Mboni Zotsutsa Milungu Yonama
“Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha.”—YESAYA 43:10.
1. Kodi Mulungu woona ndani, ndipo ndi pambali ziti zimene iye amapambana milungu yochuluka yolambiridwa lerolino?
KODI Mulungu woona ndani? Lerolino, anthu onse akuyang’anizana ndi funso lofunika limeneli. Ngakhale kuti anthu amalambira milungu yambirimbiri, ndi Mmodzi yekha amene angatipatse moyo ndi mtsogolo mwachimwemwe. Ndi Mmodzi yekha amene tinganene za iye kuti: “Mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu.” (Machitidwe 17:28) Inde, ndi Mulungu mmodzi yekha amene ayenera kulambiridwa. Monga momwe ikunenera nyimbo yoimbidwa kumwamba m’buku la Chivumbulutso: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”—Chivumbulutso 4:11.
2, 3. (a) Kodi Satana monama anatsutsa motani kuti Yehova sayenera kulambiridwa? (b) Kodi tchimo la Hava linali ndi chotulukapo chotani kwa Hava ndi ana ake, ndipo chinatulukapo nchiyani kwa Satana?
2 M’munda wa Edene, Satana monama anatsutsa kuti Yehova sayenera kulambiridwa. Mwa kugwiritsira ntchito njoka, anauza Hava kuti akaswa lamulo la Yehova ndi kudya za mtengo umene Yehova analetsa, adzakhala ngati Mulungu. Anati: “Adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:5) Hava anakhulupirira njokayo nadya chipatso choletsedwa.
3 Ndithudi, Satana ananama. (Yohane 8:44) Njira yokha imene Hava anakhala “ngati Mulungu” pamene anachimwa inali yakuti anadzitengera yekha mphamvu ya kusankha chabwino ndi choipa, zimene Yehova yekha ndiye anayenera kuchita. Ndipo mosiyana ndi bodza la Satana, anamwalira potsirizira pake. Chotero munthu yekha amene anapindula ndi tchimo la Hava anali Satana. Indetu, cholinga chake Satana chimene sanatchule posonkhezera Hava kuchimwa chinali cha kufuna kukhala mulungu iye mwini. Pamene Hava anachimwa, anakhala wotsatira wake woyamba waumunthu, ndipo posapita nthaŵi Adamu anagwirizana naye. Ana awo ochuluka sanangobadwira “m’mphulupulu” komanso anayambukiridwa ndi chisonkhezero cha Satana, ndipo panthaŵi yaifupi, panakhala dziko lathunthu lotalikirana ndi Mulungu woona.—Genesis 6:5; Salmo 51:5.
4. (a) Kodi mulungu wa dziko lino ndani? (b) Kodi nchiyani chimene chikufunikira mwamsanga?
4 Dziko limenelo linawonongedwa pa Chigumula. (2 Petro 3:6) Chitapita Chigumula panadzakhala dziko lina lotalikirana naye Yehova, ndipo likalipobe. Baibulo limati ponena za ilo: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mwa kutsutsana kwake ndi mzimu ndi malembo a lamulo la Yehova, dziko limeneli limatumikira zolinga za Satana. Iye ali mulungu wake. (2 Akorinto 4:4) Komabe, iye ndi mulungu wopanda mphamvu yeniyeni. Sangachititse anthu kukhala achimwemwe kapena kuwapatsa moyo; Yehova yekha ndiye angachite zimenezo. Nchifukwa chake, anthu amene afuna moyo watanthauzo ndi dziko labwino ayenera choyamba kudziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu woona ndiyeno kuphunzira kuchita chifuniro chake. (Salmo 37:18, 27, 28; Mlaliki 12:13) Choncho amuna ndi akazi achikhulupiriro afunikira mwamsanga kuchitira umboni, kapena kulengeza choonadi, ponena za Yehova.
