Anatiyeretsa Kuti Tichite Ntchito Zokoma
“Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.”—2 AKORINTO 7:1.
1. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira akhale otani?
“ADZAKWERA ndani m’phiri la Yehova? Nadzaima m’malo ake oyera ndani?” Mfumu Davide ya Israyeli wakale inafunsa mafunso ochititsa chidwi amenewa pa nkhani ya kulambira kumene Yehova amavomereza. Ndiyeno inayankha kuti: “Woyera m’manja, ndi woona m’mtima, ndiye; iye amene sanakweza moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga.” (Salmo 24:3, 4) Munthu ayenera kukhala waukhondo ndiponso woyera kuti Yehova, yemwe ndi woyera, amuvomereze. M’mbuyomo, Yehova anakumbutsa mpingo wa Israyeli kuti: “Dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera.”—Levitiko 11:44, 45; 19:2.
2. Kodi Paulo ndi Yakobo anatsindika bwanji kufunika kwaukhondo pa kulambira koona?
2 Kenako patapita zaka zambiri, mtumwi Paulo analembera Akristu anzake a mumzinda wa Korinto mmene munali makhalidwe oipa, kuti: “Pokhala nawo tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Zimenezi zikutsindikanso mfundo yakuti munthu ayenera kukhala waukhondo ndiponso wopanda chodetsa chilichonse chakuthupi ndi chauzimu kuti akhale bwenzi la Mulungu ndi kulandira madalitso amene walonjeza. Mofananamo, wophunzira Yakobo analemba za kulambira kumene Mulungu amavomereza kuti: “Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.”—Yakobo 1:27.
3. Kodi tiyenera kuonetsetsa kuti tikuchita chiyani kuti Mulungu avomereze kulambira kwathu?
3 Popeza kuti kukhala waukhondo, woyera, ndiponso wosadetsedwa ndi zinthu zofunika kwambiri pa kulambira koona, aliyense amene akufuna kuti Mulungu amuyanje ayenera kuonetsetsa kuti akuchita zimenezo. Komabe, popeza anthu masiku ano ali ndi miyezo ndi maganizo osiyanasiyana pankhani ya ukhondo, tifunika kudziŵa ndi kutsatira zimene Yehova amaziona kuti n’zaukhondo ndi zovomerezeka. Tifunika kudziŵa zimene Mulungu amafuna kwa olambira ake pankhani imeneyi ndiponso zimene iye wachita powathandiza kuti akhale aukhondo ndiponso ovomerezeka kwa iye.—Salmo 119:9; Danieli 12:10.
Ukhondo pa Kulambira Koona
4. Fotokozani tanthauzo la ukhondo m’Baibulo.
4 Anthu ambiri akati ukhondo amangotanthauza kukhala opanda litsiro kapena zoipa basi. Komabe m’Baibulo, mawu angapo a Chihebri ndi Chigiriki amene amasonyeza mfundo ya kukhala waukhondo amafotokoza za ukhondo wa pathupi ndi panyumba pathu koma kaŵirikaŵiri amafotokoza za ukhondo wamakhalidwe ndi wauzimu. Motero, insaikulopediya ina yofotokoza za Baibulo inati: “Mawu akuti ‘Ukhondo’ ndi ‘uve’ kaŵirikaŵiri sanena za kudzisamalira chabe, koma nthaŵi zambiri amakhudza nkhani za kulambira. Motero, ‘ukhondo’ umakhudza mbali zonse za moyo.”
5. Kodi Chilamulo cha Mose chinakhudza mbali ziti za ukhondo wa Aisrayeli?
5 Chilamulo cha Mose chinali ndi malamulo okhudza mbali iliyonse ya moyo wa Mwisrayeli. Chinafotokoza zinthu zimene zinali zoyera ndi zovomerezeka ndiponso zimene zinali zodetsa. Mwachitsanzo, m’machaputala 11 mpaka 15 a Levitiko timapeza malangizo a tsatanetsatane okhudza zinthu zodetsedwa ndi zosadetsedwa. Nyama zina zinali zodetsedwa ndipo Aisrayeli sanayenera kuzidya. Mkazi amene anabereka kumene mwana ankakhala wodetsedwa kwa nthaŵi inayake. Munthu ankakhalanso wodetsedwa chifukwa cha matenda ena a pakhungu, makamaka khate, ndiponso kukha mwazi kwa mkazi ndiponso mwamuna. Chilamulo chinafotokozanso zimene anafunika kuchita munthu akakhala wodetsedwa. Mwachitsanzo, pa Numeri 5:2 timaŵerenga kuti: “Uza ana a Israyeli kuti azitulutsa m’chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa.”
