Kodi Yesu Amapulumutsa Motani?
“Yesu amapulumutsa!” Yesu ndiye Mpulumutsi wathu!” M’mayiko ambiri padziko lonse lapansi, mawu ameneŵa amalembedwa m’makoma a nyumba ndi m’malo ena komwe anthu onse amatha kupitako. Namtindi wa anthu amakhulupirira moona mtima kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wawo. Ngati mutawafunsa kuti, “Kodi Yesu amatipulumutsa motani?” Iwo mwina angayankhe kuti, “Yesu anatifera ife,” kapena kuti, “Yesu anafera machimo athu.” Inde, imfa ya Yesu imatipulumutsadi. Koma kodi imfa ya munthu mmodzi ingalipire bwanji machimo a anthu miyandamiyanda? Ngati wina akanakufunsani kuti, “Kodi imfa ya Yesu imatipulumutsa motani?” kodi mukanayankha bwanji?
YANKHO lomwe Baibulo limapereka pa funso limeneli n’losavuta ndipo n’lomveka ndiponso n’lofunika kwambiri. Koma kuti timvetse kufunika kwake, choyamba tiyenera kuona moyo ndi imfa ya Yesu monga njira yothetsera vuto linalake lalikulu kwambiri. Tikatero titha kumvetsa bwinobwino kukula kwa mtengo wa imfa ya Yesu.
Mulungu mwa kulola Yesu kupereka moyo wake, anali kuwongola zinthu zomwe zinalakwika Adamu atachimwa. Zotsatira za tchimolo zinalitu zoopsa kwambiri. Munthu woyambayo Adamu ndi mkazi wake Hava anali angwiro. Munda wokongola wa Edene ndiwo unali mudzi wawo. Mulungu anawapatsa ntchito yokhala ndi cholinga ya kusamalira mudzi wawo wokongolawo. Anayenera kuyang’anira zamoyo zina padziko lapansi. Iwo akanatha kudzaza dziko lapansi ndi anthu a mtundu wawo ndi kufutukula paradaiso padziko lonse lapansi. (Genesis 1:28) Anawapatsatu ntchito yabwino ndi yosangalatsa bwanji! Ndiponso anali ogwirizana mwachikondi. (Genesis 2:18) Iwo sanasoŵe kanthu kalikonse. Anali oti adzakhala ndi moyo wachisangalalo kwamuyaya.
N’zovuta kumvetsa chifukwa chimene Adamu ndi Hava anachimwira. Komabe anthu aŵiri oyambirirawo anapandukira amene anawalenga weniweniyo, Yehova Mulungu. Mwa kugwiritsa ntchito njoka, mngeloyo Satana Mdyerekezi ananyenga Hava kuti asamvere Yehova ndipo Adamu anatsatira mkazi wakeyo.—Genesis 3:1-6.
Sitingachite kufunsa zomwe Mlengi akanachita ndi Adamu ndi Hava. Iye anali ataneneratu zotsatira za kusamvera kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Ndiyeno atadya, funso lofunika kwambiri linayenera kuyankhidwa.
Vuto Losaneneka la Anthu
Tchimo loyamba linabweretsa vuto ladzaoneni kwa anthu. Adamu anali ndi moyo wangwiro poyamba. Choncho, ana ake nawonso akanakhala ndi moyo wosatha wangwiro. Komabe, Adamu anachimwa asanabale mwana ndi mmodzi yemwe. Chotero pamene ankalandira chiweruzo choti: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera,” mtundu wonse wa anthu unali ukadali m’chiuno mwake. (Genesis 3:19) Choncho pamene Adamu anachimwa ndi kuyamba kufa monga momwe Mulungu ananenera, anthu onse pamodzi ndi Adamuyo anaweruzidwa kuti azifa.
Kenako moyenerera mtumwi Paulo analemba kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, [Adamu] ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Inde, chifukwa cha tchimo loyambalo, ana amene anayenera kubadwa ali angwiro ndi kukhala ndi moyo wamuyaya, anabadwa n’kumayembekezera kudwala, kukalamba, ndi kufa.
Wina anganene kuti, “Chimenechi si chilungamo. Ife sitinasankhe kusamvera Mulungu. Adamu ndiye anatero. Ndiyeno zikutheka bwanji kuti ife titaye mwayi wokhala ndi moyo wosatha ndi chimwemwe?” Tikudziŵa kuti ngati khoti litalamula mwana kuti akakhale m’ndende chifukwa choti bambo ake aba galimoto, mwanayo angadandaule moyenerera kuti: “Chimenechi si chilungamo! Ine sindinalakwe chilichonse.”—Deuteronomo 24:16.
Satana ayenera kuti ankaganiza kuti agwiritsa njakata Mulungu akanyenga mwamuna ndi mkazi oyambawo kuti achimwe. Mdyerekezi anachita zimenezi koyambirira kwenikweni kwa mbiri ya anthu, mwana ndi mmodzi yemwe asanabadwe. Adamu atachimwa, funso lofunika kwambiri linali lakuti, Kodi Yehova adzachita nawo bwanji ana amene Adamu ndi Hava adzakhale nawo?
