Kodi Mukukwaniritsa Udindo Wanu Wonse kwa Mulungu?
“Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.”—MLALIKI 12:14.
1. Kodi Yehova wawapatsa chiyani anthu ake?
YEHOVA amachirikiza awo amene nthaŵi zonse amam’kumbukira monga Mlengi wawo Wamkulu. Mawu ake ouziridwawo amawaphunzitsa zinthu zofunikira kuti azim’kondweretsa mokwanira. Mzimu woyera wa Mulungu umawatsogolera pochita chifuniro cha Mulungu ndi ‘pobala zipatso muntchito yonse yabwino.’ (Akolose 1:9, 10) Komanso, Yehova amapereka chakudya chauzimu ndi chitsogozo chateokalase kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Chotero m’njira zambiri, anthu a Mulungu ali ndi madalitso ochokera kumwamba pamene akutumikira Yehova ndi kugwira ntchito yofunikayo yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—Marko 13:10.
2. Ponena za kutumikira Yehova, kodi pangabuke mafunso otani?
2 Akristu oona amasangalala potanganitsidwa ndi utumiki wopatulika kwa Yehova. Komano ena angafooke ndipo angalingalire kuti zoyesayesa zawo n’zachabechabe. Mwachitsanzo, nthaŵi zina Akristu odzipatulira angakayikire ngati kuyesayesa kwawo moona mtima kukuthandizadi mulimonse. Poganizira za phunziro la banja ndi zochita zina, mutu wa banja ungakhale ndi mafunso onga aŵa akuti: ‘Kodi Yehova akukondweradi ndi zimene tikuchita? Kodi tikukwaniritsa udindo wathu wonse kwa Mulungu?’ Mawu anzeru a mlaliki angatithandize kuyankha mafunso ameneŵa.
Kodi Zonse Ndi Zachabe?
3. Mogwirizana ndi Mlaliki 12:8, kodi n’kuchita chiyani kumene kuli kwachabechabe kwabasi?
3 Ena angaganize kuti mawu a munthu wanzeruyo ndi osalimbikitsa kwa aliyense. Kwa achinyamata ndi okalamba omwe. “Chabe zachabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi chabe.” (Mlaliki 12:8) Inde, kunyalanyaza Mlengi Wamkulu kuunyamata, kukalamba osam’tumikira, n’kungokhala ndi ukalamba wokha monga chinthu chimene tinakwaniritsapo pamoyo wonse wautaliwo ndiko kwachabechabe kwabasi. Zonse zakhala zachabe, kapena zopanda pake, kwa munthu woteroyo, ngakhale atafera m’chuma ndi kutchuka kwa m’dziko lino limene likugona mwa woipayo, Satana Mdyerekezi.—1 Yohane 5:19.
4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti si zonse zimene zili zachabe?
4 Si zonse zimene zili zachabe kwa awo amene akundika chuma chawo kumwamba monga atumiki okhulupirika a Yehova. (Mateyu 6:19, 20) Ali ndi zochita zochuluka m’ntchito yopindulitsa ya Ambuye, ndipotu thukuta lawolo silidzapita pachabe. (1 Akorinto 15:58) Koma ngati ndife Akristu odzipatulira, kodi ndife otanganidwa ndi ntchito imene Mulungu watipatsa m’masiku ano otsiriza? (2 Timoteo 3:1) Kapena kodi takhazikika m’moyo wosasiyana kwenikweni ndi wa anansi athu ena ambiri? Angagwirizane ndi zipembedzo zosiyanasiyana ndipo angakhale akhama kwambiri moti nthaŵi zonse amapita kunyumba zawo zopempherera ndipo amayesa kuchita zimene kulambira kwawoko kumafuna kwa iwo. Zoonadi, si olengeza uthenga wa Ufumu. Alibe chidziŵitso cholongosoka chonena kuti inoyi ndi “nthaŵi ya chimaliziro” ndipo sadziŵa kufunika kwa machaŵi m’masiku amene tikukhalamowa.—Danieli 12:4.