6. Kodi Mulungu anapereka malamulo a zaukhondo n’cholinga chotani?
6 Mosakayika, malamulo a Yehova ameneŵa pamodzinso ndi ena anali ndi mfundo zokhudza mankhwala ndi zaumoyo zimene asayansi anadzazitulukira patapita zaka zambirimbiri pambuyo pake, ndipo anthu anali kupindula akatsatira malamulowo. Komabe, malamulo ameneŵa sanawapereke kuti angokhala malangizo a zaumoyo chabe kapena kuti angokhala malangizo a zamankhwala basi. Anali mbali ya kulambira koona. Malamuloŵa anakhudza moyo wa anthu wa tsiku ndi tsiku monga kudya, kubereka, nkhani za m’banja ndi zina zotero. Zimenezi zinasonyeza kuti Yehova, monga Mulungu wawo, anali ndi mphamvu kuwasankhira zimene zinali zoyenera ndi zosayenera m’mbali zonse za moyo wawo umene anaupatulira kotheratu kwa Yehova.—Deuteronomo 7:6; Salmo 135:4.
7. Kodi Aisrayeli akanalandira madalitso otani ngati akanamvera Chilamulo?
7 Chilamulo chinatetezanso Aisrayeli ku makhalidwe oipa a mitundu ya anthu imene anali nayo pafupi. Aisrayeli akanavomerezeka kutumikira Mulungu wawo ndi kulandira madalitso ake ngati akanamvera mokhulupirika Chilamulo kuphatikizapo malangizo onse oti akhale aukhondo pamaso pa Yehova. Pankhani imeneyi, Yehova anauza mtunduwo kuti: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.”—Eksodo 19:5, 6; Deuteronomo 26:19.
8. N’chifukwa chiyani Akristu lerolino afunika kumvera zimene Chilamulo chinkanena pa nkhani ya ukhondo?
8 Popeza Yehova anaphatikiza zimenezi m’Chilamulo n’cholinga choti alangize Aisrayeli mmene akanakhalira aukhondo, oyera ndiponso ovomerezeka kwa iye, kodi sikoyenera kuti lerolino Akristu aone mosamalitsa mmene akuchitira pankhani imeneyi? Ngakhale kuti Akristu sitikutsatira Chilamulo, tiyenera kukumbukira kuti zonse zimene zinali m’Chilamulo, monga mmene Paulo ananenera, “ndizo mthunzi wa zilinkudzazo; koma thupi ndi la Kristu.” (Akolose 2:17; Ahebri 10:1) Yehova Mulungu, amene anati “sindisinthika,” anaona kuti n’chinthu chofunika kwambiri kukhala woyera ndi wosadetsedwa pa kulambira koona kalelo. Ifenso lerolino tiyenera kuona ukhondo wa pathupi ndi panyumba, wamakhalidwe ndiponso wauzimu kukhala wofunika kwambiri ngati tikufuna kuti atiyanje ndi kutidalitsa.—Malaki 3:6; Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11, 31.
Timadziŵika ndi Ukhondo wa Pathupi ndi Panyumba
9, 10. (a) N’chifukwa chiyani ukhondo wa pathupi ndi panyumba ndi wofunika kwa Mkristu? (b) Kodi ndi mawu otani amene ena amanena okhudza misonkhano yaikulu ya Mboni za Yehova?
