Mapindu a Kuwopa Mulungu Woona
“Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”—YESAYA 48:17.
1. Kodi ndi masoka otani amene akanapeŵedwa ndi mantha aumulungu?
NGATI Adamu akanakulitsa mantha aumulungu, akanamletsa kuchimwa kumene kunamtsogolera ku imfa yake yamuyaya ndi zaka zikwi zambiri za chisoni kwa mbadwa zake. Ngati mtundu wa Israyeli wakale ukanalabadira uphungu wa Yehova wa kumuwopa ndi kumkonda, mtundu umenewo sukanatengeredwa ku ukapolo wa ku Babulo, ndiponso sukanakana Mwana wa Mulungu ndi kukhala ndi liwongo la kukhetsa mwazi wake. Ngati lerolino dziko likanawopa Mulungu, sipakanakhala kuipa m’maboma kapena m’zamalonda, sipakanakhalanso upandu, ndi nkhondo.—Miyambo 3:7.
2. Mosasamala kanthu za mikhalidwe yotizinga ya m’dziko, kodi nchifukwa ninji tiyenera kukulitsa kuwopa Yehova?
2 Komabe, mosasamala kanthu za zimene dziko lotizinga limachita, ife aliyense payekha, monga mabanja, ndipo monga mipingo ya atumiki a Yehova tingapindule mwa kukulitsa mantha a Mulungu woona. Zimenezi nzogwirizana ndi chikumbutso chimene Mose anapereka ku mtundu wa Israyeli: “Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziwopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kusunga malamulo a Yehova, . . . kuti kukukomereni inu?” (Deuteronomo 10:12, 13) Kodi ndi mapindu ena otani amene amadza kwa ife pamene tiwopa Yehova, Mulungu woona?
Nzeru—Yofunika Kuposa Golidi
3. (a) Kodi ndi phindu loyamba liti limene tingalandire? (b) Kodi tanthauzo la Salmo 111:10 ndi lotani?
3 Phindu loyamba ndilo nzeru yeniyeni. Salmo 111:10 limalengeza: “Kumuwopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.” Kodi zimenezo zimatanthauzanji? Nzeru ndiyo luntha la kugwiritsira ntchito bwino chidziŵitso kuthetsera mavuto, kuletsa ngozi, ndi kupeza zonulirapo zakutizakuti. Imaloŵetsamo kuweruza kolama. Chiyambi chake, mbali yoyamba, maziko a nzeru imeneyo, ndiwo kuwopa Yehova. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chilengedwe chonse chili ntchito ya manja ake. Chimadalira pa iye. Anapatsa mtundu wa anthu ufulu wa kudzisankhira komano osati kukhoza kwa kulongosola mapazi awo bwino popanda chitsogozo chake. (Yoswa 24:15; Yeremiya 10:23) Tingakhale ndi chipambano kokha ngati tingazindikire mfundo zazikulu zimenezo zonena za moyo ndi kukhala ndi moyo mogwirizana nazo. Ngati kudziŵa kwathu Yehova kutipatsa chikhutiro chosagwedezeka chakuti chifuniro cha Mulungu chidzapambanadi ndi kuti lonjezo lake ndi kukhoza kwake kufupa kukhulupirika nzotsimikizirika, pamenepo mantha aumulungu adzatisonkhezera kuchitapo kanthu mwanzeru.—Miyambo 3:21-26; Ahebri 11:6.
4, 5. (a) Kodi nchifukwa ninji maphunziro a ku yunivesite a mnyamata wina sanampatse nzeru? (b) Kodi mnyamata ameneyu ndi mkazi wake anapeza motani nzeru yeniyeni pambuyo pake, ndipo zimenezi zinasintha miyoyo yawo m’njira yotani?
