‘Ika Mtima Wako pa’ Kachisi wa Mulungu!
‘Wobadwa ndi munthu iwe, . . . ika mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe . . . fotokozera nyumba ya Israyeli zonse uziona.’—EZEKIELI 40:4.
1. Kodi anthu osankhidwa a Mulungu anali mumkhalidwe wotani mu 593 B.C.E.?
CHAKACHO chinali 593 B.C.E., chaka cha 14 cha undende wa Israyeli. Ayuda okhala m’Babulo angakhale ataona kuti dziko lawo lokondedwa linali kutali kwambiri. Ochuluka a iwo anaona Yerusalemu komaliza pamene anali malaŵi a moto okhaokha, makoma ake olimba atagwa, ndi nyumba zake zaulemerero zitakhala mabwinja. Kachisi wa Yehova—amene panthaŵi ina yake anali ulemerero wa mudziwo, malo okhawo a kulambira koyera padziko lonse—anali atawonongedwa kukhala bwinja. Tsopano chigawo chachikulu cha undende wa Israyeli chinali kutsogolo. Panali kudzapita zaka 56 kuti alanditsidwe malinga ndi lonjezo.—Yeremiya 29:10.
2. Kodi n’chifukwa chiyani Ezekieli ayenera kuti anamva chisoni pokumbukira kachisi wa Mulungu ku Yerusalemu?
2 Ezekieli, mneneri wokhulupirika, ayenera kuti anamva chisoni poganiza zakuti kachisi wa Mulungu ali mabwinja okhaokha pamtunda wa makilomita mazanamazana, pamalo apululu a nyama zakutchire. (Yeremiya 9:11) Atate wake, Buzi, anali wansembe kumeneko. (Ezekieli 1:3) Ezekielinso akanakhala ndi udindo womwewo, koma anatengedwa undende limodzi ndi akalonga a Yerusalemu mu 617 B.C.E., adakali wamng’ono. Tsopano pokhala ndi zaka pafupifupi 50 zakubadwa, Ezekieli ayenera kuti anadziŵa kuti Yerusalemu sadzamuonanso kapena kuchita nawo ntchito iliyonse yomanganso kachisi wake. Pamenepa, tayerekezerani mmene Ezekieli anamvera polandira masomphenya a kachisi waulemerero ameneyo!
3. (a) Kodi cholinga cha masomphenya a Ezekieli a kachisi chinali chiyani? (b) Kodi mbali zazikulu zinayi za masomphenyawo n’zotani?
3 Masomphenya aakulu ameneŵa, okwanira machaputala asanu ndi anayi a buku la Ezekieli, anapereka lonjezo lolimbitsa chikhulupiriro cha Ayuda omwe anali m’ndende. Kulambira koyera kunali kudzabwezeretsedwa! M’zaka mazana zotsatira, ngakhale kufika m’tsiku lathu, masomphenya ameneŵa amalimbikitsa anthu okonda Yehova. Motani? Tiyeni tipende zimene masomphenya a ulosi a Ezekieli anatanthauza kwa Aisrayeli andendewo. Ali ndi mbali zazikulu zinayi: kachisi, ansembe, kalonga, ndi dziko.
Kachisi Abwezeretsedwa
4. Kodi Ezekieli akutengeredwa kuti pachiyambi cha masomphenya ake, kodi kumeneko akuonanji, ndipo ndani akumuonetsa malowo?
4 Choyamba, Ezekieli akutengeredwa “paphiri lalitali ndithu.” Paphiripo kummwera kuli kachisi wamkulu kwambiri, monga mudzi walinga. Mngelo wa “maonekedwe ake ngati amkuwa” akutenga mneneriyo kumuonetsa malo onsewo. (Ezekieli 40:2, 3) Popitiriza masomphenyawo, Ezekieli akuona mngeloyo akupima mosamalitsa zipata ziŵiriziŵiri zotsatizana za kumbali zitatu za kachisi limodzi ndi zipinda zake za alonda, bwalo lakunja, bwalo lamkati, zipinda zodyeramo, guwa la nsembe, ndi malo opatulidwa a kachisi limodzi ndi zipinda zake, Chopatulika ndi Chopatulikitsa.
