“Akuchita Mawu” Achimwemwe
“Landirani ndi chifatso mawu ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. Khalani akuchita mawu, osati akumva okha.”—YAKOBO 1:21, 22.
1. Kodi lemba lathu la chaka cha 1996 liyenera kuonedwa motani?
“KHALANI AKUCHITA MAWU.” Mawu osavuta ameneŵa ali ndi uthenga wamphamvu. Iwo atengedwa mu “Kalata wa Yakobo” m’Baibulo, ndipo adzasonyezedwa m’Nyumba za Ufumu monga lemba la chaka la Mboni za Yehova mu 1996 yense.
2, 3. Kodi nchifukwa ninji kunali koyenera kuti Yakobo alembe kalata yotchedwa ndi dzina lake?
2 Yakobo, mbale wa Ambuye Yesu mwa atate omlera, anali wodziŵika mumpingo woyambirira Wachikristu. Nthaŵi ina pambuyo pa chiukiriro cha Yesu, Ambuye wathu anaonekera yekha kwa Yakobo ndiyeno kwa atumwi onse. (1 Akorinto 15:7) Pambuyo pake, pamene mtumwi Petro anamasulidwa m’ndende mozizwitsa, anauza gulu Lachikristu losonkhana kuti: “Muwauze Yakobo ndi abale izi.” (Machitidwe 12:17) Zikuoneka kuti Yakobo, ngakhale kuti iye sanali mtumwi, anatsogolera msonkhano wa bungwe lolamulira m’Yerusalemu pamene atumwi ndi akulu anagamula kuti Akunja otembenuka sanafunikira kudulidwa. Yakobo anafotokoza nkhaniyo mwachidule pomaliza, ndipo chigamulo chimene mzimu woyera unachirikiza chinatumizidwa ku mipingo yonse.—Machitidwe 15:1-29.
3 Mwachionekere, zigomeko za Yakobo zauchikulire zinali ndi ukumu kwambiri. Komabe, iye modzichepetsa anavomereza kuti anali chabe “kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Kristu.” (Yakobo 1:1) Kalata yake youziridwa ili ndi nkhokwe ya uphungu wabwino ndi chilimbikitso kwa Akristu lerolino. Inamalizidwa kutatsala ngati zaka zinayi kuti Aroma aukire Yerusalemu nthaŵi yoyamba pansi pa Kazembe Cestius Gallus, uthenga wabwino utalalikidwa kwambiri ‘cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Zinali nthaŵi zovuta zimenezo, ndipo atumiki a Yehova anali kudziŵa bwino kuti chiweruzo Chake chinali pafupi kuperekedwa pa mtundu Wachiyuda.
4. Kodi nchiyani chikusonyeza kuti Akristu oyambirira anali ndi chidaliro chachikulu m’Mawu a Mulungu?
4 Akristu amenewo anali nawo kale Malemba Achihebri onse ndi ochuluka a Malemba Achigiriki. Monga momwe kusonya kwawo kochuluka ku zolemba zoyambirira kumasonyezera, olemba Baibulo Achikristu mwachionekere anali ndi chidaliro chachikulu m’Mawu a Mulungu. Momwemonso, ife lerolino tifunika kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi kuwatsatira m’moyo wathu. Kuti tipirire, timafunika nyonga yauzimu ndi kulimba mtima zimene Malemba Opatulika amapereka.—Salmo 119:97; 1 Timoteo 4:13.
5. Kodi nchifukwa ninji tifunikira chitsogozo chapadera lerolino, ndipo tingachipeze kuti?
5 Lerolino anthu aima pamphembenu pa “masauko aakulu [“chisautso chachikulu,” NW], monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” (Mateyu 24:21) Chipulumutso chathu chidalira pa kukhala kwathu ndi chitsogozo cha Mulungu. Kodi tingachipeze motani? Mwa kulabadira ndi mtima wathu ziphunzitso za Mawu a Mulungu ouziridwa ndi mzimu. Zimenezi zidzatichititsa ‘kukhala akuchita mawu,’ monga atumiki okhulupirika a Yehova m’nthaŵi zakale. Tiyenera kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi kuwagwiritsira ntchito kutamanda Yehova.—2 Timoteo 2:15; 3:16, 17.
