Kodi Mdyerekezi Ndiye Amatidwalitsa?
MATENDA SAKANAKHALAKO. Mulungu anatilenga kuti tikhale ndi moyo kosatha tili ndi thanzi labwino. Cholengedwa chauzimu, Satana, ndiye anayambitsa kuti banja la anthu livutike ndi kudwala, kumva zoŵaŵa, ndi imfa pamene anapangitsa makolo athu oyambawo, Adamu ndi Hava, kuchimwa.—GENESIS 3:1-5, 17-19; AROMA 5:12.
KODI zimenezi zikutanthauza kuti mizimu ndi imene imayambitsa matenda onse mwachindunji? Monga tamvera m’nkhani yoyamba, ambiri lerolino amaganiza choncho. Agogo a Owmadji wachichepereyo amaganiza zimenezo. Koma kodi, kutsegula m’mimba kwa Owmadji—matenda omwe nthaŵi zina amapha ana m’madera otentha—ndi kochititsidwadi ndi mizimu yosaoneka?
Zomwe Satana Amachita
Baibulo limayankha funso limeneli momveka bwino. Poyamba, ilo limasonyeza kuti mizimu ya makolo athu singachite kalikonse kwa amoyo. Anthu akamwalira, “sadziŵa kanthu bi.” Alibe mzimu umene umapulumuka imfa. Amagona m’manda, mmene “mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa ngakhale nzeru.” (Mlaliki 9:5, 10) Akufa sangachititse amoyo kudwala mwanjira ina iliyonse!
Komabe, Baibulo limavumbula kuti mizimu yoipa ilipodi. Mpandu woyamba m’chilengedwe chonse ndiye cholengedwa chauzimu chimene tsopano timatcha kuti Satana. Zolengedwa zinanso zauzimu zinatsagana naye ndipo zimatchedwa ziŵanda. Kodi Satana ndi ziŵanda angayambitse matenda? Zachitika. Zina mwa zozizwitsa za kuchiritsa kwa Yesu zinaphatikizapo kuchotsa ziŵanda. (Luka 9:37-43; 13:10-16) Komabe, kuchiritsa kochitidwa ndi Yesu, nthaŵi zambiri sikunali kwa matenda oyambitsidwa ndi ziŵanda mwachindunji. (Mateyu 12:15; 14:14; 19:2) Mofananamo lerolino, matenda nthaŵi zambiri amayambitsidwa ndi zinthu zina zachilengedwe, osati ndi mizimu.
Nanga bwanji ponena zaufiti? Miyambo 18:10 amatitsimikizira kuti: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” Yakobo 4:7 amati: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” Inde, Mulungu akhoza kuteteza okhulupirira ake ku ufiti ndi ku mphamvu zauchiŵanda. Ndilo tanthauzo limodzi la mawu a Yesu akuti: “Choonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:32.
‘Bwanji nanga za Yobu?’ Ena angafunse. ‘Kodi si mzimu woipa umene unam’dwalitsa?’ Inde, Baibulo limanena kuti nthenda ya Yobu inayambitsidwa ndi Satana. Koma nkhani ya Yobu inali ina. Poyamba, Yobu kwa nthaŵi yaitali anali ndi tchinjirizo la Mulungu lomuteteza ku mphamvu za ziŵanda. Kenako, Satana anatsutsa Yehova chifukwa cha tchinjirizo lakelo pa Yobu, nafuna kukamukantha. Ndiye popeza zinaloŵetsamo nkhani zikuluzikulu, Yehova anachotsako pang’ono tchinjirizo lake pa wolambira wakeyo.
Komabe, Mulungu anaika malire. Pamene analola Satana kukavutitsa Yobu, Satana akanadwalitsa Yobu kwa nthaŵi yaitali ndithu, koma sakanamupha. (Yobu 2:5, 6) Potsirizira, mavuto a Yobu anatha, ndipo Yehova anam’patsa mfupo yaikulu chifukwa cha kukhulupirika kwake. (Yobu 42:10-17) Mfundo zimene kukhulupirika kwa Yobu kunatsimikizira zinalembedwa kalekalelo m’Baibulo ndipo n’zodziŵika kwa anthu onse. Sipafunikiranso chiyeso china changati chimenechi.
