Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
“Wodala munthuyo . . . [amene] m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.”—SALMO 1:1, 2.
1. (a) Kodi ndi chikwangwani chachikulu chotani chimene chili kumbali ina ya fakitale pa malikulu a dziko lonse a Watch Tower Society? (b) Kodi tingapindule motani ngati ife enife tilabadira chilangizocho?
“ŴERENGANI MAWU A MULUNGU BAIBULO LOPATULIKA TSIKU NDI TSIKU.” Mawu amenewo m’zilembo zazikulu amaonekera kumbali ina ya nyumba ku Brooklyn, New York, kumene ma Baibulo ndi mabuku ophunzirira Baibulo amasindikizidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society. Chilangizo chimenecho sichili chabe cha anthu akudziko amene amaona chikwangwanicho. Mboni za Yehova zimazindikira kuti nazonso ziyenera kuchilabadira. Amene amaŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ndi kuligwiritsira ntchito mwaumwini amapindula ndi chiphunzitso, chitsutsano, ndi chilangizo cha m’chilungamo chimene limapereka.—2 Timoteo 3:16, 17.
2. Kodi Mbale Russell anagogomezera motani kufunika kwa kuŵerenga Baibulo?
2 Mboni za Yehova zimayamikira kwambiri zofalitsa zawo zothandiza kuphunzira Baibulo, kuphatikizapo Nsanja ya Olonda, ndipo zimagwiritsira ntchito zimenezi nthaŵi zonse. Koma zimadziŵa kuti palibe nchimodzi chomwe chimene chimatenga malo a Baibulo. Kalelo mu 1909, Charles Taze Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Bible and Tract Society, analembera oŵerenga magazini a Watch Tower kuti: “Musaiŵale kuti Baibulo ndilo Muyezo wathu ndi kuti mulimonse mmene zithandizo zathu zingakhalire zopatsidwa ndi Mulungu, zangokhala ‘zithandizo’ chabe osati zoloŵa malo a Baibulo.”
3. (a) Kodi “Mawu a Mulungu” ali ndi chisonkhezero chotani kwa owaŵerenga? (b) Kodi Abereya anali kuŵerenga ndi kuwaphunzira kangati Malemba?
3 Malemba ouziridwa ali ndi zakuya ndi mphamvu zimene sizimapezeka m’buku lina lililonse. “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Wophunzira Luka anayamikira kwambiri anthu a ku Bereya, akumawatcha “mfulu koposa.” Iwo sanangolandira mofunitsitsa mawu olalikidwa ndi mtumwi Paulo ndi bwenzi lake Sila komanso ‘anasanthula m’Malembo masiku onse,’ kuti adziŵe maziko a Malemba a zimene anaphunzitsidwa.—Machitidwe 17:11.
Kuliŵerenga Tsiku ndi Tsiku
4. Kodi nchiyani chimene Malemba amasonyeza ponena zakuti ndi kangati kamene tiyenera kuŵerenga Baibulo?
4 Baibulo silimanena mwachindunji kuti tiyenera kuliŵerenga kangati. Komabe, lili ndi uphungu wa Yehova kwa Yoswa wa ‘kulingirira m’buku la chilamulo usana ndi usiku’ kuti achite mwanzeru ndi kukhoza kuchita ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu. (Yoswa 1:8) Limatiuza kuti aliyense amene anachita ufumu pa Israyeli wakale anayenera kuŵerenga Malemba “masiku onse a moyo wake.” (Deuteronomo 17:19) Limawonjezeranso kuti: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa . . . Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” (Salmo 1:1, 2) Ndiponso, Uthenga Wabwino wolembedwa ndi Mateyu umatiuza kuti pamene Yesu Kristu anakana zoyesayesa za Satana za kumuyesa Iye, Iye anagwira mawu m’Malemba Achihebri ouziridwa, kuti: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Kodi timafunikira chakudya chakuthupi kangati? Masiku onse! Kudya chakudya chauzimu tsiku ndi tsiku nkofunika kwambiri chifukwa kumakhudza ziyembekezo zathu za moyo wamuyaya.—Deuteronomo 8:3; Yohane 17:3.
