Kodi Ndani Adzapulumuka “Tsiku la Yehova”?
“Muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu [“Yehova,” NW].”—2 PETRO 3:11, 12.
1. Kodi ndani amene agwira ntchito ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya?
YEHOVA MULUNGU wasankha pakati pa anthu, ena amene adzakhala oloŵa nyumba anzake a Mwana wake, Yesu Kristu, mu Ufumu wakumwamba. (Aroma 8:16, 17) Pamene akali padziko lapansi, Akristu odzozedwa agwira ntchito ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya. (Luka 1:17) M’nkhani yoyambayo, taona kufanana kwina pakati pa zochita zawo ndi zija za mneneri Eliya. Koma bwanji nanga za ntchito ya wotenga malo a Eliya, mneneri Elisa?—1 Mafumu 19:15, 16.
2. (a) Kodi chozizwitsa chomaliza cha Eliya chinali chotani, nanga choyamba cha Elisa? (b) Kodi pali umboni wotani wakuti Eliya sanapite kumwamba?
2 Chozizwitsa chomaliza chimene Eliya anachita nchija chogaŵa madzi a m’Mtsinje wa Yordano mwa kuwamenya ndi chofunda chake. Zimenezi zinatheketsa Eliya ndi Elisa kudutsa panthaka youma. Pamene anali kuyenda tsidya lakummaŵa la mtsinjewo, kavumvulu ananyamula Eliya kupita naye kwina padziko lapansi. (Onani bokosi patsamba 15 lakuti “Kodi Kumwamba Kwake Nkuti Kumene Eliya Anakwera?”) Chofunda cha Eliya nchimene chinatsala. Pamene Elisa anamenya nacho Yordano, madzi ake anagaŵikanso, kumtheketsa kubwerera panthaka youma. Chozizwitsa chimenechi chinasonyeza bwino lomwe kuti Elisa anali atatenga malo a Eliya pakuchirikiza kulambira koona m’Israyeli.—2 Mafumu 2:6-15.
Mikhalidwe Yaumulungu Njofunika
3. Kodi Paulo ndi Petro ananenanji za kukhalapo kwa Yesu ndi “tsiku la Yehova”?
3 Zaka mazana ambiri masiku a Eliya ndi Elisa atapita, atumwiwo Paulo ndi Petro anagwirizanitsa “tsiku la Yehova” lomwe likudza ndi kukhalapo kwa Yesu Kristu ndi “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” zimene nthaŵiyo zinali mtsogolo. (2 Atesalonika 2:1, 2; 2 Petro 3:10-13) Kuti tipulumuke tsiku lalikulu la Yehova—pamene Mulungu adzawononga adani ake ndi kupulumutsa anthu ake—tiyenera kufunafuna Yehova ndi kusonyeza chifatso ndi chilungamo. (Zefaniya 2:1-3) Koma pali mikhalidwe inanso imene ionekera pamene tiphunzira zochitika zokhudza mneneri Elisa.
4. Kodi changu chimathandiza motani mu utumiki wa Yehova?
4 Kuti tipulumuke “tsiku la Yehova” tiyenera kukhala achangu pautumiki wa Mulungu. Eliya ndi Elisa anali achangu pautumiki wa Yehova. Ndi changu chofananacho, Akristu odzozedwa otsalira lerolino akuchita utumiki wopatulika kwa Yehova ndipo akutsogolera pantchito yolalikira uthenga wabwino.a Chiyambire m’zaka zapakati za m’ma 1930, iwo alimbikitsa onse olandira uthenga wa Ufumu komanso ofuna kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi kuti adzipatulire kwa Yehova nabatizidwe. (Marko 8:34; 1 Petro 3:21) Miyandamiyanda alabadira chilimbikitso chimenechi. Kalelo anali mumdima wauzimu, ndiponso akufa chifukwa cha uchimo, koma tsopano aphunzira choonadi cha Mulungu, alandira chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso wa padziko lapansi, ndipo ngachangu mu utumiki wa Yehova. (Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3-5) Mwa changu chawo, mgwirizano, kuchereza kwawo, ndi ntchito zina zabwino, amadzetsa mpumulo waukulu kwa abale auzimu a Kristu amene akali padziko lapansi.—Mateyu 25:31-46.
