Pitanibe Patsogolo Mwauzimu!
TSiku laubatizo wathu liyenera kukhala tsiku lapamtima ndiponso losaiŵalika kwa ife. Ndipotu limeneli ndilo tsiku limene timasonyeza poyera kuti tadzipatulira kuti titumikire Mulungu.
ANTHU ambiri amakhala atayesa ndi mphamvu zawo zonse kuti afike pamenepa—kusiya khalidwe loipa limene akhala nalo kwa nthaŵi yaitali, kusiya mabwenzi oipa, kusintha zizoloŵezi zawo zovuta.
Ngakhale zili motero, pamene ubatizo uli chochitika chosangalatsa ndiponso chofunika kwambiri pamoyo wa Mkristu, uwo wangokhala chiyambi chokha. Mtumwi Paulo anauza Akristu obatizidwa a ku Yudeya kuti: “Polekana nawo mawu a chiyambidwe cha Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu.” (Ahebri 6:1) Inde, Akristu onse afunikira ‘kufikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu.’ (Aefeso 4:13) Ngati tikula kukhala akulu msinkhu mpamene tingakhaledi “okhazikika m’chikhulupiriro.”—Akolose 2:7.
Pazaka zingapo zapitazi, olambira odzipatulira chatsopano zikwi mazana ambiri aloŵa mumpingo wachikristu. Mwina inuyo ndinu mmodzi wa iwo. Monga abale anu a m’zaka za zana loyamba, simukufuna kukhalabe khanda lauzimu. Mukufuna kukula, kupita patsogolo! Koma kodi mungakule motani? Ndipo kodi mungapite patsogolo mwa njira zina ziti?
Kupita Patsogolo mwa Phunziro Laumwini
Paulo anauza Akristu a ku Filipi kuti: “Ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezere, m’chidziŵitso [cholongosoka, NW], ndi kuzindikira konse.” (Afilipi 1:9) Kukula mu “chidziŵitso cholongosoka” nkofunika kwambiri kuti mupite patsogolo mwauzimu. ‘Kuloŵetsa chidziŵitso cha Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu’ sikumatha, kumapitirizabe pambuyo pobatizidwa.—Yohane 17:3, NW.
Mlongo wina wachikristu, amene tidzamutcha kuti Alexandra, anadzazindikira zimenezi patapita zaka khumi kuchokera pamene anabatizidwa ali ndi zaka 16. Analeredwa m’choonadi ndipo anali kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse ndi kuchita nawo ntchito yolalikira. Iye analemba kuti: “M’miyezi yochepa yapitayo, ndinaona kuti zinthu sizinali bwino mpang’ono pomwe. Ndinasankha zodzifufuza ndekha moona mtima, zimene ndimaganiza ponena za choonadi, ndiponso chifukwa chimene ndidakali m’choonadi.” Kodi anapezanji? Anapitiriza kuti: “Ndinapeza kuti zifukwa zimene ndilili m’choonadi zinandivutitsa maganizo. Ndinakumbukira kuti pamene ndinali kukula, misonkhano ndi utumiki wakumunda zinali kugogomezeredwa. Zinali monga kuti zizoloŵezi za phunziro laumwini ndi pemphero mwina zinali kudzangokhalapo zokha. Koma pamene ndinafufuza mkhalidwe wanga, ndinaona kuti zimenezi sizinachitike.”
Mtumwi Paulo anapereka chilimbikitso chakuti: “Malinga ndi pamene tafika popita patsogolo, tipitirizebe kuyenda molongosoka m’chizoloŵezi chomwechi.” (Afilipi 3:16, NW) Chizoloŵezi chingatipangitse kupita patsogolo. Musanabatizidwe, mosakayikira munali ndi chizoloŵezi chophunzira Baibulo mlungu uliwonse ndi mphunzitsi waluso. Pamene munali kukula m’chidziŵitso, paprogramu imeneyi munaphatikizapo kukonzekera phunziro la mlungu uliwonse pasadakhale, mukumaŵerenga m’Baibulo malemba onse osonyezedwa ndi zina zotero. Tsopano pamene mwabatizidwa, kodi mukupitiriza ‘kuyenda m’chizoloŵezi chomwechi’?