5. Ngati zinthu zomwe timazifuna mwachibadwa m’moyo zakhala nkhaŵa yathu yaikulu koposa, kodi tiyenera kuchitanji?
5 Ponena za nthaŵi yathu yoŵaŵitsayi, Yesu Kristu anati: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu. Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:37-39) Kudya ndi kumwa si koipa ngati kuchitidwa pamlingo woyenera, ndipo ukwati ndi makonzedwe amene Mulungu iyemwini anawayambitsa. (Genesis 2:20-24) Komano tikazindikira kuti zinthu zomwe timazifuna mwachibadwa m’moyo zakhala nkhaŵa yathu yaikulu koposa, bwanji osaitchula m’mapemphero nkhani imeneyo? Yehova angatithandize kuika zinthu za Ufumu patsogolo, kuchita zoyenera, ndi kukwaniritsa udindo wathu kwa Iye.—Mateyu 6:33; Aroma 12:12; 2 Akorinto 13:7.
Kudzipatulira Ndiponso Udindo Wathu kwa Mulungu
6. Kodi obatizidwa ena akulephera kukwaniritsa udindo wawo kwa Mulungu pa chinthu chofunika kwambiri chiti?
6 Akristu ena obatizidwa ayenera kupemphera ndi mtima wonse chifukwa chakuti sakuchita udindo wawo wautumiki umene anaulandira pamene anadzipatulira kwa Mulungu. Chaka chilichonse, anthu oposa 300,000 akhala akubatizidwa kwa zaka zingapo tsopano, koma chiŵerengero chonse cha Mboni zokangalika za Yehova sichikuwonjezeka pamlingo wofananawo. Ena amene anakhala olengeza Ufumu asiya kulengeza uthenga wabwino. Koma anthu ayenera kuchita utumiki wachikristu watanthauzo asanabatizidwe. Choncho akudziŵa ntchito imene Yesu anapatsa onse om’tsatira: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Ngati anthu obatizidwa sakutumikiranso monga Mboni zokangalika za Mulungu ndi Kristu, ndiye kuti iwo sakukwaniritsa udindo wawo wonse kwa Mlengi wathu Wamkulu, kusiyapo ngati ali ndi zovuta zazikulu kwambiri chifukwa cha thanzi kapena zinthu zina zomwe sangathe kuchitapo kalikonse.—Yesaya 43:10-12.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonkhana pamodzi nthaŵi zonse kuti tilambire?
7 Mtundu wa Israyeli wakale unali wodzipatulira kwa Mulungu, ndipo m’pangano la Chilamulo, anthu ake anali ndi maudindo pamaso pa Yehova. Mwachitsanzo, amuna onse anayenera kusonkhana pamadyerero atatu chaka chilichonse, ndipo mwamuna amene sanachite nawo Paskha mwadala anali ‘kusadzidwa’ mwa kuphedwa. (Numeri 9:13; Levitiko 23:1-43; Deuteronomo 16:16) Kuti akwaniritse udindo wawo kwa Mulungu monga anthu ake odzipatulira, Aisrayeli anayenera kusonkhana kuti alambire. (Deuteronomo 31:10-13) Chilamulo sichinanenepo kuti, ‘Muchite zimenezi ngati mungathe kuzichita popanda vuto lililonse.’ Kwa awo amene tsopano ndi odzipatulira kwa Yehova, ndithudi mfundoyi ikuchirikiza mawu a Paulo akuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane kuchikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lili kuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Inde, nthaŵi zonse kusonkhana ndi okhulupirira anzake ndi mbali ya udindo wa Mkristu wodzipatulira ndipo ayenera kuukwaniritsa kwa Mulungu.
Pendani Mosamala Zosankha Zanu!