9 Kodi ukhondo wa pathupi ndi panyumba udakali wofunikabe pa kulambira koona? Ngakhale kuti ukhondo umenewu paokha suchititsa munthu kukhala wolambira woona wa Mulungu, n’koyenera kuti olambira oona akhale aukhondo malinga ndi mmene angathere. Nthaŵi zambiri anthu amene amadzisamalira komanso kusamala panyumba pawo, makamaka masiku ano pamene anthu ambiri alibe nazo ntchito kwenikweni za ukhondo, anthu ena amene ali nawo pafupi amawaona. Zimenezi zingabweretse zotsatira zabwino, monga mmene Paulo anauzira Akristu a ku Korinto kuti: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu.”—2 Akorinto 6:3, 4.
10 Akuluakulu ena ayamikira Mboni za Yehova mobwerezabwereza chifukwa cha ukhondo wawo, kuchita zinthu mwadongosolo ndiponso makhalidwe awo abwino, zimene zimaoneka makamaka pamisonkhano yawo yaikulu. Mwachitsanzo, nyuzipepala ya La Stampa inafotokoza za msonkhano umene unachitikira m’chigawo cha Savona ku Italy, kuti: “Chochititsa chidwi kwambiri chimene munthu umaona ukamayenda pamalowo ndicho ukhondo ndi dongosolo la anthu amene akugwiritsa ntchito malowo.” Utatha msonkhano wa Mboni pa sitediyamu ya mu mzinda wa São Paulo ku Brazil, mkulu wina wa sitediyamuyo anauza woyang’anira oyeretsa pamalopo kuti: “Kuyambira lero tikufuna kuti sitediyamuyi tiziikonza monga mmene zimakonzera Mboni za Yehova.” Mkulu winanso pa sitediyamu yomweyo anati: “Mboni za Yehova zikafuna kuchita lendi sitediyamuyi, timangodera nkhaŵa za masiku amene zidzagwiritsa ntchito. Palibenso china chimene chimatidetsa nkhaŵa.”
11, 12. (a) Kodi ndi mfundo iti ya m’Baibulo imene tifunika kukumbukira pankhani ya ukhondo wa munthu payekha? (b) Kodi tingafunse mafunso ati okhudza khalidwe lathu ndi mmene timakhalira pa moyo wathu?
11 Popeza kukhala aukhondo ndi a dongosolo pa malo amene tikulambirira kumalemekeza Mulungu amene timalambira, n’zosakayikitsa kuti kusonyeza makhalidwe ameneŵa patokha n’kofunikanso kwambiri. Komabe, panyumba pathu tingaone kuti tili ndi ufulu kutayirira ndi kuchita zimene tikufuna. Ndipotu tili ndi ufulu wovala ndi kudzikongoletsa mmene tingafunire. Komabe, kwakukulukulu, ufulu wonsewu uli ndi malire. Kumbukirani kuti Paulo pokambirana ndi Akristu anzake za chakudya chimene munthu angasankhe, anawachenjeza kuti: “Yang’anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale chokhumudwitsa ofokawo.” Ndiyeno anafotokoza mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.” (1 Akorinto 8:9; 10:23) Kodi malangizo a Paulo ameneŵa akugwira ntchito bwanji kwa ife pankhani ya ukhondo?
12 Mpake kuti anthu ayembekezere mtumiki wa Mulungu kukhala waukhondo ndi wadongosolo m’moyo wake. Motero, tiyenera kuonetsetsa kuti mmene nyumba yathu ndi pakhomo pathu zikuonekera sizikuipitsa mbiri yathu monga atumiki a Mawu a Mulungu. Kodi nyumba yathu ikupereka umboni wotani ponena za ife ndi zikhulupiriro zathu? Kodi ikusonyeza kuti tikufunitsitsadi kudzakhala m’dziko latsopano lachilungamo, laukhondo ndiponso ladongosolo limene timalilengeza kwa anthu ena? (2 Petro 3:13) Mofananamo, mmene ifeyo timaonekera, kaya pocheza kapena muutumiki, zingachititse uthenga umene timalalikira kukhala wogwira mtima kapena ayi. Mwachitsanzo, taonani ndemanga yotsatirayi ya mtolankhani wa nyuzipepala ina ku Mexico: “M’gulu la Mboni za Yehova muli achinyamata ambiri, ndipo chochititsa chidwi ndicho kametedwe kawo, ukhondo wawo, ndiponso kavalidwe kawo kabwino.” N’zosangalatsa kukhala ndi achinyamata oterowo m’gulu lathu.
