Kodi Muli ndi Chikhulupiriro Chonga cha Abrahamu?
“Mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?”—LUKA 18:8.
1. Kodi n’chifukwa chiyani lerolino kuli kovuta kukhala ndi chikhulupiriro cholimba?
LEROLINO ndi kovuta kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Dziko limavutitsa Akristu kwambiri kuti liwaleketse kulingalira zinthu za uzimu. (Luka 21:34; 1 Yohane 2:15, 16) Ambiri amavutika kuti apulumuke nkhondo, masoka, matenda, ngakhalenso njala. (Luka 21:10, 11) M’mayiko ochuluka anthu amakondetsa zadziko, ndipo aliyense amene amachita zimene iye amakhulupirira amamuona kuti ndi wosaganiza, mwinanso wotengeka maganizo. Ndiponso, Akristu ambiri amazunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. (Mateyu 24:9) Funso limene Yesu anafunsa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo lilidi loyenerera: “Mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?”—Luka 18:8.
2. (a) Kodi n’chifukwa chiyani chikhulupiriro cholimba chili chofunika kwa Mkristu? (b) Ndi chitsanzo cha chikhulupiriro cha yani chimene tidzachita bwino kuchilingalira?
2 Komabe, mfundo njakuti chikhulupiriro cholimba n’chofunika kwambiri ngati tsopano lino titi tikhale ndi moyo wabwino ndi kudzalandiranso moyo wosatha wolonjezedwawo m’tsogolo. Mtumwi Paulo, pogwira mawu a Yehova kwa Habakuku, analemba kuti: “Wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m’chikhulupiriro: Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye. . . . Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa [Mulungu].” (Ahebri 10:38–11:6; Habakuku 2:4) Paulo anauza Timoteo kuti: “Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira.” (1 Timoteo 6:12) Motero, kodi zingatheke bwanji kukhala ndi chikhulupiriro chosasweka? Polingalira funso limeneli, tichita bwino kuganiza za munthu amene anakhalako zaka ngati 4,000 zapitazo, komabe amene chikhulupiriro chake chimaonedwabe kukhala chofunika kwambiri m’zipembedzo zikuluzikulu zitatu—Chisilamu, Chiyuda, ndi Chikristu. Munthu ameneyo ndi Abrahamu. Kodi n’chifukwa chiyani chikhulupiriro chake chinali chapadera kwambiri? Kodi lerolino tingamtsatire?
Kumvera Malangizo a Mulungu
3, 4. Kodi n’chifukwa chiyani Tera anasamuka ndi banja lake kuchokera ku Uri kupita ku Harana?
3 Abrahamu (yemwe poyamba ankatchedwa Abramu) akutchulidwa koyamba kuchiyambiyambi kwa Baibulo. Pa Genesis 11:26, timaŵerenga kuti: ‘Tera . . . anabala Abramu, ndi Nahori ndi Harana.’ (Genesis 11:26) Tera ndi banja lake anali kukhala ku Uri wa kwa Akaldayo, mzinda wokhupuka kumwera kwa Mesopotamiya. Komabe, sanakhalitseko. “Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harana, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai [Sara] mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nawo ku Uri wa kwa Akaldayo kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harana, nakhala kumeneko.” (Genesis 11:31) Mbale wake wa Abrahamu, Nahori, nayenso anasamukira ku Harana ndi banja lake. (Genesis 24:10, 15; 28:1, 2; 29:4) Komabe, kodi n’chifukwa chiyani Tera anasamuka ku Uri wokhupukayo ndi kupita kutali ku Harana?
4 Zaka pafupifupi 2,000 kuchokera m’nthaŵi ya Abrahamu, munthu wokhulupirika Stefano, akulankhula m’bwalo la Sanhedrin yachiyuda, anafotokoza chifukwa chake banja la Tera linasamuka moteremu. Iye anati: “Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m’Mesopotamiya, asanayambe kukhala m’Harana; nati kwa iye, Tuluka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe. Pamenepo anatuluka m’dziko la Akaldayo namanga m’Harana.” (Machitidwe 7:2-4) Tera anagonjera ku chifuno cha Yehova pa Abrahamu pamene anasamukira ku Harana ndi ana ake.