8. N’chifukwa chiyani wachinyamata wodzipatulira ayenera kulingalira mwapemphero ponena za utumiki wake wopatulika?
8 Mwina ndinu wachinyamata wodzipatulira kwa Yehova. Mudzakhala ndi madalitso aakulu ngati muika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo wanu. (Miyambo 10:22) Mwapemphero ndi kulinganiza bwino, mungathere zaka zanu zaunyamata mumtundu winawake wa utumiki wanthaŵi zonse. Ndiyo njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti mukukumbukira Mlengi wanu Wamkulu. Apo ayi, mungayambe kuthera nthaŵi yanu ndi chidwi chanu pazinthu zakuthupi. Mofanana ndi ena ambiri, mungakwatire msanga ndi kuloŵa m’ngongole kuti mupeze zinthu zakuthupi. Ntchito yamalipiro abwino ingakudyereni nthaŵi ndi nyonga yanu yochuluka. Ngati muli ndi ana, mungafunikire kusamalira maudindo a m’banja kwa zaka zambirimbiri. (1 Timoteo 5:8) Mungakhale kuti simunaiŵale Mlengi wanu Wamkulu, koma ili nzeru kuzindikira kuti kukonzekereratu, kapena kusakonzekereratu, kungasonyeze zomwe muzidzachita m’moyo wanu mutakula. Kuuchikulire, mungadzakumbukire zaka zakumbuyo ndi kuganiza kuti zikanakhala bwino mukanathera nthaŵi yochuluka ya unyamata wanu muutumiki wopatulika kwa Mlengi wathu Wamkulu. Bwanji panopo osalingalirapo za tsogolo lanu mwapemphero, kuti mukhutire ndi utumiki wanu wopatulika kwa Yehova m’zaka zaunyamata wanu?
9. Kodi n’chiyani chimene chingakhale chotheka kwa munthu yemwe wakalamba amenenso kale anali ndi udindo waukulu mumpingo?
9 Lingalirani mmenenso zinthu zingakhalire kwa munthu amene anatumikirapo monga mbusa wa “gulu la Mulungu.” (1 Petro 5:2, 3) Pazifukwa zina, anatula udindowo mwa kufuna kwake. Inde, wakalamba tsopano, ndipo zingakhale zovuta kwambiri kwa iye kupitirizabe muutumiki wa Mulungu. Koma kodi ayenera kukalamiriranso maudindo ateokalase? Munthu woteroyo angadzetse madalitso ochuluka zedi kwa ena ngati angathe kukhala ndi maudindo owonjezeka mumpingo! Ndiponso popeza kuti palibe amene adzikhalira ndi moyo yekha, mabwenzi ndi okondedwa adzasangalala ngati angawonjezere utumiki wake, modzetsera Mulungu ulemerero. (Aroma 14:7, 8) Koposa zonse, Yehova sadzaiŵala zimene aliyense akuchita pom’tumikira. (Ahebri 6:10-12) Choncho, kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kukumbukira Mlengi wathu Wamkulu?
Zothandizira Kukumbukira Mlengi Wathu Wamkulu
10. N’chifukwa chiyani mlaliki anali ndi ziyeneretso zabwino kwambiri zoperekera zitsogozo pankhani ya kukumbukira Mlengi wathu Wamkulu?
10 Mlaliki anali ndi ziyeneretso zabwino kwambiri zoperekera zitsogozo ponena za kukumbukira Mlengi wathu Wamkulu. Yehova anayankha mapemphero ake ochokera pansi pa mtima mwa kum’patsa nzeru zodabwitsa. (1 Mafumu 3:6-12) Solomo anafufuza mosamala kwambiri zochitika zonse za anthu. Ndiponso, anauziridwa ndi Mulungu kuti alembe zimene anapeza kuti ena adzapindule nazo. Analemba kuti: “Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri. Mlalikiyo anasanthula akapeze mawu okondweretsa, ndi zolemba zowongoka ngakhale mawu oona.”—Mlaliki 12:9, 10.
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kulandira uphungu wanzeru wa Solomo?
11 Septuagint yachigiriki imatembenuza mawu ameneŵa kuti: “Ndiponso, chifukwa chakuti mlaliki anali wanzeru, chifukwa anaphunzitsa mtundu wa anthu nzeru; kuti khutu lipeze zosangalatsa m’mafanizo, mlaliki anafufuza mwakhama kuti apeze mawu osangalatsa, ndi kulemba mawu achilungamo, mawu a choonadi.” (The Septuagint Bible, lotembenuzidwa ndi Charles Thomson) Cholinga cha Solomo chinali kufika mtima oŵerenga zolemba zake mwa mawu okondweretsa ndi nkhani zochititsadi chidwi ndiponso zofunika. Popeza kuti mawu ake opezeka m’Malemba ndi ouziridwa ndi mzimu woyera, tingalandire zotsatira za kafukufuku wakeyo ndi uphungu wake wanzeru ndi mtima wonse.—2 Timoteo 3:16, 17.