Kodi Satana Amachita Zinthu Motani?
Pafupifupi nthaŵi zonse, mgwirizano womwe ulipo pakati pa Satana ndi kudwala kwa anthu ndiwo wakuti Satana ananyenga banja la anthu loyambiriralo, ndipo linachimwa. Iye ndi ziŵanda zake sindiwo amachititsa mwachindunji mitundu yonse ya matenda. Komabe, sikuti Satana samayesa kutisonkhezera kusankha mopusa ndi kutitayitsa chikhulupiriro chathu, zimene zingawonongetse thanzi lathu. Iye sanalodze, kupha, kapena kukantha Adamu ndi Hava ndi matenda. Iye anasonkhezera Hava kusamvera Mulungu, ndipo Adamu anam’tsatira Hava m’kusamverako. Matenda ndi imfa ndizo zina mwa zotsatirapo zake.—Aroma 5:19.
Mneneri wosakhulupirikayo, Balamu, anagulidwa ndi mfumu ya Moabu kuti atemberere mtundu wa Israyeli, umene unali utamanga misasa m’malire a dziko la Moabu ndi kuchititsa mantha anthu m’dzikolo. Balamu anayesa kutemberera Israyeli, koma analephera chifukwa chakuti mtunduwo unali ndi tchinjirizo la Yehova. Pambuyo pake, Amoabu anayesa kukopa Israyeli kuti azipembedza mafano ndi kuchita nawo zachiwerewere. Aisrayeli anakopekadi, ndipo anataya tchinjirizo la Yehova.—Numeri 22:5, 6, 12, 35; 24:10; 25:1-9; Chivumbulutso 2:14.
Tingatengepo phunziro lofunika kwambiri pachochitika chakale chimenecho. Thandizo la Mulungu limapatsa alambiri ake okhulupirika tchinjirizo ku kukanthidwa kwachindunji ndi mizimu yoipa. Komabe, Satana angayeseyesebe kupangitsa athu kuti asiye chikhulupiriro chawo. Angayese kuwakopa kuti achite chisembwere. Kapena, monga mkango wobuma, angayese kuwaopseza kuti achite chinthu chimene chingawachotsere tchinjirizo la Mulungu. (1 Petro 5:8) Ndicho chifukwa chake mtumwi Paulo anatcha Satana kuti “iye amene anali nayo mphamvu ya imfa.”—Ahebri 2:14.
Agogo a Owmadji anayesetsa kukakamiza Hawa kuti agwiritse ntchito njirisi ndi zithumwa monga zom’teteza ku matenda. Kodi chikanachitika n’chiyani ngati Hawa akanagonjera? Akanasonyeza kukhala wopanda chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu, ndiponso sakanakhala ndi tchinjirizo lake.—Eksodo 20:5; Mateyu 4:10; 1 Akorinto 10:21.
Satana anayeseranso kukakamiza Yobu. Kum’phera banja lake, kumuwonongera chuma chake ndi thanzi lake sikunali kokwanira. Yobu anapatsidwanso uphungu woipa kwambiri ndi mkazi wake pamene anati: “Chitira Mulungu mwano, ufe.” (Yobu 2:9) Kenako, “mabwenzi” atatu anam’chezera ndipo mogwirizana anayesa kum’tsimikizira kuti iyeyo ndiye anali ndi tchimo, ndipo n’chifukwa chake anali kudwala. (Yobu 19:1-3) Mwanjira imeneyi, Satana anatengerapo mwayi Yobu atavutika kwambiri kuti am’fooketse ndi kusokoneza chikhulupiriro chake ponena za chilungamo cha Yehova. Koma ngakhale zidali choncho, Yobu anapitiriza kudalira Yehova monga chiyembekezo chake.—Yerekezerani ndi Salmo 55:22.