5. Kodi kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kungatithandize bwanji ‘kuyenda koyenera Yehova’ pamene tikumana ndi ziyeso za chikhulupiriro chathu?
5 Ife tonse tifunikira kulimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku. Masiku onse—panyumba, kuntchito, kusukulu, m’makwalala, pogula zinthu, mu utumiki wathu—timakumana ndi mavuto oyesa chikhulupiriro chathu. Kodi zimenezi tidzachita nazo bwanji? Kodi tidzakumbukira msanga malamulo ndi miyezo ya Baibulo? M’malo molimbikitsa mzimu wa kudzidalira, Baibulo limachenjeza: “Iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:12) Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kudzatithandiza ‘kuyenda koyenera Yehova kukamkondweretsa monsemo’ m’malo mwa kulola dzikoli kutikanikizira m’chikombole chake.—Akolose 1:9, 10; Aroma 12:2.
Kufunika kwa Kuŵerenga Baibulo Mobwerezabwereza
6. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kuŵerenga Baibulo mobwerezabwereza?
6 Kuŵerenga Baibulo ndi kosiyana kwambiri ndi kuŵerenga buku la nthano. Nthano zambiri zodziŵika zimalembedwa kuti ziŵerengedwe kamodzi; munthu atangodziŵa nkhaniyo ndi mapeto ake, samafunanso kuiŵerenga. Kusiyana ndi zimenezo, mosasamala kanthu za nthaŵi zambiri zimene taliŵerenga Baibulo, timapindula kwambiri mwa kuliŵerenganso. (Miyambo 9:9) Kwa munthu wozindikira, Malembawo nthaŵi zonse amakhala ndi tanthauzo latsopano. Iye amamvetsetsa kwambiri maulosi a masiku otsiriza chifukwa cha zimene waona, kumva, ndi kukumana nazo payekha m’miyezi yaposachedwapa. (Danieli 12:4) Pamene kudziŵa zinthu kwake m’moyo kukula ndipo alimbana ndi mavuto, woŵerenga Baibulo wozindikira amamvetsetsa kwambiri uphungu umene poyamba angakhale atangoŵerenga mwawamba. (Miyambo 4:18) Ngati wadwala kwambiri, malonjezo a Baibulo a kuchotsedwa kwa zopweteka ndi kubwezeretsedwa kwa thanzi labwino amakhala ndi tanthauzo lakuya kwambiri kwa iye kuposa ndi kale lonse. Pamene mabwenzi apamtima ndi a m’banja amwalira, lonjezo la chiukiriro limakhaladi lapadera kwambiri.
7. Kodi nchiyani chimene chingatithandize titakhala ndi mathayo atsopano m’moyo, ndipo chifukwa ninji?
7 Mungakhale mutaŵerenga Baibulo pa inu nokha ndi kugwiritsira ntchito uphungu wake kwa zaka zambiri. Koma tsopano mwinamwake mukukhala ndi mathayo atsopano m’moyo. Kodi mukuganiza za kukwatira? Kodi mudzakhala kholo? Kodi mwaikiziridwa thayo mumpingo la kukhala mkulu kapena mtumiki wotumikira? Kodi mwakhala mlaliki wanthaŵi yonse, wokhala ndi mipata yowonjezereka ya kulalikira ndi kuphunzitsa? Kungakhale kopindulitsa chotani nanga kuŵerenganso Baibulo lonse mukumaganiza za mathayo atsopano amenewo!—Aefeso 5:24, 25; 6:4; 2 Timoteo 4:1, 2.
8. Kodi kusintha kwa mikhalidwe kungasonyeze motani kufunika kwa kuphunzira zambiri ponena za zinthu zimene tinaganiza kuti tinali kuzidziŵa kale?