5. (a) Kodi Yehova akumutsimikiziranji Ezekieli? (b) Kodi “mitembo ya mafumu awo” imene inayenera kuchotsedwa m’kachisi inali chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zinali zofunika?
5 Ndiyeno, Yehova mwiniyo akuonekera m’masomphenyawo. Akuloŵa m’kachisi natsimikizira Ezekieli kuti Iyeyo adzakhala mmenemo. Koma Yehova akulamula kuti ayeretse nyumba Yake, nati: “Ataye tsono chigololo chawo ndi mitembo ya mafumu awo kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pawo kosatha.” (Ezekieli 43:2-4, 7, 9) Malinga ndi umboni, “mitembo ya mafumu” imeneyi inali mafano. Olamulira ndi anthu ena opanduka m’Yerusalemu anaipitsa kachisi wa Mulungu ndi mafano, motero, anapanga mafanowo kukhala mafumu awo. (Yerekezerani ndi Amosi 5:26.) Pokhala sanali milungu kapena mafumu amoyo, mafano ameneŵa anali zinthu zakufa ndiponso zonyansa pamaso pa Yehova. Anayenera kuwataya.—Levitiko 26:30; Yeremiya 16:18.
6. Kodi kupima kachisi kunatanthauzanji?
6 Kodi mfundo yake ya mbali imeneyi ya masomphenya inali yotani? Inatsimikizira andende kuti kulambira koyera pakachisi wa Mulungu kudzabwezeretsedwa kotheratu. Ndiponso, kupima kachisi kunali chitsimikizo cha Mulungu chakuti masomphenyawo adzakwaniritsidwa kosalephera ayi. (Yerekezerani ndi Yeremiya 31:39, 40; Zekariya 2:2-8.) Kalikonse kokhudzana ndi kupembedza mafano anali kudzakachotsa. Yehova anali kudzadalitsanso nyumba yake.
Ansembe ndi Kalonga
7. Kodi pakuperekedwa chidziŵitso chotani chokhudza Alevi ndi ansembe?
7 Ansembenso anafunikira kuwayeretsa, kapena kuwayenga. Alevi anayenera kudzudzulidwa polola kupembedza mafano, pamene ana a Zadoki ansembe anayenera kuthokozedwa ndi kufupidwa pokhalabe oyera.a Komabe, magulu onse aŵiriwo anali kudzakhala ndi udindo wotumikira m’nyumba ya Mulungu yomangidwanso—mosakayikira zikumadalira pa kukhulupirika kwawo aliyense payekha. Ndiponso, Yehova analamula kuti: “Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.” (Ezekieli 44:10-16, 23) Chotero ansembe anali kudzayambiranso, ndiponso anali kudzafupidwa chifukwa cha kupirira kwawo kokhulupirika.
8. (a) Kodi akalonga a m’Israyeli wakale anali ayani? (b) Kodi kalonga wa m’masomphenya a Ezekieli anali wokangalika motani pa kulambira koyera?
8 Masomphenyawo akuonetsanso wina wake wotchedwa kalonga. Kuyambira masiku a Mose, mtunduwo unali ndi akalonga. Liwu lachihebri lotanthauza kalonga, na·siʼʹ, linkatanthauzanso mutu wa banja lakuchimuna, fuko, ngakhalenso mtundu. M’masomphenya a Ezekieli, kagulu ka olamulira a Israyeli kakudzudzulidwa chifukwa chopondereza anthu ndipo kakulimbikitsidwa kusayang’ana nkhope ndi kutsata chilungamo. Ngakhale sali m’gulu la ansembe, kalonga akukangalika kwambiri pa kulambira koyera. Akuloŵa ndi kutuluka m’bwalo lakunja limodzi ndi mafuko osakhala a ansembe, akhala m’khonde la Chipata cha Kummaŵa, ndipo akonza zina za nsembe zoti anthu apereke. (Ezekieli 44:2, 3; 45:8-12, 17) Chotero masomphenyawo anatsimikizira anthu a m’nthaŵi ya Ezekieli kuti mtundu wobwezeretsedwawo udzadalitsidwa ndi atsogoleri achitsanzo chabwino, amuna amene adzachirikiza ansembe polinganiza anthu a Mulungu ndi kukhala zitsanzo zabwino pankhani zauzimu.