Kupirira Mwachimwemwe
6. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala achimwemwe m’mayesero?
6 Potsegulira kalata yake, Yakobo akutchula chimwemwe, chipatso chachiŵiri cha mzimu wa Mulungu. Akulemba kuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero amitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasoŵa kanthu konse.” (Yakobo 1:2-4; Agalatiya 5:22, 23) Kodi tinganene motani kuti ndiko “chimwemwe chokha” kukumana ndi mayesero ambiri? Eya, ngakhale Yesu anati mu Ulaliki wake wa pa Phiri: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m’mwamba.” (Mateyu 5:11, 12) Timakhala okhutira ndi achimwemwe poona dalitso la Yehova pa zoyesayesa zathu pamene tikulimbikira kulinga ku mphotho ya moyo wosatha.—Yohane 17:3; 2 Timoteo 4:7, 8; Ahebri 11:8-10, 26, 35.
7. (a) Kodi nchiyani chingatithandize kupirira? (b) Mofanana ndi Yobu, kodi tingafupidwe motani?
7 Yesu mwiniyo anapirira “chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake.” (Ahebri 12:1, 2) Poyang’anitsitsa chitsanzo cha Yesu cha kulimba mtima, nafenso tingapirire! Monga mmene Yakobo akutchulira kumapeto kwa kalata yake, Yehova amafupa kwambiri anthu osunga umphumphu. “Taonani tiwayesa odala opirirawo,” akutero Yakobo. “Mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Kumbukirani mmene Yobu anafupidwira chifukwa cha umphumphu wake pamene anakhalanso ndi thanzi labwino nasangalala ndi moyo wokhutiritsa ndi wachimwemwe limodzi ndi okondedwa ake. Chipiriro posunga umphumphu chingakudzetsereni chisangalalo chonga chimenecho m’Paradaiso wolonjezedwa wa dziko latsopano la Mulungu, monga chimake cha chimwemwe cha kutumikira Yehova tsopano.
Kufunafuna Nzeru
8. Kodi tingaipeze motani nzeru yeniyeni, yogwira ntchito, ndipo pemphero lili ndi mbali yotani pa zimenezi?
8 Phunziro lathu lakhama la Mawu a Mulungu, limodzi ndi kuwachita, zidzatipatsa nzeru yaumulungu, yotikhozetsa kupirira mayesero pakati pa dongosolo loipa lomafa la Satana. Kodi tingatsimikize motani kuti tidzapeza nzeru yotero? Yakobo akutiuza kuti: “Wina wa inu ikamsoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuŵinduka nayo.” (Yakobo 1:5, 6) Tiyenera kupemphera mwakhama, ndi chidaliro chosagwedera chakuti Yehova adzamva zopempha zathu ndi kuti adzatiyankha panthaŵi yake ndi mwanjira yake.
9. Kodi Yakobo akuifotokoza motani nzeru yaumulungu ndi mmene imagwirira ntchito?
9 Nzeru yaumulungu ili mphatso yochokera kwa Yehova. Pofotokoza mphatso zotero, Yakobo akuti: “Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.” Pambuyo pake m’kalata yake, Yakobo akufotokoza zotulukapo za kupeza nzeru yeniyeni pamene akuti: “Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa. . . . Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.”—Yakobo 1:17; 3:13-17.
10. Kodi chipembedzo chonyenga chimasiyana motani ndi choona?
10 Mu ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, kaya m’Dziko Lachikristu kaya m’maiko ena, nthaŵi zambiri olambira amakonda kuimba nyimbo, kumvetsera mapemphero obwerezabwereza, ndipo mwinamwake kumvetsera ulaliki. Samalimbikitsidwa kulengeza uthenga wa chiyembekezo, pakuti zipembedzo zambiri zilibe chiyembekezo cha mtsogolo mwabwino. Chiyembekezo chaulemerero cha Ufumu Waumesiya wa Mulungu samachitchula nkomwe kapena samachimvetsetsa konse. Ponena za anthu otsatira Dziko Lachikristu, Yehova molosera akuti: “Anthu anga anachita zoipa ziŵiri; anandisiya ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong’aluka, zosakhalamo madzi.” (Yeremiya 2:13) Alibe madzi a choonadi. Iwasoŵa nzeru yakumwamba.