5. Kodi ‘mtambo wa mboni’ umene Paulo anatchula nchiyani? Tchulani anthu ena amene iye wandandalika.
5 Kuyambira pachiyambi penipeni, anthu okhulupirika otero akhalapo padziko. Mtumwi Paulo, mu Ahebri chaputala 11, akupereka mpambo wawo wautali ndi kuwatcha “mtambo waukulu wotere wa mboni.” (Ahebri 12:1) Abele, mwana wachiŵiri wa Adamu ndi Hava, anali woyamba pampambo wa Paulo. Enoke ndi Nowa akutchulidwanso kuyambira Chigumula chisanachitike. (Ahebri 11:4, 5, 7) Wotchuka kwambiri ndi Abrahamu, kholo la fuko la Ayuda. Abrahamu, wotchedwanso “bwenzi la Mulungu,” anakhala kholo la Yesu, “mboni yokhulupirika ndi yoona.”—Yakobo 2:23; Chivumbulutso 3:14.
Umboni wa Abrahamu wa Choonadi
6, 7. Kodi moyo wa Abrahamu ndi zochita zake zinakhala motani umboni wakuti Yehova ndiye Mulungu woona?
6 Kodi Abrahamu anakhala motani mboni? Mwa chikhulupiriro chake cholimba mwa Yehova ndi kumumvera kwake kokhulupirika. Pamene anamuuza kuchoka mumzinda wa Uri ndi kukakhala moyo wake wonse kudziko lakutali, Abrahamu anamvera. (Genesis 15:7; Machitidwe 7:2-4) Kaŵirikaŵiri, anthu oyendayenda amasiya moyo wawo woyendayenda nasankha moyo wotetezereka mumzinda. Nchifukwa chake, pamene Abrahamu anasiya mzindawo kukakhala m’mahema, anasonyeza umboni wamphamvu wa kudalira kwake Yehova Mulungu. Kumvera kwake kunali umboni kwa openyerera. Yehova anamdalitsa kwambiri Abrahamu kaamba ka chikhulupiriro chake. Angakhale anali kukhala m’mahema, Abrahamu anakhala ndi chuma chochuluka. Pamene Loti ndi banja lake anagwidwa ukapolo, Yehova anadalitsa ulendo wa Abrahamu pamene analondola, kwakuti anakhoza kuwalanditsa. Mkazi wa Abrahamu anabala mwana mu ukalamba wake, chotero lonjezo la Yehova lakuti Abrahamu adzabala mbewu linatsimikizidwa. Kupyolera mwa Abrahamu, anthu anaona kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo wokwaniritsa malonjezo ake.—Genesis 12:1-3; 14:14-16; 21:1-7.
7 Pobwerako kukalanditsa Loti, Abrahamu anakumana ndi Melikizedeke, mfumu ya Salemu (wotchedwa Yerusalemu pambuyo pake), amene analandira Abrahamu, akumati: “Abramu adalitsike [wa Mulungu Wam’mwambamwamba, NW].” Nayonso mfumu ya Sodomu inakumana naye ndipo inafuna kumupatsa mphatso. Abrahamu anakana. Chifukwa? Sanafune kuti pakhale kukayikira kulikonse ponena za Magwero a madalitso ake. Anati: “Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale chingwe cha nsapato, ngakhale kanthu kalikonse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu.” (Genesis 14:17-24) Anali mboni yabwino chotani nanga Abrahamu!
Mtundu wa Mboni
8. Kodi Mose anasonyeza motani chikhulupiriro chachikulu mwa Yehova?
8 Mose, mbadwa ya Abrahamu, nayenso akupezeka pampambo wa Paulo wa mboni. Mose anafulatira chuma cha Aigupto ndipo pambuyo pake anayang’anizana molimba mtima ndi wolamulira wa ulamuliro waukulu wa dziko lonse kuti atsogolere ana a Israyeli ku ufulu. Kodi kulimba mtimako anakupeza kuti? M’chikhulupiriro chake. Paulo akuti: “[Mose] anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27) Milungu ya Aigupto inali yooneka, yokhudzika. Ngakhale lero, anthu amachita nawo chidwi mafano ake. Koma Yehova, angakhale anali wosaoneka, analidi weniweni kwa Mose kuposa milungu yonse yonamayo. Mose sanakayikire kukhalako kwa Yehova ndi kuti adzafupa alambiri Ake. (Ahebri 11:6) Mose anakhala mboni yapadera.
