Mbiri ya Moyo Wanga
“Sindingasinthe Kanthu!”
YOSIMBIDWA NDI GLADYS ALLEN
Nthaŵi zina ena amandifunsa kuti, “Kodi mutati muyambirenso moyo wanu, kodi mungasinthe chiyani pa zimene munachita?” Ndimayankha moona mtima kuti, “Sindingasinthe kanthu!” Taimani ndifotokoze chifukwa chake ndimatero.
M’CHILIMWE cha 1929, ndili ndi zaka ziŵiri, abambo anga a Matthew Allen anapeza chinthu chabwino kwambiri. Anapeza kabuku kakuti Millions Now Living Will Never Die! (Mamiliyoni Okhala Ndi Moyo Tsopano Sadzafa Konse!), kofalitsidwa ndi Ophunzira Baibulo a Padziko Lonse, dzina la Mboni za Yehova nthaŵi imeneyo. Abambo ataŵerenga mwachidwi masamba angapo, anati, “Izi n’zofunika zedi kuposa zina zonse zimene ndinaŵerengapo!”
Patapita nthaŵi pang’ono, Abambo anapeza mabuku ena a Ophunzira Baibulo. Nthaŵi yomweyo anayamba kuuza anansi awo onse zimene anali kuphunzira. Koma, m’dera lathu lakumidzi limene tinkakhala munalibe mpingo uliwonse wa Mboni za Yehova. Abambo pozindikira kufunika kosonkhana ndi Akristu nthaŵi zonse, anasamukira ndi banja lawo lonse ku tauni ya Orangeville, ku Ontario, ku Canada, mu 1935 chifukwa kumeneko mpingo unaliko.
Masiku amenewo, ana sanali kuwalimbikitsa kuchita nawo misonkhano yampingo, kaŵirikaŵiri ankakhala panja kumaseŵera mpaka anthu akuluakulu amalize misonkhano. Abambo sankasangalala nazo zimenezi. Ankaganiza kuti, “Ngati misonkhano ndi yofunika kwa ine, ndiye kuti ndi yofunikanso kwa ana anga.” Choncho ngakhale kuti Abambo anangoyamba kumene kusonkhana, anauza ine, mchimwene wanga Bob, ndi akulu anga Ella ndi Ruby, kuti tizikhala nawo pamisonkhanoyo. Ndipo tinachitadi zimenezo. Posakhalitsa ana a Mboni zina anayambanso kupezeka pamisonkhano. Kupezeka ndiponso kuyankha pa misonkhano kunakhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu.
Abambo ankakonda Baibulo, ndipo anali ndi njira yosangalatsa yochitira maseŵero nkhani za m’Baibulo. Mwa kuchita zimenezi, anakhomereza m’mitima yathu yantheteyo maphunziro ofunika amene ndimawakumbukirabe ndi kuwakonda kwambiri. Limodzi mwa maphunziro amene ndimakumbukira n’loti Yehova amadalitsa anthu amene amamumvera.
Abambo anatiphunzitsanso kugwiritsa ntchito Baibulo potsimikizira chikhulupiriro chathu. Tinkakonda kuchita maseŵero a zimenezi. Abambo ankanena monga izi, “Ndimakhulupirira kuti ndikadzafa n’dzapita kumwamba. Choncho ndipatseni umboni wakuti sindidzapita.” Ine ndi Ruby kuti tipeze malemba otsutsa mfundo imeneyo, tinkafufuza m’buku limene limandandalika mawu a m’Baibulo ndi pamene amapezeka. Tikawaŵerengera malemba amene tapeza, Abambo ankati, “Zikumveka, kungoti sindinakhutire.” Choncho tinkafufuzanso malemba ena m’buku lomwe lija. Izi zinkatenga maola angapo mpaka Abambo atakhutira ndi mayankho athu. Chifukwa cha zimenezi, ine ndi Ruby tinali okonzeka kufotokoza ndi kutsimikizira chikhulupiriro chathu.
Kuthetsa Kuopa Anthu
Ngakhale kuti ndinali kuphunzira maphunziro abwino kunyumba ndi kumisonkhano yampingo, kunena zoona panali mbali zina zachikristu zimene zinali zondivuta. Monga achinyamata ambiri, sindinkasangalala kukhala wosiyana ndi ena, makamaka ndi anzanga am’kalasi. Chikhulupiriro changa chinayesedwa koyamba ndi zimene tinkati ndawala yofalitsa uthenga.
Zomwe zinkachitika n’zakuti gulu la abale ndi alongo linali kunyamula zikwangwani zolembedwa mawu n’kumayenda pang’onopang’ono m’misewu ikuluikulu. Anthu a m’tauni yathu ya anthu pafupifupi 3,000 tinkadziŵana. Panthaŵi ina ya ndawala yofalitsa uthengayi, ndinali kumapeto kwa gulu limene linanyamula zikwangwani za mawu akuti “Chipembedzo ndi Msampha komanso Malonda.” Anzanga ena akusukulu anandiona, ndipo nthaŵi yomweyo anafika kumbuyo kwanga n’kumayenda nafe limodzi akuimba kuti “Mulungu Pulumutsani Mfumu.” Kodi ndinachitanji? Ndinapemphera mochokera pansi pamtima kuti andipatse mphamvu kuti ndipitirize. Ndawalayo itatha, ndinathamangira ku Nyumba ya Ufumu kukasiya chikwangwanicho kuti ndizipita kunyumba. Koma, amene ankatsogolera ndawalayi anandiuza kuti ndawala ina iyamba posachedwa koma pakusoŵeka munthu m’modzi woti atenge chikwangwani china. Choncho ndinapitanso, ndipo ndinapemphera kwambiri kuposa poyamba paja. Komabe, apa n’kuti anzanga am’kalasi aja atatopa ndipo anapita kwawo. Mapemphero anga opempha mphamvu anasanduka mapemphero oyamika!—Miyambo 3:5.
