Kodi Atumiki a Mulungu Ndani Lerolino?
“Kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu; amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano.”—2 AKORINTO 3:5, 6.
1, 2. Ndi udindo uti umene Akristu onse a m’zaka za zana loyamba anali nawo, koma zinthu zinasintha motani?
M’ZAKA za zana loyamba m’Nyengo Yathu ino, Akristu onse anali ndi udindo winawake wofunika kwambiri—ntchito yolalikira uthenga wabwino. Onse anali odzozedwa ndiponso anali atumiki a pangano latsopano. Ena anali ndi maudindo owonjezeka, monga kuphunzitsa mumpingo. (1 Akorinto 12:27-29; Aefeso 4:11) Makolo anali ndi ntchito yaikulu m’banja. (Akolose 3:18-21) Koma onse ankachita nawo ntchito yoyambirira ndiponso yofunika kwambiri ya kulalikira. M’Chigiriki choyambirira cha m’Malemba Achikristu, udindo umenewo unali di·a·ko·niʹa—utumiki.—Akolose 4:17.
2 M’kupita kwa nthaŵi, zinthu zinasintha. Panabadwa gulu la atsogoleri achipembedzo, amene sanalole winanso kukhala ndi mwayi wolalikira koma iwo okha. (Machitidwe 20:30) Gulu limeneli linali laling’ono poliyerekeza ndi anthu onse odzitcha Akristu. Ochuluka otsalawo anangokhala okhulupirira wamba. Ngakhale kuti okhulupirira ameneŵa aphunzitsidwa kuti ali ndi zochita zina zomwe ayenera kukwaniritsa, kuphatikizapo kupereka zopereka zochirikizira atsogoleri awo, ambiri a iwo amangomvetsera nkhani yolalikirayi mwamphwayi.
3, 4. (a) Kodi anthu amatha motani kukhala atumiki m’Matchalitchi Achikristu? (b) Kodi ndani amayesedwa mtumiki m’Matchalitchi Achikristu, nanga n’chifukwa chiyani sizili zotero pakati pa Mboni za Yehova?
3 Atsogoleri achipembedzo amati ndi atumiki (kutembenuza mawu achilatini akuti di·aʹko·nos). a Kuti zimenezi zitheke, amayenera kumaliza maphunziro ena ake ku koleji kapena ku seminale ndipo kenako amaikidwa kukhala atumiki. Buku lamaumboni lotchedwa The International Standard Bible Encyclopedia limati: “Mawuwa akuti ‘kuika munthu kukhala mtumiki’ ndi ‘kuikidwa pautumiki’ kwenikweni akukhudza ulamuliro wapadera umene atumiki kapena ansembe amapatsidwa mwa mwambo winawake wa tchalitchi, wosonyeza kuti apatsidwa ulamuliro wolalikira Mawu kapena wochititsa mwambo wa tchalitchi, kapena wochita zonse ziŵiri.” Ndani amaika atumiki ameneŵa? Buku lamaumboni la The New Encyclopædia Britannica limati: “M’matchalitchi momwe adakali ndi mabishopu, nthaŵi zonse bishopu ndiye mtumiki woika anthu paudindo. M’matchalitchi a Pulesibiteriyani, kuika munthu kukhala mtumiki kumachitidwa ndi atumiki a m’bungwe lolamulira la m’deralo.”
4 Chotero, m’Matchalitchi Achikristu, anthu ochepa kwenikweni ndi amene amatha kupeza mwayi wokhala atumiki. Koma si mmene zilili ndi Mboni za Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti si mmene zinalili mumpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba.
Kodi Kwenikweni Atumiki a Mulungu Ndani?
