Gulu la Yehova Limachirikiza Utumiki Wanu
“Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha.”—CHIVUMBULUTSO 14:6.
1. Kodi Mboni za Yehova zayesedwa motani, nanga nchifukwa ninji zachirimika?
KODI nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kuzindikira ntchito ya gulu la Yehova lakumwamba yochirikiza utumiki wachikristu? Chabwino, kodi Mboni za Yehova zikanatha kukwaniritsa ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu wa Mulungu m’dziko lonse laudanili popanda chichirikizo cha makamu a Yehova akumwamba? Mboni zachita ntchito yolalikira imeneyi m’zaka za zana lodzala ndi utundu womkitsa, olamulira andale ankhanza, nkhondo zadziko lonse, ndiponso masoka osiyanasiyana. Popanda thandizo la Yehova, kodi Mboni zimenezi zikanatha kuchirimika pachopinga cha chizunzo chankhanza ndiponso kaŵirikaŵiri choopsa chomwe zimayang’anizana nacho?—Salmo 34:7.
Kuchirimikabe Mosasamala Kanthu za Chitsutso cha Padziko Lonse
2. Kodi pali kufanana kotani pakati pa Akristu oona a m’zaka za zana loyamba ndi a lerolino?
2 M’zaka zino za zana la 20, adani achipembedzo ndiponso andale, adzetsa zopinga zosiyanasiyana, zokhudzana ndi malamulo ndi zinanso zambiri, pofuna kulepheretsa kapena kufooketsa ntchito ya Yehova. Abale ndi alongo achikristu azunzidwa, kunenezedwa—ambirinso aphedwa—ndipo kaŵirikaŵiri amasonkhezera zimenezo ndiwo atsogoleri achipembedzo a Babulo Wamkulu. Tinganene mofanana ndi mmene ananenera za Akristu oyambirira kuti, “pakuti za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.” Mongadi momwe atsogoleri achipembedzo achiyuda a m’nthaŵi ya Kristu anamenyera zolimba kuti alepheretse utumiki wake, atsogoleri achipembedzo ndi ampatuko, mogwirizana ndi mabwenzi awo andale, ayesetsa kulepheretsa ntchito yaikulu yochitira umboni ya anthu a Yehova.—Machitidwe 28:22; Mateyu 26:59, 65-67.
3. Kodi tingaphunzireponji pa kukhulupirika kwa Henryka Żur?
3 Mwachitsanzo, tiyeni tilingalirepo zomwe zinachitika ku Poland pa March 1, 1946. Henryka Żur, mtsikana wa Mboni wazaka 15 wokhala pafupi ndi Chełm, anatsagana ndi wa Mboni wina, mbale, paulendo wokachezera anthu okondwerera a m’mudzi wapafupi nawo. Iwo anagwidwa ndi gulu lankhondo la Akatolika lotchedwa Narodowe Siły Zbrojne (Ankhondo a m’Dzikomo). Mbaleyo anamenyedwa kwambiri koma anathaŵa napulumutsa moyo wake. Koma sizinali choncho ndi Henryka. Iye anazunzidwa mwankhanza kwa maola ambiri pamene anali kuyesa kumkakamiza kuti asonyeze chizindikiro cha mtanda chachikatolika. Mmodzi mwa amene anali kumzunzawo anati: “Kaya uli ndi chikhulupiriro chotani, ife tikungofuna kuti usonyeze chizindikiro cha mtanda chachikatolika basi. Ngati ulephera kutero tikuombera mfuti!” Kodi iye anafooka pachikhulupiriro chake? Ayi. Anthu achipembedzo opanda nzeruwo anamguguzira m’nkhalango ina namuombera mfuti. Komatu iye anapambanabe! Iwo analephera kufooketsa chikhulupiriro chake.a—Aroma 8:35-39.