Dziko
9. (a) Kodi dziko linali kudzagaŵidwa motani, koma kodi ndani amene sanali kudzalandira choloŵa? (b) Kodi chopereka chopatulika chinali chiyani, ndipo chinali ndi chiyani?
9 Pomaliza, masomphenya a Ezekieli anaphatikizapo malongosoledwe a dziko lonse la Israyeli. Linayenera kugaŵidwa, fuko lililonse likumalandira gawo lake. Kalonganso anali kudzalandira choloŵa chake. Koma ansembe sanali kudzalandira, pakuti Yehova anati, “Ine ndine choloŵa chawo.” (Ezekieli 44:10, 28; Numeri 18:20) Masomphenyawo anasonyeza kuti dziko logaŵidwa kwa kalonga lidzakhala kumbali zonse za dera lapadera lotchedwa chopereka chopatulika. Malo ameneŵa anali olingana mbali zonse zinayi ndipo anagaŵidwa patatu—chigawo chapamwamba chinali cha Alevi olapa, chapakati cha ansembe, ndipo chakumunsi cha mudzi limodzi ndi minda yake. Kachisi wa Yehova anali kudzakhala m’chigawo cha ansembe, pakati pa choperekacho cholingana mbali zonse zinayi.—Ezekieli 45:1-7.
10. Kodi ulosi wogaŵa dziko unatanthauzanji kwa Ayuda andendewo?
10 Zimenezi ziyenera kuti zinawalimbikitsa kwambiri andende aja! Banja lililonse analitsimikizira kuti lidzalandira choloŵa m’dzikolo. (Yerekezerani ndi Mika 4:4.) Kulambira koyera kunali kudzakhala pamalo okwezeka apakati. Ndipo taonani m’masomphenya a Ezekieli kuti kalonga, monga ansembe, anali kudzakhala pamalo operekedwa ndi anthu. (Ezekieli 45:16) Chotero m’dziko lobwezeretsedwalo, anthu anayenera kupereka thandizo pa ntchito ya aja amene Yehova anaŵaika kukhala atsogoleri, kuwachirikiza mwa kuwamvera. Mwachidule, dziko limeneli linasonyeza kuti panali dongosolo, kugwirizana, ndi chisungiko.
11, 12. (a) Kodi Yehova akutsimikizira motani anthu ake mwaulosi kuti adzadalitsa dziko lawo lobwezeretsedwa? (b) Kodi mitengo ya m’mbali mwa mtsinje inaimiranji?
11 Kodi Yehova anali kudzadalitsa dziko lawo? Ulosiwo ukuyankha funso limeneli ndi mafotokozedwe okhudza mtima. Kasupe akutuluka m’kachisi, akumka namakula kumene akupita, mpaka atakhala mtsinje waukulu wamphamvu ndithu pamene uloŵa m’Nyanja Yakufa. Mmenemo usandutsa madzi opanda zamoyo kukhala amoyo, ndipo kugombe lake anthu ayamba ntchito yaikulu yausodzi. M’mbali mwa mtsinjewo muli mitengo yambiri yobala zipatso chaka chonse, kupereka chakudya ndi kuchiritsa.—Ezekieli 47:1-12.