5. Kodi nchifukwa ninji kuchitira “abale” a Yesu zinthu zabwino nkofunika kwambiri, ndipo tili ndi chitsanzo chotani cha m’tsiku la Elisa?
5 Amene achitira “abale” a Yesu zabwino chifukwa chakuti odzozedwawa ali otsatira ake ali ndi chiyembekezo cha kupulumuka “tsiku la Yehova.” Mwamuna wina ndi mkazi wake m’mudzi wa Sunemu anadalitsidwa kwambiri chifukwa chokomera mtima ndi kuchereza Elisa ndi mnyamata wake. Okwatirana ameneŵa analibe mwana, ndipo mwamunayo anali wokalamba. Koma Elisa analonjeza mkazi wa ku Sunemu ameneyu kuti adzabala mwana wamwamuna, ndipo zinaterodi. Pamene mwana wamwamuna yekhayu anafa zaka zambiri pambuyo pake, Elisa anapita ku Sunemu nakamuukitsa. (2 Mafumu 4:8-17, 32-37) Anali mapindu aakulu chotani nanga a kuchereza Elisa!
6, 7. Kodi Namani anapereka chitsanzo chotani, ndipo kodi chimenechi chimakhudza motani kupulumuka “tsiku la Yehova”?
6 Tifunikira kudzichepetsa kuti tilandire chitsogozo cha m’Malemba chochokera kwa “abale” a Kristu ndi kukhala ndi chiyembekezo chokapulumuka tsiku la Yehova. Namani, kazembe wa khamu lankhondo wachiaramu wakhateyo anadzichepetsa kuti amve lingaliro la buthu lachiisrayeli logwidwa ndi kufunafuna machiritso mwa kupita ku Israyeli kukapeza Elisa. M’malo motuluka m’nyumba mwake kukaonana ndi Namani, Elisa anamtumizira uthenga uwu wakuti: “Kasambe m’Yordano kasanu ndi kaŵiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.” (2 Mafumu 5:10) Namani wonyadayo anapwetekedwa mtima, ndipo anakwiya, koma atapita modzichepetsa nakamira kasanu ndi kaŵiri m’Yordano, “mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng’ono, nakonzeka.” (2 Mafumu 5:14) Asanabwerere kwawo, Namani anayendanso ulendo wobwerera ku Samariya kukathokoza mneneri wa Yehova. Pokhala wotsimikiza mtima kusapanga phindu lakuthupi ndi mphamvu zopatsidwa ndi Mulungu, Elisa anatuluka kukaonana ndi Namani koma anakana kulandira mphatso iliyonse. Modzichepetsa, Namani anauza Elisa kuti: “Mnyamata wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu ina, koma kwa Yehova.”—2 Mafumu 5:17.
7 Mwa kutsatira modzichepetsa uphungu wa m’Malemba wa odzozedwa, miyandamiyanda adalitsidwa kwambiri lerolino. Ndiponso, mwa kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu, anthu oona mtima ameneŵa ayeretsedwa mwauzimu. Iwo tsopano ali ndi mwaŵi wa kukhala mabwenzi a Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. (Salmo 15:1, 2; Luka 16:9) Ndipo kudzipereka kwawo kwa Mulungu ndi utumiki wake kudzafupidwa mwa kupulumuka kwawo chiwonongeko chosatha chimene chili pafupi kugwera ochimwa onyada ndi osalapa pa “tsiku la Yehova” limene likufika msangali.—Luka 13:24; 1 Yohane 1:7.
“Ali Ndi Ine Ndani? Ndani?”
8. (a) Kodi ndi motani mmene awo amene adzapulumuka “tsiku la Yehova” amaonera kuchita chifuniro cha Mulungu? (b) Kodi Yehu anapatsidwa ntchito yotani? (c) Kodi nchiyani chinali kudzachitikira Yezebeli?