11, 12. (a) Kodi nzeru ya Mulungu iyenera kutisonkhezera motani? (b) Kodi nzeru ya Mulungu imatichenjeza za chiyani?
11 Zinthu nzosiyana chotani nanga pakati pa Mboni za Yehova lerolino! Pokhala ndi mphamvu yolimba imene Mulungu wawapatsa, iwo akudzaza dziko lapansi ndi uthenga wabwino wa Ufumu Wake ukudzawo. Nzeru imene amalankhula njozikidwa zolimba pa Mawu a Mulungu. (Yerekezerani ndi Miyambo 1:20; Yesaya 40:29-31.) Inde, amagwiritsira ntchito chidziŵitso chenicheni ndi kuzindikira polengeza zifuno zazikulu za Mulungu wathu ndi Mlengi wathu. Chikhumbo chathu chiyenera kukhala chakuti onse mumpingo “adzazidwe ndi chizindikiritso [“chidziŵitso cholongosoka,” NW] cha chifuniro [cha Mulungu] mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu.” (Akolose 1:9) Pokhala ndi maziko ameneŵa, achichepere ndi achikulire omwe adzasonkhezereka nthaŵi zonse ‘kukhala akuchita mawu.’
12 “Nzeru yochokera kumwamba” imatichenjeza za machimo amene angatitayitse chiyanjo cha Mulungu. “Mudziŵa, abale anga okondedwa,” akutero Yakobo. “Kuti munthu aliyense akhale [wofulumira, NW] [ku]tchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.” Inde, tiyenera kufulumira, kufunitsitsa, kumvetsera uphungu wa Mulungu ndi kuuchita. Komabe, tiyenera kusamala kuti sitikugwiritsira ntchito molakwa ‘chiŵalo chaching’onocho,’ lilime. Mwa kudzikuza, miseche yosayenera, kapena kukamba moumirira nganganga pa zoganiza za munthuwe, lilime mophiphiritsira lingayatse “nkhuni zambiri.” Chotero tifunika kukulitsa ukoma ndi kudziletsa m’mayanjano athu onse.—Yakobo 1:19, 20; 3:5.
13. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa ife kulandira ‘mawu ookedwa mwa ife’?
13 “Mwa ichi,” akulemba motero Yakobo, “mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mawu ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.” (Yakobo 1:21) Dzikoli laumbombo, limodzi ndi moyo wake wodzionetsera, wokonda chuma, wodzikonda ndi makhalidwe ake oipa, lili pafupi kupita. “Koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.” (1 Yohane 2:15-17) Choncho, nkofunika chotani nanga kuti tilandire ‘mawu ookedwa mwa ife’! Nzeru yoperekedwa ndi Mawu a Mulungu njosiyana kwambiri ndi kuipa kwa dziko lomafali. Sitifuna kuipa kuli konse kumeneko. (1 Petro 2:1, 2) Tifunika kukhala ndi chikondi cha choonadi ndi chikhulupiriro cholimba chozikika m’mitima yathu, kuti tikhale otsimikiza kusapatuka panjira zolungama za Yehova. Koma kodi kungomva Mawu a Mulungu nkokwanira?
Kukhala “Akuchita Mawu”
14. Kodi tingakhale motani “akumva” ndiponso “akuchita” Mawu?
14 Pa Yakobo 1:22, timaŵerenga kuti: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.” “Khalani akuchita mawu”! Ndithudi mawuŵa akugogomezeredwa m’kalata ya Yakobo. Tiyenera kumva, ndiyeno kuchita “momwemo”! (Genesis 6:22) Anthu ambiri lerolino amati kuli kokwanira kumva ulaliki kapena kutengamo mbali mwamwambo m’kulambira kwina kwake nthaŵi zina, koma sachita zoposa pamenepo. Iwo angaganize kuti malinga ngati ali ndi ‘moyo wabwino’ mogwirizana ndi miyezo yawo, basi nzokwanira. Koma Yesu Kristu anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine.” (Mateyu 16:24) Ndithudi Akristu oona amafunika kudzimana ndi chipiriro potsanzira chitsanzo cha Yesu pakuchita chifuniro cha Mulungu. Kwa iwo, chifuniro cha Mulungu lerolino chidakali monga momwe chinalili m’zaka za zana loyamba pamene Yesu woukitsidwayo analamula kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu amitundu yonse.” (Mateyu 28:19) Kodi mukuchita motani pambaliyi?