Ngati simukutero, mwina mufunikira kupendanso zinthu zimene mumatsogoza, ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.’ (Afilipi 1:10, NW) Popeza timakhala ndi zochita zambiri, timafunikira kudzilanga kuti tipatule nthaŵi yoŵerenga Baibulo ndi kuchita phunziro laumwini. Koma mapindu ake ngabwinodi. Lingaliraninso zimene zinachitikira Alexandra. “Ndinganene kuti ndakhala m’choonadi kwa zaka 20 kapena zowonjezereka mwa kungopita kumisonkhano ndi kuchita utumiki wakumunda,” anavomereza motero. Komabe, anapitiriza kuti, “Ndadziŵa kuti ngakhale kuti zinthu zimenezi nzofunika, pa izo zokha sizingandichirikize pamene zinthu ziyamba kuvuta. Zonsezi zaonekera chifukwa chakuti ndilibe chizoloŵezi cha phunziro laumwini, ndiponso ndimangopemphera apa ndi apo komanso kungopemphera mwamwambo. Tsopano ndazindikira kuti ndiyenera kusintha malingaliro anga ndi kuyamba programu yothandiza yophunzira kuti ndimdziŵedi Yehova ndi kumkonda ndi kuzindikira bwino zimene Mwana wake watipatsa.”
Ngati mukufuna thandizo kuti mukhazikitse chizoloŵezi chabwino chomachita phunziro laumwini, akulu ndi Akristu ena ofikapo a mumpingo mwanu ngofunitsitsa kukuthandizani. Ndiponso, nkhani za m’makope a May 1, 1995; August 15, 1993; ndi May 15, 1986 a Nsanja ya Olonda zikufotokoza njira zambiri zothandiza.
Kufunika kwa Kuyandikira kwa Mulungu
Mbali inanso imene muyenera kuyesetsa kupita patsogolo ndiyo unansi wanu ndi Mulungu. Nthaŵi zina kufunika kumeneku kungakhale kwakukulu zedi. Lingalirani za Anthony amene anabatizidwa adakali wamng’ono. “Ndinali mwana woyamba kubatizidwa m’banja mwathu,” akusimba motero. “Nditabatizidwa, amayi anandikupatira mwachikondi. Kanali koyamba kuwaona atakondwera motero. Tinakondwera kwambiri, ndipo ndinalimbikitsidwa kwambiri.” Komabe, panali mbali ina. “Kwa nthaŵi yaitali ndithu, munalibe achinyamata obatizidwa mumpingo mwathu,” akupitiriza kusimba Anthony. “Choncho ndinali wonyada kwambiri. Ndinanyadanso chifukwa cha ndemanga ndi nkhani zanga pamisonkhano. Kupeza chitamando ndi chithokozo cha anthu kunakhala kofunika kwambiri kwa ine koposa kupereka chitamando kwa Yehova. Kwenikweni sindinali paunansi wathithithi ndi iye.”
Monga momwe anachitira Anthony, mwina ena anadzipatulira kwenikweni chifukwa chofuna kukondweretsa ena osati kukondweretsa Yehova. Ngakhale zitatero, Mulungu amayembekezerabe oterowo kusunga pangano lawo lakuti adzamtumikira. (Yerekezerani ndi Mlaliki 5:4.) Koma popanda kuyandikana ndi Mulungu, nzovuta kuti iwo achite zimenezi. Anthony akukumbukira kuti: “Chimwemwe chachikulu chimene ndinali nacho paubatizo wanga sichinakhalitse. Chaka choyamba sichinathe kuchokera paubatizo wanga ndipo ndinachita tchimo lalikulu ndi kudzudzulidwa ndi akulu mumpingo. Chifukwa cha khalidwe loipa lobwerezabwereza ndinachotsedwa mumpingo. Zaka zisanu ndi chimodzi kuchokera pakudzipatulira kwanga kwa Yehova, ndinamangidwa ndi kuponyedwa m’ndende chifukwa cha kupha munthu.”
