Kuŵala kwa Kuunika M’nthaŵi za Atumwi
“Kuunika kufesekera wolungama, ndi chikondwerero owongoka mtima.”—SALMO 97:11.
1. Kodi Mboni za Yehova lerolino zimafanana motani ndi Akristu oyambirira?
IFE monga Akristu oona timamvetsetsa kwambiri chotani nanga mawu a Salmo 97:11! ‘Kuunika kwatifesekera’ mobwerezabwereza. Inde, enafe taona kuŵala kounikira kwa Yehova zaka zambiri. Zonsezi zimatikumbutsa Miyambo 4:18, yomwe imati: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.” Chifukwa cha kumvetsetsa kwathu Malemba m’malo mwa miyambo, ife Mboni za Yehova timafanana ndi Akristu oyambirira. Mkhalidwe wawo umaonekera bwino lomwe m’mabuku a mbiri a Malemba Achigiriki Achikristu ndi makalata ake, olembedwa mouziridwa ndi Mulungu.
2. Kodi ndi ziti zomwe zinali pakati pa kuŵala koyamba kwa kuunika kumene otsatira Yesu analandira?
2 Pakati pa kuŵala koyamba kwa kuunika kumene otsatira Yesu Kristu oyambirira analandira panali kuja konena za Mesiya. Andreya anauza mbale wake Simoni Petro kuti: “Tapeza ife Mesiya.” (Yohane 1:41) Patapita nthaŵi ina, Atate wake kumwamba anakhozetsa mtumwi Petro kuchitira umboni zimenezo pamene iye anati kwa Yesu Kristu: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”—Mateyu 16:16, 17; Yohane 6:68, 69.
Kuunika pa Ntchito Yawo ya Kulalikira
3, 4. Ataukitsidwa, kodi ndi chidziŵitso chotani chimene Yesu anapatsa otsatira ake ponena za ntchito yawo yamtsogolo?
3 Yesu Kristu ataukitsidwa, iye anapereka kuŵala kwa kuunika ponena za thayo limene otsatira ake onse anali nalo. Iye mosakayikira ayenera kukhala atanena kwa ophunzirawo 500 amene anasonkhana ku Galileya kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20; 1 Akorinto 15:6) Pambuyo pake, otsatira onse a Kristu anali kudzakhala alaliki, ndipo ntchito yawo yolalikira sinali kudzachitidwa kwa “nkhosa zosokera za banja la Israyeli” zokha. (Mateyu 10:6) Ndipo sanali kudzachita ubatizo wa Yohane wosonyeza kulapa kuti machimo awo akhululukidwe. M’malo mwake, anali kudzabatiza anthu “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.”
4 Yesu atatsala pang’ono kukwera kumwamba, atumwi ake okhulupirika 11 anamfunsa: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” M’malo moyankha funsolo, Yesu anapereka malangizo ena a ntchito yawo ya kulalikira, kuti: “Mudzalandira mphamvu, mzimu woyera [u]tadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” Kufikira panthaŵiyo, iwo anali kokha mboni za Yehova, koma tsopano akakhalanso mboni za Kristu.—Machitidwe 1:6-8.
5, 6. Kodi ndi kuŵala kotani kwa kuunika kumene ophunzira a Yesu analandira pa Pentekoste?
5 Patangopita masiku khumi chabe, otsatira Yesu analandira kuŵala kwakukulu kotani nanga kwa kuunika! Patsiku la Pentekoste wa 33 C.E., kwa nthaŵi yoyamba, anamvetsetsa tanthauzo la Yoweli 2:28, 29: “[Ine Yehova] ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya; ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.” Ophunzira a Yesu anaona mzimu woyera, wonga malilime a moto, utakhala pamitu pawo onse—amuna ndi akazi pafupifupi 120—osonkhana m’Yerusalemu.—Machitidwe 1:12-15; 2:1-4.
6 Ndiponso patsiku la Pentekoste, ophunzirawo kwa nthaŵi yoyamba anamvetsetsa kuti mawu a Salmo 16:10 anali kunena za Yesu Kristu woukitsidwayo. Wamasalmo anati: “[Yehova Mulungu] simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.” Ophunzirawo anazindikira kuti mawuwo sanali kunena za Mfumu Davide, pakuti manda ake anali nawo kufikira tsikulo. Nchifukwa chake pafupifupi 3,000 mwa aja amene anamva kufotokozedwa kwa kuunika kwatsopano kumeneku anakhulupiriradi nabatizidwa tsiku lomwelo!—Machitidwe 2:14-41.
