŵera muunansi wa pangano ndi Yehova, akulu mumipingo ya Mboni za Yehova amathandiza awo amene adzipatulira posachedwapa kupenda zimene iko kwenikweni kumatanthauza. Amagwiritsira ntchito mafunso okonzedwa kutsimikizira kuti aliyense akumvetsetsa bwino lomwe ziphunzitso za maziko za Baibulo ndipo akuzindikira zimene kukhala Mboni ya Yehova kumatanthauza. Ndiyeno, mwambo wosonyezera poyera kudzipatulirako ngwoyenera ndithu. Mwachibadwa, munthu wodzipatulira chatsopano amafunitsitsa kudziŵitsa ena kuti waloŵa muunansi wapadera umenewu ndi Yehova. (Yerekezerani ndi Yeremiya 9:24.) Zimenezi zimachitidwa moyenerera mwa ubatizo wa m’madzi kusonyeza kudzipatulirako. Kumizidwa m’madzi ndiyeno kuvuulidwa kumaphiphiritsira kuti iye wafa ku moyo wakale wofuna za iye yekha ndipo waukitsidwira ku moyo watsopano, wa kuchita chifuniro cha Mulungu. Si sakaramenti, kapenanso dzoma longa la Chishinto la misogi limene munthu amanenedwa kuti wayeretsedwa ndi madzi.a M’malo mwake, ubatizo ndi chilengezo chapoyera cha kudzipatulira kumene kwachitidwa kale m’pemphero.
18. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti kudzipatulira kwathu sikudzakhala kosaphula kanthu?
18 Nthaŵi yolemekezeka imeneyi ili chochitika chosaiŵalika, ikumakumbutsa mtumiki watsopano wa Mulungu za unansi wachikhalire umene ali nawo tsopano ndi Yehova. Mosiyana ndi kudzipatulira kumene woyendetsa ndege wa kamikaze anachita ku dziko lake ndi mfumu, kudzipatulira kumeneku kwa Yehova sikudzakhala kosaphula kanthu, pakuti iye ndi Mulungu wamphamvuyonse wamuyaya amene amachita zonse zimene anena kuti adzachita. Iye yekhayo ndiye amene ayenerera kudzipereka kwathu kwa mtima wonse.—Yesaya 55:9-11.
19. Kodi chimene chidzapendedwa m’nkhani yotsatira nchiyani?
19 Komabe, kudzipatulira kumaphatikizapo zambiri. Mwachitsanzo, kodi kudzipatulira kumayambukira motani moyo wathu wa tsiku ndi tsiku? Zimenezi zidzapendedwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Mankind’s Search for God, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 194-5.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji kudzipatulira kochitika kudziko kwakhala kogwiritsa mwala?
◻ Kodi chimene chinasonkhezera Aisrayeli kudzipatulira kwa Yehova nchiyani?
◻ Kodi chimene chimatisonkhezera kudzipatulira kwa Yehova lerolino nchiyani?
◻ Kodi timadzipatulira motani kwa Mulungu?
◻ Kodi tanthauzo la ubatizo wa m’madzi nchiyani?
[Chithunzi patsamba 10]
Israyeli pa Sinai anadzipatulira kwa Yehova