Moyo Wangwiro Si Loto Chabe!
Kodi dziko langwiro limatanthauzanji kwa inu? Talingalirani za chitaganya cha anthu momwe mulibe upandu, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, njala, umphaŵi, kapena kusoŵa chilungamo. Onse akusangalala ndi thanzi labwino la malingaliro ndi lakuthupi. Kulibe chisoni kapena kukhumudwa chifukwa ngakhale imfa yathetsedwa. Kodi kukhumba dziko lotero n’kwanzeru?
NGAKHALE kuti akudziŵa za kupita patsogolo kwa sayansi ndi njira zake, anthu ambiri sakhulupirira n’komwe kuti nzeru za anthu kapena maphunziro akuya zidzadzetsa dziko langwiro momwe onse adzakhala mu mtendere ndi chimwemwe. Kumbali ina, kunena zoona anthu ali n’cholinga chofuna kukonza zinthu ndi kuthetsa kupanda ungwiro. Inde, maloto wamba sangathandize opanda nyumba ndi osauka, kapena kukhutiritsa opuwala ndi odwala omwe akufunitsitsa kuthandizidwa mavuto awo. Dziko langwiro si anthu omwe adzalidzetsa. Ngakhale kuti chizunzo ndi kuponderezana n’zofala lerolino, komabe pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti dziko lomwe munganene kuti n’langwiro layandikiradi.
Pamene mukuganiza za moyo wangwiro, moyo wa Yesu Kristu ungafike m’malingaliro anu. Yesu sanali yekhayo munthu wangwiro amene anakhalako padziko lapansi. Adamu ndi Hava, olengedwa m’chifanizo cha Mulunguwo, anasangalala ndi moyo wangwiro m’paradaiso. Komabe, anataya malo awo aulemerero chifukwa cha kupandukira kwawo Atate wawo wakumwamba. (Genesis 3:1-6) Ngakhale kuti zili choncho, Mlengi anaika chikhumbo cha kukhala ndi moyo kosatha mwa anthu. Mlaliki 3:11 akuchitira umboni kuti: “Chinthu chilichonse [Mulungu] anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.”
Pamene kuli kwakuti kupanda ungwiro ndi uchimo zinatsogolera mtundu wa anthu ku moyo ‘wautsiru’ ndi “ukapolo wa chivundi,” tamverani mawu otonthoza a mtumwi Paulo. Iye akuti: “Chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:19-21) Baibulo likunena momveka bwino kuti kubwezeretsa moyo wangwiro wa anthu komwe Mulungu adzachita n’kotheka kupyolera mwa Yesu Kristu.—Yohane 3:16; 17:3.
Kuwonjezera pa chiyembekezo chosangalatsa cham’tsogolochi, tonsefe tingathe kukula mwauzimu, kuchititsa kupita kwathu patsogolo kuonekera ngakhale tsopano lino.
Yesani Kusachita zinthu Monkitsa
Yesu Kristu analingalira nkhani ya ungwiro kukhala yofunika kwambiri kotero kuti anauza khamu la anthu kuti: “Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa kumwamba ali wangwiro.” (Mateyu 5:48) Kodi Yesu anali kuyembekezeradi kuti ife tikhale angwiro m’dongosolo loipa lino? Ayi. Ndithudi tiyenera kuyesetsa kukulitsa mikhalidwe ya kuwoloŵa manja, chifundo, ndi chikondi kwa anthu anzathu, komatu nthaŵi zonse timalephera kuchita chomwe chili chabwino. Ngakhalenso mmodzi wa atumwi a Yesu analemba kuti: “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse. Tikanena kuti sitinachimwa, timuyesa Iye wonama, ndipo mawu ake sakhala mwa ife.”—1 Yohane 1:9, 10.
Komabe, tingawongolere momwe timadzionera ndi kuchitira ena, tikumapeŵa kuchita monyanyira. Ndani angapeze uphungu wabwino wokhalira wachikatikati, wopezera umunthu wabwino kuposa womwe ukupezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo? Kukulitsa makhalidwe monga chimwemwe ndi kusapambanitsa kudzatithandiza kukhala ogwirizana ndi anzathu kuntchito, ndi mnzathu wa muukwati, ndiponso makolo kapena ana athu. Mtumwi Paulo analangiza Akristu kuti: “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani. Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse.”—Afilipi 4:4, 5.
Mapindu a Kusachita Zinthu Monkitsa
Ngati muli wosapambanitsa m’ziyembekezo zanu ndipo mumapeŵa kudzizunza ndi kudzigonjetsa nokha poyesa kuchita zinthu mosalakwitsa kanthu, mumapindula inu eni komanso kupindulitsa ena. Kudziŵa zomwe mungathedi kuchita kumafuna nzeru ndi kukhala wosapambanitsa pa zomwe mukufuna kuchitazo. Kumbukirani, Mulungu anatilenga kuti tikhale padziko lino lapansi ndikuti tikhutire ndi ntchito yatanthauzo yomwe idzapindulitsa ife ndi anthu ena.—Genesis 2:7-9.