4 Talingalirani chitsanzo ichi. Zaka makumi angapo zapitazo, mnyamata wina anali pa University of Saskatchewan, ku Canada. Maphunziro ake anaphatikizapo biology, ndipo anaphunzitsidwa chisinthiko. Atamaliza maphunziro, anasankha kukhala katswiri wa atomic physics, akumapatsidwa ndalama zopitirizira maphunziro ake ku University of Toronto. Pamene anali kuphunzira, anaona umboni wodabwitsa wa dongosolo ndi kulinganizika kwa mipangidwe ya maatomu. Koma palibe mayankho amene anaperekedwa pa mafunso akuti: Kodi ndani amene analinganiza zonsezi? Liti? Ndipo chifukwa ninji? Popanda mayankho ake, kodi akanakhoza kugwiritsira ntchito mwanzeru chidziŵitso chake m’dziko limene panthaŵiyo linali pankhondo? Kodi nchiyani chimene chikanamtsogolera? Utundu? Chikhumbo cha mphotho za zinthu zakuthupi? Kodi iye analidi atapeza nzeru yeniyeni?
5 Pasanapite nthaŵi yaitali pambuyo pa kumaliza maphunziro ake, mnyamatayo ndi mkazi wake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. M’Mawu a Mulungu mwini, iwo anayamba kupeza mayankho amene anali kuwasoŵa kalelo. Anafikira pa kudziŵa Mlengi, Yehova Mulungu. Pamene anaphunzira za Mose pa Nyanja Yofiira ndi za Danieli ndi mabwenzi ake ku Babulo, anadziŵa za kufunika kwa kuwopa Mulungu osati anthu. (Eksodo 14:10-31; Danieli 3:8-30) Mantha aumulungu otero limodzi ndi chikondi chenicheni cha pa Yehova zinayamba kuwasonkhezera. Posapita nthaŵi njira yonse ya miyoyo yawo inasintha. Mnyamatayo anadziŵa Uyo amene ntchito ya manja ake anaiphunzira mu biology. Anayamba kumvetsetsa chifuno cha Uyo amene nzeru yake anaiona ikusonyezedwa m’kuphunzira kwake physics. M’malo mwa kugwiritsira ntchito chidziŵitso chake kupangira zida zimene zikanawononga anthu anzake, iye ndiponso mkazi wake anafuna kuthandiza ena kukonda Mulungu ndi kukonda mnansi wawo. Analembetsa utumiki wanthaŵi yonse monga olengeza Ufumu wa Mulungu. Pambuyo pake, analoŵa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ndipo anatumizidwa monga amishonale.
6. Ngati tili ndi nzeru yozikidwa pa kuwopa Yehova, kodi ndi zonulirapo zosapita patali zotani zimene tidzapeŵa, ndipo m’malo mwake tidzakhala tikuchitanji?
6 Ndithudi, si aliyense amene angakhale mmishonale. Koma tonsefe tingakhale ndi nzeru imene ili yozikidwa pa kuwopa Yehova. Ngati tikulitsa nzeru imeneyo, sitidzakhala otanganitsidwa ndi kuloŵetsa m’malingaliro athu nthanthi za anthu amene kwenikweni amangolota ponena za tanthauzo la moyo. Tidzachita khama kuphunzira Baibulo, louziridwa ndi Chitsime cha moyo, Yehova Mulungu, uyo amene angatipatse moyo wosatha. (Salmo 36:9; Akolose 2:8) M’malo mwa kukhala akapolo a dongosolo la malonda limene lili kudzandira kupita kuchiwonongeko, tidzalabadira uphungu wa Yehova wa kukhala okhutira ndi chakudya ndi zofunda, pamene tikuchititsa unansi wathu ndi Mulungu kukhala chinthu choyamba m’moyo. (1 Timoteo 6:8-12) M’malo mwa kuchita zinthu monga ngati kuti mtsogolo mwathu mukudalira pa kukhala wopeza bwino m’dzikoli, tidzakhulupirira Mawu a Yehova pamene amatiuza kuti dziko lipita ndi chilakolako chake, koma iye wakuchita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.—1 Yohane 2:17.