12. M’mawu anu, mungalongosole motani zimene Solomo ananena zolembedwa pa Mlaliki 12:11, 12?
12 Ngakhale kusanakhale njira zamakono zosindikizira mabuku, kunali mabuku ambiri m’tsiku la Solomo. Kodi mabuku amenewo anayenera kuonedwa motani? Iye anati: “Mawu a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mawu amene mbusa mmodzi awapatsa mawu awo akunga misomali yokhomedwa zolimba. Pamodzi ndi izi [“kupatulapo izi,” NW], mwananga, tachenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.”—Mlaliki 12:11, 12.
13. Kodi mawu a anthu okhala ndi nzeru zaumulungu angakhale motani ngati zisonga, ndipo ndi ayani amene ali ngati “misomali yokhomedwa zolimba”?
13 Mawu a anthu okhala ndi nzeru zaumulungu amakhala ngati zisonga. Motani? Amasonkhezera oŵerenga kapena omvetsera ake kupita patsogolo mogwirizana ndi mawu amene aŵerenga kapena kumva. Ndiponso, awo amene amadzitangwanitsa ndi ‘kukundika mawu,’ kapena kuti zonena zanzerudi ndi zofunika, ali ngati “misomali yokhomedwa zolimba,” kapena yozikika zedi. Zingakhale chonchi chifukwa chakuti mawu abwino a anthu ameneŵa amasonyeza nzeru za Yehova ndipo angachirikize oŵerenga kapena omvetsera ndi kuwapangitsa kukhala okhazikika. Ngati ndinu kholo loopa Mulungu, kodi simuyenera kuyesetsa momwe mungathere kuti mukhomereze nzeru imeneyi m’maganizo ndi mumtima wa mwana wanu?—Deuteronomo 6:4-9.
14. (a) Kodi ndi “kuphunzira kwambiri” mabuku a mtundu wotani kumene kulibe phindu? (b) Kodi ndi mabuku ati amene tiyenera kuwakonda kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani?
14 Komano n’chifukwa chiyani Solomo ananena mawu amenewo ponena za mabuku? Eya, poyerekeza ndi Mawu a Yehova, mabuku osatha ambirimbiri a dziko lino ali ndi malingaliro wamba a anthu. Ambiri mwa malingaliro ameneŵa ndi malingaliro a Satana Mdyerekezi. (2 Akorinto 4:4) Chotero, “kuphunzira kwambiri” mabuku akudziko oterowo kulibe phindu lenileni lokhalitsa. Kwenikweni, ambiri mwa iwo angakhale owononga mwauzimu. Mofanana ndi Solomo, tiyeni tisinkhesinkhe pa zimene Mawu a Mulungu amanena ponena za moyo. Zimenezi zidzalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kutiyandikizitsa kwa Yehova. Kukondetsa mabuku ena kapena malangizo ochokera kwina kungatitopetse. Mabuku amenewo amakhala oipa ndi owononga chikhulupiriro mwa Mulungu ndi zifuno zake makamaka ngati ali ndi malingaliro akudziko otsutsana ndi nzeru yaumulungu. Chotero, tiyeni tikumbukire kuti mabuku opindulitsa zedi m’tsiku la Solomo ndi lathu ndi aja amene amasonyeza nzeru ya “mbusa mmodzi,” Yehova Mulungu. Iye wapereka mabuku 66 a Malemba Opatulika, ndipo ndiwo mabuku amene tiyenera kuwakondetsetsa. Baibulo ndi zofalitsa zothandiza za “kapolo wokhulupirika” zimatithandiza kukhala ‘om’dziŵadi Mulungu.’—Miyambo 2:1-6.
Udindo Wathu Wonse kwa Mulungu
15. (a) Kodi mungawalongosole motani mawu a Solomo onena za “udindo wonse wa anthu”? (b) Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikwaniritse udindo wathu kwa Mulungu?