8 Ofuna kupulumuka “tsiku la Yehova” ayeneranso kukhala otsimikiza pochita chifuniro cha Mulungu. Molimba mtima, Eliya ananeneratu za chiwonongeko cha banja lambanda ndi lolambira Baala la Mfumu Ahabu. (1 Mafumu 21:17-26) Komabe, chiwonongeko chimenechi chisanachitike, wotenga malo a Eliya, Elisa, anayenera kumaliza ntchito ina yosamalizidwa. (1 Mafumu 19:15-17) Panthaŵi yake ya Yehova, Elisa analamula mnyamata wake kukadzoza kazembe wankhondo Yehu kukhala mfumu yatsopano ya Israyeli. Atatsanulira mafuta pamutu pa Yehu, mthengayo anamuuza kuti: “Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisrayeli. Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebeli. Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzawonongeka.” Mfumukazi yoipayo Yezebeli inali kudzaponyedwa kwa agalu ndi kusaikidwa m’manda mwamwambo.—2 Mafumu 9:1-10.
9, 10. Kodi mawu a Eliya onena za Yezebeli anakwaniritsidwa motani?
9 Anyamata a Yehu anazindikira kuti iye wadzozedwadi ndipo anamlengeza kuti ndiye mfumu yatsopano ya Israyeli. Pochitapo kanthu motsimikiza, Yehu anathamangira ku Yezreeli kukayamba ntchito yake ya kupha atsogoleri ampatuko a kulambira Baala. Woyamba kuphedwa ndi muvi wakupha wa Yehu anali mwana wa Ahabu, Mfumu Yoramu. Anapita pagaleta kunja kwa mzinda kukafunsa ngati Yehu anadza ndi mtendere. “Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mayi wako Yezebeli?” anayankha motero Yehu. Atatero, muvi wa Yehu unapyoza mtima wa Yoramu.—2 Mafumu 9:22-24.
10 Akazi oopa Mulungu samafuna kukhala ngati Yezebeli kapena aliyense wonga iyeyo. (Chivumbulutso 2:18-23) Pomwe Yehu amadzafika ku Yezreeli, Yezebeli anali atayesa kudzikongoletsa. Akumasuzumira pazenera, anamlonjera ndi chiopsezo. Yehu anafunsa anyamata a mkaziyo nati: “Ali ndi ine ndani? Ndani?” Pomwepo, adindo aŵiri kapena atatu anasuzimira. Kodi anali kumbali ya Yehu? “Mgwetsereni pansi,” anawauza motero. Pomwepo, anachitapo kanthu motsimikiza, kuponya Yezebeli woipayo kunja pazenera. Anampondaponda, mwina ndi akavalo. Pamene anthu anabwera kudzamuika, “sanapezako kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.” Kunalidi kukwaniritsidwa kochititsa chidwi kwa mawu a Eliya akuti: “Agalu adzadya mnofu wa Yezebeli”!—2 Mafumu 9:30-37.
Kuchirikiza Kulambira Koona ndi Mtima Wonse
11. Kodi Yehonadabu anali yani, ndipo anasonyeza motani kuti akuchirikiza kulambira koona?
11 Awo ofuna kupulumuka “tsiku la Yehova” ndi kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi ayenera kuchirikiza kulambira koona ndi mtima wonse. Ayenera kukhala monga Yehonadabu, kapena kuti Yonadabu, wolambira Yehova wosakhala Mwiisrayeli. Pamene Yehu anapitiriza kuchita ntchito yake mwachangu, Yehonadabu anafuna kusonyeza chiyanjo chake ndi chichirikizo chake. Choncho anapita kukakumana ndi mfumu yatsopano ya Israyeli, imene inali kupita ku Samariya kukapha otsalira a nyumba ya Ahabu. Ataona Yehonadabu, Yehu anafunsa kuti: “Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nawo mtima wako?” Kuvomera kwa Yehonadabu kunachititsa Yehu kutansa dzanja lake ndi kuitanira Yehonadabu m’galeta lake lankhondo, nati: “Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova.” Mosazengereza, Yehonadabu analandira mwaŵiwo wosonyeza kuti akuchirikiza wakupha wodzozedwa wa Yehova.—2 Mafumu 10:15-17.
12. Kodi nchifukwa ninji Yehova amafuna kulambira kosagaŵanika moyenerera?
12 Kuchirikiza kulambira koona ndi mtima wonse nkoyeneradi, popeza Yehova ndiye Mlengi ndi Mfumu ya Chilengedwe Chonse, amene moyenerera amafuna kulambira kosagaŵanika ndipo ngwoyenereradi kukulandira. Analamula Aisrayeli kuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi padziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.” (Eksodo 20:4, 5) Ofuna kupulumuka “tsiku la Yehova” ayenera kulambira yekhayo basi, kuchita zimenezo “mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:23, 24) Ayenera kukhala osasunthika pa kulambira koona, monga Eliya, Elisa, ndi Yehonadabu.