7. (a) Kodi Miyambo 16:16 imatithandiza motani kukhala ndi lingaliro loyenera la zinthu zofunika? (b) Kodi ndi mfupo zotani zimene zimadza chifukwa cha kupanga chifuniro cha Mulungu kukhala chinthu chachikulu m’miyoyo yathu?
7 Miyambo 16:16 imatilimbikitsa mwa kunena moonadi: “Kodi kulandira nzeru [nzeru imene imayamba ndi kuwopa Yehova] sikupambana ndi golidi, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?” Nzeru yotero ndi luntha zidzatisonkhezera kupanga chifuniro cha Mulungu kukhala chinthu chachikulu m’miyoyo yathu. Ndipo kodi ndi ntchito yotani imene Mulungu waiikizira Mboni zake m’nyengo ino ya mbiri ya munthu? Kulalikira za Ufumu wake ndi kuthandiza anthu oona mtima kukhala ophunzira enieni a Yesu Kristu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Imeneyi ndiyo ntchito imene imadzetsa mfupo zambiri za chikhutiro choona ndi chimwemwe chochuluka. Pamenepo, limodzi ndi chifukwa chabwino, Baibulo limati: “Wodala ndi wopeza nzeru.”—Miyambo 3:13.
Chitetezo pa Cholakwa
8. (a) Tchulani phindu lachiŵiri limene limadza chifukwa cha kuwopa Mulungu. (b) Kodi ndi zoipa zotani zimene timatetezeredwako? (c) Kodi ndimotani mmene mantha aumulungu amakhalira nyonga yamphamvu yosonkhezera?
8 Phindu lachiŵiri la kuwopa Mulungu nlakuti timatetezeredwa pa kuchita choipa. Awo amene amalemekeza kwambiri Mulungu samadzisankhira chabwino ndi choipa. Samaona zimene Mulungu amanena kuti nzabwino kukhala zoipa, ndiponso samalingalira zinthu zimene Mulungu amati nzoipa kukhala zabwino. (Salmo 37:1, 27; Yesaya 5:20, 21) Ndiponso, munthu amene amasonkhezeredwa ndi mantha aumulungu samangolekezera pa kudziŵa zimene Yehova amanena kuti nzabwino ndi zimene amanena kuti nzoipa. Munthu wotero amakonda zimene Yehova amakonda ndi kuda zimene Yehova amada. Chotero, amachita mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Chifukwa chake, monga momwe kwanenedwera pa Miyambo 16:6, “apatuka pa zoipa powopa Yehova.” Mantha aumulungu otero amakhala mphamvu yaikulu yosonkhezera kuchita zinthu zimene mwina mwake munthu sangathe kuchita mwa nyonga yake.
9. Kodi ndimotani mmene chikhumbo champhamvu cha kusafuna kukhumudwitsa Mulungu chinasonkezerera chosankha cha mkazi wina ku Mexico, ndipo ndi chotulukapo chotani?
9 Ngakhale ngati mantha aumulungu akungoyamba kumene kukula mwa munthu, angamlimbikitse kupeŵa kuchita kanthu kena kamene angachite nako chisoni m’moyo wake wonse. Mwachitsanzo, mkazi wina wokhala ndi pakati ku Mexico anafunsa mmodzi wa Mboni za Yehova ponena za kuchotsa mimba. Mboniyo inaŵerengera mkaziyo malemba angapo ninena kuti: “Kwa Mlengi, moyo ngwofunika kwambiri, ngakhale moyo wa awo amene sanabadwebe.” (Eksodo 21:22, 23; Salmo 139:13-16) Kupima kwa kuchipatala kunasonyeza kuti mwina mwanayo angakhale wopunduka. Koma tsopano, atasonkhezeredwa ndi zimene anaona m’Mawu a Mulungu, mkaziyo anasankha kubala mwana wake. Dokotala wake anakana kudzamuonanso, ndipo mwamuna wake anamuwopseza kumsiya, koma iye anachirimika. M’kupita kwa nthaŵi, anabala mwana wamkazi—wabwinobwino, wanthanzi, ndi wokongola. Posonkhezeredwa ndi chiyamikiro, mkaziyo anafunafuna Mboni, ndipo zinayamba kuphunzira naye Mawu a Mulungu. M’chaka chimodzi iyeyo ndi mwamuna wake anabatizidwa. Pambuyo pa zaka zingapo, pamsonkhano wachigawo, iwo anali okondwa kukumananso ndi Mboni yoyamba ija ndi kuisonyeza mwana wawo wamkazi wokongolayo wa zaka zinayi. Ulemu woyenerera kwa Mulungu ndi chikhumbo champhamvu cha kusafuna kumkhumudwitsa zimayambukiradi mwamphamvu moyo wa munthu.