8 Kale mungakhale munali kuchita bwino kusonyeza zipatso za mzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Komabe kusintha kwa mikhalidwe kungafune kuti muphunzire zambiri ponena za mikhalidwe yaumulungu imeneyo. (Yerekezerani ndi Ahebri 5:8.) Amene anali woyang’anira woyendayenda yemwe anaona kufunikira kwa kuleka utumiki wake wapadera kuti akasamalire makolo ake okalamba anati: “Ndinkaganiza kuti ndinali kuchita bwino kwambiri pa kusonyeza zipatso za mzimu. Tsopano ndikumva ngati kuti ndikuyambiranso.” Momwemonso, amuna ndi akazi amene anzawo a muukwati akudwala kwambiri kapena ali opsinjika mtima angapeze kuti powasamalira mwa iwo eni, amagwiritsidwa mwala nthaŵi zina chifukwa cha kupanikizika, zimene zimawalefula. Kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kuli magwero a chitonthozo chachikulu ndi chithandizo.
Pamene Kuŵerenga Baibulo Kungachitidwe
9. (a) Kodi nchiyani chimene chingathandize munthu wotanganitsidwa kwambiri kupeza nthaŵi ya kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku? (b) Kodi nchifukwa ninji kuŵerenga Mawu a Mulungu kuli makamaka kofunika kwa akulu?
9 Ndithudi, kwa anthu amene ali kale otanganitsidwa kwambiri, kupeza nthaŵi yochita kanthu kena kowonjezera masiku onse nkovuta. Komabe, tingapindule ndi chitsanzo cha Yehova. Baibulo limavumbula kuti iye amachita zinthu ‘panthaŵi yoikidwiratu.’ (Genesis 21:2; Eksodo 9:5; Luka 21:24; Agalatiya 4:4) Kuzindikira kufunika kwake kwa kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse kungatithandize kuika nthaŵi yake pandandanda yathu ya tsiku ndi tsiku. (Aefeso 5:15-17) Makamaka akulu afunikira kupatula nthaŵi ya kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kuti uphungu umene amapereka ukhale wozikidwa kotheratu pa malamulo a Baibulo ndi kuti mzimu umene amasonyeza usonyeze “nzeru yochokera kumwamba.”—Yakobo 3:17; Tito 1:9.
10. Kodi ndi liti pamene aja amene amaŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku amapeza nthaŵi ya kuliŵerenga?
10 Ambiri amene amakhoza pa programu yawo ya kuŵerenga Baibulo amaliŵerenga mmamaŵa asanayambe zochita za tsikulo. Ena amapeza kuti akhoza bwino lomwe kuchita zimenezo nthaŵi zonse panthaŵi ina. Makaseti a Baibulo (kumene amapezeka) amathandiza apaulendo kugwiritsira ntchito bwino nthaŵi ya paulendo, ndipo Mboni zina zimawamvetsera pamene zikuchita ntchito ya masiku onse ya panyumba. Maprogramu amene agwira ntchito kwa Mboni zosiyanasiyana ku Ulaya, Afirika, North America, South America, ndi Kummaŵa asonyezedwa pamasamba 20 ndi 21, m’nkhani yakuti “Pamene Amaŵerenga ndi Mmene Amapindulira.”
11. Kodi kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kungachitidwe motani ngakhale ngati nthaŵi imene ilipo ili yocheperapo?
11 Chofunika koposa si kuchuluka kwa nthaŵi imene mumathera pa kuŵerenga Baibulo kwanu panthaŵi imodzi koma kuliŵerenga nthaŵi zonse. Mwina kungakhale kopindulitsa kwa inu kuliŵerenga kwa ola limodzi kapena kuposapo panthaŵi imodzi, mukumawonjezapo kufufuza ndiponso mukumamwerekera kwambiri ndi nkhaniyo. Koma kodi ndandanda yanu imakulolani kuchita zimenezo nthaŵi zonse? M’malo mwa kulola masiku kupita popanda kuŵerenga Baibulo konse, kodi sikungakhale kwabwino kwambiri kuliŵerenga kwa mphindi 15 kapena ngakhale 5 masiku onse? Tsimikizirani kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Ndiyeno wonjezani kufufuza kozama pa kuŵerengako ngati kuli kotheka.