12 Kwa andende, lonjezo limeneli linawakumbutsa ndi kuwatsimikizira za maulosi oyambirira a kubwezeretsa omwe anali kuwakhulupirira kwambiri. Nthaŵi zingapo, aneneri a Yehova ouziridwa anafotokozapo za Israyeli wobwezeretsedwa, wokhalamonso anthu monga paradaiso. Maulosiwo ankanena mobwerezabwereza zakuti madera apululu adzakhala amoyo. (Yesaya 35:1, 6, 7; 51:3; Ezekieli 36:35; 37:1-14) Chotero anthu akanayembekezera kuti dalitso la Yehova lopatsa moyo lidzayenda ngati mtsinje kuchokera m’kachisi womangidwanso. Pomaliza pake, mtundu wakufa mwauzimu udzakhalanso ndi moyo. Anthu obwezeretsedwawo anali kudzadalitsidwa ndi amuna apadera auzimu—amuna olungama ndi olimba ngati mitengo yokhala m’mbali mwa mtsinje wa m’masomphenya, amuna amene adzatsogolera pokonza dziko labwinjalo. Yesayanso analemba za “mitengo ya chilungamo” imene ‘idzamanga mabwinja akale.’—Yesaya 61:3, 4.
Kodi Masomphenyawo Akukwaniritsidwa Liti?
13. (a) Kodi Yehova anadalitsa anthu ake ndi “mitengo yachilungamo” m’lingaliro lotani? (b) Kodi ulosi wonena za Nyanja Yakufa unakwaniritsidwa motani?
13 Kodi andende obwererawo anagwiritsidwa mwala? Kutalitali! Otsalira obwezeretsedwa anabwerera kudziko lawo lokondedwa mu 537 B.C.E. M’kupita kwa nthaŵi, motsogozedwa ndi “mitengo ya chilungamo” imeneyi—monga Ezara mlembi, mneneri Hagai ndi mneneri Zekariya, ndi mkulu wa ansembe Yoswa—mabwinja akale anamangidwanso. Akalonga, mwachitsanzo Nehemiya ndi Zerubabele, analamulira dzikolo mosayang’ana nkhope ndi mwachilungamo. Kachisi wa Yehova anamangidwanso, ndipo zogaŵira zake za moyo—madalitso a kusunga pangano lake—anayambiranso kuyenda. (Deuteronomo 30:19; Yesaya 48:17-20) Dalitso lina limene analandira ndi chidziŵitso. Ansembe anayambiranso ntchito yawo, ndipo anaphunzitsa anthu Chilamulo. (Malaki 2:7) Chotero, anthu anakhalanso amoyo mwauzimu ndipo anakhalanso atumiki a Yehova obala zipatso, monga momwe inachirira Nyanja Yakufa ndi kuyambitsanso ntchito yosodza yothandiza kwambiri.
14. Kodi n’chifukwa chiyani ulosi wa Ezekieli unali kudzakwaniritsidwa mokulirapo kuposa mmene unachitira Ayuda atabwerako ku undende wa ku Babulo?
14 Kodi masomphenya a Ezekieli anangokwaniritsidwa ndi zochitika zimenezi zokha? Ayi; akusonyezanso zinthu zina zazikulu kwambiri. Talingalirani: Kachisi yemwe Ezekieli anaona sanamangidwe monga anafotokozedwera. N’zoona kuti Ayuda anawakhulupirira zedi masomphenyawo natsatiradi zinthu zina pomanganso kachisi.b Komabe, kachisi wa m’masomphenyawo anali wamkulu kwambiri wosathanso kukwana pa Phiri la Moriya, malo amene kachisi wakale anamangidwapo. Ndiponso, kachisi wa Ezekieli sanali m’mudzi koma kwina kwake kutali pamalo apadera, pamene kuli kwakuti kachisi wachiŵiri anamangidwa pamalo amene wakale anali, m’mudzi wa Yerusalemu. (Ezara 1:1, 2) Komanso, m’kachisi wa Yerusalemu simunatulukepo mtsinje weniweni uliwonse. Chotero Israyeli wakale anangoona kukwaniritsidwa kochepa kwa ulosi wa Ezekieli. Zimenezi zikutanthauza kuti masomphenya ameneŵa ayenera kukwaniritsidwa mwauzimu ndipo mokulirapo.
15. (a) Kodi kachisi wauzimu wa Yehova anakhalako liti? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti masomphenya a Ezekieli sanakwaniritsidwe pamene Kristu anali padziko lapansi?