7. Kodi ndi kuŵala kwakukulu kotani kumene mtumwi Petro analandira paulendo wake kwa kazembe Wachiroma Korneliyo?
7 Kwa zaka mazana ambiri, Aisrayeli anali kudziŵa zimene Mulungu ananena za iwo: “Inu nokha ndinakudziŵani mwa mabanja onse a pa dziko lapansi.” (Amosi 3:2) Chotero mtumwi Petro ndi aja omwe anatsagana naye kunyumba ya kazembe Wachiroma Korneliyo analandiradi kuŵala kwakukulu kwa kuunika pamene mzimu woyera kwa nthaŵi yoyamba unatsikira pa okhulupirira Akunja osadulidwa. Nkokondweretsa kudziŵa kuti ndi panthaŵi yokhayi pamene mzimu woyera unaperekedwa ubatizo usanachitike. Koma zinayeneradi kukhala choncho. Mwinamwake, Petro sakanadziŵa kuti Akunja osadulidwa ameneŵa anayenerera ubatizo. Pozindikira bwino lomwe tanthauzo la chochitikachi, Petro anafunsa: “Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe [Akunja] aŵa, amene alandira mzimu woyera ngatinso ife?” Inde, panalibe ndi mmodzi yemwe amene akanatsutsa pa zifukwa zabwino, choncho ubatizo wa Akunjawo unachitika.—Machitidwe 10:44-48; 8:14-17.
Kulibenso Mdulidwe
8. Kodi nchifukwa ninji Akristu ena oyambirira zinawavuta kusiya mdulidwe?
8 Kuŵala kwina kwakukulu kwa choonadi kunatulukira pankhani ya mdulidwe. Mwambo wa mdulidwe unayamba mu 1919 B.C.E. limodzi ndi pangano la Yehova ndi Abrahamu. Panthaŵiyo Mulungu anauza Abrahamu kuti iye ndi amuna ena onse a banja lake adulidwe. (Genesis 17:9-14, 23-27) Motero mdulidwe unakhala chizindikiro chodziŵira mbadwa za Abrahamu. Ndipo anaunyadira chotani nanga mchitidwe umenewu! Chifukwa chake, mawu akuti “wosadulidwa” anali onyoza. (Yesaya 52:1; 1 Samueli 17:26, 27) Nkwapafupi kuona chifukwa chake Akristu Achiyuda ena oyambirira anafuna kusunga chizindikiro chimenechi. Ena a iwo anatsutsana kwambiri ndi Paulo ndi Barnaba pankhaniyi. Kuti aithetse, Paulo ndi enawo anapita ku Yerusalemu kukafunsa bungwe lolamulira Lachikristu.—Machitidwe 15:1, 2.
9. Kodi ndi kuŵala kotani kwa kuunika kumene kunavumbulidwa kwa bungwe lolamulira loyambirira, monga momwe kwalembedwera m’Machitidwe chaputala 15?
9 Panthaŵiyi, Akristu oyambawo sanalandire kuunika mwanjira imene mwachionekere inali yozizwitsa yosonyeza kuti mdulidwe sunalinso kufunika kwa atumiki a Yehova. M’malo mwake, analandira kuunika kowonjezerekako mwa kufufuza Malemba, kudalira mzimu woyera kaamba ka chitsogozo, ndi kumvetsera zokumana nazo za Petro ndi Paulo za kutembenuka kwa Akunja osadulidwa. (Machitidwe 15:6-21) Chigamulo chawo chinaperekedwa m’kalata imene mbali yake inati: “Chinakomera mzimu woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola ndi dama.” (Machitidwe 15:28, 29) Motero Akristu oyambirira anamasulidwa ku lamulo la kuchita mdulidwe ndi pa zofunika zina za Chilamulo cha Mose. Chifukwa chake, Paulo anauza Akristu a ku Galatiya kuti: “Kristu anatisandutsa mfulu.”—Agalatiya 5:1.