13. Monga momwe mtima wa Yehonadabu unavomerezerana ndi wa Yehu, kodi ndani akuvomera Mfumu Yaumesiya, ndipo kodi akuzisonyeza motani?
13 Atapha a m’nyumba ya Ahabu, Mfumu Yehu anachitaponso kanthu kuti adziŵe olambira Baala ndi kuchotsa chipembedzo chonyengachi m’Israyeli. (2 Mafumu 10:18-28) Lerolino, Mfumu yakumwamba Yesu Kristu yaikidwa kupha adani a Yehova ndi kukweza uchifumu Wake. Monga momwe mtima wa Yehonadabu unavomerezerana ndi wa Yehu, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za Yesu lerolino zimavomera ndi mtima wonse kuti Kristu ndiye Mfumu Yaumesiya ndipo imagwirizana ndi abale ake auzimu padziko lapansi. (Chivumbulutso 7:9, 10; Yohane 10:16) Amapereka umboni wa zimenezi mwa kukhala m’chipembedzo choona ndi kuchita nawo mwachangu mu utumiki wachikristu, kuchenjeza adani a Mulungu za “tsiku la Yehova” limene likufika msangalo.—Mateyu 10:32, 33; Aroma 10:9, 10.
Zochitika Zoopsa Zili Patsogolopa!
14. Kodi nchiyani chikuyembekezera chipembedzo chonyenga mtsogolomu?
14 Yehu anachitapo kanthu kuti athetse kulambira Baala m’Israyeli. M’tsiku lathu, kudzera mwa Yehu Wamkulu, Yesu Kristu, Mulungu adzawononga Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Posachedwapa tidzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a mngelo kwa mtumwi Yohane akuti: “Nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo [Babulo Wamkulu], nizidzamkhalitsa wabwinja wausiŵa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto. Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwawo kuchita za m’mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wawo kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mawu a Mulungu.” (Chivumbulutso 17:16, 17; 18:2-5) “Nyanga khumi” zimaimira maulamuliro andale ankhondo amene akulamulira dziko lapansi. Ngakhale kuti tsopano iwo ali paunansi wachisembwere mwauzimu ndi Babulo Wamkulu, nthaŵi yake yafupika. Ulamuliro wandale wa dzikoli udzawononga chipembedzo chonyenga, ndipo “chilombo”—United Nations—chidzachita mbali yaikulu pamodzi ndi “nyanga khumi” pomuwononga.b Ndi nthaŵi yabwino chotani nanga yotamandira Yehova.—Chivumbulutso 19:1-6.
15. Kodi chidzachitika nchiyani atayesa kuwononga gulu la Mulungu la padziko lapansi?
15 Mfumu Yehu atafafaniza kulambira Baala, nyumba yake yachifumu inasumika maganizo pa mitundu yodana ndi Israyeli. Mfumu Yesu Kristu adzachitanso chimodzimodzi. Maulamuliro andale adzakhalapobe chipembedzo chonyenga chonga cha Baala chitawonongedwa. Mosonkhezeredwa ndi Satana Mdyerekezi, adani ameneŵa a uchifumu wa Yehova adzaukira mwamphamvu gulu la padziko lapansi la Mulungu kuti aliwononge. (Ezekieli 38:14-16) Koma Yehova adzalola Mfumu Yesu Kristu kuwakantha mwa kuwawononga pa Har–Magedo, “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” kukwaniritsa kotheratu kukwezeka kwa uchifumu wa Yehova!—Chivumbulutso 16:14, 16; 19:11-21; Ezekieli 38:18-23.
Kutumikira Ndi Changu cha Elisa
16, 17. (a) Kodi tikudziŵa motani kuti Elisa anali wachangu mpaka kumapeto kwa moyo wake? (b) Kodi tiyenera kuchitanji ndi mivi ya choonadi?