Njira Zosiyanasiyana Zoŵerengera Baibulo
12. Kodi ndi programu yotani ya kuŵerenga Baibulo imene abanja la Beteli atsopano ndi ophunzira sukulu ya Gileadi ali nayo?
12 Pali njira zambiri zimene Baibulo lingaŵerengedwere. Kuli kopindulitsa kuliŵerenga kuyambira ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso. Abanja la Beteli onse padziko lonse amene akutumikira pa malikulu a dziko lonse kapena pa imodzi ya nthambi za Sosaite afunikira kuŵerenga Baibulo lonse m’chaka choyamba cha utumiki wawo wa pa Beteli. (Kaŵirikaŵiri zimenezo zimatanthauza kuŵerenga machaputala atatu kapena asanu, kudalira pa kutalika kwawo, kapena masamba anayi kapena asanu, patsiku.) Ophunzira Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ayeneranso kuŵerenga Baibulo lonse asanamalize maphunziro awo. Zimenezi ziyenera kuti zimawathandiza kuchititsa kuŵerenga Baibulo kukhala mbali ya moyo wawo.
13. Kodi ndi chonulirapo chotani chimene chili choyenera kwa Mboni zobatizidwa chatsopano?
13 Kuli kopindulitsa kwa Mboni zobatizidwa chatsopano kudziikira chonulirapo cha kuŵerenga Baibulo lonse. Mu 1975, panthaŵi imene mnyamata wina ku France anali kukonzekera ubatizo, mkulu wina anamfunsa ngati anali ndi programu yoikika ya kuŵerenga Baibulo. Chiyambire pamenepo, iye waŵerenga Baibulo lonse chaka ndi chaka, kaŵirikaŵiri akumaliŵerenga mmaŵa asanapite kuntchito. Ponena za zotulukapo zake, iye akuti: “Ndafikira pakumdziŵa bwino kwambiri Yehova. Nditha kuona mmene zonse zimene amachita zimakhudzira chifuno chake ndi mmene amachitira patabuka zopinga. Ndimaona kuti Yehova ali, ponse paŵiri, wolungama ndi wabwino m’zochita zake zonse.”
14. (a) Kuti munthu alinganize programu yopitiriza yaumwini ya kuŵerenga Baibulo, nchiyani chifunika? (b) Kodi nchiyani chimene chingatithandize kukumbukira chithunzi chonse cha buku lililonse la Baibulo pamene tikuliŵerenga?
14 Kodi inu mwaŵerenga Baibulo lonse? Ngati simunatero, ino ndiyo nthaŵi yabwino kuyamba. Linganizani programu yoikika, ndiyeno imamatireni. Sankhani ndi masamba angati kapena machaputala amene mudzaŵerenga tsiku ndi tsiku, kapena ingosankhani nthaŵi imene mudzatherapo ndi tsiku lake. Si onse amene akhoza kumaliza Baibulo m’chaka chimodzi, koma chofunika ndicho kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, kumachita zimenezo tsiku ndi tsiku ngati kuli kotheka. Poŵerenga Baibulo, mungapeze kuti kugwiritsira ntchito mabuku ena amaumboni kungakuthandizeni kukhomereza m’maganizo mwanu chithunzi chonse cha nkhaniyo. Ngati mumaŵerenga Chingelezi, musanayambe kuŵerenga bukulo la Baibulo, pendani mpambo waufupi wa mfundo zake zazikulu umene uli mu Insight.a Makamaka yang’anani pa mitu ya zilembo zazikulu pampambowo. Kapena mungagwiritsirenso ntchito mwa njira imodzimodziyo mawu achidule okhala ndi zambiri a m’buku la “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial.”b
15. (a) Kodi ndi malingaliro ati operekedwa pamasamba 16 ndi 17 amene angakuthandizeni kuwongolera kuŵerenga kwanu Baibulo? (b) M’malo mwa kungoŵerenga masamba akutiakuti mwa mwambo, kodi ndi mbali iti yofunika imene tiyenera kusamalira kwambiri?
