Mitengo Imene Imakhalitsa
Patherezi pamaoneka kuti si malo abwino kukhalapo, makamaka ngati ndi pamwamba penipeni pa phiri. Komabe, ngakhale kuti maloŵa ndi oipa, mitengo ina ya m’phiri imakangamira zolimba patherezipo ndipo imapirira kuzizira kwadzaoneni nthaŵi ya chisanu ndi chilala nthaŵi ya chilimwe.
NTHAŴI zambiri, mitengo yolimba kwambiri imeneyi ndi yaing’ono poiyerekeza ndi mitundu ina yofanana nayo imene imakhala m’zigwa. Thunthu lawo n’lokakala ndi lopiringidzika ndipo imakula mopinimbira. Mitengoyi imakulira m’nyengo yoipa mmene dothi lakenso n’lochepa ndipo zimenezi zimaiumba ndi kuitengulira.
Popeza imapirira m’dera loipa kwambiri padziko lapansi, mwina mungaganize kuti imangokhala ndi moyo kwa nthaŵi yochepa chabe. Komatu sizili choncho. Ena akuti Metusela, mtengo wa bristlecone pine umene uli pamtunda wa mamita 3,000 m’phiri la White Mountains ku California, uli ndi zaka 4,700. Buku lakuti The Guinness Book of Records 1997 likuti umenewu ndi mtengo wamoyo wakale kwambiri papulaneti lino. Edmund Schulman amene anafufuza za mitengo yakale imeneyi anafotokoza kuti: “[Mitengo ya ] bristlecone pine . . . ikuoneka ngati imakhalabe ndi moyo chifukwa cha zovuta. Mitengo yonse yaikulu [ya pine] ku White Mountains imapezeka pamtunda wa mamita pafupifupi 3,000 m’chipululu chouma cha miyala.” Schulman anapezanso kuti mitengo yakale kwambiri ya mitundu ina ya pine imakuliranso m’malo oipa kwambiri.
Ngakhale kuti imalimbana ndi zovuta, mitengo yopirira imeneyi imapindula kwambiri ndi madalitso aŵiri amene ili nawo. Popeza mitengoyi imakhala kwayokha kumene zomera zina zimapezeka mwa apo ndi apo, imatetezeka ku moto wolusa wa m’nkhalango womwe umawononga kwambiri mitengo yokhwima. Chachiŵiri, mitengoyi ndi yolimba kwambiri chifukwa mizu yake imazikika zolimba pathanthwe ndipo ndi chivomezi chokha chimene chingaisunthe.
M’Baibulo atumiki okhulupirika a Mulungu anawayerekeza ndi mitengo. (Salmo 1:1-3; Yeremiya 17:7, 8) Iwonso amakumana ndi zovuta chifukwa cha mmene zinthu zilili m’dziko limene akukhalali. Kuzunzika, matenda, kapena umphaŵi zimayesa chikhulupiriro chawo modetsa nkhaŵa, makamaka ngati ziyesozo zikupitiriza chaka ndi chaka. Komabe, Mlengi wawo, amene analenga mitengo imene imapirira zovuta, akuwatsimikizira olambira ake kuti awathandiza. Baibulo likulonjeza amene akupirirabe kuti: “Adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.”—1 Petro 5:9, 10.
Verebu lachigriki lotembenuzidwa kuti “pirira” m’Baibulo limatanthauza ‘kukhalabe wosasunthika, wolimba, kapena kuchitabe khama.’ Mofanana ndi mitengo ya m’mapiri, munthu afunika mizu yamphamvu kuti apirire. Akristu ayenera kuzika mizu mwa Yesu Kristu kuti akhale olimba. Paulo analemba kuti: “Monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye, ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m’chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.”—Akolose 2:6, 7.
Paulo anadziŵa kufunika kozika mizu yauzimu mwamphamvu. Iyenso analimbana ndi “munga m’thupi,” ndipo anapirira chizunzo chankhanza mu utumiki wake wonse. (2 Akorinto 11:23-27; 12:7) Koma anapeza kuti mwa mphamvu ya Mulungu anatha kupitiriza utumiki wake. Ananena kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”—Afilipi 4:13.
Monga tikuonera chitsanzo cha Paulo, Mkristu atha kupirira osati kokha pamene zinthu zili bwino. Monga mitengo ya m’mapiri imene imapirira mikuntho kwa zaka zambiri, tingakhalebe osasunthika ngati tizika mizu mwa Kristu ndi kudalira mphamvu zimene Mulungu amatipatsa. Ndiponso, ngati tipirira mpaka chimaliziro, tidzaona Mulungu akukwaniritsa lonjezo lina lakuti: “Monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga.”—Yesaya 65:22; Mateyu 24:13.