9. Kodi mtundu wa Israyeli unayenera kutumikira monga yani kwa Yehova?
9 Atatsogolera Aisrayeli ku ufulu, Mose anakhala nkhoswe ya pangano la pakati pa Yehova ndi mbadwa za Abrahamu kudzera mwa Yakobo. Motero, mtundu wa Israyeli unakhala chuma chapadera cha Yehova. (Eksodo 19:5, 6) Kupereka umboni monga mtundu kunayenera kuchitika nthaŵi yoyamba. Mawu a Yehova kwa Yesaya, zaka pafupifupi 800 pambuyo pake, anagwira ntchito malinga ndi zolinga zake kuyambira pachiyambi pamene mtunduwo unakhalako: “Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziŵe, ndi kundikhulupirira ine, ndi kuzindikira, kuti ine Ndine.” (Yesaya 43:10) Kodi mtundu watsopano umenewu ukanatumikira motani monga mboni za Yehova? Mwa chikhulupiriro chawo ndi kumvera ndiponso mwa zochita za Yehova kaamba ka iwo.
10. Kodi zochita zamphamvu za Yehova kaamba ka Israyeli zinapereka motani umboni, ndipo zotulukapo zake zinali zotani?
10 Zaka pafupifupi 40 kuchokera pachiyambi chake, Israyeli anali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Azondi anatumidwa kukazonda mzinda wa Yeriko, ndipo Rahabi, nzika ya Yeriko, anawatetezera. Chifukwa? Iye anati: “Tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m’Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka m’Aigupto; ndi chija munachitira mafumu aŵiri a Aamori okhala tsidya la Yordano, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawawononga konse. Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m’mwamba umo, ndi pa dziko lapansi.” (Yoswa 2:10, 11) Lipoti la ntchito zamphamvu za Yehova linasonkhezera Rahabi ndi banja lake kuchoka m’Yeriko ndi kusiya milungu yonama ndi kukalambira Yehova limodzi ndi Israyeli. Ndithudi, Yehova anapereka umboni wamphamvu kupyolera mwa Israyeli.—Yoswa 6:25.
11. Kodi makolo onse Achiisrayeli anali ndi thayo lotani pa kuchitira umboni?
11 Pamene Aisrayeli anali mu Igupto, Yehova anatuma Mose kwa Farao kuti: “Loŵa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pawo, ndi kuti ufotokozere m’makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita m’Aigupto, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pawo; kuti mudziŵe kuti ine ndine Yehova.” (Eksodo 10:1, 2) Aisrayeli omvera anayenera kusimbira ana awo zochita zamphamvu za Yehova. Ana awonso, anayenera kuzisimba kwa ana awo, choncho anatero kumibadwomibadwo. Motero, anakumbukira zochita zamphamvu za Yehova. Lerolinonso, makolo ali ndi thayo la kuchita umboni kwa ana awo.—Deuteronomo 6:4-7; Miyambo 22:6.
12. Kodi dalitso la Yehova pa Solomo ndi Israyeli linakhala umboni motani?
12 Madalitso ochuluka amene Yehova anadzetsa pa Israyeli pamene anali wokhulupirika anakhala umboni kwa mitundu yozungulira. Monga momwe Mose ananenera atasimba za madalitso olonjezedwa a Yehova: “Anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuwopani.” (Deuteronomo 28:10) Solomo anapatsidwa nzeru ndi chuma chifukwa cha chikhulupiriro chake. Mu ulamuliro wake mtunduwo unakhupuka nukhala ndi mtendere nthaŵi yaitali. Ponena za nthaŵiyo timaŵerenga zotere: “Anafikako anthu a mitundu yonse kudzamva nzeru ya Solomo, ochokera kwa mafumu onse a dziko lonse lapansi, amene adamva mbiri ya nzeru yake.” (1 Mafumu 4:25, 29, 30, 34) Amene anali wotchuka mwa alendowo a Solomo anali mfumukazi ya Seba. Atadzionera yekha dalitso la Yehova pa mtunduwo ndi mfumu yake, anati: “Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Israyeli.”—2 Mbiri 9:8.