15 Mwachionekere, tiyenera kufunafuna kukwaniritsidwa kwakukulu kwa masomphenya a Ezekieli m’kachisi wauzimu wamkulu wa Yehova, amene mtumwi Paulo akufotokoza mwatsatanetsatane m’buku la Ahebri. Kachisi ameneyo anakhalako pamene Yesu Kristu anadzozedwa kukhala Mkulu wake wa Ansembe mu 29 C.E. Koma kodi masomphenya a Ezekieli anakwaniritsidwa m’tsiku la Yesu? Mwachionekere ayi. Yesu, monga Mkulu wa Ansembe, anakwaniritsa tanthauzo laulosi la Tsiku la Chitetezo mwa ubatizo wake, imfa yake yansembe, ndi kuloŵa kwake m’Malo Opatulikitsa, kumwamba. (Ahebri 9:24) Koma chochititsa chidwi n’chakuti masomphenya a Ezekieli satchula konse za mkulu wa ansembe kapena Tsiku la Chitetezo. Chotero zikuoneka kuti masomphenyawo sanali kusonya ku zaka za zana loyamba C.E. Nangano, kodi akunena za nthaŵi iti?
16. Kodi malo a masomphenya a Ezekieli akutikumbutsa za ulosi wina uti, ndipo zimenezi zikutithandiza motani kuzindikira nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwakukulu kwa masomphenya a Ezekieli?
16 Kuti tiyankhe, tiyeni tiyang’anenso masomphenyawo. Ezekieli analemba kuti: “M’masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m’dziko la Israyeli, nandikhalitsa pa phiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mudzi kumwera.” (Ezekieli 40:2) Malo a masomphenya ameneŵa, “phiri lalitali ndithu,” akutikumbutsa za Mika 4:1, amene amati: “Kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda, ndi mitundu ya anthu idzayendako.” Kodi ulosi umenewu ukukwaniritsidwa liti? Mika 4:5 akusonyeza kuti ukuyamba kukwaniritsidwa pamene amitundu adakali kulambira milungu yonama. Kwenikweni, ndi m’nthaŵi yathu ino, “masiku otsiriza,” pamene kulambira koyera kwakwezedwa, kubwezeretsedwa pamalo ake oyenera m’miyoyo ya atumiki a Mulungu.
17. Kodi ulosi wa pa Malaki 3:1-5 umatithandiza motani kudziŵa pamene kachisi wa m’masomphenya a Ezekieli anayeretsedwa?
17 Kodi n’chiyani chinatheketsa kubwezeretsa kumeneku? Kumbukirani kuti pachochitika chachikulu kwambiri m’masomphenya a Ezekieli, Yehova akufika pakachisi nalamula kuti nyumba yake iyeretsedwe kuchotsamo kupembedza mafano. Kodi kachisi wauzimu wa Mulungu anayeretsedwa liti? Pa Malaki 3:1-5, Yehova akulosera nthaŵi pamene “adzadza ku Kachisi wake” limodzi ndi “mthenga [wake] wa chipangano,” Yesu Kristu. Cholinga chake? “Adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka.” Kuyenga kumeneku kunayamba panthaŵi ya nkhondo yoyamba ya dziko. Zotsatira zake? Yehova wakhala m’nyumba yake ndipo wadalitsa dziko lauzimu la anthu ake kuyambira 1919 kupita m’tsogolo. (Yesaya 66:8) N’chifukwa chake tinganene kuti kukwaniritsidwa kofunika kwa ulosi wa Ezekieli wonena za kachisi kukuchitika m’masiku otsiriza.
18. Kodi masomphenya a kachisi adzakwaniritsidwa komaliza liti?
18 Mofanana ndi maulosi ena akubwezeretsa, masomphenya a Ezekieli adzakwaniritsidwanso komaliza m’Paradaiso. Ndi kokha panthaŵiyo pamene anthu a mtima wowongoka adzalandira mapindu onse a makonzedwe a kachisi wa Mulungu. Panthaŵiyo Kristu adzagwiritsa ntchito mtengo wa nsembe yake ya dipo, limodzi ndi ansembe ake akumwamba a 144,000. Anthu onse omvera olamulidwa ndi Kristu adzakhala angwiro. (Chivumbulutso 20:5, 6) Komabe, Paradaiso sangakhale nthaŵi yofunika kwambiri ya kukwaniritsidwa kwa masomphenya a Ezekieli. Chifukwa?