5. Kodi Abrahamu anapita kuti atate ake atamwalira? Chifukwa?
5 Banja la Tera linakhazikika mu mzinda wawo watsopanowo. Zaka zochuluka pambuyo pake pamene Abrahamu anati “dziko langa,” anali kunena dera la Harana osati Uri. (Genesis 24:4) Komabe, Abrahamu sanali kudzakhaliratu m’Harana. Malinga ndi kunena kwa Stefano, “atamwalira atate wake [wa Abrahamu], Mulungu anamsuntha aloŵe m’dziko lino, mmene mukhalamo tsopano.” (Machitidwe 7:4) Pomvera malangizo a Yehova, Abrahamu, pamodzi ndi Loti, anawoloka Firate ndi kuloŵa m’dziko la Kanani.a
6. Kodi Yehova anamlonjeza chiyani Abrahamu?
6 Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anachititsa Abrahamu kusamukira ku Kanani? Chifukwa chake chiyenera kuti chinakhudza chifuno cha Mulungu pa munthu wokhulupirika ameneyo. Yehova anati kwa Abrahamu: “Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kumka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.” (Genesis 12:1-3) Abrahamu anali kudzakhala kholo la mtundu waukulu umene udzatetezedwa ndi Yehova ndi umene udzakhala m’dziko la Kanani. Lonjezo labwinodi! Koma kuti alandire dziko limenelo, Abrahamu anafunikira kusintha moyo wake kwambiri.
7. Kodi Abrahamu anafunika kukonzekera kusintha chiyani kuti alandire lonjezo la Yehova?
7 Pamene Abrahamu anachoka ku Uri, anachoka mu mzinda wokhupuka ndipo mwinanso anasiya banja lalikulu la atate ake—zinthu zimene zinkateteza anthu kwambiri m’nthaŵi zokhulupirira makolo zimenezo. Pamene anachoka ku Harana, analekana ndi mbumba ya atate ake kuphatikizapo banja la mbale wake Nahori, ndi kusamukira kudziko losadziŵika. Ku Kanani, sanafune kukhala wosungika mumzinda wa malinga. Chifukwa chiyani? Abrahamu atangoloŵa m’dzikolo, Yehova anamuuza kuti: ‘Uyendeyende m’dzikoli m’litali mwake ndi m’mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.’ (Genesis 13:17) Abrahamu yemwe anali ndi zaka zakubadwa 75, ndi mkazi wake Sara amene anali ndi zaka 65, anatsatira malangizo amenewa. “Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo ku dziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m’mahema.”—Ahebri 11:9; Genesis 12:4.
Chikhulupiriro Chonga cha Abrahamu Lerolino
8. Polingalira za chitsanzo cha Abrahamu ndi mboni zina zakale, kodi tiyenera kukhala ndi chiyani?
8 Abrahamu ndi banja lake anatchulidwa pamodzi ndi ‘mtambo waukulu wa mboni [za nthaŵi yachikristu isanafike]’ umene ukutchulidwa mu Ahebri chaputala 11. Polingalira za chikhulupiriro cha atumiki oyambirira amenewa a Mulungu, Paulo analimbikitsa Akristu ‘kutaya cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli [kupanda chikhulupiriro] limangotizinga.’ (Ahebri 12:1) Inde, ‘tingazingidwe mosavuta’ ndi kupanda chikhulupiriro. Koma m’tsiku la Paulo ndiponso m’tsiku lathu, Akristu enieni akhala ndi chikhulupiriro cholimba chofanana ndi chija cha Abrahamu ndi anthu ena a m’nthaŵi zakale. Paulo, ponena za iye mwini ndi Akristu anzake, anati: “Ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.”—Ahebri 10:39.
9, 10. Kodi pali umboni wotani wakuti anthu ambiri lerolino ali ndi chikhulupiriro chonga cha Abrahamu?
9 Zoonadi, dzikoli likusiyana ndi mmene linalili m’masiku a Abrahamu. Komabe, tikutumikirabe “Mulungu wa Abrahamu” yemweyo, ndipo iye sasinthika. (Machitidwe 3:13; Malaki 3:6) Yehova ndi woyenera kulambiridwa lerolino monga mmene analili m’masiku a Abrahamu. (Chivumbulutso 4:11) Anthu ambiri amadzipereka kotheratu kwa Yehova ndipo, mofanana ndi Abrahamu, amasintha zilizonse zimene angafunike kusintha pamoyo wawo kuti achite chifuno cha Mulungu. Chaka chatha, anthu 316,092 anasonyeza poyera kudzipatulira kwawo mwa kubatizidwa m’madzi “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.”—Mateyu 28:19.