15 Pomaliza kulongosola zotsatira za kufufuza kwake, mlalikiyo, Solomo, anati: “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi [“pakuti ndiwo udindo wonse wa anthu,” NW]. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.” (Mlaliki 12:13, 14) Mantha oyenerera, kapena kuti kusonyeza ulemu waukulu, kwa Mlengi wathu Wamkulu kudzatiteteza, ngakhalenso mabanja athu, kuti tisalondole zochitika zoika moyo pachiswe zimene zingadzetsere ifeyo ndi okondedwa athu chisoni chosaneneka. Mantha oyenerera a Mulungu ali oyera ndipo ndiwo chiyambi cha nzeru ndi chidziŵitso. (Salmo 19:9; Miyambo 1:7) Ngati tili ndi nzeru zozikidwa pa Mawu ouziridwa a Mulungu ndi kutsatira uphungu wake pazinthu zonse, tidzakhala tikukwaniritsa “udindo [wathu] wonse” kwa Mulungu. Sizofunika kuti tichite kulemba mpambo wa maudindowo iyayi. M’malo mwake, chofunika n’chakuti tiyang’ane ku Malemba pofuna kuthetsa mavuto a m’moyo ndi kuchita zinthu m’njira ya Mulungu nthaŵi zonse.
16. Ponena za chiweruzo, kodi Yehova adzachitanji?
16 Tiyenera kuzindikira kuti palibe chimene Mlengi wathu Wamkulu amalephera kuona. (Miyambo 15:3) Iye “adzanena mlandu wa zochita zonse.” Inde, Wamkulukuluyo adzaweruza zinthu zonse, kuphatikizapo zimene anthu sanaone. Kuzindikira mfundo zimenezi kungatisonkhezere kumvera malamulo a Mulungu. Koma chotisonkhezera chachikulu chiyenera kukhala chikondi cha pa Atate wathu wakumwamba, popeza mtumwi Yohane analemba kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Komanso popeza kuti malamulo a Mulungu analinganizidwa kuti atithandize kukhala ndi moyo wabwino kosatha, ndithudi kuwamvera sikoyenera chabe komanso n’kwanzerudi. Kuchita zimenezo sikolemetsa kwa okonda Mlengi Wamkulu. Iwo amafuna kukwaniritsa udindo wawo kwa iye.
Kwaniritsani Udindo Wanu Wonse
17. Kodi tidzachitanji ngati tikufunadi kukwaniritsa udindo wathu wonse kwa Mulungu?
17 Ngati ndife anzeru ndipo tikulakalakadi kukwaniritsa udindo wathu wonse kwa Mulungu, kuphatikiza pa kumvera malamulo ake, tidzakhalanso ndi mantha oopa kusam’kondweretsa. Zoonadi, “kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru,” ndipo omvera malamulo ake ali ndi “chidziŵitso chokoma.” (Salmo 111:10; Miyambo 1:7) Chotero tiyeni tichite zinthu mwanzeru ndi kumvera Yehova pazinthu zonse. Zimenezi n’zofunika makamaka tsopano, popeza Mfumu Yesu Kristu ilipo, ndipo tsiku limene idzapereka chiweruzo monga Woweruza woikidwa lili pafupi.—Mateyu 24:3; 25:31, 32.
18. Kodi n’chiyani chidzakhala chotsatira chake kwa ife ngati tikwaniritsa udindo wonse kwa Yehova Mulungu?
18 Aliyense wa ife tsopano akuyang’aniridwa ndi Mulungu. Kodi timakonda zinthu zauzimu, kapena kodi zisonkhezero zakudziko zafooketsa unansi wathu ndi Mulungu? (1 Akorinto 2:10-16; 1 Yohane 2:15-17) Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kuti tikondweretse Mlengi wathu Wamkulu. Ngati timvera Yehova ndi kusunga malamulo ake, tidzakana zinthu zachabe za dziko lomwe likupitali. Ndiyeno tingakhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dongosolo lazinthu latsopano lomwe Mulungu walonjeza. (2 Petro 3:13) Chimenechitu n’chiyembekezo chachikulu kwa onse amene akukwaniritsa udindo wawo wonse kwa Mulungu!
Kodi Mungayakhe Motani?
◻ N’chifukwa chiyani munganene kuti si zonse zimene zili zachabe?
◻ N’chifukwa chiyani Mkristu wachinyamata ayenera kulingalira mwapemphero ponena za utumiki wake wopatulika?
◻ Kodi ndi “kuphunzira kwambiri” mabuku a mtundu wotani kumene kulibe phindu?
◻ Kodi “udindo wonse wa anthu” n’chiyani?
[Chithunzi patsamba 20]
Si zonse zimene zili zachabe kwa amene akutumikira Yehova
[Chithunzi patsamba 23]
Mosiyana ndi mabuku ambiri a m’dzikoli, Mawu a Mulungu amatsitsimula ndipo n’ngopindulitsa