Masomphenyawo Akusumika pa Tsiku Lathu
19, 20. Kodi n’chifukwa chiyani kukwaniritsidwa kwakukulu kwa masomphenyawo kuyenera kuchitika lerolino ndipo osati m’Paradaiso?
19 Ezekieli anaona kachisi yemwe anafunikira kuyeretsedwa kuchotsamo kupembedza mafano ndi chigololo chauzimu. (Ezekieli 43:7-9) Kunena zoona zimenezi sizingakhudze kulambira Yehova m’Paradaiso. Ndiponso, ansembe a m’masomphenyawo amaimira kagulu ka ansembe odzozedwa pamene adakali padziko lapansi, osati ataukitsidwira kumwamba kapena mkati mwa Zaka Chikwi. Chifukwa? Onani kuti ansembewo akusonyezedwa akutumikira m’bwalo lamkati. Nkhani za m’makope apitawo a Nsanja ya Olonda zasonyeza kuti bwalo limeneli limaimira kaimidwe kauzimu kapadera ka ansembe aang’ono a Kristu pamene adakali padziko lapansi.c Onaninso kuti masomphenya amenewo akugogomezera kupanda ungwiro kwa ansembewo. Akuuzidwa kupereka nsembe za machimo awo. Akuchenjezedwa za ngozi ya kukhala wodetsedwa—mwauzimu ndi mwakhalidwe. Chotero sakuimira odzozedwa oukitsidwa, amene mtumwi Paulo analemba za iwo kuti: ‘Lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda.’ (1 Akorinto 15:52; Ezekieli 44:21, 22, 25, 27) Ansembe a m’masomphenya a Ezekieli akukhalira limodzi ndi anthu ndi kuwatumikira mwachindunji. Si mmene zidzakhalira m’Paradaiso, pamene kagulu ka ansembe kadzakhala kumwamba. Chotero, masomphenyawo akuonetsa chithunzi chabwino cha njira imene odzozedwa amagwirira ntchito mogwirizana ndi “khamu lalikulu” padziko lapansi lerolino.—Chivumbulutso 7:9; Ezekieli 42:14.
20 Chotero, masomphenya a Ezekieli a kachisi akusonyeza zotsatirapo zabwino za kuyeretsa kwauzimu kumene kukuchitika lerolino. Koma kodi zimenezo zikutanthauzanji kwa inu? Umenewu si mwambi wa zaumulungu wongolankhulapo basi. Masomphenya ameneŵa amakhudza kwambiri kulambira kwanu kwa tsiku ndi tsiku kwa Mulungu yekha woona, Yehova. M’nkhani yathu yotsatira, tidzaona chifukwa chake zimenezo zili choncho.
[Mawu a M’munsi]
a Zimenezi zingakhale zitamukhudza Ezekieli mwiniyo, pakuti amati nayenso anali wa banja la Zadoki la ansembe.
b Mwachitsanzo, Mishnah yakale imati m’kachisi womangidwanso, guwa la nsembe, zipata za kachisi zazitseko ziŵiri, ndi malo ophikira zinamangidwa motsatira masomphenya a Ezekieli.
c Onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 1996, tsamba 16; yachingelezi ya December 1, 1972, tsamba 718.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi kukwaniritsidwa koyamba kwa masomphenya a Ezekieli a kachisi ndi ansembe kunali kotani?
◻ Kodi masomphenya a Ezekieli a kugaŵa dziko anakwaniritsidwa motani poyamba?
◻ Pamene Israyeli wakale anabwezeretsedwa, kodi ndani anali akalonga ndipo ndani anali “mitengo ya chilungamo”?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani masomphenya a Ezekieli ayenera kukwaniritsidwa pamlingo waukulu m’masiku otsiriza?