Kukulitsa Unansi Wathithithi ndi Yehova
Kaya kwa inu zinthu zili motani, Akristu onse ayenera kumvera pempho la Baibulo lakuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Mosakayikira pamene munayamba kuphunzira Baibulo munali kukulitsa unansi ndi Mulungu. Munaphunzira kuti Mulungu si mulungu wosadziŵikayo wolambiridwa m’Dziko Lachikristu, koma ndi munthu wokhala ndi dzina, Yehova. Munaphunziranso kuti ali ndi mikhalidwe yochititsa chidwi, kuti iye ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka.”—Eksodo 34:6.
Komabe, kuti mukhale mogwirizana ndi kudzipatulira kwanu kuti mutumikire Mulungu, muyenera kuyandikirabe kwa iye! Motani? Wamasalmo anapemphera kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.” (Salmo 25:4) Phunziro laumwini la Baibulo ndi zofalitsa za Sosaite lingakuthandizeni kumdziŵa bwino Yehova. Kupemphera mochokera mumtima nthaŵi zonse nkofunikanso. Wamasalmo analimbikitsa kuti: “Tsanulirani mitima yanu pamaso pake.” (Salmo 62:8) Pamene muona mapemphero anu akuyankhidwa, mudzaona kuti Mulungu amakukondani inuyo panokha. Zimenezi zidzakuthandizani kuyandikana naye kwambiri.
Mayesero ndi mavuto ena amaperekanso mpata wina woyandikirira kwa Mulungu. Mungakumane ndi mavuto ndi ziyeso zina zoyesa chikhulupiriro chanu, monga kudwala, kuvutitsidwa kusukulu ndi kuntchito, kapena kuvuta kwa ndalama. Mwinanso zingachitike kuti zochita za nthaŵi zonse zateokrase za kupita nawo mu utumiki, kusonkhana, kapena kuphunzira Baibulo ndi ana anu nzovuta kuti muzichite. Mavuto oterewa musalimbane nawo nokha! Pemphani Mulungu kuti akuthandizeni, mukumampempha chitsogozo chake. (Miyambo 3:5, 6) Mpempheni mzimu wake woyera! (Luka 11:13) Pamene muona thandizo lachikondi la Mulungu, mudzayandikana naye kwambiri. Monga momwe wamasalmo Davide ananenera, “talaŵani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino; wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.”—Salmo 34:8.
Bwanji ponena za Anthony? “Ndinayamba kuganizira za nthaŵi pamene ndinali ndi zolinga zauzimu zambiri zokhudzana ndi kuchita chifuniro cha Yehova,” akukumbukira motero. “Zimenezi zinandipweteka mtima. Koma ngakhale ndinapwetekedwa mtima ndi kuchita chisoni motero, ndinakumbukira chikondi cha Yehova. Zinanditengera nthaŵi ndisanayambe kupemphera kwa Yehova, koma ndinachitabe zimenezo, ndipo ndinatsanulira mtima wanga kwa iye, kupempha chikhululukiro chake. Ndinayambanso kuŵerenga Baibulo ndipo ndinadabwa poona kuchuluka kwa zinthu zimene ndinaiŵala ndiponso poona kuti sindinali kudziŵadi zambiri ponena za Yehova.” Ngakhale kuti Anthony sanamalizebe chilango cha m’ndende chifukwa cha upandu wake, iye amathandizidwa ndi Mboni za kumeneko ndipo akuchira mwauzimu. Moyamikira, Anthony akuti: “Chifukwa cha Yehova ndi gulu lake, ndakwanitsa kuvula umunthu wakale, ndipo ndikuyesetsa kuvala watsopano tsiku lililonse. Unansi wanga ndi Yehova ndiwo wofunika koposa tsopano.”
Kupita Patsogolo Mwauzimu mu Utumiki Wanu
Yesu Kristu analamula otsatira ake kuti akhale alaliki a “uthenga . . . wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 24:14) Pokhala wofalitsa watsopano wa uthenga wabwino, mwina simunazoloŵere kwambiri kuchita utumikiwu. Choncho, mungapite motani patsogolo kuti ‘mukwaniritse utumiki wanu’?—2 Timoteo 4:5.
Njira ina ndiyo kukhala ndi kaonedwe kabwino. Phunzirani kuona ntchito yolalikira monga “chuma,” mwayi. (2 Akorinto 4:7) Ndiwo mpata wosonyezera chikondi chathu ndi kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Ntchitoyo imatilolanso kusonyeza kuti anansi athu timawadera nkhaŵa. Ngati tidzipereka kotheratu pantchitoyi tingapeze chimwemwe chenicheni.—Machitidwe 20:35.