10. Kodi mantha aumulungu angalimbitse anthu kuwonjoka m’zolakwa zotani?
10 Mantha aumulungu amatilimbitsa pa kupeŵa zoipa zambiri. (2 Akorinto 7:1) Pamene akulitsidwa moyenera, angathandize munthu kuleka kuchita machimo amseri, ongodziŵika kwa iye mwini ndi Yehova. Angamthandize kuwonjoka muukapolo wa kumwetsa zakumwa zaukali ndi wa anamgoneka. Yemwe kale anali womwerekera ndi anamgoneka ku South Africa akufotokoza kuti: “Pamene ndinkaloŵetsa chidziŵitso cha Mulungu, ndinakulitsanso kuwopa kumkhumudwitsa kapena kumkwiyitsa. Ndinadziŵa kuti iye anali kundiona, ndipo ndinali ndi chikhumbo cha kukhala wovomerezeka pamaso pake. Chinandisonkhezera kuwononga anamgoneka amene ndinali nawo mwa kuwagujumulira m’chimbudzi.” Mantha aumulungu athandiza zikwi zambiri mofananamo.—Miyambo 5:21; 15:3.
Chinjirizo pa Kuwopa Anthu
11. Kodi kuwopa Yehova kwabwino kungatitetezere pa msampha wodziŵika wotani?
11 Kuwopa Mulungu kwabwino kumatitetezeranso pa kuwopa munthu. Anthu ochuluka amavutika ndi kuwopa munthu kwambiri kapena pang’ono. Ngakhale atumwi a Yesu Kristu anamsiya ndi kuthaŵa pamene iye anagwidwa ndi asilikali m’munda wa Getsemane. Pambuyo pake, m’bwalo la nyumba ya mkulu wansembe, atazunguzika ndipo atagwidwa ndi mantha, Petro anakana zonena kuti anali mmodzi wa ophunzira a Yesu ndi kuti iye sanamdziŵe nkomwe. (Marko 14:48-50, 66-72; Yohane 18:15-27) Koma atumwiyo anathandizidwa kupezanso nyonga yauzimu. Ndiponso, m’masiku a Mfumu Yehoyakimu, Uriya mwana wa Semaya anagwidwa ndi mantha aakulu kwakuti analeka utumiki wake monga mneneri wa Yehova nathaŵa m’dzikolo, nkudzagwidwa pambuyo pake ndi kuphedwa.—Yeremiya 26:20-23.
12. (a) Kodi ndi chitetezero chotani chimene Miyambo 29:25 imasonyeza pa kuwopa munthu? (b) Kodi kukhulupirira Mulungu kumakulitsidwa motani?