Kuunika m’Mauthenga Abwino
10. Kodi kuŵala kwina kwa kuunika kumene kunavumbulidwa mu Uthenga Wabwino wa Mateyu kunali kotani?
10 Nkosakayikitsa kuti Uthenga Wabwino wa Mateyu, wolembedwa pafupifupi mu 41 C.E., uli ndi kuŵala kochuluka kwa kuunika kopindulitsa oŵerenga ake. Ndi Akristu oŵerengeka okha a m’zaka za zana loyamba amene anamva Yesu akuphunzitsa mwachindunji. Makamaka, Uthenga Wabwino wa Mateyu unagogomezera kuti mutu wa ulaliki wa Yesu unali Ufumu. Ndipo Yesu anagogomezeradi kwambiri chotani nanga kufunika kwa kukhala ndi cholinga chabwino! Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, m’mafanizo ake (monga aja olembedwa m’chaputala 13), ndi mu ulosi wake waukulu m’machaputala 24 ndi 25, munali kuŵala kwa kuunika kotani nanga! Zonsezi zinasonyezedwa kwa Akristu oyambirira m’nkhani ya Uthenga Wabwino wa Mateyu wolembedwa zaka zisanu ndi zitatu zokha pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E.
11. Kodi nchiyani chimene chinganenedwe pa za mkati mwa Uthenga Wabwino wa Luka ndi wa Marko?
11 Patapita zaka pafupifupi 15, Luka analemba Uthenga wake Wabwino. Pamene kuli kwakuti mbali yake yaikulu ili yofanana ndi nkhani ya Mateyu, 59 peresenti yake ili yowonjezeredwa. Luka analemba zisanu ndi chimodzi za zozizwitsa za Yesu ndi mafanizo Ake oŵirikiza kaŵiri kuposa pamenepo osatchulidwa ndi alembi ena a Mauthenga Abwino. Mwachionekere, patangopita zaka zingapo, Marko analemba Uthenga wake Wabwino, akumasonyeza mwamphamvu kuti Yesu Kristu anali munthu wachangu, wochita zozizwitsa. Pamene kuli kwakuti Marko kwakukulukulu anasimba za zochitika zimene Mateyu ndi Luka anasimba, iye analemba fanizo lina limene iwo sanalembe. M’fanizo limenelo, Yesu anayerekezera Ufumu wa Mulungu ndi mbewu yomera, imene imakula, ndi kubala zipatso m’kupita kwa nthaŵi.a—Marko 4:26-29.
12. Kodi Uthenga Wabwino wa Yohane unapereka chidziŵitso china kufikira pati?
12 Ndiyeno panali Uthenga Wabwino wa Yohane, wolembedwa zaka zoposa 30 Marko atalemba nkhani yake. Ndi kuŵala kotani nanga kwa kuunika kumene Yohane anaunikira nako utumiki wa Yesu, makamaka mwa kumatchula nthaŵi zambiri kukhalapo Kwake asanakhale munthu! Yohane yekha ndiye amene amasimba nkhani ya chiukiriro cha Lazaro, ndipo ndiye yekha amene amatiuza ambiri a mawu abwino amene Yesu anauza atumwi ake okhulupirika limodzinso ndi pemphero lake logwira mtima pa usiku umene anaperekedwa, zolembedwa m’machaputala 13 mpaka 17. Kwenikweni, kwanenedwa kuti 92 peresenti ya Uthenga Wabwino wa Yohane imangopezeka mokhamo.
Kuŵala kwa Kuunika m’Makalata a Paulo
13. Kodi nchifukwa ninji ena aona kalata ya Paulo kwa Aroma monga ngati Uthenga Wabwino?
13 Mtumwi Paulo anagwiritsiridwa ntchito kwambiri kupereka kuŵala kwa choonadi kwa Akristu okhala m’nthaŵi za atumwi. Mwachitsanzo, pali kalata ya Paulo kwa Aroma, yolembedwa pafupifupi 56 C.E.—mwinamwake panthaŵi imodzimodzi imene Luka analemba Uthenga wake Wabwino. M’kalata imeneyi Paulo akugogomezera kuti mkhalidwe wolungama umaperekedwa chifukwa cha chisomo cha Mulungu ndi kupyolera mwa chikhulupiriro cha mwa Yesu Kristu. Kugogomezera kwa Paulo mbali imeneyi ya uthenga wabwino kwachititsa ena kuona kalata yake kwa Aroma monga ngati Uthenga Wabwino wachisanu.
