Moyo Wanu—Kodi Chifuno Chake Nchiyani?
“Mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, . . . kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani . . . masiku onse a moyo wawo.”—MLALIKI 2:3.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji sikulakwa kusamala za munthu mwini molinganiza?
INU mumasamala za inu mwini, si choncho kodi? Zimenezo zili bwino. Ndicho chifukwa chake timadya tsiku ndi tsiku, timagona titatopa, ndipo timakonda kukhala ndi mabwenzi ndi okondedwa athu. Nthaŵi zina timaseŵera, kusambira, kapena kuchita zinthu zina zimene timasangalala nazo, kusonyeza kuti timasamala za ife eni molinganiza.
2 Kusamala za umwini koteroko kumagwirizana ndi zimene Mulungu anasonkhezera Solomo kulemba: “Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake?” Mwa chidziŵitso cha zokumana nazo, Solomo anawonjezera nati: “Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera ku dzanja la Mulungu. Pakuti ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine.”—Mlaliki 2:24, 25.
3. Kodi ndi mafunso othetsa nzeru otani omwe anthu ochuluka satha kuwapezera mayankho?
3 Komabe mudziŵa inu kuti moyo suli chabe kudya, kumwa, kugona, ndi kuchita zinthu zina zabwino. Palinso zopweteka, zokhumudwitsa, ndi nkhaŵa zambiri. Ndipo timakhala otangwanidwa kwambiri kotero kuti sitimalingalira za cholinga cha moyo. Kodi sizili choncho kwa inunso? Vemont Royster, mkonzi wakale wa magazini a The Wall Street Journal, poona kukula kwa chidziŵitso ndi maluso a anthu, analemba kuti: “Chodabwitsa ndi ichi. Polingalira za munthu ndi mavuto ake, ndiponso za malo ake m’chilengedwe chonse, sitimadziŵa zambiri kwenikweni kuposa pachiyambi. Tidakali ndi mafunso akuti kodi ndife ayani, nchifukwa ninji tili ndi moyo ndipo tikupita kuti.”
4. Kodi nchifukwa ninji aliyense wa ife amafuna kukhala wokhoza kuyankha mafunso otikhudza?
4 Kodi mungawayankhe motani mafunsowa: Kodi ndife ayani? Nchifukwa ninji tili ndi moyo? Ndipo tikupita kuti? July wathayu, a Bambo Royster anamwalira. Kodi muganiza kuti iye anafa atapeza mayankho okhutiritsa? Tilunjikitse funso, Kodi pali njira imene mungapezere mayankhowo? Ndipo kutero kungakuthandizeni motani kukhala ndi moyo wachimwemwe chachikulu ndi wopindulitsa kwambiri? Tiyeni tione.
Magwero Opambana a Chidziŵitso
5. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kufuna chidziŵitso kwa Mulungu pamene tikufuna kupeza mayankho pa mafunso onena za cholinga chake cha moyo?
5 Akanatisiya kuti tifunefune tokha chifuno cha moyo wathu, sitikanatha kuchipeza, monga momwe amuna ndi akazi ambiri alepherera, ngakhale aja ophunzira kwambiri ndi odziŵa zochuluka. Koma sitili tokha. Mlengi wathu wapereka thandizo. Mutaganiza za iye, kodi sindiye Magwero opambana a chidziŵitso ndi nzeru, wokhalako “kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha,” ndi wodziŵa zonse za chilengedwe ndi mbiri yonse yakale? (Salmo 90:1, 2) Iye adalenga anthu ndipo waona moyo wonse wa munthu, choncho kuli kwa Iye kumene tingapeze chidziŵitso, osati kwa anthu opanda ungwiro, achidziŵitso chochepa ndi kuzindikira kwakung’ono.—Salmo 14:1-3; Aroma 3:10-12.
6. (a) Kodi Mlengi wapereka motani chidziŵitso chofunikira? (b) Kodi Solomo akuloŵetsedwamo motani?
6 Pamene kuli kwakuti sitingayembekezere Mlengi kutinong’onera m’khutu za cholinga cha moyo, iye wapereka magwero a chidziŵitso—Mawu ake ouziridwa. (Salmo 32:8; 111:10) Buku la Mlaliki nlothandiza kwambiri pankhaniyi. Mulungu anauzira mlembi wake, kotero kuti “nzeru ya Solomo inaposa nzeru za anthu onse a kummaŵa.” (1 Mafumu 3:6-12; 4:30-34) ‘Nzeru ya Solomo’ inachititsa chidwi kwambiri mfumukazi yodzacheza kwakuti iyo inali itangouzidwa dera lokha ndi kuti omvetsera nzeru yakewo adzakhaladi achimwemwe.a (1 Mafumu 10:4-8) Ifenso tingapeze chidziŵitso ndi chimwemwe m’nzeru yaumulungu imene Mlengi wathu anapereka kwa Solomo.