12 Kodi nchiyani chimene chingathandize munthu kugonjetsa kuwopa munthu? Itachenjeza kuti “kuwopa anthu kutchera msampha,” Miyambo 29:25 imawonjezera kuti: “Wokhulupirira Yehova adzapulumuka.” Kukhulupirira Yehova ndiko mfungulo. Kukhulupirira kotero kwazikidwa pa chidziŵitso ndi zokumana nazo. Mwa kuphunzira Mawu ake, timaona umboni wa kulondola kwa njira za Yehova. Timafikira pa kudziŵa zochitika zosonyeza kudalirika kwake, kutsimikizirika kwa malonjezo ake (kuphatikizapo aja a chiukiriro), chikondi chake ndi mphamvu yake yaikulu koposa. Ndiyeno pamene tichitapo kanthu mogwirizana ndi chidziŵitso chimenecho, kuchita zinthu zimene Yehova amalamula ndi kukana mwamphamvu zimene amatsutsa, timayamba kudzionera tokha chisamaliro chachikondi ndi kudalirika kwake. Timadzionera tokha umboni wakuti mphamvu yake imagwira ntchito kukwaniritsa chifuniro chake. Chidaliro chathu mwa iye chimakula limodzinso ndi chikondi chathu pa iye ndi chikhumbo chathu chachikulu cha kupeŵa kusamkondweretsa. Chikhulupiriro chotero chimamangidwa pamaziko olimba. Chimakhala ngati linga loletsa kuwopa munthu.
13. Kodi ndimotani mmene mantha aumulungu angatithandizire kuntchito, panyumba, ndi kusukulu?
13 Kukhulupirira kwathu Yehova, limodzi ndi mantha aumulungu, kudzatilimbitsa kuchita chabwino ngati wotilemba ntchito atiwopseza kutichotsa ntchito chifukwa cha kukana kukhala ndi phande m’machitidwe osaona mtima m’malonda. (Yerekezerani ndi Mika 6:11, 12.) Mantha aumulungu otero amatheketsa zikwi zambiri za Akristu kupitirizabe kulambira koona poyang’anizana ndi chitsutso chochokera ku ziŵalo za m’banja. Amapatsanso kulimba mtima kwa achichepere amene amapita kusukulu kuti adzidziŵikitse monga Mboni za Yehova, ndipo amawalimbitsa kuti alimbane ndi chitonzo cha anzawo a m’kalasi amene amapeputsa miyezo ya Baibulo. Motero, Mboni ina yachichepere inati: “Zimene amaganiza zilibe kanthu. Zimene Yehova amaganiza nzimene zili zofunika.”
14. Kodi atumiki a Yehova amakhoza bwanji kulaka ngakhale pamene miyoyo yawo iwopsezedwa?
14 Kutsimikiza mtima kumodzimodziko kumalimbitsa Akristu oona kuumirira mwamphamvu pa njira za Yehova ngakhale pamene miyoyo yawo iwopsezedwa. Amadziŵa kuti ayenera kuyembekezera chizunzo kudziko. Amazindikira kuti atumwi anakwapulidwa ndi kuti Yesu Kristu mwiniyo anamenyedwa ndi kuphedwa ndi anthu oipa. (Marko 14:65; 15:15-39; Machitidwe 5:40; yerekezerani ndi Danieli 3:16-18.) Koma atumiki a Yehova ali ndi chidaliro chachikulu chakuti iye angawalimbitse kuti apirire; kuti limodzi ndi thandizo la Mulungu angalakike; kuti mosalephera Yehova adzafupa awo amene ali okhulupirika—ngati kuli kofunikira ngakhale mwa kuwaukitsira ku moyo m’dziko latsopano. Chikondi chawo pa Mulungu limodzi ndi mantha aumulungu zimawasonkhezera mwamphamvu kupeŵa kuchita kanthu kalikonse kamene kangamkhumudwitse.