13. Kodi tingatani kuti tionetsetse kuti mbali zonse za moyo wathu wa tsiku ndi tsiku n’zaukhondo ndiponso zadongosolo?
13 N’zoona kuti n’zovuta kuonetsetsa kuti thupi lathu, zinthu zathu ndiponso nyumba yathu n’zaukhondo ndi zolongosoka nthaŵi zonse. Zimene zikufunika ndizo kulinganiza bwino zinthu ndi kuchita khama nthaŵi zonse osati kukhala ndi zinthu zapamwamba ndiponso zipangizo zodula ayi. Tifunika kupatula nthaŵi yosamba, kuchapa zovala, kuyeretsa panyumba, kutsuka galimoto, ndi zina zotero. Kutanganidwa ndi utumiki, kupita kumisonkhano, ndiponso phunziro laumwini—kuphatikiza pa kuchita zinthu zina m’moyo wa tsiku ndi tsiku—sizichititsa kuti tisakhale aukhondo ndi kuvomerezeka pamaso pa Mulungu ndi anthu. Mfundo yozoloŵereka kwambiri yakuti “kalikonse kali ndi nthaŵi yake” imagwiranso ntchito pa mbali imeneyi.—Mlaliki 3:1.
Mtima Wosadetsedwa
14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ukhondo wamakhalidwe ndi wauzimu ndi wofunika kwambiri kuposa ukhondo wa pathupi ndi panyumba?
14 N’kofunika kwambiri kuonetsetsa kuti thupi lathu pamodzi ndi nyumba yathu n’zaukhondo, komatu, kuonetsetsa kuti ndife aukhondo m’makhalidwe ndiponso mwauzimu n’kofunika kwambiri kuposa pamenepo. Tikutero pokumbukira kuti Yehova anakana mtundu wa Aisrayeli chifukwa chakuti unali wauve mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu osati chifukwa cha uve wa pathupi ndi panyumba. Yehova anawauza kudzera mwa mneneri Yesaya kuti chifukwa choti anali “mtundu wochimwa . . . anthu olemedwa ndi mphulupulu,” nsembe zawo, kusunga kwawo tsiku lokhala mwezi ndi la sabata, ngakhale mapemphero awo omwe, Yehova analema nazo. Kodi akanatani kuti Mulungu awayanjenso? Yehova anati: “Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa.”—Yesaya 1:4, 11-16.
15, 16. Kodi Yesu anati n’chiyani chimadetsa munthu, ndipo tingapindule bwanji ndi zimene Yesu ananena?
15 Kuti timvetse bwino kufunika kwa ukhondo wamakhalidwe ndi wauzimu, tiyeni tione zimene Yesu ananena pamene Afarisi ndi alembi ananena kuti ophunzira ake anali odetsedwa chifukwa chakuti sanasambe m’manja asanadye chakudya. Yesu anawawongolera mwa kuwauza kuti: “Si chimene chiloŵa mkamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka mkamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.” Ndiyeno anafotokoza kuti: “Zakutuluka mkamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu. Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano; izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ayi.”—Mateyu 15:11, 18-20.
16 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yesu ananenazi? Iye anali kusonyeza kuti ntchito zoipa ndi zodetsa zimayamba chifukwa cha mtima woipa ndi wodetsedwa. Monga mmene wophunzira Yakobo ananenera, “munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga.” (Yakobo 1:14, 15) Motero, ngati sitikufuna kuchita machimo aakulu amene Yesu anawatchula, tiyenera kuchotseratu mumtima mwathu chilakolako cha zinthu zimenezi ndiponso osalola kuti tiziziganizira n’komwe. Kuti tichite zimenezo tiyenera kusamala ndi zimene timaŵerenga, kuonerera ndi kumvetsera. Masiku ano, malinga ndi ufulu wa kulankhula ndi ufulu wa akatswiri amaluso osiyanasiyana, makampani okonza zosangulutsa ndi otsatsa malonda akupanga nyimbo ndi zithunzi zankhaninkhani zimene zikukwaniritsa zofuna za thupi lochimwali. Tiyenera kutsimikiza mtima kusalola maganizo oterowo kuzika mizu mumtima mwathu. Mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti tifunika kukhalabe tcheru kuti tikhale aukhondo ndiponso osadetsedwa mumtima mwathu kuti tisangalatse Mulungu ndi kuti ativomereze.—Miyambo 4:23.