13. Kodi ndi uti umene ungakhale unali umboni wa Israyeli wogwira mtima koposa, ndipo tikali kupindula nawo motani?
13 Mtumwi Paulo anatchula umene mwina unali umboni wa Israyeli wogwira mtima koposa. Pofotokoza Israyeli wakuthupi kwa mpingo Wachikristu ku Roma, anati: “Mawu a Mulungu anaperekedwa kwa iwo.” (Aroma 3:1, 2) Kuyamba ndi Mose, Aisrayeli ena okhulupirika anauziridwa kulemba zochita za Yehova ndi Israyeli, ndiponso malangizo ake, malamulo ake, ndi maulosi ake. Mwa zolemba zimenezi alembi akale amenewo anachita umboni kwa mibadwo yonse yamtsogolo—kuphatikizapo wathu lerolino—kuti pali Mulungu mmodzi yekha, ndipo dzina lake ndi Yehova.—Danieli 12:9; 1 Petro 1:10-12.
14. Kodi nchifukwa ninji ena amene anachitira umboni Yehova anazunzidwa?
14 Mwa tsoka lake, Israyeli nthaŵi zambiri analephera kusonyeza chikhulupiriro, ndipo Yehova anatumiza mboni ku mtundu wakewo. Ambiri a iwo anazunzidwa. Paulo anati ena “anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m’ndende.” (Ahebri 11:36) Analidi mboni zokhulupirika! Nzachisoni chotani nanga kuti kaŵirikaŵiri amene anawazunza anali anzawo a mtundu wosankhika wa Yehova umenewo! (Mateyu 23:31, 37) Ndipotu, tchimo la mtunduwo linakula kwambiri kwakuti mu 607 B.C.E., Yehova anabweretsa Ababulo kudzawononga Yerusalemu ndi kachisi wake ndi kutenga ukapolo unyinji wa Aisrayeli otsala. (Yeremiya 20:4; 21:10) Kodi amenewo ndiwo anali mapeto a kupereka kwawo umboni monga mtundu ponena za dzina la Yehova? Iyayi.
Kuyesa Milungu
15. Kodi umboni unaperekedwa motani ngakhale mu ukapolo wa Babulo?
15 Angakhale mu ukapolo ku Babulo, okhulupirika a mtunduwo sanazengereze kuchitira umboni za Umulungu wa Yehova ndi mphamvu yake. Mwachitsanzo, Danieli molimba mtima anamasulira maloto a Nebukadinezara, anafotokozera Belisazara mawu olembedwa pakhoma, ndipo anakana kugonja kwa Dariyo pankhani ya pemphero. Nawonso Ahebri atatu, pokana kugwadira fano, anapereka umboni wabwino kwambiri kwa Nebukadinezara.—Danieli 3:13-18; 5:13-29; 6:4-27.
16. Kodi Yehova analosera motani kubwerera kwa Israyeli ku dziko lawo, ndipo chifuno cha kubwerera kumeneko chinali chotani?
16 Chikhalirechobe, chifuno cha Yehova chinali chakuti iwo akaperekenso umboni monga mtundu m’dziko la Israyeli. Ezekieli, amene analosera pakati pa Ayuda andende ku Babulo, analemba za cholinga cha Yehova padziko labwinja limenelo: “Ndidzakuchulukitsirani anthu nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi, ndi m’midzimo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa midzi.” (Ezekieli 36:10) Kodi Yehova anafuniranji kuchita zimenezo? Kwenikweni kuti umboni uperekedwe wa dzina lake. Kupyolera mwa Ezekieli anati: “Sindichichita ichi chifukwa cha inu, nyumba ya Israyeli, koma chifukwa cha dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu.”—Ezekieli 36:22; Yeremiya 50:28.
17. Kodi nkhani yake ya mawu a Yesaya 43:10 ndi yotani?
17 Mneneri Yesaya anauziridwa kulemba mawu a Yesaya 43:10, kuti Israyeli anali mboni ya Yehova, mtumiki wake, pamene anali kulosera za kubwerako kwa Israyeli ku ukapolo wa Babulo. Mu Yesaya 43 ndi 44, Yehova akufotokozedwa monga Mlengi wa Israyeli, Woumba, Mulungu, Woyera, Mpulumutsi, Mombolo, Mfumu ndi Mpangi. (Yesaya 43:3, 14, 15; 44:2) Analola ukapolo wa Israyeli chifukwa chakuti mtunduwo mobwerezabwereza unalephera kumulemekeza malinga ndi zimenezo. Komabe, anali anthu ake ndithu. Yehova anati kwa iwo: “Usawope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga.” (Yesaya 43:1) Ukapolo wa Israyeli ku Babulo unali kudzatha.