5. Malinga ndi Baibulo, otumikira monga atumiki akuphatikizapo ndani?
5 Malinga ndi Baibulo, olambira onse a Yehova—akumwamba ndi apadziko lapansi—ndi atumiki. Angelo anatumikira Yesu. (Mateyu 4:11; 26:53; Luka 22:43) Angelonso ‘amatumikira iwo amene adzaloŵa chipulumutso.’ (Ahebri 1:14; Mateyu 18:10) Yesu anali mtumiki. Iye anati: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira.” (Mateyu 20:28; Aroma 15:8) Chotero, popeza kuti otsatira a Yesu anayenera ‘kulondola mapazi ake,’ n’zosadabwitsa kuti iwonso ayenera kukhala atumiki.—1 Petro 2:21.
6. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti ophunzira ake ayenera kukhala atumiki?
6 Kutatsala pang’ono kuti apite kumwamba, Yesu anati kwa ophunzira ake: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Ophunzira a Yesu anayenera kukhala opanga ophunzira—atumiki. Ophunzira atsopanowo omwe akawapanga akayenera kusunga zinthu zonse zimene Yesu analamula, kuphatikizapo lamulo loti akapange ophunzira. Mwamuna kapena mkazi, wachikulire kapena mwana, wophunzira weniweni wa Yesu Kristu akayenera kukhala mtumiki.—Yoweli 2:28, 29.
7, 8. (a) Ndi malemba ati amene amasonyeza kuti Akristu onse ndi atumiki? (b) Pankhani ya kuikidwa pautumiki, kodi pakubuka mafunso otani?
7 Mogwirizana ndi zimenezi, patsiku la Pentekoste 33 C.E., ophunzira onse a Yesu omwe analipo, amuna ndi akazi, analankhulira pamodzi “zazikulu za Mulungu.” (Machitidwe 2:1-11) Kuwonjezera apo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndi mtima munthu asonyeza chikhulupiriro cha chilungamo, koma ndi pakamwa alengeza kwa ena za chipulumutso.” (Aroma 10:10, NW) Polemba, Paulo sanalembere mawuŵa kwa kagulu kapadera ka atsogoleri achipembedzo, koma “kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu.” (Aroma 1:1, 7) Mofananamo, onse ‘oyera mtima amene anali m’Efeso, ndi iwo okhulupirika mwa Kristu Yesu’ anayenera ‘kuveka mapazi awo ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere.’ (Aefeso 1:1; 6:15) Ndipo onse amene anamvetsera kalata yolembedwa kwa Ahebri anayenera ‘kugwiritsa chilengezo chapoyera cha chiyembekezo chawo mosagwedera.’—Ahebri 10:23.
8 Komano, kodi ndi liti pamene munthu amakhala mtumiki? M’mawu ena, kodi amaikidwa liti kukhala mtumiki? Ndipo ndani amamuika pautumikiwo?
Kuikidwa Kukhala Mtumiki—Liti?
9. Kodi Yesu anaikidwa liti kukhala mtumiki, ndipo anamuika ndani?
9 Pafunso loti munthu amaikidwa liti kukhala mtumiki ndiponso ndani amamuika, tiyeni titenge chitsanzo cha Yesu Kristu. Iye analibe chikalata chonena kuti waikidwa kapena digiri ya ku seminale yochitira umboni kuti anali mtumiki, ndiponso sanaikidwe ndi munthu aliyense. Nangano tikuneneranji kuti anali mtumiki? Chifukwa chakuti mawu ouziridwa a Yesaya anakwaniritsidwa mwa iye. Mawuwo amati: “Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino.” (Luka 4:17-19; Yesaya 61:1) Mawuwo amapereka umboni wonse wakuti Yesu anatumidwa kudzalalikira uthenga wabwino. Anatumidwa ndi yani? Popeza kuti mzimu wa Yehova unam’dzoza kuchita ntchitoyo, mosakayikira Yesu anaikidwa ndi Yehova Mulungu. Kodi zimenezi zinachitika liti? Kwenikweni, mzimu wa Yehova unadza pa Yesu pamene anabatizidwa. (Luka 3:21, 22) Motero, iye anaikidwa kukhala mtumiki nthaŵi imene anabatizidwa.