7. (a) Kodi Solomo ananenanji ataona zochitika zambiri pansi pa thambo? (b) Kodi nchitsanzo chotani chosonyeza kuti kupenda kwa Solomo kunali koona mtima?
7 Mlaliki akusonyeza nzeru yopatsidwa ndi Mulungu, imene inasonkhezera mtima ndi ubongo wa Solomo. Pokhala nayo nthaŵi, nyonga ndi chidziŵitso, Solomo anasanthula “zonse zimachitidwa pansi pa thambo.” Anaona kuti zambiri zinali “chabe ndi kungosautsa mtima,” kumene kunali kupenda zinthu kouziridwa kumene tiyenera kukumbukira pamene tilingalira za chifuno chathu m’moyo. (Mlaliki 1:13, 14, 16) Solomo analankhula mosabisa mawu ndi moona mtima. Mwachitsanzo, talingaliraninso mawu ake opezeka pa Mlaliki 1:15, 18. Mukudziŵa kuti kwa zaka mazana ambiri anthu ayesa njira zosiyanasiyana za maboma, nthaŵi zina ayesa moona mtima kuti athetse mavuto ndi kuwongolera mkhalidwe wa anthu. Komabe, kodi pali boma lililonse limene lawongoladi zinthu ‘zokhotakhota’ za dongosolo lopanda ungwiroli? Ndipo mwina mwaona kuti pamene munthu akhala ndi chidziŵitso chochuluka, mpamene amazindikiranso kuti m’nyengo yaifupi ya moyo wa munthu, nkosatheka kuwongolera zinthu zonse mokwanira. Kuzindikira koteroko kumalefula ambiri, koma osati ife ayi.
8. Kodi ndi zobwerezabwereza zotani zimene zakhalapo kuyambira kalekale?
8 Mfundo ina yoilingalira ndiyo kubwerezabwereza kwa zinthu kotikhudza, monga kutuluka ndi kuloŵa kwa dzuŵa kapena kayendedwe ka mphepo ndi madzi. Izo zinaliko m’masiku a Mose, Solomo, Napoléon, ndi m’masiku a agogo a agogo athu. Ndipo zidakapitirizabe. Mofananamo, “mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika.” (Mlaliki 1:4-7) Malinga ndi kuona kwa munthu, ndi zochepa zomwe zasintha. Anthu akale ndi amakono akhala ndi zochita zofanana, ziyembekezo, zikhumbo, ndi zipambano. Ngakhale kuti munthu winawake anatchuka kapena kupambana m’maonekedwe kapena maluso ena, kodi iye ali kuti tsopano? Anapita ndipo mwina ndi kuiŵalika anaiŵalika. Sitikunena zimenezi chifukwa cha mantha iyayi. Anthu ambiri satha ngakhale kutchula maina a agogo a agogo awo kapena kumene anabadwira kapena kumene anaikidwa. Mukhoza kuona chifukwa chake Solomo moona mtima anaona kuti zochita za munthu ndi zoyesayesa zake ndi chabe.—Mlaliki 1:9-11.
9. Kodi kupeza chidziŵitso chenicheni cha mkhalidwe wa anthu kungatithandize motani?
9 M’malo motilefula, chidziŵitso chaumulungu chimenechi ponena za mkhalidwe weniweni wa munthu chingatipindulitse, kutithandiza kusaika mtima wonse pa zonulirapo kapena zolinga zimene posachedwapa zidzapita ndi kuiŵalika. Chiyenera kutithandiza kupenda zimene tikupeza m’moyo ndi zimene tikuyesa kukwaniritsa. Mwachitsanzo, m’malo mokhala ndi moyo wodzimana zonse, tingapeze chimwemwe mwa kudya ndi kumwa molinganiza. (Mlaliki 2:24) Ndiponso, monga momwe tidzaonera, Solomo akumaliza ndi mfundo yabwino ndi yolimbikitsa kwambiri. Mwachidule, ndiyo yakuti tiyenera kuyamikira kwambiri unansi wathu ndi Mlengi wathu, yemwe angatithandize kupeza chimwemwe chosatha, mtsogolo mokhala ndi cholinga. Solomo anagogomezera kuti: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—Mlaliki 12:13.