14-16. (a) M’kalata yake yoyamba kwa Akristu a ku Korinto, kodi ndi kuunika kotani kumene Paulo anaŵalitsira pa kufunika kwa umodzi? (b) Kodi ndi kuunika kwina kotani kwa khalidwe kumene Akorinto Woyamba ali nako?
14 Paulo analemba za nkhani zina zimene zinali kusautsa Akristu ku Korinto. Kalata yake kwa Akorinto imaphatikizapo uphungu wochuluka wouziridwa umene wapindulitsa Akristu kufikira tsiku lathuli. Choyamba, anafuna kuwatsegula maso Akorinto kuti aone kuphophonya kumene anali kuchita mwa kupanga timagulu totsatira anthu ena. Mtumwiyo anawaongolera, akumawauza molimba mtima kuti: “Ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mumtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.”—1 Akorinto 1:10-15.
15 Chisembwere chonyansa chinali kulekereredwa mumpingo Wachikristu ku Korinto. Mwamuna wina kumeneko anatenga mkazi wa atate wake, motero akumachita ‘chigololo chotere chonga sichinamveka mwa amitundu.’ Mosapita m’mbali, Paulo analemba kuti: “Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” (1 Akorinto 5:1, 11-13) Zimenezo zinali zatsopano mumpingo Wachikristu—kuchotsa. Nkhani ina imene mpingo wa ku Korinto unafunikira kutsegulidwa maso inali yakuti ziŵalo zake zina zinali kupereka abale awo auzimu kumabwalo a milandu kuti akaweruzidwe. Paulo anawadzudzula mwamphamvu pa zimenezo.—1 Akorinto 6:5-8.
16 Nkhani inanso imene inaloŵerera mpingo ku Korinto inali ya kugonana. Mu 1 Akorinto chaputala 7, Paulo anasonyeza kuti chifukwa cha kufalikira kwa chisembwere, kukakhala koyenera kwa mwamuna aliyense kukhala ndi mkazi wa iye yekha ndi mkazi aliyense kukhala ndi mwamuna wa iye yekha. Paulo anasonyezanso kuti pamene kuli kwakuti mbeta zikhoza kutumikira Yehova popanda zocheukitsa zambiri, si onse amene anali ndi mphatso ya umbeta. Ndipo mwamuna wa mkazi wina akamwalira, iye anali womasuka kukwatiwanso koma “mwa Ambuye.”—1 Akorinto 7:39.
17. Kodi ndi kuunika kotani kumene Paulo anaŵalitsira pa chiphunzitso cha chiukiriro?
17 Ndi kuŵala kwa kuunika kotani nanga konena za chiukiriro kumene Ambuye anaŵalitsa kupyolera mwa Paulo! Kodi Akristu odzozedwa adzaukitsidwa ndi thupi lotani? “Lifetsedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu,” analemba motero Paulo. Matupi anyama sadzatengedwa kumwamba, pakuti “thupi ndi mwazi sizingathe kuloŵa Ufumu wa Mulungu.” Paulo anawonjezera kuti si odzozedwa onse amene adzagona mu imfa, koma kuti pa kukhalapo kwa Yesu ena adzaukitsidwa ku moyo wosafa m’kamphindi atangomwalira.—1 Akorinto 15:43-53.
18. Kodi ndi kuunika kotani konena za mtsogolo kumene kalata yoyamba ya Paulo kwa Atesalonika inali nako?
18 M’kalata yake kwa Akristu a ku Tesalonika, Paulo anagwiritsiridwa ntchito kuŵalitsa kuunika pa za mtsogolo. Tsiku la Yehova likadza monga mbala usiku. Paulo anafotokozanso kuti: “Pamene angonena, Mtendere ndi [chisungiko!, NW], pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka.”—1 Atesalonika 5:2, 3.
19, 20. Kodi ndi kuŵala kotani kwa kuunika kumene Akristu a ku Yerusalemu ndi Yudeya analandira m’kalata ya Paulo kwa Ahebri?