15 Kuŵerenga Baibulo kotsatizana kuli kopindulitsa, koma musamangoliŵerenga mwa mwambo. Musaŵerenge masamba akutiakuti tsiku lililonse kokha kuti muzinena kuti mumaŵerenga Baibulo lonse chaka ndi chaka. Monga momwe bokosi lakuti “Malingaliro Owongolera Kuŵerenga Kwanu Baibulo” (pamasamba 16 ndi 17) likusonyezera, pali njira zambiri zimene mungaŵerengere Baibulo ndi kupindula nalo. Mosasamala kanthu za njira imene mumatsatira, tsimikizirani kuti mukudyetsa maganizo ndi mtima wanu womwe.
Pezani Lingaliro la Zimene Mukuŵerenga
16. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kupatula nthaŵi tikumasinkhasinkha zimene tikuŵerenga?
16 Pophunzitsa ophunzira ake, Yesu anagogomezera kufunika kwakuti iwo amvetsetse zimene iye ananena. Chimene chinali chofunika sindicho kungomva ndi nzeru zokha, koma kupeza “[lingaliro lake, NW] ndi mtima wawo” kotero kuti aligwiritsire ntchito m’moyo wawo. (Mateyu 13:14, 15, 19, 23) Mulungu amaŵerengera chimene munthu alidi mkati, ndipo nchimene mtima umaimira. (1 Samueli 16:7; Miyambo 4:23) Motero, kuwonjezera pa kuona kuti tikumvetsetsa zimene malemba a Baibulo akunena, tifunikira kuwasinkhasinkha, kulingalira mmene amakhudzira moyo wathu.—Salmo 48:9; 1 Timoteo 4:15.
17. Kodi ndi mfundo zina ziti zimene tingagwiritsire ntchito kusinkhasinkhira zimene tikuŵerenga m’Malemba?
17 Yesayesani kupeza mzimu wake wa nkhani za m’Baibulo kuti muugwiritsire ntchito m’mikhalidwe imene mumayang’anizana nayo. (Yerekezerani ndi Mateyu 9:13; 19:3-6.) Pamene mukuŵerenga ndi kusinkhasinkha za mikhalidwe ya Yehova yabwino koposa, gwiritsirani ntchito mwaŵi umenewo kulimbitsa unansi wanu ndi iye, kukulitsa mwa inu mwini mkhalidwe wolimba wa kudzipereka kwaumulungu. Pamene mukuŵerenga za mawu onena za chifuno cha Yehova, ganizani za zimene muyenera kuchita kuti mugwirizane nawo. Pamene mukuŵerenga za uphungu wolunjika, m’malo mwakungonena kuti, ‘Ndikudziŵa zimenezo,’ dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikuchita zimene ukunena?’ Ngati mukutero, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi njira ziti zimene ndingachitire zimenezo “mochuluka koposa”?’ (1 Atesalonika 4:1) Pamene mukuphunzira za zofuna za Mulungu, samalaninso zitsanzo zenizeni za m’Baibulo za aja amene anachita mogwirizana ndi zofuna zimenezo ndi aja amene sanatero. Ganizani za chifukwa chimene anachitira zimenezo ndi zimene zinatulukapo. (Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11) Pamene mukuŵerenga za moyo wa Yesu Kristu, kumbukirani kuti Yesu ndiye amene Yehova waika kuchita ufumu pa dziko lonse lapansi; gwiritsirani ntchito mwaŵi umenewo kulimbitsa chikhumbo chanu cha dziko latsopano la Mulungu. Ndiponso, lingalirani za njira zimene mungatsanzirire kwambiri Mwana wa Mulungu.—1 Petro 2:21.