Ngati mwakhala mukufuna kuchita zomwe simungathe, bwanji osayang’ana kwa Yehova m’pemphero? Kupeza chiyanjo cha Mulungu kudzakupatsani mpumulo wochuluka. Yehova akudziŵa mapangidwe athu ndi kupanda ungwiro kwathu, chotero iye safuna zonkitsa komanso ndi wosavuta kum’khutiritsa. Wamasalmo akutitsimikizira kuti: “Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:13, 14) Tiyeneratu kuyamikira kwambiri kuti Mulungu amachita ndi anthu mwachifundo choncho! Amadziŵa zophophonya zathu, komabe ndife amtengo wapatali zedi kwa iye monga ana okondedwa.
M’malo moyesa kuchita zinthu mosalakwitsa kanthu, n’chanzeru kwabasi kukulitsa kuzindikira kwauzimu ndi kuchita zinthu mosamala! Komanso, tingatsimikizire kuti palibe munthu yemwe angalepheretse Yehova kukwaniritsa zifuno zake kubwezeretsa mtundu wa anthu ku ungwiro mu Ufumu wa Mulungu. Komabe kodi ungwiro wa munthu umatanthauzanji?
Moyo Wangwiro Wabwino Kuposa Malingaliro Ofuna Zangwiro Zokhazokha
Ungwiro sutanthauza kungokhala ndi malingaliro ofuna zangwiro zokhazokha. Awo amene ali ndi mwayi wodzakhala m’Paradaiso padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu ndithudi sadzakhala anthu ofuna zonkitsa, kapena odzilungamitsa. Chimodzi mwa zofunika kuti munthu adzapulumuke chisautso chachikulu ndicho kuyamikira nsembe ya dipo kuchokera mumtima. Mtumwi Yohane anafotokoza za khamu lalikulu lochokera mwa mtundu uliwonse kuti linachita zimenezo pamene linati: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Onse opulumuka chisautso chachikulu chomwe chayandikiracho adzakhala oyamikira kwambiri kuti mofunitsitsa Kristu anaŵafera ndikutinso anafera onse okhulupirira iye. Nsembe yake yachikondiyo inayala maziko odzetsera mpumulo wosatha kuchotsa kupanda ungwiro ndi zofooka zawo.—Yohane 3:16; Aroma 8:21, 22.
Kodi moyo wangwiro udzakhala wotani? M’malo mochita mpikisano ndi kukhala ndi zikhumbo zadyera, chikondi ndi chifundo pakati pa anthu zidzapanga moyo kukhala wosangalatsa, zidzathetsa nkhaŵa ndi kusadzidalira. Chifukwa cha chimenecho, moyo wangwiro sudzakhala wotopetsa kapena wonyong’onya. Mawu a Mulungu safotokoza zonse za Paradaiso koma amalongosola mtundu wa moyo womwe tiyenera kuuyembekezera. Mawuwo amati: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku amtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo.”—Yesaya 65:21-23.
M’malo movutika m’malingaliro za mtundu wa zosangalatsa, masitolo, sayansi, kapena mtengatenga zomwe Ufumuwo udzadzetsa, yerekezani inuyo mukusangalala ndi kukwaniritsidwa kwa mawu awa: “Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng’ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m’phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.” (Yesaya 65:25) Moyo wangwiro udzakhalatu wosiyana kwambiri ndi zomwe mukupeza lerolino! Ngati ndinu mmodzi wa oŵerengedwa kudzakhala ndi moyo m’nthaŵi imeneyo, mungakhale ndi chifukwa chokhulupirira kuti Atate wanu wachikondi wakumwamba adzalingalira za inu limodzi ndi banja lanu. “Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.”—Salmo 37:4.
Moyo wangwiro si loto chabe. Chifuno chachikondi cha Yehova chokhudza mtundu wa anthu chidzakwaniritsidwa ndithu. Inu ndi banja lanu mungakhale amodzi mwa omwe adzaukitsidwira ku moyo wangwiro waumunthu ndi kukhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Baibulo linaneneratu kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
[Chithunzi patsamba 6]
Tingawongolere momwe timadzionera ndi mmene timaonera ena, kupeŵa malingaliro ofuna zangwiro basi kapena kusafuna kulakwitsa zinthu
[Chithunzi patsamba 7]
Bwanji osadziyerekeza kuti mwayamba kale kusangalala m’mikhalidwe yamtendere ndi yolungama m’Paradaiso?