Cholinga cha Moyo Poona Kubwerezabwereza Kwake
10. Kodi Solomo anayerekezera motani nyama ndi anthu?
10 Nzeru yaumulungu yosonyezedwa m’buku la Mlaliki ingatithandizenso kulingalira za chifuno cha moyo. Motani? Mwakuti Solomo anasumika maganizo moona mtima pa mfundo zina zoona zimene sitimaziganizira kaŵirikaŵiri. Ina ikunena za kufanana kwa anthu ndi nyama. Yesu anafanizira otsatira ake ndi nkhosa, komabe anthu samafuna kufanizidwa ndi nyama. (Yohane 10:11-16) Komabe Solomo anatchula mfundo zina zosakanika: “Mulungu awayese [ana a anthu] ndi kuti akazindikire eni ake kuti ndiwo nyama za kuthengo. Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; . . . ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe. . . . Onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.”—Mlaliki 3:18-20.
11. (a) Kodi moyo wa nyama ungalongosoledwe motani? (b) Kodi mumamva motani poona zimenezo?
11 Lingalirani za nyama imene mumakonda kuipenyerera, mwinamwake mbira kapena kalulu. (Deuteronomo 14:7; Salmo 104:18; Miyambo 30:26) Kapena mungalingalire za gologolo; iye ali m’mitundu 300 padziko lonse. Kodi moyo wake uli motani? Atabadwa, mayi wake amamlera kwa milungu ingapo. Posapita nthaŵi amatuluka ubweya ndi kuyamba kuyendayenda pabwalo pa chisa. Mutha kumuona akudumphadumpha uku ndi uku kufuna chakudya. Koma kaŵirikaŵiri amangoseŵera, akumasangalala paubwana wake. Atakula chaka chimodzi kapena zoposerapo, amapeza mkazi. Ndiyeno amamanga chisa kapena nkhwimba ndi kulereramo ana ake. Ngati apeza zipatso zokwanira, mtedza, ndi mbewu, banja la gologolo limanenepa ndipo limapeza nthaŵi yofutukula nyumba yawo. Koma patangopita zaka zoŵerengeka, nyamayo imakalamba ndipo siichedwa kugwera m’ngozi kapena kudwala. Pafupifupi zaka khumi amamwalira. Umenewo ndiwo moyo wa gologolo, kungosiyana pang’ono ndi mitundu yake ina.
12. (a) Kunena moona, kodi nchifukwa ninji moyo wa anthu ambiri uli wofanana ndi nyama? (b) Kodi tidzakumbukira chiyani tikadzaona nyama yomwe tinali nayo m’maganizo?
12 Anthu ochuluka sangadandaule ndi moyo woterowo ponena za nyama, ndipo samalingalira za gologolo kukhala ndi chifuno chabwino m’moyo. Komabe, moyo wa anthu ambiri sumasiyana kwambiri ndi umenewo, si choncho kodi? Iwo amabadwa ndi kuleredwa monga makanda. Amadya, kukula, ndi kuseŵera adakali achichepere. Posapita nthaŵi amakhala achikulire, amapeza wokwatirana naye, amafuna malo okhala ndi ntchito yopezera chakudya. Ngati ziwayendera bwino, amanenepa ndi kufutukula nyumba yawo (chisa) yosungiramo ana. Koma zaka zimatha msanga, ndipo amakalamba. Ngati achita mwaŵi, angamwalire atapyola zaka 70 kapena 80 zodzala ndi “chivuto ndi chopanda pake.” (Salmo 90:9, 10, 12) Mudzakumbukire mfundo zoona zimenezi pamene mudzaonanso gologolo (kapena nyama ina iliyonse imene munali nayo m’maganizo).
13. Kodi nchiyani chomwe chimachitikira nyama ndi anthu omwe?
13 Mutha kuona chifukwa chake Solomo anayerekezera moyo wa anthu ndi wa nyama. Analemba kuti: “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake . . . mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira.” Kunena za imfa, imagwera munthu ndi nyama yomwe, “monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso.” Anawonjeza kuti: “Onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.”—Mlaliki 3:1, 2, 19, 20.