19 Mwa kulemba kalata yake kwa Ahebri, Paulo anapereka kuŵala kwa kuunika kwa Akristu oyambirira m’Yerusalemu ndi m’Yudeya. Anasonyeza mwamphamvu chotani nanga kupambana kwa njira yolambirira Yachikristu pa njira yolambirira ya m’nthaŵi ya Mose! M’malo motsatira Chilamulo choperekedwa ndi angelo, Akristu ali ndi chikhulupiriro m’chipulumutso chimene chinalankhulidwa choyamba ndi Mwana wa Mulungu, amene aposa amithenga aungelo amenewo. (Ahebri 2:2-4) Mose anali chabe mtumiki m’nyumba ya Mulungu. Komabe, Yesu Kristu amayang’anira nyumba yonseyo. Kristu ndi mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melikizedeke, wokhala ndi malo apamwamba kuposa unsembe wa Aroni. Paulo anatchulanso kuti Aisrayeli sanaloŵe mumpumulo wa Mulungu chifukwa cha kusoŵa chikhulupiriro ndi kumvera, koma Akristu amaloŵamo chifukwa cha kukhulupirika kwawo ndi kumvera.—Ahebri 3:1–4:11.
20 Ndiyenonso, pangano latsopano liposa pangano la Chilamulo. Monga momwe ulosi unanenera zaka 600 kumbuyoko pa Yeremiya 31:31-34, aja amene ali m’pangano latsopano chilamulo cha Mulungu ncholembedwa m’mitima yawo ndipo amapeza chikhululukiro chenicheni cha machimo. M’malo mokhala ndi mkulu wa ansembe amene anafunikira kupereka nsembe chaka ndi chaka za machimo ake ndi aja a anthu, Akristu ali ndi Yesu Kristu monga Mkulu wa Ansembe wawo, wopanda uchimo ndi yemwe anapereka nsembe ya machimo kamodzi kwatha. M’malo moloŵa m’malo opatulika omangika ndi manja kukapereka nsembe yake, iye analoŵa kumwamba komwe, kukaonekera pamaso pa Yehova. Ndiponso, nsembe zanyama m’pangano la Chilamulo cha Mose sizinathe kuchotseratu machimo, poti zikanatero sizikanaperekedwa chaka ndi chaka. Koma nsembe ya Kristu, yoperekedwa kamodzi kwatha, imachotsadi machimo. Zonsezi zimaŵalitsa kuunika pa kachisi wamkulu wauzimu, amene m’mabwalo ake amatumikiramo otsalira odzozedwa ndi “nkhosa zina” lerolino.—Yohane 10:16; Ahebri 9:24-28.
21. Kodi nkhaniyi yatisonyezanji ponena za kukwaniritsidwa kwa Salmo 97:11 ndi Miyambo 4:18 m’nthaŵi za atumwi?
21 Malo achepa operekera zitsanzo zina, monga kuŵala kwa kuunika kopezeka m’makalata a mtumwi Petro ndi aja a mtumwi Yakobo ndi Yuda. Koma zimene takambitsiranazo ziyenera kukhala zokwanira kusonyeza kuti Salmo 97:11 ndi Miyambo 4:18 inakwaniritsidwa mochititsa chidwi m’nthaŵi za atumwi. Choonadi chinayamba kupita patsogolo kuchokera pa zophiphiritsa ndi zochitira chithunzi kufikira pa kukhala zochitika ndi zenizeni.—Agalatiya 3:23-25; 4:21-26.
22. Kodi chinachitika nchiyani pambuyo pa imfa ya atumwi, ndipo kodi nkhani yotsatira idzasonyezanji?
22 Atumwi a Yesu atamwalira ndiponso mpatuko woloseredwawo utayamba, kuunika kwa choonadi kunaŵala moziyaziya. (2 Atesalonika 2:1-11) Komabe, malinga ndi lonjezo la Yesu, Mbuyeyo anabwera patapita zaka mazana ambiri napeza “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akumapatsa “banja” chakudya chawo panthaŵi yake. Chifukwa chake, Yesu Kristu anamuika kapoloyo “woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyu 24:45-47) Kodi ndi kuŵala kwa kuunika kotani kumene kunatsatira? Zimenezi zidzakambidwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Panopa nthaka ikutanthauza malo amene Mkristu amasankha kukulitsirako mikhalidwe yaumunthu wake.—Onani Nsanja ya Olonda, December 15, 1980, masamba 18-19.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi malemba ati a Baibulo amene amasonyeza kuti kumvetsetsa choonadi kumadza pang’onopang’ono?
◻ Kodi ndi kuŵala kwina kotani kwa kuunika kumene kwalembedwa m’buku la Machitidwe?
◻ Kodi ndi kuunika kotani kumene kumapezeka m’Mauthenga Abwino?
◻ Kodi makalata a Paulo ali ndi kuŵala kotani kwa kuunika?