Anatiyeretsa Kuti Tichite Ntchito Zokoma
17. N’chifukwa chiyani Yehova anayeretsa anthu ake?
17 Ndi mwayi wamtengo wapatali ndiponso chitetezo chathu kuti tikhale aukhondo pamaso pa Yehova mothandizidwa ndi iye. (2 Akorinto 6:14-18) Komabe, tikudziŵanso kuti Yehova wayeretsa anthu ake n’cholinga chinachake. Paulo anauza Tito kuti Kristu Yesu “anadzipereka yekha m’malo mwa ife, kuti akatiwombole ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.” (Tito 2:14) Monga anthu oyeretsedwa, kodi tiyenera kukhala achangu pantchito ziti?
18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife achangu pantchito zokoma?
18 Choyamba, tiyenera kudzipereka kulengeza kwa anthu onse uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Mwakuchita zimenezo, timapatsa anthu kulikonse chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi limene silidzaipitsidwa m’pang’ono pomwe. (2 Petro 3:13) Inanso mwa ntchito zathu zokoma zimene tingachite ndiyo kuonetsa chipatso cha mzimu wa Mulungu pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, ndipo kutero kumalemekeza Atate wathu wakumwamba. (Agalatiya 5:22, 23; 1 Petro 2:12) Ndiponso sitiiŵala anthu amene sali m’choonadi omwe ali m’mavuto aakulu chifukwa cha masoka a chilengedwe kapena mavuto oyambitsa anthu. Timakumbukira langizo la Paulo lakuti: “Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Ntchito zonsezi, zimene timachita kuchokera mumtima wosadetsedwa ndiponso tili ndi zolinga zabwino, zimasangalatsa Mulungu.—1 Timoteo 1:5.
19. Kodi tidzapeza madalitso otani ngati tikhalabe ndi muyezo wapamwamba wa ukhondo wa pathupi ndi panyumba, wamakhalidwe ndi wauzimu?
19 Ife monga atumiki a Wam’mwambamwamba, timamvera mawu a Paulo akuti: “Ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.” (Aroma 12:1) Tiyenitu tipitirize kuyamikira mwayi woyeretsedwa ndi Yehova ndi kuchita zonse zimene tingathe kuti tikhalebe ndi muyezo wapamwamba wa ukhondo wa pathupi ndi panyumba, wamakhalidwe ndiponso wauzimu. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kukhala odzilemekeza ndiponso kukhala ndi moyo wosangalatsa pakalipano. Ndiponso, tidzakhala ndi chiyembekezo chodzaona “zoyambazo,” zimene zili dziko loipa ndiponso lodetsedwa lino, zikupita pamene Mulungu ‘adzachita zonse zikhale zatsopano.’—Chivumbulutso 21:4, 5.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani Aisrayeli anawapatsa malamulo ambiri okhudza ukhondo?
• Kodi ukhondo wa pathupi ndi panyumba umathandiza bwanji kuti uthenga umene timalalikira ukhale wogwira mtima kwambiri?
• N’chifukwa chiyani ukhondo wamakhalidwe ndi wauzimu ndi wofunika kwambiri kuposa ukhondo wa pathupi ndi panyumba?
• Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife anthu “achangu pa ntchito zokoma”?
[Zithunzi patsamba 21]
Ukhondo wa pathupi ndi panyumba umachititsa uthenga umene timalalikira kukhala wogwira mtima kwambiri
[Chithunzi patsamba 22]
Yesu anachenjeza kuti maganizo oipa amayambitsa ntchito zoipa
[Zithunzi patsamba 23]
Monga anthu oyeretsedwa, Mboni za Yehova n’zachangu kuchita ntchito zokoma