4. Kodi magulu andale ndi achipembedzo ayesa motani kuthetsa ntchito yolalikira Ufumu?
4 Kwa zaka zoposa zana limodzi, atumiki amakono a Mulungu akhala akuchitiridwa mwankhanza ndiponso mopanda ulemu. Popeza kuti Mboni za Yehova sizili, ndipo sizifuna kukhala mbali ya zipembedzo za Satana zamakono, izo zimaonedwa monga zoyenerera kunenezedwa zabodza ndi kuukiridwa. Izo zaukiridwa mochititsa mantha ndi magulu andale. Mboni zambiri zaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ngakhale maboma omwe amati ngokomera anthu onse ayesanso kulepheretsa ntchito yolalikira uthenga wabwino. Kalelo mu 1917 ku Canada ndi ku United States, atsogoleri achipembedzo analimbikitsa zotsutsa Ophunzira Baibulo, dzina lapanthaŵiyo la Mboni. Akuluakulu a Watch Tower Society anaponyedwa m’ndende popanda chifukwa koma pambuyo pake anamasulidwa.—Chivumbulutso 11:7-9; 12:17.
5. Kodi ndi mawu ati omwe alimbikitsa atumiki a Yehova?
5 Satana wagwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana poyesa kulepheretsa ntchito yochitira umboni ya abale ake a Kristu ndi anzawo okhulupirika. Komabe, monga momwe zokumana nazo zambirimbiri zikusonyezera, ziopsezo, zikakamizo, kumenyedwa, kuponyedwa m’ndende, m’misasa yachibalo, ndipo ngakhale imfa yeniyeniyo sinafooketse Mboni za Yehova. Ndipotu zimenezi zakhala zikuchitika kuyambira kalekale. Mobwerezabwereza, mawu awa a Elisa akhala olimbikitsa: “Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” Chifukwa china nchakuti angelo okhulupirika ali ochuluka kuposa makamu a Mdyerekezi!—2 Mafumu 6:16; Machitidwe 5:27-32, 41, 42.
Yehova Adalitsa Olalikira Mwakhama
6, 7. (a) Kodi ndi njira zoyambirira ziti zomwe zinagwiritsiridwa ntchito polalikira uthenga wabwino? (b) Kodi ndi kusintha kothandiza kuti komwe kunachitika kuyambira mu 1943?
6 M’zaka zonse za zana la 20, Mboni za Yehova zagwiritsira ntchito njira zambiri zasayansi kuti zifutukule ndi kufulumiza ntchito yaikulu yochitira umboni mapeto asanafike. Kalelo mu 1914, Pasitala Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Bible and Tract Society, anayambitsa zogwiritsira ntchito zithunzi zapakanema zofotokozedwa pogwiritsira ntchito nkhani ya m’Baibulo yojambulidwa pamalekodi a galamafoni m’kanema ya maola asanu ndi atatu yotchedwa “The Photo-Drama of Creation” (Seŵero Lapakanema la Chilengedwe). Linachititsa chidwi anthu openyerera m’maiko ambiri panthaŵiyo. Pambuyo pake, m’ma 1930 ndi m’ma 1940, Mboni zinatchuka ndi ntchito yawo yolalikira kunyumba ndi nyumba pogwiritsira ntchito magalamafoni osavuta kunyamula, okhala ndi nkhani za m’Baibulo zojambulidwa zokambidwa ndi J. F. Rutherford, pulezidenti wachiŵiri wa Sosaite.
7 Mu 1943, anayamba kugwiritsira ntchito njira ina mopanda mantha motsogoleredwa ndi Nathan H. Knorr, pulezidenti wachitatu wa Sosaite, pamene analinganiza zokhazikitsa sukulu ya utumiki mumpingo uliwonse. Mbonizo zinali kuphunzitsidwa mmene zingalalikirire ndi kuphunzitsa kunyumba ndi nyumba popanda kugwiritsira ntchito zojambula za pagalamafoni. Kuyambira nthaŵiyo, masukulu ena akhazikitsidwanso ophunzitsa amishonale, apainiya a nthaŵi zonse, akulu a m’mipingo, ndi oyang’anira odalirika a nthambi za Watch Tower Society. Kodi chotsatirapo chake chakhala chotani?
8. Kodi Mboni zinasonyeza motani chikhulupiriro chachikulu mu 1943?
8 Mu 1943, Nkhondo Yadziko II ikumenyedwabe, panali Mboni zokangalika 129,000 zokha m’maiko 54. Komabe, ndizo zinali ndi chikhulupiriro chachikulu ndi chidaliro chakuti Mateyu 24:14 adzakwaniritsidwa mapeto asanafike. Iwo anatsimikiza kuti Yehova adzaonetsetsa kuti uthenga wofunika wochenjeza ulengezedwe kaye zisanadze zochitika zosiyanasiyana zomwe zidzathetsa dongosolo loipa lilipoli. (Mateyu 24:21; Chivumbulutso 16:16; 19:11-16, 19-21; 20:1-3) Kodi khama lawolo lafupidwa?
9. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zikusonyeza kuti ntchito yochitira umboni yapita patsogolo?
9 Tsopano pali maiko pafupifupi 13 omwe ali ndi Mboni zokangalika zoposa 100,000 m’dziko lililonse. Angapo a maikowa ndi maiko amene Tchalitchi cha Katolika chinafalikira kwambiri. Komabe, taonani zochitikazi. Dziko la Brazil lili ndi ofalitsa uthenga wabwino okwanira 450,000, ndipo anthu oposa 1,200,000 anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu mu 1997. Chitsanzo china ndicho Mexico yemwe ali ndi Mboni pafupifupi 500,000 ndipo anthu oposa 1,600,000 anapezeka paphwando la Chikumbutso. Maiko ena achikatolika ndiwo Italy (wokhala ndi Mboni ngati 225,000), France (Mboni pafupifupi 125,000), Spain (Mboni zoposa 105,000), ndi Argentina (Mboni zoposa 115,000). Ku United States, kumene kuli zipembedzo zambiri zachiprotestanti, Chikatolika, ndi Chiyuda, kuli Mboni 975,000 ndipo anthu oposa 2,000,000 anapezeka pa Chikumbutso. Ndithudi, khamu lalikulu likuchoka ku Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, wokhala ndi ziphunzitso zosamveka ndipo akutembenukira ku malonjezo a Mulungu osavuta kumva ndi oona a “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano.”—2 Petro 3:13; Yesaya 2:3, 4; 65:17; Chivumbulutso 18:4, 5; 21:1-4.
Kuchita Mogwirizana ndi Zosoŵa za Anthu
10. Kodi mikhalidwe yasintha motani m’madera ena?
10 Ambiri amene atembenukira kwa Yehova kudzera mwa Kristu Yesu anafikiridwa pamaulendo a kunyumba ndi nyumba. (Yohane 3:16; Machitidwe 20:20) Koma pali njira zinanso zomwe zagwiritsiridwa ntchito. Zinthu zasintha, ndipo mkhalidwe wa zachuma wapangitsa kuti akazi ambiri tsopano aziloŵa ntchito. Kaŵirikaŵiri, mkati mwa mlungu, pali anthu ochepa amene amapezeka panyumba. Choncho, Mboni za Yehova zikuchita mogwirizana ndi mkhalidwewu. Monga Yesu ndi ophunzira oyambirira, iwo amapita kumene kumapezeka anthu ndipo amapitako panthaŵi yake.—Mateyu 5:1, 2; 9:35; Marko 6:34; 10:1; Machitidwe 2:14; 17:16, 17.
11. Kodi nkuti komwe Mboni za Yehova zikulalikira lerolino, ndipo kodi zotsatirapo zake nzotani?
11 Mboni zikuchitapo kanthu kuti zilalikire mwanzeru kwa anthu m’malo akuluakulu oimikapo magalimoto, m’masitolo, m’mafakitale, m’maofesi ndi m’malo a zamalonda, m’masukulu, kupolisi, pamalo omwetsera mafuta, m’mahotela ndi m’malesitilanti, ndiponso m’misewu. Ndithudi, izo zimalalikira kulikonse kumene kumapezeka anthu. Ndipo ngati anthu ali panyumba, Mboni zimapitirizabe kuwafikira panyumbapo. Njira imeneyi yosavuta ndiponso yothandiza yachititsa kuti zofalitsa zambiri zofotokoza Baibulo zigaŵiridwe. Anthu onga nkhosa akupezeka. Maphunziro atsopano a Baibulo akuyambidwa. Ntchito yophunzitsa yaikulu kwambiri m’mbiri yonse ya mtundu wa anthu ikuchitika mwachangu ndi atumiki odzifunira oposa mamiliyoni asanu ndi theka! Kodi muli ndi mwayi wokhala mmodzi wa iwo?—2 Akorinto 2:14-17; 3:5, 6.
Kodi Nchiyani Chomwe Chimasonkhezera Mboni za Yehova?