15. (a) Kodi ndi fanizo lotani limene Yakobo akupereka, losonyeza mmene tingakhalire achimwemwe monga “akuchita mawu”? (b) Kodi nchifukwa ninji kulambira wamba sikuli kokwanira?
15 Ngati tipenyererabe m’Mawu a Mulungu, iwo angakhale ngati kalirole wotisonyeza mtundu wa munthu amene ife tili. Yakobo akuti: “Wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiŵala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.” (Yakobo 1:23-25) Inde, adzakhala ‘wakuchita mawu’ wodala. Ndiponso, nkofunika kukhala ‘wochita’ m’mbali iliyonse ya moyo wathu Wachikristu. Tisadzinyenge tokha kuganiza kuti kulambira wamba nkokwanira. Yakobo akutilangiza kuchita mbali zina za kulambira koona zimene ngakhale Akristu achangu angakhale atanyalanyaza. Akulemba kuti: “Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.”—Yakobo 1:27.
16. Kodi Abrahamu anakhala motani ‘bwenzi la Yehova,’ nanga ife tingakhale motani mabwenzi Ake?
16 Si kokwanira kungonena kuti, ‘Ndimakhulupirira Mulungu,’ ndi kuimira pamenepo. Monga momwe Yakobo 2:19 akunenera: “Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziŵanda zikhulupiranso, ndipo zinthunthumira.” Yakobo akugogomezera kuti “chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo,” ndiyeno akutchula Abrahamu kuti: “Chikhulupiriro [chake] chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro [chake] chidayesedwa changwiro.” (Yakobo 2:17, 20-22) Ntchito za Abrahamu zinaphatikizapo kupatsa mpumulo achibale ake, kuchereza alendo, kukonzekera kupereka nsembe Isake, ndi ‘kulengeza poyera,’ (NW) chikhulupiriro chake chosagwedera m’malonjezo a Mulungu a “mudzi wokhala nawo maziko,” Ufumu Waumesiya wamtsogolo. (Genesis 14:16; 18:1-5; 22:1-18; Ahebri 11:8-10, 13, 14; 13:2) Moyenerera, Abrahamu “anatchedwa bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:23) Nafenso tingayesedwe ‘mabwenzi a Yehova’ pamene tilengeza mwachangu chikhulupiriro ndi chiyembekezo chathu mu Ufumu wake ukudzawo wolungama.
17. (a) Kodi nchifukwa ninji Rahabi “anayesedwa wolungama,” ndipo anafupidwa motani? (b) Kodi ndi mpambo wautali wotani umene Baibulo limasonyeza wa aja amene ‘akhala akuchita mawu’? (c) Kodi Yobu anafupidwa motani, ndipo chifukwa ninji?
17 Amene ‘akhala akuchita mawu’ ‘amayesedwadi olungama ndi ntchito zawo, osati ndi chikhulupiriro chokha.’ (Yakobo 2:24) Wina amene anawonjezera ntchito pa chikhulupiriro chake mu “mawu” amene anamva onena za ntchito zamphamvu za Yehova anali Rahabi. Anabisa azondi Achiisrayeli nawathandiza kuthaŵa, ndiyeno anasonkhanitsa banja la atate wake kuti lipulumuke. Pachiukiriro, iye adzakondwera chotani nanga kudziŵa kuti chikhulupiriro chake, chochirikizidwa ndi ntchito, chinamchititsa kukhala kholo la Mesiya! (Yoswa 2:11; 6:25; Mateyu 1:5) Ahebri chaputala 11 ali ndi mpambo wautali wa ena amene ‘anakhala akuchita’ mwa kusonyeza chikhulupiriro chawo, ndipo adzafupidwa kwambiri. Ndipo sitiyenera kuiŵala Yobu, amene poyesedwa kowopsa anati: “Lidalitsike dzina la Yehova.” Monga momwe taonera kale, chikhulupiriro chake ndi ntchito zinadzetsa mphotho yaikulu. (Yobu 1:21; 31:6; 42:10; Yakobo 5:11) Momwemonso, chipiriro chathu lerolino monga “akuchita mawu” chidzatidzetsera chiyanjo cha Yehova.