10. Kodi mtumiki wachikristu amakhala ‘woyeneretsedwa mokwanira’ ndi yani?
10 Nanga bwanji za otsatira a Yesu a m’zaka za zana loyamba? Iwonso anapatsidwa udindo wokhala atumiki ndi Yehova. Paulo anati: “Kukwanira kwathu [“kuyeneretsedwa kwathu mokwanira,” NW] kuchokera kwa Mulungu; amenenso anatikwaniritsa [“anatiyeneretsa mokwanira,” NW] ife tikhale atumiki a pangano latsopano.” (2 Akorinto 3:5, 6) Kodi Yehova amayeneretsa motani alambiri ake kukhala atumiki? Tiyeni titenge chitsanzo cha Timoteo, amene Paulo anamutcha kuti “mtumiki wa Mulungu m’Uthenga Wabwino wa Kristu.”—1 Atesalonika 3:2.
11, 12. Kodi Timoteo anapita motani patsogolo kuti akhale mtumiki?
11 Mawu aŵa olembedwa kwa Timoteo akutithandiza kumvetsa mmene anakhalira mtumiki: “Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziŵa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 3:14, 15) Maziko a chikhulupiriro cha Timoteo, chimene chinam’sonkhezera kudzilengeza poyera, chinali chidziŵitso cha Malemba. Kodi anali kungoŵerenga payekha? Iyayi. Timoteo anafunikira thandizo kuti apeze chidziŵitso cholongosoka ndi kuzindikira kwauzimu pa zinthu zimene anali kuŵerenga. (Akolose 1:9) Chotero Timoteo ‘anatsimikiza mtima.’ Popeza kuti anadziŵa Malemba “kuyambira ukhanda,” alangizi ake oyambirira ayenera kuti anali amayi ake ndi agogo ake, popeza atate ake akuoneka kuti sanali okhulupirira.—2 Timoteo 1:5.
12 Komabe, panalinso zina zambiri zothandiza kuti Timoteo akhale mtumiki. Chinthu china n’chakuti chikhulupiriro chake chinalimbitsidwa mwa kuyanjana ndi Akristu a m’mipingo yoyandikana nayo. Tikudziŵa bwanji? Chifukwa chakuti Paulo atakumana ndi Timoteo nthaŵi yoyamba, mnyamatayo “anam’chitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.” (Machitidwe 16:2) Komanso, m’masiku amenewo abale ena ankalembera mipingo makalata owalimbikitsa. Ndipo oyang’anira anali kuichezera mipingoyo pofuna kuilimbikitsa. Makonzedwe ngati ameneŵa anathandiza Akristu monga Timoteo kupita patsogolo mwauzimu.—Machitidwe 15:22-32; 1 Petro 1:1.
13. Kodi Timoteo anaikidwa liti kukhala mtumiki, ndipo munganenerenji kuti kupita kwake patsogolo mwauzimu sikunathere pamenepo?
13 Mogwirizana ndi lamulo la Yesu lolembedwa pa Mateyu 28:19, 20, ndife otsimikiza kuti panthaŵi ina chikhulupiriro cha Timoteo chinam’sonkhezera kutsanzira Yesu ndi kubatizidwa. (Mateyu 3:15-17; Ahebri 10:5-9) Chimenechi chinali chizindikiro chakuti Timoteo wadzipatulira kwa Mulungu ndi mtima wonse. Panthaŵi ya ubatizo wake Timoteo anakhala mtumiki. Kuyambira pamenepo, moyo wake, nyonga zake, ndi zonse zomwe anali nazo zinakhala za Mulungu. Ndiyo inali mbali yofunika kwambiri ya kulambira kwake, “utumiki wopatulika.” Komabe, Timoteo sanangokhala, n’kukhutira ndi zimenezo. Iye anapitirizabe kukula mwauzimu, kukhala mtumiki wokhwima wachikristu. Zimenezi zinatheka chifukwa chakuti Timoteo ankayanjana kwambiri ndi Akristu okhwima monga Paulo, ankachita phunziro laumwini, komanso chifukwa cha ntchito yake yolalikira mwachangu.—1 Timoteo 4:14; 2 Timoteo 2:2; Ahebri 6:1.