10 Ochuluka a Akristu atsopano amenewa sanapite kutali kudziko lachilendo kuti akwaniritse kudzipereka kwawo. Komabe m’lingaliro lauzimu, ambiri a iwo anayenda ulendo wautali ndithu. Mwachitsanzo, ku Mauritius, Elsie ankachita za matsenga. Aliyense anali kumuopa. Mpainiya wapadera anakonza zomaphunzira Baibulo ndi mwana wake wa Elsie, ndipo izi zinatsegula njira yoti Elsie “atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika.” (Machitidwe 26:18) Poona chidwi cha mwana wake, Elsie anavomera kuphunzira Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Anali kuphunzira katatu pa mlungu chifukwa anali kufunika chilimbikitso nthaŵi zonse. Sanapeze chimwemwe ndi zochita zake za mizimuzo, ndipo anali ndi mavuto ambiri. Komabe pomalizira pake anatsiriza ulendo wautaliwo wochokera ku kulambira ziŵanda kupita ku kulambira koona. Pamene anthu anali kubwera kuti adzawathandize, anali kulongosola kuti ndi Yehova yekha amene angawateteze ku zoipa. Tsopano Elsie ndi Mboni yobatizidwa ndipo anthu 14, ena a pabanja lake ndi ena mabwenzi ake, alandira choonadi.
11. Kodi aja amene amadzipatulira kwa Yehova amakhala ofunitsitsa kupanga masinthidwe otani?
11 Ambiri a aja amene anadzipatulira chaka chatha kuti atumikire Mulungu sanapange masinthidwe akulu oterowo. Koma onse anachoka pakukhala akufa mwauzimu ndi kukhala amoyo mwauzimu. (Aefeso 2:1) Ngakhale kuti akukhalabe m’dzikoli, saalinso mbali ya dziko. (Yohane 17:15, 16) Mofanana ndi Akristu odzozedwa, amene ‘ufulu wawo uli Kumwamba,’ ali ngati “alendo ndi ogonera.” (Afilipi 3:20; 1 Petro 2:11) Anagwirizanitsa miyoyo yawo ndi miyezo ya Mulungu, mosonkhezeredwa kwambiri ndi kukonda Mulungu ndi anansi awo. (Mateyu 22:37-39) Sakhala ndi zolinga zadyera, kukondetsa zinthu zakuthupi kaya kumva kuti afunika kukwaniritsa china chake m’dzikoli. M’malo mwake, amayang’ana dwii palonjezo la ‘miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’mene mudzakhalitsa chilungamo.’—2 Petro 3:13; 2 Akorinto 4:18.
12. Kodi ndi ntchito yotani imene inachitidwa lipoti chaka chatha imene imasonyeza kuti Yesu m’nthaŵi ya kukhalapo kwake wapeza “chikhulupiriro padziko lapansi”?
12 Pamene Abrahamu anasamukira ku Kanani, analiko ndi banja lake lokha ndipo Yehova anali yekhayo amene anawachirikiza ndi kuwateteza. Komabe, Akristu 316,092 obatizidwa chatsopanowa saali okha. Inde, Yehova akuwachirikiza ndi kuwateteza ndi mzimu wake, monga anachitira ndi Abrahamu. (Miyambo 18:10) Komanso, iye akuwachirikiza ndi “mtundu” wachangu, wapadziko lonse umene uli waukulu kuposa mitundu ina yadziko lerolino. (Yesaya 66:8) Chaka chatha, chiŵerengero chapamwamba cha anthu 5,888,650 a mtundu umenewo chinapereka umboni wakuti ali ndi chikhulupiriro chamoyo mwa kulankhula ndi anansi awo za malonjezo a Mulungu. (Marko 13:10) Anathera chiŵerengero chachikulu cha maola 1,186,666,708 m’ntchito imeneyi, pofuna kupeza anthu ofuna kuphunzira. Monga chotsatirapo chake, anachititsa maphunziro a Baibulo 4,302,852 ndi anthu amene akufuna kukhala ndi chikhulupiriro. Monga umboni wowonjezereka wa changu chawo, anthu 698,781 a “mtundu” umenewu anachita utumiki waupainiya, kaya kwa nthaŵi zonse kapena kwa mwezi umodzi kapena yoposapo. (Tsatanetsatane wa ntchito imene Mboni za Yehova zinachita chaka chatha akupezeka pa masamba 12 kufika 15) Ziŵerengero zapamwamba zimenezi ndi yankho labwino ndi looneka la funso la Yesu lija, “Mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?”
Kukhulupirika Mosasamala Kanthu za Ziyeso
13, 14. Longosolani ena mwa mavuto amene Abrahamu ndi banja lake anakumana nawo ku Kanani.