14. Kodi anthu ena amayesa motani kusintha mkhalidwe wa moyo, koma chotsatirapo chimakhala chotani?
14 Kupenda zinthu moona mtima kumeneku tisakuone monga kofuna kukukhwethemulani. Kunena zoona ena ayesa kusintha mkhalidwe, monga kugwira ntchito zolimba kuti apeze chuma kuposa chimene makolo awo anali nacho. Angawonongere zaka zambiri kusukulu kuti apeze moyo wapamwamba, akumayesanso kukulitsa chidziŵitso chawo pa moyo. Kapena angasumike maganizo kuchita maseŵero olimbitsa thupi kapena kutsatira malangizo akadyedwe kena kake kopatsa thanzi labwinopo ndi kotalikitsako moyo pang’ono. Ndipo zoyesayesa zonsezi zingakhale ndi mapindu ena ake. Koma kodi ndani angatsimikize kuti zoyesayesa zimenezo zidzamthandiza? Ngakhale ngati zithandiza, kodi zingatero kufikira liti?
15. Kodi ndi kupenda kosabisa kanthu kotani kwa moyo wa anthu ambiri kumene kuli koona?
15 Solomo anafunsa kuti: “Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji? Pakuti ndani adziŵa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka mtsogolo mwake?” (Mlaliki 6:11, 12) Popeza imfa imadukiza msanga zoyesayesa za munthu, kodi palidi phindu lenileni kuti munthu alimbikire kupeza chuma chochuluka kapena kuwonongera zaka zambiri kusukulu kuti adzapeze zinthu zochuluka? Ndipo poti moyo ngwaufupi choncho, wodutsa ngati mthunzi, ena aona kuti pakhala palibenso nthaŵi ina yoti nkuyambiranso pa cholinga china chaumunthu atalephera pa cholinga chawo; ndi kuti munthu sangadziŵenso zimene zingachitikire ana ake “mtsogolo mwake.”
Ndi Nthaŵi Yopanga Dzina Labwino
16. (a) Kodi tiyenera kuchitanji zimene nyama sizitha kuchita? (b) Kodi ndi choonadi china chotani chomwe chiyenera kukhudza maganizo athu?
16 Kusiyana ndi nyama, ife anthu tili ndi nzeru ya kuganiza, ‘Kodi nchifukwa ninji ndili ndi moyo? Kodi wangokhala ulendo wokhala ndi polekezera, wokhala ndi nthaŵi yakubadwa ndi yakumwalira?’ Pa zimenezi, kumbukirani choonadi cha mawu a Solomo ponena za munthu ndi nyama: “Onse abweranso kufumbi.” Kodi zimenezo zikutanthauza kuti imfa ndiyo mapeto enieni a kukhalapo kwa munthu? Chabwino, Baibulo limasonyeza kuti anthu samakhala ndi sou yosafa imene imasiya thupi. Anthu ndiwo sou, ndipo sou imene ichimwa imafa. (Ezekieli 18:4, 20, NW) Solomo anafotokoza mfundoyo kuti: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiŵalika. Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”—Mlaliki 9:5, 10.
17. Kodi Mlaliki 7:1, 2 ayenera kutisonkhezera kulingalira za chiyani?
17 Chifukwa cha mfundo yosakanika imeneyo, lingalirani za mawuŵa: “Mbiri [“Dzina,” NW] yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa. Kumka ku nyumba ya maliro kupambana kumka ku nyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.” (Mlaliki 7:1, 2) Tiyenera kuvomereza kuti imfa yakhala “matsiriziro a anthu onse.” Palibe munthu amene anakhoza kutalikitsa moyo wake mwa kumwa mankhwala otalikitsa moyo, kudya msanganizo wa mavitameni, kutsatira njira ya kadyedwe, kapena mwa kuchita maseŵero alionse olimbitsa thupi. Ndipo kaŵirikaŵiri “angoiŵalika” mwamsanga atamwalira. Choncho nchifukwa ninji dzina “liposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa”?
18. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti Solomo anakhulupirira chiukiriro?
18 Monga momwe taonera, Solomo anali kunena zenizeni. Anadziŵa za makolo ake Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, omwe anapanga dzina labwino ndi Mlengi wathu. Pokhala wodziŵana bwino ndi Abrahamu, Yehova Mulungu analonjeza kumdalitsa iye ndi mbewu yake. (Genesis 18:18, 19; 22:17) Inde, Abrahamu anali ndi dzina labwino kwa Mulungu, nakhala bwenzi lake. (2 Mbiri 20:7; Yesaya 41:8; Yakobo 2:23) Abrahamu anadziŵa kuti moyo wake ndi moyo wa mwana wake sunali chabe mbali ya ulendo wosatha wa kubadwa ndi kumwalira. Panalidi cholinga chachikulu m’moyo kuposa zimenezo. Iwo anali ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kukhalanso ndi moyo, osati kuti anali ndi sou yosafa, koma chifukwa adzaukitsidwa. Abrahamu anali wotsimikiza kuti “Mulungu ngwokhoza kuukitsa [Isake], ngakhale kwa akufa.”—Ahebri 11:17-19.