Yesu iyemwini anali ndi kaonedwe kabwino pantchito yolalikira. Kuuzako ena choonadi cha Baibulo kunali ngati “chakudya” kwa iye. (Yohane 4:34) Choncho kufunitsitsa kwake kuthandiza ena kungafotokozedwe mwachidule m’mawu ake akuti, “Ndifuna.” (Mateyu 8:3) Yesu ankawamvera chifundo anthu, makamaka awo amene anali “okambululudwa ndi omwazikana” chifukwa cha dziko la Satana. (Mateyu 9:35, 36) Kodi inunso ‘mumafuna’ kuthandiza awo amene ali mumdima wauzimu ndiponso amene afunikira kuunikiridwa ndi Mawu a Mulungu? Ndiye kuti mudzasonkhezeredwa kumvera lamulo la Yesu lakuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19) Ndithudi, mudzasonkhezeredwa kuchita zonse zimene mungathe pantchitoyi malinga ndi thanzi lanu ndi mikhalidwe yanu.
Njira ina yopitira patsogolo ndiyo kuchita nawo utumiki nthaŵi zonse—mlungu uliwonse ngati mungathe. Kuchita zimenezo kungathandize kuchepetsa mantha amene munthu wolalikira apa ndi apo amakhala nawo. Kuchita nawo utumiki wakumunda nthaŵi zonse kudzakupindulitsani m’njira zinanso. Kudzachulukitsa chidziŵitso chanu cha choonadi, kulimbitsa chikondi chanu cha Yehova ndi anansi anu, ndi kukuthandizani kusumika maso anu pa chiyembekezo cha Ufumu.
Komano bwanji ngati mkhalidwe wanu panopo sukukupatsani mpata waukulu wochita ntchito yolalikira? Ngati simungathe kuusintha, pezani chitonthozo podziŵa kuti Mulungu amakondwera ndi zilizonse zimene mungathe kuchita mu utumiki wanu, malinga ngati mukuuchita ndi mtima wonse. (Mateyu 13:23) Mwina mungapite patsogolo m’njira zinanso, monga kukulitsa maluso anu a kulalikira. Mumpingo, Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi Msonkhano Wautumiki zimapereka maphunziro abwino kwambiri pankhaniyi. Mwachibadwa, tidzasangalala kwambiri ndi utumiki titakhala aluso kwambiri ndipo tidzapeza zotsatirapo zabwino.
Choncho nzoonekeratu kuti kupita patsogolo mwauzimu sikuyenera kulekezera patsiku laubatizo. Mtumwi Paulo analemba ponena za chiyembekezo chake cha kulandira moyo wosafa wakumwamba kuti: “Abale, ine sindiŵerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira; koma chinthu chimodzi ndichichita; poiŵaladi zammbuyo, ndi kutambalitsira zamtsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu. Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu.”—Afilipi 3:13-15.
Inde, Akristu onse, kaya akuyembekezera kukakhala ndi moyo wosafa kumwamba kapena moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi, ayenera “kutambalitsira zamtsogolo”—kuyesetsa zolimba, kunena kwake titero, kuti apeze cholinga chawo chimene chili moyo! Munayamba bwino mwa kubatizidwa, koma kuteroko kwangokhala chiyambi chokha. Pitirizani kuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu. Mwa misonkhano ndi phunziro laumwini, ‘khalani akulu misinkhu m’chidziŵitso.’ (1 Akorinto 14:20) ‘Zindikirani kupingasa, ndi utali, ndi kukwera’ kwa choonadi. (Aefeso 3:18) Kupita patsogolo kumene mudzapanga sikudzakuthandizani kungokhala ndi chimwemwe tsopano komanso kudzakuthandizani kupeza malo m’dziko latsopano la Mulungu, mmene mudzatha kupita patsogolo kosatha mu ulamuliro wa Ufumu wake wakumwamba!
[Chithunzi patsamba 29]
Timafunikira kudzilanga kuti tipatule nthaŵi yochita phunziro laumwini
[Chithunzi patsamba 31]
Kukhala ndi kaonedwe kabwino kungatithandize kusangalala ndi utumiki