13 Kaŵirikaŵiri Abrahamu ndi banja lake zinthu zinali kuwavuta ku Kanani. Panthaŵi ina kunali njala yaikulu imene inawachotsa ku Kanani ndi kuwapititsa ku Aigupto. Ndiponso, wolamulira wa ku Aigupto ndi wolamulira wa ku Gerari (pafupi ndi Gaza) anafuna kukwatira Sara, mkazi wa Abrahamu. (Genesis 12:10-20; 20:1-18) Panalinso ndewu pakati pa abusa a Abrahamu ndi abusa a Loti, ndipo zimenezi zinachititsa kuti mabanja aŵiriwo agaŵikane. Mosadzikonda, Abrahamu anauza Loti kuti asankhe malo amene akufuna, ndipo Loti anasankha chigwa cha Yordano, chimene chinali kuoneka kuti chinali cha nthaka yabwino ndi chokongola ngati munda wa Edeni.—Genesis 13:5-13.
14 Ndiyeno, Loti anapezeka pakati pankhondo yapakati pa mfumu ya dziko lakutali la Elamu ndi ophatikana naye anzake a mfumuyi ndi mafumu a mizinda isanu m’chigwa cha Sidimu. Mafumu obwerawo anagonjetsa mafumu a m’deralo ndipo anafunkha zinthu zambiri, kuphatikizapo Loti ndi katundu wake. Pamene Abrahamu anamva zimene zinachitika, molimba mtima anathamangira mafumu obwerawo ndipo analanditsa Loti ndi mbumba yake, komanso katundu wa mafumu a m’deralo. (Genesis 14:1-16) Komatu, zimenezi sindizo zinali zinthu zovuta kwambiri zimene Loti anakumana nazo m’Kanani. Pazifukwa zina, iye anakakhazikika mu Sodomu mosasamala kanthu za mbiri yoipa ya anthu a m’mzindawo.b (2 Petro 2:6-8) Atachenjezedwa ndi angelo aŵiri kuti mzindawo udzawonongedwa, Loti anathaŵa pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake. Komabe, mkazi wa Loti ananyalanyaza malangizo achindunji amene angelo anawapatsa motero iye anasanduka chulu cha mchere. Loti anafika pakutha, ndipo kwa kanthaŵi anali kukhala m’phanga ku Zoari ndi ana ake aakazi aŵiri. (Genesis 19:1-30) Zochitika zonsezi ziyenera kuti zinamsautsa mtima kwambiri Abrahamu, makamaka chifukwa chakuti Loti anabwera ku Kanani monga mbumba ya Abrahamu.
15. Mosasamala kanthu za mavuto amene Abrahamu anakumana nawo pamene anali kukhala m’mahema m’dziko lachilendo, kodi ndi kalingaliridwe kolakwika kati kamene mwachionekere anakapewa?
15 Kodi Abrahamu analingalirapo kuti bwenzi iye ndi Loti anakakhala osungika mu Uri ndi banja lalikulu la atate ake kapena mu Harana ndi mbale wake Nahori? Kodi iye anakhumbapo kuti chikhala anakakhazikika mu mzinda wosungika wamalinga m’malo momakhala m’mahema? Kapena, kodi iye anakayikirapo ngati kunali kwanzeru kuti anali kukhala ndi moyo wodzimana monga munthu wosamukasamuka? Ponena za Abrahamu ndi banja lake, mtumwi Paulo anati: “Akadakumbukira lijalo adatulukamo akadaona njira yakubwera nayo.” (Ahebri 11:15) Komatu iwo sanabwerere. Popanda kukhumudwa ndi mavuto, iwo anakhalabe kumene Yehova anafuna kuti akhale.
Kupirira Lerolino
16, 17. (a) Kodi Akristu ambiri akukumana ndi mavuto otani lerolino? (b) Kodi Akristu ali ndi malingaliro abwino otani? Chifukwa?
16 Lerolinonso Akristu akupirira mavuto mofananamo. Ngakhale kuti amasangalala kwambiri potumikira Mulungu, moyo ndi wovuta kwa Akristu oona m’masiku otsiriza ano. Ngakhale kuti ali mu paradaiso wauzimu, iwo akukumanabe ndi mavuto azachuma monga anthu ena onse. (Yesaya 11:6-9) Ambiri aphedwa popanda chifukwa m’nkhondo za mitundu, ndipo ena afikira pokhala amphaŵi kwambiri popanda chomwe iwo alakwapo. Ndiponso, amapirira vuto lokhala kagulu kodedwa. M’mayiko ambiri amalalikira uthenga wabwino kwa anthu amene salabadira n’komwe. M’mayiko ena amavutika ndi anthu amene mwachinyengo ‘amapanga chovuta kukhala lamulo namtsutsa wa mwazi wosachimwa.’ (Salmo 94:20, 21) Ngakhale m’mayiko amene Akristu savutitsidwa ndi kumene amatamandidwa chifukwa cha makhalidwe awo a pamwamba, amazindikira kuti ayenera kukhala osiyana ndi anzawo a kusukulu ndi ogwira nawo ntchito—monga ngati Abrahamu, amene anali kukhala m’mahema pamene anthu ambiri amene anali kukhala nawo pafupi anali kukhala m’mizinda. Kulidi kovuta kukhala m’dziko koma ndi ‘kusakhala’ wadziko.—Yohane 17:14.