Yehova Mulungu anachita chilungamo. Munthu wolungama Elihu anati: “N’kutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.” (Yobu 34:10) Ndipo mneneri Mose analemba za Yehova kuti: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; Pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Njira yomwe Mulungu woona anakonza yothetsera vuto lomwe tchimo la Adamu linabweretsa simachotsa konse mwayi wathu wodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso.
Mulungu Anakonza Njira Yangwiro Yothetsera Vutolo
Talingalirani njira yothetsera vutolo yomwe Mulungu anakonza. Njirayo anaifotokoza limodzi ndi chiweruzo chomwe anapatsa Satana Mdyerekezi. Yehova anati kwa Satana: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, [gulu lakumwamba la Mulungu] ndi pakati pa mbewu yako [dziko lapansi lomwe Satana amalamulira] ndi mbewu yake; [Yesu Kristu] ndipo idzalalira mutu wako, [wa Satana] ndipo iwe udzalalira chitende chake [kupha Yesu].” (Genesis 3:15) Mu ulosi wa m’Baibulo woyambawu, Yehova anali kunena cholinga chake choti Mwana wake wauzimu wakumwamba Yesu adzabwera padziko lapansi, n’kudzakhala ndi moyo monga munthu wangwiro, kenako n’kufa, kapena kuti kuzuzundidwa chitende ali wosachimwa.
N’chifukwa chiyani Mulungu anafuna imfa ya munthu wangwiro? Eya, kodi chiweruzo cha Yehova Mulungu kwa Adamu ngati atachimwa chinali chotani? Kodi sichinali choti adzafa? (Genesis 2:16, 17) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Adamu analipira tchimo lake mwa kufa iye mwini. Anamupatsa moyo koma Adamu anasankha kuchimwa ndipo anafa chifukwa cha tchimo lakelo. (Genesis 3:19) Koma bwanji nanga za chilango chomwe anthu onse analandira chifukwa cha tchimolo? Imfa inali yofunika kuti ifafanize machimo awo. Koma kodi inali imfa ya ndani imene ikanafafaniza machimo a anthu onse?
Chilamulo cha Mulungu ku mtundu wakale wa Israyeli chinkafuna “moyo kulipa moyo.” (Eksodo 21:23) Malinga ndi lamulo limeneli, imfa yomwe ikanafafaniza machimo a anthu, inayenera kukhala ya moyo wofanana ndi womwe Adamu anataya. Imfa ya munthu wina wangwiro ndiyo ikanafafaniza mphoto ya uchimo. Yesu ndiye anali munthu woteroyo. Inde, Yesu anali “chiwombolo” chopulumutsa anthu onse ochokera mwa Adamu omwe atha kuwomboledwa.—1 Timoteo 2:6; Aroma 5:16, 17.
Imfa ya Yesu ndi ya Mtengo Wapatali
Imfa ya Adamu ilibe phindu. Iye analidi woyenera kufa chifukwa cha tchimo lake. Koma imfa ya Yesu inali ya mtengo wapatali chifukwa anafa wosachimwa. Yehova Mulungu anavomereza mtengo wa imfa ya munthu wangwiro Yesu monga dipo loombolera mbadwa zomvera za Adamu wochimwayo. Komanso mtengo wa nsembe ya Yesu sunathere pongotiwombola ku machimo athu akale ayi. Ukanatero ndiye kuti tikanakhala opanda tsogolo. Chifukwa anthufe tinabadwa ochimwa, timalakwalakwa. (Salmo 51:5) Timayamikiratu kwambiri kuti imfa ya Yesu imatipatsa mwayi wokapeza moyo wangwiro womwe Yehova poyamba anafuna kuti mbadwa za Adamu ndi Hava zikhale nawo!
Adamu tingamuyerekezere ndi tate yemwe wamwalira ndi kutisiya ife tili m’ngongole yaikulu (uchimo) moti palibe njira yoti tingathe kulipirira ngongoleyo. Mosiyana ndi Adamu, Yesu ali ngati tate wabwino yemwe wamwalira ndi kusiya chuma chambiri chamasiye osati chongolipirira ngongole yomwe Adamu anatisiyira komanso chotikwanira kuti tikhale ndi moyo kwamuyaya. Choncho, imfa ya Yesu imafafaniza machimo athu akale komanso ndiyo njira yopezera tsogolo labwino.
Inde, Yesu amapulumutsa chifukwa chakuti anatifera. Ndipotu imfa yake ndi njira ya mtengo wapatali kwambiri! Tikamaona imfa imeneyi monga njira yomwe Mulungu anakonza yothetsera vuto lalikulu la tchimo la Adamu, chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi mmene amachitira zinthu chimalimbikitsidwa. Inde, imfa ya Yesu ndiyo njira yopulumutsira “yense wakukhulupirira” iye ku uchimo, matenda, ukalamba, ndiponso imfa. (Yohane 3:16) Kodi mumayamikira Mulungu chifukwa chokonza mwachikondi njira ya chipulumutso chathu imeneyi?
[Chithunzi patsamba 5]
Adamu anabweretsa uchimo ndi imfa kwa anthu
[Chithunzi patsamba 6]
Yehova anakonza njira yangwiro yothetsera vutoli