14. Lerolino, kodi munthu ‘wofuna moyo wosatha’ amapita motani patsogolo kuti akhale mtumiki?
14 Lerolino, kuikidwa pautumiki wachikristu n’kofanana. Munthu amene ali ‘wofuna moyo wosatha’ amathandizidwa kuphunzira za Mulungu ndi zifuno zake mwa phunziro la Baibulo. (Machitidwe 13:48, NW) Munthuyo amaphunzira kutsatira mfundo zamakhalidwe za m’Baibulo m’moyo wake ndipo amaphunziranso kupemphera mwatanthauzo kwa Mulungu. (Salmo 1:1-3; Miyambo 2:1-9; 1 Atesalonika 5:17, 18) Amayanjana ndi okhulupirira ena ndipo amapindula ndi zogaŵira ndi makonzedwe a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47; Miyambo 13:20; Ahebri 10:23-25) Motero amapita patsogolo mwa maphunziro olinganizidwa bwino.
15. Chimachitika n’chiyani munthu akabatizidwa (Muonenso mawu a mmunsi.)
15 M’kupita kwa nthaŵi, wophunzira Baibuloyo atakulitsa chikondi chake pa Yehova Mulungu ndiponso atakhala ndi chikhulupiriro cholimba m’nsembe ya dipo, amafuna kupatulira moyo wake wonse kwa Atate wake wakumwamba. (Yohane 14:1) Amadzipatulira moteremu m’pemphero lapayekha ndipo kenako amabatizidwa monga chizindikiro chapoyera cha kudzipatulira kumene anachita payekha kumeneko. Ubatizo wake ndiwo mwambo wake wa kuikidwa pautumiki chifukwa m’pamene amadziŵika kuti ndi mtumiki wodzipatulira kotheratu, di·aʹko·nos, wa Mulungu. Ayenera kukhala wopatukana ndi dziko. (Yohane 17:16; Yakobo 4:4) Wadzipereka mwathunthu monga “nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu” popanda kulingalira zinanso. (Aroma 12:1)b Iye ndi mtumiki wa Mulungu, wotsanzira Kristu.
Kodi Utumiki Wachikristu N’chiyani?
16. Kodi zina mwa ntchito za Timoteo monga mtumiki zinali zotani?
16 Kodi utumiki wa Timoteo unaphatikizapo chiyani? Anali ndi ntchito zapadera monga mnzake wa Paulo woyendayenda naye. Ndipo atakhala mkulu, Timoteo analimbikira kuphunzitsa ndi kulimbitsa Akristu anzake. Koma mbali yaikulu ya utumiki wake, monga momwe zinalili ndi Yesu ndi Paulo, inali kulalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 4:23; 1 Akorinto 3:5) Paulo anauza Timoteo kuti: ‘Koma iwe, khala maso m’zonse, imva zoŵaŵa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.’—2 Timoteo 4:5.
17, 18. (a) Kodi Akristu amachita utumiki uti? (b) Kodi ntchito yolalikira ndi yofunika motani kwa mtumiki wachikristu?
17 Zilinso momwemo ndi atumiki achikristu lerolino. Iwo amachita utumiki wothandiza anthu, ntchito yolalikira uthenga wabwino, kutsogolera ena ku chipulumutso pamaziko a nsembe ya Yesu ndi kuphunzitsa ofatsa kuitanira pa dzina la Yehova. (Machitidwe 2:21; 4:10-12; Aroma 10:13) Amapereka umboni wa m’Baibulo wosonyeza kuti Ufumu ndiwo chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu wovutikawu ndipo amasonyeza kuti ngakhale tsopano zinthu zimakhala zabwinopo ngati titsatira mfundo zamakhalidwe zaumulungu. (Salmo 15:1-5; Marko 13:10) Koma mtumiki wachikristu salalikira kungoti awongolere zovuta za anthu zalero zokha iyayi. M’malo mwake, amaphunzitsa kuti ‘kupembedza kukhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’—1 Timoteo 4:8.