18. Kodi chimasuko cha Israyeli kuchoka m’Babulo chinasonyeza motani kuti Yehova ndiye Mulungu woona yekha?
18 Ndithudi, Yehova anapanga chimasuko cha Israyeli kuchoka m’Babulo kukhala njira yoyesera milungu. Anauza milungu yonama kutulutsa mboni zawo, ndipo anatcha Israyeli mboni yake. (Yesaya 43:9, 12) Pamene anathyola magoli a ukapolo wa Israyeli, anasonyeza kuti milungu ya Babulo siinali konse milungu ndi kuti iye ndiye Mulungu woona yekha. (Yesaya 43:14, 15) Pamene anatcha Koresi Mperisiyo monga mtumiki wake womasula Ayuda zaka ngati 200 zimenezo zisanachitike, anapereka umboni wina wa Umulungu wake. (Yesaya 44:28) Israyeli anali kudzamasulidwa. Chifukwa? Yehova akuti: “Kuti [Israyeli] aonetse matamando anga.” (Yesaya 43:21) Zimenezo zinali kudzapereka mpata wina wa umboni.
19. Kodi chiitano cha Koresi chakuti Aisrayeli abwerere ku Yerusalemu ndiponso zochita za Ayuda okhulupirika atabwerera zinapereka umboni wotani?
19 Nthaŵiyo itafika, Koresi Mperisiyo anagonjetsa Babulo malinga ndi ulosiwo. Koresi, ngakhale kuti anali wachikunja, analengeza Umulungu wa Yehova pamene anapereka chilengezo kwa Ayuda ku Babulo kuti: “Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kumka ku Yerusalemu, ndiwo m’Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israyeli; iye ndiye Mulungu [woona, NW] wokhala m’Yerusalemu.” (Ezara 1:3) Ayuda ambiri anamvera. Anabwerera ku Dziko Lolonjezedwa nakamanga guwa la nsembe pa malo a kachisi wakale. Ngakhale kuti panali zolefula ndi chitsutso cholimba, anakhoza kumanganso kachisi ndi mzinda wa Yerusalemu potsirizira pake. Zonsezi zinachitika, monga mwa zimene Yehova mwiniyo ananena, “ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi mzimu [wake].” (Zekariya 4:6) Zipambano zimenezi zinapereka umboni wina wakuti Yehova ndiye Mulungu woona.
20. Mosasamala za zofooka za Israyeli, kodi tinganenenji za kuchitira kwawo umboni dzina la Yehova m’dziko lakale?
20 Motero, Yehova anapitiriza kugwiritsira ntchito Israyeli monga mboni yake, ngakhale kuti unali mtundu wa anthu opanda ungwiro ndipo nthaŵi zina opanduka. M’dziko la Chikristu chisanakhaleko, mtundu umenewo, ndi kachisi wake ndi ansembe, unali malikulu a dziko lonse a kulambira koona. Aliyense woŵerenga Malemba Achihebri ponena za zochita za Yehova kwa Israyeli sangakayikire konse kuti pali Mulungu woona mmodzi yekha, ndipo dzina lake ndi Yehova. (Deuteronomo 6:4; Zekariya 14:9) Komabe, umboni waukulu koposa unali kudzaperekedwa ku dzina la Yehova, ndipo tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Abrahamu anapereka motani umboni wakuti Yehova ndiye Mulungu woona?
◻ Kodi ndi mkhalidwe uti wapadera wa Mose umene unamkhozetsa kukhala mboni yokhulupirika?
◻ Kodi Israyeli anapereka motani umboni monga mtundu ponena za Yehova?
◻ Kodi chimasuko cha Israyeli kuchoka m’Babulo chinakhala motani chisonyezero chakuti Yehova ndiye Mulungu woona yekha?
[Chithunzi patsamba 10]
Mwa chikhulupiriro chake ndi kumvera, Abrahamu anapereka umboni wapadera wa Umulungu wa Yehova