Nafenso titadwala tingapsinjike mtima. M’zochitika ngati zimenezo, Satana amachita changu kwambiri kuyesa kutichititsa zinthu mosemphana ndi chikhulupiriro chathu. Ndicho chifukwa chake, pamene tikudwala, ndi bwino kumakumbukira kuti gwero lenileni la mavuto athuwo ndi kupanda ungwiro kobadwa nako, osati mphamvu inayake yauchiŵanda. Kumbukirani, Isake wokhulupirikayo anakhala wakhungu zaka zingapo asanamwalire. (Genesis 27:1) Zoyambitsa matendawo sizinali mizimu yoipa koma ukalamba. Rakele anamwalira pakubereka, osati chifukwa cha Satana, koma chifukwa cha kufooka kwa thupi. (Genesis 35:17-19) Pomalizira, okhulupirika onse akalewo anamwalira—osati chifukwa cha kulodzedwa kapena kutembereredwa, koma chifukwa cha kupanda ungwiro kobadwa nako.
Kulingalira kuti mizimu yosaoneka ndi imene imayambitsa mwachindunji matenda alionse otigwera ndi msampha. Zingatichititse kuopa mizimu mopambanitsa. Kenako, tikadwala, tingafune kuti tisangalatse ziŵanda m’malo motalikirana nazo. Ngati Satana atiopseza kuti tiyambe kukhulupirira mizimu, chimenecho chingakhale chinyengo kwa Mulungu woona, Yehova. (2 Akorinto 6:15) Tiyenera kutsogozedwa ndi mantha aulemu kwa Mulungu, osati ndi mantha opanda pake a Mdani wake.—Chivumbulutso 14:7.
Owmadji wachichepereyo ndi wotetezeka bwino kale ku mizimu yoipa. Malinga ndi kunena kwa mtumwi Paulo, Mulungu amamuona mtsikanayo kukhala “woyera” chifukwa ali ndi mayi wokhulupirira, ndipo amayi wakeyo angapemphere kwa Mulungu kuti akhale ndi mwanayo mwa mzimu woyera. (1 Akorinto 7:14) Pokhala ndi chidziŵitso cholongosoka chimenechi, Hawa anatha kufunafuna thandizo labwino la Owmadji m’malo modalira njirisi.
Magwero Osiyanasiyana a Matenda
Anthu ambiri sakhulupirira mizimu. Akadwala, amapita kwa dokotala—ngati angathe. Inde, munthu wodwala angapite kwa dokotala koma osachirabe. Madokotala sangachite zozizwitsa. Koma ambiri amene amakhulupirira malodza, anthu amenenso akanachiritsidwa, amapita kwa dokotala mochedwa kwambiri. Iwo amayamba ayesa machiritso okhudzana ndi mizimu kaye, kenako pomalizira pake zitalephereka m’pamene amapita kwa dokotala. Ambiri ataya miyoyo yawo pamene akanatha kuchira.
Ena amamwalira mwadzidzidzi chifukwa chosadziŵa. Sadziŵa zizindikiro za matenda ndi njira zothandiza kuti apeŵe matendawo. Chidziŵitso chimathandiza kupeŵa mavuto achisawawa. Chochititsa chidwi n’chakuti ndi amayi ophunzira ochepa amene amatayikidwa ana muimfa poyerekezera ndi amayi osaphunzira. Inde, umbuli ungakhale wakupha.
Kusasamala ndiyo njira inanso yoyambitsira matenda. Mwachitsanzo, ambiri amadwala chifukwa cholekerera tizilombo kumangoyendayenda pa chakudya asanayambe kudya kapenanso chifukwa chakuti amene wakonza chakudyacho sanasambe m’manja asanayambe kuchigwira. Kugona opanda ukonde waudzudzu m’madera omwe malungo ndi ofala kwambiri kulinso koopsa.a M’nkhani za umoyo, ndi zoona kuti “kupeŵa kuposa kuchiza.”
Makhalidwe osasamala achititsa anthu miyandamiyanda kudwala ndi kumwalira mofulumira. Thanzi la anthu ambiri lawonongeka chifukwa chauchidakwa, chiwerewere, kugwiritsira ntchito mankhwala molakwika, ndi kusuta fodya. Ngati wina atsatira zilakolako zoipa zimenezi ndiyeno n’kudwala, kodi chingakhale chifukwa chakuti wina wamulodza kapena ndi mzimu wamudwalitsa? Ayi. Wadzidwalitsa yekha. Kunena kuti ndi mizimu imene yam’dwalitsa kungakhale kukana mlandu wa makhalidwe ake oipawo.