12. (a) Kodi Yehova akuphunzitsa anthu ake motani? (b) Kodi zotsatirapo za chiphunzitso chimenechi nzotani?
12 Kodi gulu la Mulungu lakumwamba limathandizapo motani pantchito yonseyi? Yesaya analosera kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Yehova akuphunzitsa abale ogwirizana a padziko lonse ameneŵa kudzera mwa gulu lake looneka la padziko lapansi—pa Nyumba za Ufumu, pamisonkhano yaikulu. Zimenezi zimadzetsa umodzi ndi mtendere. Chiphunzitso cha Yehova chadzetsa anthu apadera, ophunzitsidwa kukondana wina ndi mnzake ndi kukonda mnansi wawo monga momwe adzikondera iwo eni, osati kuda anansi awo, ndipo amachita zimenezi kulikonse kumene amakhala m’dziko lino latsankhu ndi logaŵanika.—Mateyu 22:36-40.
13. Kodi tingatsimikizire motani kuti angelo amatsogolera pantchito yolalikira?
13 Chikondi ndicho chimasonkhezera Mboni za Yehova kuti zipitirizebe kulalikira mosasamala kanthu kuti pali ena amene safuna kumvetsera kapena amene amawazunza. (1 Akorinto 13:1-8) Izo zimadziŵa kuti ntchito yawo imeneyi yopulumutsa moyo ikutsogozedwa kuchokera kumwamba, monga momwe Chivumbulutso 14:6 chikunenera. Kodi ndi uthenga wotani umene ukulalikidwa mwa chitsogozo cha angelo? “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe a madzi.” Ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu imakweza dzina la Yehova. Anthu akupemphedwa kupereka ulemerero kwa Mlengi, Mulungu, osati kwa zolengedwa ndi chisinthiko chopanda pakecho ayi. Ndipo kodi nchifukwa ninji ntchito yolalikira imeneyi ifunikira kuchitidwa mwachangu? Chifukwa chakuti ola lachiweruzo lafika—chiweruzo cha Babulo Wamkulu ndi mbali zonse za dongosolo la zinthu looneka la Satana.—Chivumbulutso 14:7; 18:8-10.
14. Kodi ndani amene akuchita ntchito yolalikira yaikulu imeneyi?
14 Palibe Mkristu wodzipatulira aliyense amene ntchito yolalikirayi sikumkhudza. Akulu osamala zinthu zauzimu amatsogolera pantchito yolalikira pamodzi ndi mpingo. Apainiya ophunzitsidwa bwino ali otanganika ndi ntchito imeneyi. Ofalitsa okangalika a uthenga wa Ufumu, kaya amalalikira kwa maola ochepa pamwezi kapena maola ambiri, onsewo akufalitsa uthengawu padziko lonse lapansi.—Mateyu 28:19, 20; Ahebri 13:7, 17.
15. Kodi nchiyani chomwe chili umboni wakuti anthu akukhudzidwa ndi ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova?
15 Kodi dziko lapansili lakhudzidwa ndi ntchito yaikulu imeneyi? Umboni wapafupi wosonyeza kuti laterodi ndiwo nkhani zambiri zokhudza Mboni za Yehova zosonyezedwa pamaprogramu a pa TV ndi m’manyuzipepala. Nkhani zimenezi nthaŵi zambiri zimafotokoza za khama ndi kufunitsitsa kwathu kufikira aliyense. Ndithudi, khama lathu ndi kufikira anthu mobwerezabwereza zimachititsa chidwi anthu ngakhale kuti ambiri amakana uthenga ndi amithengawo!