18 Zoonadi, atumiki ochuluka lerolino ali ndi njira zowonjezera zotumikirira, zimene zingakhale zosiyana kwa Mkristu aliyense. Ambiri ali ndi maudindo a pabanja. (Aefeso 5:21–6:4) Akulu ndi atumiki otumikira ali ndi ntchito za mumpingo. (1 Timoteo 3:1, 12, 13; Tito 1:5; Ahebri 13:7) Akristu ambiri amathandiza pomanga Nyumba za Ufumu. Ena ali ndi mwayi wosangalatsa zedi wogwira ntchito monga antchito odzifunira pa imodzi mwa nyumba za Beteli za Watch Tower Society. Komabe, atumiki onse achikristu amalalikira nawo uthenga wabwino. Palibe kupatula. Kuchita nawo ntchito yolalikirayi n’kumene kumasonyeza munthu poyera kuti ndi mtumiki weniweni wachikristu.
Maganizo a Mtumiki Wachikristu
19, 20. Kodi atumiki achikristu ayenera kukulitsa maganizo otani?
19 Atumiki ambiri a m’Matchalitchi Achikristu amayembekezera kulandira ulemu wapadera, ndipo amalandira mayina aulemu monga “levulendi” ndi “abambo.” Komabe, mtumiki wachikristu amadziŵa kuti Yehova yekha ndiye woyenera kuopedwa chotero. (1 Timoteo 2:9, 10) Palibe mtumiki wachikristu amene amafuna kulandira ulemu waukulu ngati umenewo kapena amene amafuna kutchedwa mayina apadera. (Mateyu 23:8-12) Amadziŵa kuti tanthauzo lenileni la di·a·ko·niʹa ndilo “utumiki.” Verebu lake nthaŵi zina limagwiritsidwa ntchito m’Baibulo ponena za kutumikira munthu, monga kuperekera zakudya ku thebulo. (Luka 4:39; 17:8; Yohane 2:5) Ngakhale kuti mawuwo amagwiritsidwa ntchito pofotokoza utumiki wapamwamba kwambiri wachikristu, di·aʹko·nos ndi mtumikibe.
20 Chotero palibe mtumiki wachikristu amene ayenera kudzimva ngati wofunika kuposa ena. Atumiki enieni achikristu—ngakhale awo okhala ndi udindo wapadera mumpingo—ndi akapolo odzichepetsa. Yesu anati: “Amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.” (Mateyu 20:26, 27) Posonyeza ophunzira ake maganizo oyenera kuwakulitsa, Yesu anasambitsa mapazi awo, kuchita ntchito ya kapolo wotsika koposa. (Yohane 13:1-15) Utumikitu wodzichepetsa kwabasi! Chotero, atumiki achikristu amatumikira Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu modzichepetsa. (2 Akorinto 6:4; 11:23) Amasonyeza kudzichepetsa kwa mumtima potumikirana. Ndipo pamene alalikira uthenga wabwino, iwo amatumikira anansi awo osakhulupirira mosadzikonda.—Aroma 1:14, 15; Aefeso 3:1-7.
Pirirani mu Utumiki
21. Kodi Paulo anafupidwa motani popirira mu utumiki?
21 Kwa Paulo, kukhala mtumiki kunafuna kupirira. Anauza Akolose kuti anavutika kwambiri kuti alalikire uthenga wabwino kwa iwo. (Akolose 1:24, 25) Komabe, chifukwa chakuti anapirira, ochuluka analandira uthenga wabwino ndipo anakhala atumiki. Iwo anabadwa monga ana aamuna a Mulungu ndiponso abale ake a Yesu Kristu, oyembekeza kukhala zolengedwa zauzimu pamodzi ndi iye kumwamba. Ndi mphoto yaikulu kwambiri ya kupirira!