18, 19. Kodi abale amene atsenderezedwa nthaŵi yaitali ‘akhala motani akuchita mawu,’ ndipo ntchito yawo yadzetsa dalitso lotani?
18 Ena amene apirira kwambiri zaka zonsezi ndi abale athu ku Eastern Europe. Popeza ziletso zambiri zachotsedwa tsopano, ameneŵa ‘akhaladi akuchita mawu’ m’malo awo atsopano. Amishonale ndi apainiya ochokera kumaiko apafupi asamukira kumeneko kukawathandiza kuphunzitsa ndi kulinganiza zinthu. Nthambi ya Finland ndi nthambi zina zapafupi za Watch Tower Society zatumiza akatswiri omanga nyumba, ndipo zopereka za abale padziko lonse zachirikiza kumangidwa kwa maofesi a nthambi ndi Nyumba za Ufumu.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:14, 15.
19 Abale amene anatsenderezedwa nthaŵi yaitali amenewo akhaladi achangu chotani nanga m’munda! Iwo ‘akugwiritsa ntchito ndi kuyesetsa’ kuti aupeze, titero kunena kwake, mwaŵi umene analibe mu “nthaŵi yovuta” imeneyo. (1 Timoteo 4:10; 2 Timoteo 4:2, NW) Mwachitsanzo, m’April wapita ku Albania, kumene anaponderezedwa mwankhanza, mitokoma yonse ya Uthenga wa Ufumu wamutu wakuti “Nchifukwa Ninji Moyo Uli ndi Mavuto Ochuluka Motere” inagaŵiridwa m’masiku atatu okha. Chimenechi chinali chochitika chosangalatsa pambuyo pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu, pamene panapezeka anthu 3,491—ochuluka kwambiri kuposa ofalitsa ake okangalika 538.
20. Kodi ziŵerengero zaposachedwapa za opezeka pa Chikumbutso zikusonyezanji, ndipo ambiri angathandizidwe motani?
20 Maiko enanso anawonjezerapo kwambiri pa chiŵerengero chapamwamba koposa cha opezeka pa Chikumbutso chimene chawonjezereka pazaka zaposachedwapa kuposa 10,000,000. M’madera ambiri, pokhala kuti chikhulupiriro chawo chalimbitsidwa mwa kupezekapo ndi kuchita Chikumbutso, atsopano ‘akukhala akuchita mawu.’ Kodi tingalimbikitse ambiri mwa atsopano ameneŵa kuti ayenerere mwaŵi umenewo?
21. Mogwirizana ndi lemba lathu la chaka, kodi tiyenera kulondola njira iti, ndi chonulirapo chotani?
21 Mofanana ndi Akristu aja achangu a m’zaka za zana loyamba, ndi ena ambiri chiyambire nthaŵiyo, tiyeni titsimikize mtima kuyesetsa ‘kulondola polekezerapo [“chonulirapo,”NW]’ cha moyo wosatha, kaya chikhale cha Ufumu wakumwamba kaya pa dziko lapansi. (Afilipi 3:12-14) Tiyenera kuyesayesa kuti tikapeze chonulirapocho. Ino si nthaŵi ya kubwevuka kukhala akumva okha, koma ndiyo nthaŵi yofunika koposa ya ‘kulimbika ndi kuchita ntchito.’ (Hagai 2:4; Ahebri 6:11, 12) Pokhala talandira ‘mawu ookedwa mwa ife,’ tiyeni ‘tikhale akuchita mawu achimwemwe’ tsopano ndi ku nthaŵi za nthaŵi.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi tingapirire motani ndi chimwemwe?
◻ Kodi “nzeru yochokera kumwamba” nchiyani, ndipo tingaifunefune motani?
◻ Nchifukwa ninji tiyenera ‘kukhala akuchita mawu, osati akumva okha’?
◻ Kodi ndi malipoti otani amene ayenera kutisonkhezera kukhala “akuchita mawu”?
[Chithunzi patsamba 17]
Nafenso tiyeni titsegule mitima yathu kuti ilandire chiphunzitso chaumulungu
[Chithunzi patsamba 18]
Yobu anafupidwa chifukwa cha umphumphu wake mwa kukhalanso ndi moyo wokhutiritsa ndi wachimwemwe limodzi ndi okondedwa ake