Inde, pali zina zomwe sitingathe kuzipeŵa. Mwachitsanzo, tingadwale chifukwa cha tizilombo ting’onoting’ono toyambitsa matenda kapena zinthu zoipitsidwa. Ndicho chimene chinachitikira Owmadji. Amayi wake sankadziwa chomwe chimayambitsa kutsegula m’mimbako. Ana ake sadwala kaŵirikaŵiri monga amachitira ana ena, chifukwa chakuti Hawa amasamala pakhomo pake ndi m’nyumba mwake ndiponso nthaŵi zonse amasamba m’manja asanayambe kukonza chakudya. Koma ana onse amadwalabe. Pali tizilombo tosiyanasiyana mitundu pafupifupi 25 timene tingayambitse matenda otsegula m’mimba. Mwina palibe amene angadziŵe kachilombo kamene kanayambitsa matenda a Owmadji.
Njira Yothetseratu Matenda
Kuti anthu azidwala sikulakwa kwa Mulungu. “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Ngati mmodzi wa alambiri ake adwala, Yehova amam’chirikiza mwauzimu. “Yehova adzam’gwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake.” (Salmo 41:3) Inde, Mulungu n’ngwachifundo. Iye amafuna kutithandiza, osati kutivulaza.
Inde, Yehova ali ndi njira yothetseratu matenda onse, ndiyo imfa ndi chiukiriro cha Yesu. Mwa nsembe ya dipo ya Yesu, anthu oongoka mtima amaomboledwa mu mkhalidwe wawo wauchimo ndipo potsiriza adzakhala ndi thanzi labwino ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Mateyu 5:5; Yohane 3:16) Zozizwitsa zimene Yesu anachita zinachitira chitsanzo kuchiritsa kwenikweni kumene Ufumu wa Mulungu udzabweretse. Mulungu adzachotsa Satana ndi ziŵanda zake. (Aroma 16:20) Inde, Yehova wasungira awo amene akum’khulupirira zinthu zabwino kwambiri. Tikungofunikira kukhala ofatsa ndi opirira.
Panthaŵi ino, Mulungu akugaŵira nzeru zothandiza ndi chitsogozo chauzimu kudzera m’Baibulo ndi mwa ubale wapadziko lonse wa alambiri okhulupirika. Amatisonyeza mmene tingapeŵere makhalidwe oipa amene angawononge thanzi lathu. Ndiponso amatipatsa mabwenzi oona amene angatithandize pamavuto.
Talingaliraninso za Yobu. Chikanakhala chinthu choipa kwambiri ngati Yobu akanapita kukaombeza kwa sing’anga! Zikanamuchotsera tchinjirizo la Mulungu, ndiponso akanaphonya madalitso onse amene amamuyembekezera pambuyo pa chiyeso chachikulucho. Mulungu sanaiŵale Yobu, ndiponso sangatiiŵale ifeyo. “Mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye,” anatero wophunzira Yakobo. (Yakobo 5:11) Nafenso ngati sitilema, tidzalandira madalitso abwino zedi m’nthaŵi yoikika ya Mulungu.
Kodi chinam’chitikira n’chiyani Owmadji wachichepereyo? Amayi wake anakumbukira nkhani ina m’magazini anzake a Nsanja ya Olonda, otchedwa Galamukani!, yonena za mankhwala akumwa obwezeretsa madzi m’thupi.b Anatsatira malangizo ake ndi kukonza mankhwalawo n’kum’mwetsa Owmadji. Tsopano msungwanayo alibwino ndiponso ali ndi thanzi labwino.
[Mawu a M’munsi]
a Anthu pafupifupi 500,000,000 amadwala malungo. Pafupifupi 2,000,000 amamwalira ndi matendaŵa pachaka, makamaka mu Afirika.
b Onani nkhani yakuti “A Salty Drink That Saves Lives!” (Chakumwa Chamchere Chimene Chimapulumutsa Moyo) mu Galamukani! yachingelezi ya September 22, 1985, masamba 24-5.
[Zithunzi patsamba 7]
Yehova wakonza njira yothetseratu matenda onse