19. Kodi tingapeze chidziŵitso chotani kwa Yobu ponena za tanthauzo la Mlaliki 7:1?
19 Imeneyo ndiyo kiyi kuti timvetse mmene kulili kuti ‘dzina labwino liposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.’ Monga Yobu iye asanakhaleko, Solomo anakhulupirira kuti Uyo amene analenga moyo wa munthu akhoza kuubwezeretsa. Akhoza kuukitsa anthu amene anafa. (Yobu 14:7-14) Yobu wokhulupirikayo anati: “[Yehova] mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:15) Talingalirani zimenezo! Yehova ‘kukhumba’ za atumiki ake okhulupirika omwe anamwalira. (“Mukanakonda kuonanso ntchito ya manja anu.”—The Jerusalem Bible.) Mwa kugwiritsira ntchito nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, Mlengiyo akhoza kuukitsa anthu. (Yohane 3:16; Machitidwe 24:15) Mwachionekere, anthu akhoza kusiyana ndi nyama wamba zomwe zimafa.
20. (a) Kodi ndi liti pamene tsiku la kumwalira lingapose tsiku la kubadwa? (b) Kodi chiukiriro cha Lazaro chiyenera kuti chawakhudza motani anthu ambiri?
20 Izi zikutanthauza kuti tsiku la imfa lingapose tsiku la kubadwa, ngati munthuyo anapanga dzina labwino kwa Yehova, amene akhoza kuukitsa okhulupirika amene amwalira. Solomo Wamkulu, Yesu Kristu, anasonyeza kuti zimenezo nzoona. Mwachitsanzo, anaukitsa mwamuna wokhulupirikayo Lazaro. (Luka 11:31; Yohane 11:1-44) Talingalirani, aja onse omwe anaona kuukitsidwa kwa Lazaro anakhudzidwa kwambiri, nakhulupirira Mwana wa Mulungu. (Yohane 11:45) Kodi muganiza iwo analibe chifuno m’moyo, osadziŵa kuti anali ayani ndi kumene anali kupita? M’malo mwake, anakhoza kuona kuti sanali monga nyama zongobadwa, kukhala ndi moyo kanthaŵi, ndiyeno nkufa. Chifuno chawo m’moyo chinali chogwirizana kwambiri ndi kudziŵa Atate wake wa Yesu ndi kuchita chifuniro Chake. Bwanji inuyo? Kodi nkhaniyi yakuthandizani kuona, kapena kuona bwino, mmene moyo wanu ungakhalire ndi chifuno chenicheni, ndi kuti uyeneradi kutero?
21. Kodi ndi mbali iti ya kupeza cholinga cha moyo imene tikufuna kudzaipenda?
21 Komabe, kukhala nacho chifuno chenicheni ndiponso chopindulitsa m’moyo kumaphatikizapo zoposa kulingalira za imfa ndi kukhalanso ndi moyo pambuyo pake. Kumaphatikizapo zimene timachita ndi moyo wathu tsiku ndi tsiku. Solomo anamveketsanso bwino zimenezo m’Mlaliki, monga tidzaonera m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a “Nkhani yonena za Mfumukaziyo ya ku Seba imagogomezera nzeru ya Solomo, ndipo nkhaniyo kaŵirikaŵiri yatchedwa nthano (1 M. 10:1-13). Koma nkhani yonse ikusonyeza kuti ulendo wa mfumukaziyo kwa Solomo kwenikweni unali wa zamalonda, ndipo zimenezi nzomveka; kuchitika kwake m’mbiri sikuyenera kukayikidwa.”—The International Standard Bible Encyclopedia (1988), Voliyumu IV, tsamba 567.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nyama ndi anthu ngolingana m’njira zotani?
◻ Kodi imfa imasonyeza motani kuti zoyesayesa zambiri za munthu ndi ntchito zake ndi chabe?
◻ Kodi tsiku la imfa lingapose motani tsiku la kubadwa?
◻ Kodi kukhala kwathu ndi chifuno chopindulitsa m’moyo kumadalira pa unansi wotani?
[Zithunzi patsamba 10]
Kodi moyo wanu umasiyana kwambiri motani ndi wa nyama?