15. Kodi nchiyani chimene chinakhozetsa Mboni za Yehova kusunga umphumphu wawo m’misasa yachibalo ya Nazi?
15 Chisonkhezero chimenechi chinakhozetsa Mboni za Yehova kupirira nkhanza zowopsa za m’misasa yachibalo ya Nazi mkati mwa ma 1930 ndi ma 1940. Zinalabadira uphungu wa Yesu wopezeka pa Luka 12:4, 5: “Ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musawope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita. Koma ndidzakulangizani amene muzimuwopa; tawopani iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndi inu opani ameneyo.” Motero, Gustav Auschner, Mboni imene inali mumsasa wachibalo wa Sachsenhausen, pambuyo pake analemba kuti: ‘A SS anawombera August Dickmann ndipo anawopseza kuwombera otsalafe ngati tikakana kusayina chikalata chokana chikhulupiriro chathu. Palibe aliyense wa ife amene anasayina. Tinawopa kwambiri kukhumudwitsa Yehova kuposa kuwopa zipololo zawo.’ Kuwopa munthu kumachititsa kulolera molakwa, koma kuwopa Mulungu kumalimbitsa munthu kuchita chimene chili chabwino.
Kupulumutsa Moyo
16. Kodi nchiyani chimene chinakhozetsa Nowa kutsatira njira yoyenera zaka ndi zaka kufikira pa Chigumula, ndipo kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo kwa iye ndi banja lake?
16 Nowa anakhala ndi moyo m’masiku otsiriza a dziko lokhalako chigumula chisanadze. Yehova anasankha kuwononga dziko loipa la nthaŵiyo chifukwa cha kuipa kwa anthu. Komabe, izi zili choncho, Nowa anali kukhala m’dziko limenelo limene linali lodzazidwa ndi chiwawa, chisembwere choipitsitsa, ndi mphwayi kulinga ku chifuniro cha Mulungu. Mosasamala kanthu za kulalikira chilungamo kwa Nowa, “iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” (Mateyu 24:39) Komabe Nowa sanalefulidwe pa ntchito imene Mulungu anampatsa. “Monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Genesis 6:22) Kodi nchiyani chimene chinakhozetsa Nowa kuumirira pa njirayo chaka ndi chaka kufikira pa Chigumula? Ahebri 11:7 akuyankha: “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, [anasonyeza mantha aumulungu, NW].” Chifukwa chake, iye ndi mkazi wake ndi ana ake ndi akazi awo anapulumuka Chigumula.
17. (a) Mosasamala kanthu za zimene anthu ena amachita, kodi ife tiyenera kuchitanji? (b) Kodi nchifukwa ninji awo amene amawopa Yehova alidi anthu achimwemwe?
17 Ife tikukhala m’nyengo yofanana ndi ya m’tsiku la Nowa m’mbali zambiri. (Luka 17:26, 27) Chenjezo likuperekedwanso. Chivumbulutso 14:6, 7 chimasimba za mngelo wouluka pakati pa mlengalenga amene akulimbikitsa anthu a mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ‘kuwopa Mulungu, ndi kumpatsa ulemerero.’ Mosasamala kanthu za zimene zikuchitidwa ndi dziko lokuzingani, labadirani mawu amenewo, ndiyeno perekani pempholo kwa ena. Monga Nowa, chitanipo kanthu ndi chikhulupiriro ndi kusonyeza mantha aumulungu. Kuchita kwanu motero kungakutsogolereni kukupulumutsa moyo wanu ndi miyoyo ya enanso ambiri. Pamene tisinkhasinkha mapindu olandiridwa ndi awo amene amawopa Mulungu woona, tingagwirizanedi ndi wamasalmo wouziridwa amene anaimba kuti: “Wodala munthu wakuwopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.”—Salmo 112:1.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndi mapindu ena apadera ati amene amadza chifukwa cha kuwopa Mulungu woona?
◻ Kodi nzeru imene ili yozikidwa pa mantha aumulungu ingatitetezere motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji mantha aumulungu amatisonkhezera kupeŵa choipa?
◻ Kodi ndimotani mmene mantha aumulungu amatitetezerera pa kuwopa munthu?
◻ Kodi nchiyambukiro chotani chimene mantha aumulungu ali nacho pa ziyembekezo zathu za moyo za mtsogolo?
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
“Wodala munthu wakuwopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.”—Salmo 112:1