Kodi Mudzatamanda Yehova?
“MONGA dzina lanu, Mulungu, momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi.” Aŵa ndi mawu a m’nyimbo yaulosi ya ana a Kora. (Salmo 48:10) Lerolino, mang’ombe aakulu operekedwa ndi mamiliyoni a Mboni za Yehova akutamanda Mulungu ndi kudziŵitsa dzina lake mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wake. Mwa kuchita chimenechi m’maiko 232 ndi zisumbu za m’nyanja ndi m’zinenero zoposa 300, iwo akufika “ku malekezero a dziko lapansi” m’lingaliro lenileni.
Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera anthu osiyanasiyana m’miyambo, makhalidwe, zinenero ndi makulidwe kuti atamande Yehova? Chiyamikiro chawo cha chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu, Baibulo, ndicho chifukwa chachikulu. Choonadi chauzimu chawamasula ku malaulo ndi zikhulupiriro za chipembedzo zoika munthu muukapolo zonga chizunzo chosatha. (Yohane 8:32) Choonadi chimawathandizanso kuzindikira mikhalidwe ya Mulungu yabwino koposa, yonga chikondi chake, mphamvu, nzeru, ndi chilungamo cholinganizidwa bwino ndi chifundo. Kuzindikira za kupereka kwa Mulungu Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu, monga nsembe ya dipo kaamba ka mtundu wa anthu kumasonkhezera anthu owongoka mtima kutamanda Yehova ndi kumtumikira.
Malinga ndi kunena kwa buku la Baibulo la Chivumbulutso, mang’ombe akumwamba amalengeza kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) Chitamando choterocho sichichititsidwa ndi lingaliro chabe la kuchita zimenezo. M’malo mwake, limachititsidwa ndi ulemu kwa Yehova.
Tamandani Mulungu mwa Kulengeza Uthenga Wabwino
Potamanda Yehova, munthu amakhala akutsanzira chitsanzo chopambana cha Yesu Kristu, wotamanda Mulungu wamkulu. Kulondola mapazi a Yesu kumaphatikizapo kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 4:17: 23; 24:14) Ntchito yolalikira imeneyi ya kutamanda Yehova yakhala yaikulu koposa padziko lonse.
Ntchito yolalikira imeneyi njofunika kwambiri kwakuti Baibulo limaigwirizanitsa moonekera bwino ndi chipulumutso. Aroma 10:13-15 amati: “Amene ali yense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”
Chaka chatha chokha, Mboni za Yehova zinathera maola oposa mamiliyoni chikwi chimodzi m’ntchito yolalikira. Ndipo kutamanda Mulungu kumeneku kunatulutsa zabwino zotani nanga! Pafupifupi 314,000 anagwirizana nawo pa kuimba mang’ombe a atamandi mwa kusonyeza kudzipatulira kwa Yehova ndi ubatizo wa m’madzi.
Komabe, kodi nchiyani chimene chinganenedwe za okwanira pafupifupi 12,288,917 amene anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu cha 1994? Pakati pawo panali oposa pa 7,000,000 amene sanayambebe kutamanda Yehova monga alaliki a uthenga wabwino. Koma kukhalapo kwawo pachochitika chofunika kwambiri chimenechi potsirizira pake kungawonjezere mamiliyoni ena pa mang’ombe a atamandi. Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuti tithandize okondwerera ameneŵa kukhala atamandi a Yehova?
Chithandizo Chimene Chilipo
Okondwerera ambiri angakhale ndi chikhumbo cha kutamanda Yehova koma namalingalira kuti sangafitse zofunika. Iwo angachite bwino kukumbukira mawu a wamasalmo akuti: “Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.” (Salmo 121:1, 2) Mwachionekere, wamasalmo anakweza maso ake ku mapiri a Yerusalemu kumene kunali kachisi wa Yehova ndi malikulu a boma lake la teokrase la pa dziko lapansi. Mwa zimenezi tinganene bwino lomwe kuti chithandizo chofunikira pa kutamanda Mulungu ndi kulengeza uthenga wa Ufumu chimachokera kokha kwa Yehova ndi gulu lake.—Salmo 3:4; Danieli 6:10.
Lerolino, awo amene akukhumba kutamanda Yehova angayembekezere chithandizo cha chikondi chochokera ku gulu lake la pa dziko lapansi. Mwachitsanzo, Mboni za Yehova zimapereka chithandizo mwa kuchititsa maphunziro a Baibulo aulere kwa anthu ofuna. Programu ya kuphunzitsa imeneyi imaphatikizapo zoposa chabe kuphunzira ziphunzitso za Baibulo. Imathandiza wophunzirayo kukulitsa chiyamikiro pa zimene akuphunzira ndi pa gulu limene Yehova akuligwiritsira ntchito.