22, 23. (a) N’chifukwa chiyani atumiki achikristu lerolino afunikira kupirira? (b) Kodi ndi zipatso zosangalatsa zotani zimene zimadza ndi kupirira kwachikristu?
22 Kupirira n’kofunika kwambiri lerolino kwa awo omwe ndi atumiki enieni a Mulungu. Ochuluka a iwo akulimbana ndi matenda kapena zopweteka zodza ndi ukalamba tsiku ndi tsiku. Makolo—ochuluka opanda mnzawo wa muukwati—akulimbikira kwambiri kulera ana awo. Molimba mtima, ana akupeŵa zisonkhezero zoipa zowazinga kusukulu. Akristu ochuluka ali pamavuto aakulu a ndalama. Ndiponso ambiri akuvutika ndi chizunzo kapena akuyang’anizana ndi zovuta zina chifukwa cha “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino! (2 Timoteo 3:1) Inde, atumiki a Yehova oposa mamiliyoni asanu ndi imodzi lerolino akugwirizana ndi mtumwi Paulo ponena kuti: “M’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m’kupirira kwambiri.” (2 Akorinto 6:4) Atumiki achikristu saleka. Ayeneradi kuyamikiridwa pa kupirira kwawo.
23 Kuwonjezera apo, monga momwe zinalili ndi Paulo, kupirira kumadzetsa zipatso zosangalatsa. Mwa kupirira, timasunga unansi wathu ndi Yehova ndi kukondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Timalimbitsa chikhulupiriro chathu ndipo timapanga ophunzira, kuwonjezera unyinji wa abale achikristu. (1 Timoteo 4:16) Yehova wachirikiza atumiki ake ndipo wadalitsa utumiki wawo m’masiku ano otsiriza. Chotsatira chake n’chakuti omalizira a m’gulu la 144,000 asonkhanitsidwa, ndipo anthu mamiliyoni ambiri ali ndi chiyembekezo chotsimikizirika chodzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Luka 23:43; Chivumbulutso 14:1) Ndithudi, utumiki wachikristu n’chizindikiro cha chifundo cha Yehova. (2 Akorinto 4:1) Tiyeni tonsefe tiusamalire kwambiri ndi kuyamikira kuti zipatso zake zidzakhalapo kosatha.—1 Yohane 2:17.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu achigiriki akuti di·aʹko·nos ndiwo gwero la mawu akuti “dikoni,” munthu waudindo winawake m’tchalitchi. M’matchalitchi ena, akazi amatha kukhalanso paudikoni.
b Ngakhale kuti Aroma 12:1 kwenikweni amanena za Akristu odzozedwa, mfundo yakeyo imakhudzanso “nkhosa zina.” (Yohane 10:16) Ameneŵa “adziphatika okha kwa Yehova, kuti am’tumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake.”—Yesaya 56:6.
Kodi Mungalongosole?
• Kodi Akristu onse a m’zaka za zana loyamba anali ndi udindo wotani?
• Kodi mtumiki wachikristu amaikidwa liti ndipo amamuika ndani?
• Kodi mtumiki wachikristu ayenera kukhala ndi maganizo otani?
• N’chifukwa chiyani mtumiki wachikristu ayenera kupirira pokumana ndi mavuto?
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Timoteo anaphunzitsidwa Mawu a Mulungu kuyambira paukhanda. Iye anakhala mtumiki woikidwa atabatizidwa
[Chithunzi patsamba 18]
Ubatizo umasonyeza kuti munthu wadzipatulira kwa Mulungu ndipo m’pamene munthu amaikidwa kukhala mtumiki
[Chithunzi patsamba 20]
Atumiki achikristu ndi okonzeka kutumikira