17 Pamenepa, kodi timadziringa kuti tinadzipatulira kwa Mulungu? Kodi timakhumba tikanakhala a dziko lapansi, monga mmene ena alili? Kodi timadandaula ndi zinthu zimene tadzimana potumikira Yehova? Kutalitali! M’malo mokhumbira zakumbuyo, timazindikira kuti chilichonse chimene tinasiya sichinali chopindulitsa kwenikweni poyerekezera ndi madalitso amene tili nawo tsopano ndiponso amene tidzakhala nawo m’tsogolo. (Luka 9:62; Afilipi 3:8) Komanso, kodi anthu ndi achimwemwe m’dzikoli? Zoonadi n’zoti ambiri a iwo akufunafuna mayankho a mafunso amene ife tikuwadziŵa kale. Amavutika chifukwa chosatsatira chitsogozo chimene ife timatsatira choperekedwa ndi Mulungu m’Baibulo. (Salmo 119:105) Ndipo ambiri a iwo amafuna ubwenzi wachikristu ndi mayanjano osangalatsa amene ife timakhala nawo ndi okhulupirira anzathu.—Salmo 133:1; Akolose 3:14.
18. Pamene Akristu asonyeza kulimba mtima ngati Abrahamu, kodi pamapeto pake pamakhala zotulukapo zotani?
18 Zoonadi, nthaŵi zina timafunikira kukhala olimba mtima monga Abrahamu pamene anathamangitsa omwe anagwira Loti. Koma pamene tili olimba mtima motero, Yehova amadalitsa zotsatirapo zake. Mwachitsanzo, ku Northern Ireland anthu akudana kwambiri chifukwa cha chiwawa cha magulu ampatuko, ndipo pamafunika kulimba mtima kuti usaloŵererepo. Komabe, Akristu okhulupirika atsatira mawu a Yehova kwa Yoswa akuti: “Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhaŵa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.” (Yoswa 1:9; Salmo 27:14) Akupatsidwa ulemu tsopano chifukwa chokhala osaopa panthaŵi yonseyi, ndipo lero amalalikira momasuka m’madera onse a dziko limenelo.
19. Kodi Akristu amasangalala kukhala kuti, ndipo kodi mwachidaliro amayembekezera chiyani pamene atsatira malangizo a Yehova?
19 Tisakayikire, mkhalidwe uliwonse umene tingakumane nawo, ngati titsatira malangizo a Yehova, chotsatirapo chake chidzakhala chomlemekeza ndi chotipindulitsa kwanthaŵi yaitali. Mosasamala kanthu za zovuta ndi zimene timafunika kudzimana, palibe malo ena amene tingakonde kukhalamo kusiyana ndi kukhala mu utumiki wa Yehova, kusangalala ndi kuyanjana ndi abale athu achikristu ndi kuyembekezera ndi chidaliro tsogolo losatha limene Mulungu walonjeza.
[Mawu a M’munsi]
a Mwinamwake Abrahamu anayamba kukhala ndi Loti pamene atate ake a Loti, mbale wake wa Abrahamu, anamwalira.—Genesis 11:27, 28; 12:5.
b Ena alingalira kuti Loti anakakhazikika mumzinda pofuna kukhala wosungika kwambiri pambuyo pogwidwa ndi mafumu anayi aja.
Kodi Mukukumbukira?
◻ N’chifukwa chiyani chikhulupiriro cholimba chili chofunika?
◻ Kodi Abrahamu anasonyeza motani kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba?
◻ Kodi kudzipatulira kumatsagana motani ndi kusintha kwa moyo wa munthu?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani timasangalala ndi kutumikira Mulungu mosasamala kanthu za mavuto amene tingakumane nawo?
[Zithunzi patsamba 7]
Abrahamu anali wofunitsitsa kusintha moyo wake kwambiri kuti alandire lonjezo
[Zithunzi patsamba 9]
Umboni ukusonyeza kuti Yesu wapeza “chikhulupiriro padziko lapansi” panthaŵi ya kukhalapo kwake