Mogwirizana ndi zimenezi, Mboni imene imachititsa phunziro la Baibulo imayesayesa kutsimikizira kuti ziphunzitso za choonadi chopezedwa chatsopanocho zimafika ndi mumtima momwe, osati m’mutu chabe. Ndipo mphunzitsiyo sayenera kuzengereza kusonyeza wophunzirayo mmene Yehova akugwiritsirira ntchito gulu Lake kukwaniritsa chifuno Chake pa dziko lapansi. Brosha lakuti Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi ndi tepi ya vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name zakhaladi zothandiza pa kuchita zimenezi.
Misonkhano Yachikristu yachitanso mbali yaikulu pa kuthandiza oyembekezeredwa kukhala atamandi a Yehova. M’masiku oyambirira a phunziro la Baibulo, wophunzirayo angaitanidwe kufika pamisonkhano Yachikristu. M’kupita kwa nthaŵi, adzadziŵa kufunika kwa kufika nthaŵi zonse ndi kukhala ndi phande m’misonkhano yonse ya mpingo. (Ahebri 10:24, 25) Oyang’anira angapereke chithandizo cha mtengo wapatali kwa okhulupirira anzawo ndi oyembekezeredwa kukhala atamandi a Yehova mwa kukonza misonkhano imeneyi ili yomangirira mwauzimu ndi yopindulitsa.
Thandizani Ana Kutamanda Yehova
Ana ali pakati pa anthu ambiri amene ali othekera kukhala ofalitsa uthenga wabwino posachedwapa. Makamaka atate ndiwo amene ali ndi thayo la m’Baibulo la kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Pamene aphunzitsidwa bwino lomwe ndi makolo aumulungu, ngakhale ana aang’ono kwambiri angakulitse chikhumbo cha kutamanda Yehova.
Kamtsikana kena ku Argentina kanafikira akulu a mpingo mobwerezabwereza kwa miyezi ingapo, kakumapempha chithandizo chawo kuti kayeneretsedwe kukhala wofalitsa Ufumu. M’kupita kwa nthaŵi, makolo ake ndi akuluwo anavomereza kuti kakhale wofalitsa wosabatizidwa. Iko kanayamba kale kulalikira uthenga wa Ufumu mogwira mtima pamakomo. Ngakhale kuti kamtsikana kameneka kali ndi zaka zisanu zokha ndipo sikamadziŵa kuŵerenga, kanaloŵeza malo a malemba ena a Baibulo. Katapeza lemba, kamapempha mwininyumba kuliŵerenga, ndiyeno iko kamalifotokoza.
Nkwachionekere kuti akulu ndi makolo angachite zochuluka mwa kulimbikitsa ndi kuthandiza amene akupita patsogolo kuti akhale atamandi a Yehova.—Miyambo 3:27.
Unansi Wamuyaya ndi Yehova
Komabe, bwanji ngati kuti inu mwakhala mukuyanjana ndi Mboni za Yehova kwa nthaŵi yotalikirapo koma simunagwirizanebe nazo m’ntchito yawo yolalikira? Kungakhale kopindulitsa kudzifunsa mafunso aŵa, ‘Kodi ndimakhulupirira kuti ndapeza choonadi ndi kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona? Kodi ndili wokhutiritsidwa kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo mankhwala okha othetsera mavuto a anthu? Kodi ndasiya zipembedzo zonse zonyenga ndi miyambo ya dziko ndi kuleka kuchita zimene zimakwiyitsa Yehova? Kodi ndili nacho chikondi chozama kwa Mulungu ndi pa zofunika zake zolungama?’ (Salmo 97:10) Ngati mungayankhe moona mtima kuti inde pamafunso ameneŵa, kodi nchiyaninso chimene chikukuletsani kutamanda Yehova?—Yerekezerani ndi Machitidwe 8:36.
Kutamanda Yehova kumaloŵetsamo zoposa chabe kulalikira uthenga wabwino. Ngati mwapeza chidziŵitso cholongosoka, mwakhala ndi chikhulupiriro choona, ndipo mwagwirizanitsa moyo wanu ndi zofunika za Mulungu, mufunikira kulimbitsa unansi wanu ndi Mulungu. Motani? Mwa kudzipatulira kwa iye m’pemphero ndiyeno kukusonyeza mwa ubatizo wa m’madzi. Moyo wosatha uli pachiswe. Chifukwa chake, chitanipo kanthu tsopano lino pa uphungu wa Yesu wakuti: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”—Mateyu 7:13, 14.
Pokhala kuti dongosolo la zinthu lilipoli likufika kumapeto ake atsoka, ino sindiyo nthaŵi ya kuzengereza. Chitanipo kanthu mwamsanga pa kupalana ubwenzi wamuyaya ndi Yehova. Ndithudi, ino ndiyo nthaŵi ya kuyankha movomereza funso lakuti, Kodi mudzatamanda Yehova?