18. Kodi tingalinganize motani kuŵerenga Baibulo ndi kugwiritsira ntchito kwathu zofalitsa zophunzirira zoperekedwa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?
18 Zoona, kuŵerenga Baibulo sikuyenera kuloŵa m’malo kugwiritsira ntchito kwanu zofalitsa zabwino koposa zophunzirira zimene zaperekedwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Nazonso zili mbali ya zogaŵira za Yehova—zamtengo wake. (Mateyu 24:45-47) Tsimikizirani kuti kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse kuli ndi malo oyamba m’moyo wanu. Ngati kuli kotheka, “ŴERENGANI MAWU A MULUNGU BAIBULO LOPATULIKA TSIKU NDI TSIKU.”
[Mawu a M’munsi]
a Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuŵerengako Baibulo masiku onse?
◻ Kodi nchifukwa ninji tifunikira kuŵerenga Baibulo mobwerezabwereza?
◻ Malinga ndi ndandanda yanu, kodi nthaŵi yabwino ya kuŵerenga Baibulo ndi iti?
◻ Pamene mukuŵerenga Baibulo mobwerezabwereza, kodi nchiyani chimene chingachititse programu yanu kukhala ndi zinthu zosiyanasiyana?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kusinkhasinkha zimene tikuŵerenga?
[Bokosi pamasamba 16, 17]
Malingaliro owongolera kuŵerenga kwanu Baibulo
(1) Anthu ambiri amaŵerenga mabuku a Baibulo malinga ndi ndandanda imene amasindikizidwira, kuyambira ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso. Nanunso mukhoza kuwaŵerenga malinga ndi ndandanda imene analembedweramo poyamba. Kumbukirani kuti Baibulo ndi mpukutu wa mabuku ouziridwa 66, laibulale yaumulungu. Kuti mukhale ndi kuŵerenga kosiyanasiyana, mwina mungakonde kuŵerenga ena a mabukuwo amene ali ndi mbiri, ndiyeno ena amaulosi okhaokha, motsatiridwa ndi aja amene ali makalata a uphungu, m’malo mwa kungotsatira manambala a masamba. Musaiŵale pamene mwaŵerenga, ndipo tsimikizirani kuŵerenga Baibulo lonse.
(2) Mutaŵerenga chigawo cha Malemba, dzifunseni zimene chikusonyeza ponena za Yehova, chifuno chake, njira yake yochitira zinthu; mmene chiyenera kukhudzira moyo wanu; mmene mungachigwiritsirire ntchito kuthandiza wina.
(3) Mukumagwiritsira ntchito tchathi chakuti “Main Events of Jesus’ Earthly Life” chofalitsidwa pamutu wakuti “Jesus Christ” mu Insight on the Scriptures (ndiponso mu “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial”), monga chokutsogolerani, ŵerengani nkhani zofanana nazo m’chigawo chilichonse cha Mauthenga Abwino, motsatizana. Wonjezanipo kufufuza zigawo zofanana nazo m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.
(4) Pamene mukuŵerenga nkhani ya moyo ndi utumiki wa Paulo m’Machitidwe a Atumwi, ŵerenganinso makalata ouziridwa okhudza nkhaniyo. Chotero, pamene mizinda yosiyanasiyana kapena madera kumene Paulo analalikira zikutchulidwa, imani kaye ndi kuŵerenga makalata amene iye pambuyo pake analembera Akristu anzake akumalowo. Kulinso kothandiza kutsatira maulendo ake pamapu, onga aja ali mkati kuchikuto chakumapeto cha New World Translation.
(5) Pamene mukuŵerenga Eksodo mpaka Deuteronomo, ŵerengani kalata ya kwa Ahebri kuti mupeze malongosoledwe a zitsanzo zambiri zaulosi. Pamutu wakuti “Law” mu Insight on the Scriptures, pendani tchathi chakuti “Some Features of the Law Covenant.”