Kukangalika Kwathu Pofuna Kukwaniritsa Umboni
16. Kodi ndi mzimu wotani womwe tiyenera kusonyeza tsopano pomwe takhala ndi nthaŵi yochepa?
16 Sitikudziŵa kuti kwakhala nthaŵi yaitali motani kuti dongosolo lazinthu lilipoli lithe, ndiponso sitifunikira kudziŵa nthaŵi yake, malinga ngati cholinga chathu chotumikira Yehova chili choyenera. (Mateyu 24:36; 1 Akorinto 13:1-3) Koma tikudziŵa kuti pofuna kuti chikondi, mphamvu, ndi chilungamo cha Yehova zisonyezedwe, uthenga wabwino uyenera kulalikidwa ‘choyamba.’ (Marko 13:10) Choncho, mosasamala kanthu kuti kaya takhala tikuyembekezera mapeto a dziko loipa, lopanda chilungamo, ndi lachiwawali kwa zaka zambiri, tiyenera kukhala mogwirizana kotheratu ndi kudzipatulira kwathu mogwirizana ndi mikhalidwe yathu. Mwina ndife okalamba kapena odwala, koma tingatumikirebe Yehova ndi changu chomwe tinali nacho m’masiku amene tinali achinyamata kapena a thanzi labwino. Mwina sitingathenso kuthera nthaŵi yambiri mu utumiki monga momwe tinkachitira kale, koma ndithudi tingathe kupereka kwa Yehova nsembe yachitamando yofananayo.—Ahebri 13:15.
17. Simbani chokumana nacho chosangalatsa chomwe chingatithandize tonsefe.
17 Choncho, kaya ndife achinyamata kapena okalamba, tiyeni tikhale okangalika pogaŵana uthenga wathu wolimbikitsa wa dziko latsopano ndi onse amene tikumana nawo. Tiyeni tikhale monga mtsikana wamanyazi wazaka zisanu ndi ziŵiri wa ku Australia yemwe anapita kusitolo ndi amake. Iye anamva pa Nyumba ya Ufumu kuti nkofunika kuti aliyense azilalikira, choncho anaika mabrosha aŵiri ofotokoza Baibulo m’chikwama mwake. Pamene amakewo anali pakauntala kugula zinthu, mtsikana wamng’onoyo anachokapo. Pamene amakewo anali kumufunafuna, anampeza akugaŵira brosha kwa mkazi wina! Amakewo anafika pamalopo kukapepesa mkaziyo ngati mwanayo anachita zilizonse zokhumudwitsa. Koma mkaziyo analandira broshalo mokondwera. Pamene amakewo analinso paokha ndi mwanayo, anamfunsa chomwe chinamlimbitsa mtima kuti afikire mlendoyo. Iye anayankha kuti, “Ndinangoti, Basi, Ndakonzeka! Ndipo ndinapitadi!”
18. Kodi tingasonyeze motani mzimu wofunikawu?
18 Tonsefe tifunikira kukhala ndi mzimu wofanana ndi wa mtsikana wa ku Australia ameneyu, makamaka pamene tifuna kufikira alendo kapena ngakhale akuluakulu a boma ndi uthenga wabwino. Mwina tingaope kuti adzakana. Tisaiŵaletu zimene Yesu ananena kuti: “Musade nkhaŵa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mawu otani, kapena mukanena chiyani; pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthaŵi yomweyo zimene muyenera kuzinena.”—Luka 12:11, 12.
19. Kodi utumiki wanu mumauona motani?
19 Choncho, dalirani thandizo la mzimu wa Mulungu pamene mufikira anthu mokoma mtima ndi uthenga wabwino. Anthu mamiliyoni ambiri kaŵirikaŵiri amadalira amuna ndi akazi osapindulitsa amene amangokhalapo nthaŵi yochepa. Ife timadalira Yehova ndi gulu lake lakumwamba—Kristu Yesu, angelo oyera, ndi Akristu odzozedwa oukitsidwa—amene adzakhalapo kosatha! Choncho, kumbukirani kuti: “Okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo”!—2 Mafumu 6:16.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna zitsanzo zina zowonjezereka, onani 1994 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 217-20.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi gulu la Mulungu lakumwamba lathandiza motani anthu a Yehova kuti achirimike?
◻ Kodi ndi magulu achipembedzo ndi andale ati omwe aukira Mboni za Yehova m’zaka za zana la 20?
◻ Kodi Mboni za Yehova zasintha motani utumiki wawo pofuna kuchita mogwirizana ndi kusintha kwa zinthu?
◻ Kodi nchiyani chomwe chimakusonkhezerani kuti muzilalikira?
[Chithunzi patsamba 17]
Henryka Żur
[Zithunzi patsamba 18]
Japan
Martinique
United States
Kenya
United States
Mboni za Yehova zimalalikira kulikonse komwe kumapezeka anthu ndipo zimalalikira nthaŵi iliyonse
[Chithunzi patsamba 20]
Kuchiyambi kwa zaka za zana lino, magalamafoni anali kugwiritsiridwa ntchito polalikira uthenga wa Ufumu