16 Mpaka pamene “tsiku la Yehova” lidzathetse dongosolo lonse loipa la zinthu la Satana, atumiki a Mulungu adzakhalabe olimba mtima ndi achangu monga Elisa. Kusiyapo ntchito yake monga mnyamata wa Eliya, Elisa anatumikira payekha monga mneneri wa Yehova zaka zoposa 50! Ndipo Elisa anali wachangu mpaka kumapeto a moyo wake wautaliwo. Kutangotsala pang’ono kuti afe, mdzukulu wa Yehu, Mfumu Yoasi, anamchezera. Elisa anamuuza kulasa muvi kunja pazenera. Muviwo unathamanga kukamenya chandamale chake, ndipo Elisa anafuula nati: “Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m’Afeki mpaka mudzawatha.” Atapemphedwa ndi Elisa, Yoasi kenako analasa pansi ndi mivi yake. Koma zimenezi sanazichite mwachangu, nalasa katatu kokha. Kenako Elisa anati, chifukwa cha chimenecho, Yoasi adzapatsidwa chilakiko pa Aaramu katatu kokha, ndipo ndizo zinachitikadi. (2 Mafumu 13:14-19, 25) Mfumu Yoasi sanawakanthe kotheratu Aaramu, ‘mpaka kuwatha.’
17 Komabe, ndi changu monga cha Elisa, otsalira odzozedwa akupitirizabe kumenyana ndi kulambira konyenga. Atsamwali awo oyembekezera kukhala padziko lapansi akuchitanso chimodzimodzi. Ndiponso, onse ofuna kupulumuka “tsiku la Yehova” amachita bwino kukumbukira mawu a Elisa wachanguyo onena za kulasa dziko lapansi. Tiyeni titenge mivi ya choonadi ndi kuiponya mwachangu—mobwerezabwereza—inde, mpaka Yehova atati ntchito yathu ndi miviyo yatha.
18. Kodi tiyenera kuwalabadira motani mawu a pa 2 Petro 3:11, 12?
18 “Tsiku la Yehova” posachedwapa lidzathetsa dongosolo loipa la zinthu lilipoli. Chotero mawu olimbikitsa a mtumwi Petro atisonkhezere. “Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero,” Petro anatero, “muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo [“kudzipereka kwaumulungu,” NW], akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:11, 12) Mbali iliyonse ya dongosolo lino itasungunuka ndi moto wa ukali wa Mulungu wosonyezedwa kudzera mwa Yesu Kristu, okhawo a mbiri ya mayendedwe oongoka ndi kudzipereka kwaumulungu ndiwo adzapulumuka. Chiyero chamakhalidwe ndi chauzimu nchofunika. Momwemonso chikondi cha pa anthu anzathu, chosonyezedwa mwa kusamalira zosoŵa zawo, makamaka mwauzimu mwa utumiki wathu wachikristu.
19. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikapulumuke “tsiku la Yehova”?
19 Kodi mawu anu ndi zochita zanu zimakudziŵikitsani kuti ndinu mtumiki wa Mulungu wokhulupirika ndi wachangu? Ngati zili choncho, mutha kuyembekezera kupulumuka “tsiku la Yehova” kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu lolonjezedwalo. Inde, mukhoza kupulumuka ngati muchitira abale a Kristu auzimu zabwino chifukwa chakuti ali otsatira ake, monga momwe banja lija la ku Sunemu linacherezera Elisa. Kuti mupulumuke muyenera kukhalanso monga Namani, amene analandira malangizo aumulungu modzichepetsa nakhala wolambira Yehova. Ngati mukulakalaka kudzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso wa padziko lapansi, muyenera kuchirikiza kulambira koona ndi mtima wonse, monga anachitira Yehonadabu. Ndiye kuti mudzakhala pakati pa atumiki okhulupirika a Yehova, amene posachedwapa adzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu akuti: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.”—Mateyu 25:34.
[Mawu a M’munsi]
a Onani mitu 18 ndi 19 ya buku la “Let Your Name Be Sanctified,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Onani masamba 254-6 a Revelation—Its Grand Climax At Hand!, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndi mikhalidwe ina yotani yofunika kuti tipulumuke “tsiku la Yehova”?
◻ Kodi banja la ku Sunemu m’tsiku la Elisa linapereka chitsanzo chotani?
◻ Kodi tingaphunzirepo phunziro lotani pankhani ya Namani?
◻ Kodi chitsanzo cha Yehonadabu tingachitsatire motani?
◻ Kodi 2 Petro 3:11, 12 ayenera kutikhudza motani?