(6) Poŵerenga mabuku aulosi, patulani nthaŵi ya kupenda nkhani zina za m’mbiri zowakhudza m’Baibulo. Mwachitsanzo, poŵerenga buku la Yesaya, pendani zimene zikunenedwa kwina ponena za mfumu Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, amene akutchulidwa pa Yesaya 1:1. (2 Mafumu, machaputala 15-20; 2 Mbiri, machaputala 26-32) Kapena poŵerenga Hagai ndi Zekariya, patulani nthaŵi ya kupenda zimene zili m’buku la Ezara.
(7) Sankhani buku la Baibulo, ŵerengani chigawo chake (mwina chaputala chimodzi), ndiyeno fufuzani, mukumagwiritsira ntchito Watch Tower Publications Index kapena Watchtower Library ya pakompyuta. Gwiritsirani ntchito nkhaniyo m’moyo wanu. Igwiritsireni ntchito m’nkhani zanu ndi mu utumiki wakumunda. Ndiyeno pitirizani kuŵerenga chigawo china.
(8) Ngati pali chofalitsa cha Watch Tower chimene chili ndi ndemanga pa buku lina la Baibulo kapena chigawo chake, chiŵerengeni nthaŵi zonse pamene mukuŵerenga mbali imeneyo ya Baibulo. (Mwachitsanzo: pa Nyimbo ya Solomo, The Watchtower, December 1, 1957, masamba 720-34; pa Ezekieli, “The Nations Shall Know That I Am Jehovah”—How?; pa Danieli, “Your Will Be Done on Earth” kapena Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu; pa Hagai ndi Zekariya, Paradise Restored to Mankind—By Theocracy!; pa Chivumbulutso, Revelation—Its Grand Climax At Hand!)
(9) Pamene mukuŵerenga, funafunani malifalensi ena osonyezedwa. Kumbukirani kuti pali ndime 320 za m’Malemba Achihebri zimene zagwidwa mawu m’Malemba Achigiriki Achikristu monga momwe alili ndi kukumbukiranso za malifalensi a ndime zina mazanamazana, ndiponso matanthauzo ake. Malifalensi amasonyeza kukwaniritsidwa kwa ulosi wolembedwa m’Baibulo, mbiri ya munthu ndi mafotokozedwe a malo, ndi malingaliro ofanana amene angamveketse mawu amene mwina amakuvutani kumva.
(10) Mukumagwiritsira ntchito Reference Edition ya New World Translation, ngati muli nayo m’chinenero chanu, pendani mawu amtsinde ndi nkhani zowonjezera zokhudza zimene mukuŵerenga. Zimenezi zimasonyeza chifukwa chake mawuwo anamasuliridwa motero ndi njira zina zimene mawu ofunika angatembenuzidwire. Mwina mungafunenso kuyerekezera mmene mavesi ena anamasuliridwa m’matembenuzidwe ena a Baibulo.
(11) Mutaŵerenga chaputala chilichonse, lembani mawu achidule kwambiri onena za lingaliro lalikulu la m’chaputalacho. Agwiritsireni ntchito monga maziko a kubwereza ndi kusinkhasinkha kwa pambuyo pake.
(12) Pamene mukuŵerenga Baibulo, chongani malemba osankhidwa amene mudzafuna kwambiri kukumbukira, kapena alembeni pamakadi ndi kuwaika pamene mukhoza kumawaona masiku onse. Aloŵezeni pamtima; asinkhesinkheni; agwiritsireni ntchito. Musayese kuloŵeza ambiri panthaŵi imodzi, mwina limodzi kapena aŵiri pamlungu umodzi; ndiyeno sankhani owonjezereka panthaŵi yotsatira imene muŵerenga Baibulo.
[Zithunzi patsamba 15]
Kodi mumaŵerenga Baibulo kapena kumvetsera makaseti ake masiku onse?