Nthaŵi zonse kunyumba kwathu tinali kulandira mosangalala atumiki anthaŵi zonse. Anali anthu achimwemwe ndiponso abwino kucheza nawo. Zinthu zakale zimene ndikukumbukira n’zakuti makolo athu nthaŵi zonse ankatiuza anafe kuti utumiki wanthaŵi zonse ndi ntchito yabwino kwambiri.
Mu 1945, ndinayamba utumiki wanthaŵi zonse potsatira zimene anali kundilimbikitsa. Patapita nthaŵi ndinakakhala ndi mkulu wanga Ella, amene anali kuchita upainiya ku London, ku Ontario. Kumeneko, ndinaphunzira mtundu wina wa utumiki umene ndinkaona kuti sindingauthe n’komwe. Abale ankapita ku bala, n’kumagaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Consolation (imene tsopano ndi Galamukani!) kwa makasitomala pa tebulo lililonse m’balamo. Mwayi wake, zimenezi zinali kuchitika Loŵeruka madzulo, choncho mlungu wonse ndinali ndi nthaŵi yopemphera kuti andilimbitse mtima kuti ndithe kupita ku utumiki umenewu. Ayi ndithu, ntchitoyi inkandivuta koma inali yopindulitsa.
Komanso ndinaphunzira zimene ndingachite pogaŵira magazini apadera a Consolation okamba za momwe abale athu kumisasa ya ukaidi ya Nazi anali kuzunzikira, makamaka kugaŵira kwa amalonda otchuka a ku Canada, komanso atsogoleri a mabungwe akuluakulu. Kwa zaka zambiri, ndaona kuti Yehova nthaŵi zonse amatithandiza kokha ngati tim’dalira kuti atipatse mphamvu. Zili monga momwe Abambo ankanenera kuti, Yehova amadalitsa anthu amene amamumvera.
Ndinalola Kukatumikira ku Quebec
Pa July 4, 1940, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa ku Canada. M’kupita kwanthaŵi, anachotsa chiletsocho, komabe ku chigawo cha Roma Katolika ku Quebec anali kutizunzabe. Tinachita ndawala yapadera kuulula nkhanza zimene zinali kuchitikira abale athu kumeneko pogwiritsa ntchito thirakiti la mawu amphamvu lakuti Quebec’s Burning Hate for God and Christ and Freedom Is the Shame of All Canada (Chidani Chachikulu Chimene Anthu a ku Quebec Anali Nacho pa Mulungu ndi Kristu Komanso Ufulu wa Anthu Onse ku Canada Ndi Womvetsa Chisoni). Nathan H. Knorr, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anakumana ndi apainiya ambiri zedi mu mzinda wa Montreal kutifotokozera zimene zingakhale zotsatira za zimene tinali pafupi kuchitazo. Mbale Knorr, anatiuza kuti tikalola kuchita ndawalayo, tikhoza kugwidwa ndi kumangidwa. Zinalitu zoona zimenezi. M’kupita kwanthaŵi, ndinali n’tamangidwa ka 15. Popita mu utumiki wakumunda, tinkaonetsetsa kuti tatenga mswachi ndi chipeso kuchitira kuti mwina tikagona ku ndende.
Poyamba tinkagwira kwambiri ntchito imeneyi usiku, kuti anthu ambiri asatidziŵe. Ndinkakonda kunyamula mathirakiti ena m’chikwana chimene ndinkakoloweka m’khosi, pamwamba pake m’kuvala jasi. Chikwama chodzaza ndi mathirakiti chimenechi chinali chachikulu zedi, moti ndinkaoneka ngati kuti ndine woyembekezera. Zimenezi zinandithandiza kwambiri popita m’gawo ngati ndakwera galimoto yodzaza. Maulendo angapo amuna ena amachoka pampando wawo n’kundiuza ine mayi “woyembekezera” kuti ndikhalepo.
M’kupita kwanthaŵi, tinayamba kugaŵira mathirakiti masana. Tinkasiya mathirakiti panyumba zitatu kapena zinayi, ndiyeno n’kukapitiriza m’gawo lina. Nthaŵi zambiri, zimenezi zinkatiyendera bwino. Komabe, wansembe wa Katolika akadziŵa kuti tinali m’dera lawo, tinkadziŵa kuti zitivuta. Nthaŵi ina, wansembe wina anasonkhanitsa anthu okwana 50 kapena 60, akulu ndi ana omwe kuti atigende ndi tomato komanso mazira. Tinabisala m’nyumba ya mlongo wina, komwe usiku wake tinagona pansi penipeni.
Ku Quebec kunalibe apainiya amene akanalalikira anthu olankhula Chifalansa, choncho mu December 1958, ine ndi mkulu wanga Ruby tinayamba kuphunzira Chifalansa. Ndiyeno anatipatsa madera angapo m’chigawocho kumene anali kulankhulako Chifalansa. Ntchito iliyonse inali ndi pokomera pake. M’dera lina, tinayenda kunyumba ndi nyumba kwa maola asanu ndi atatu patsiku kwa zaka ziŵiri popanda wotuluka kudzatilankhula. Anthu ankagobwera pakhomo n’kusuzumira pa makatani. Komabe sitinaleke. Lerolino, m’tauni imeneyi muli mipingo iŵiri yomwe ikuchitabe bwino.
Yehova Anandithandiza M’zonse
Mu 1965 tinayamba upainiya wapadera. M’gawo lina limene tinali kuchita upainiya wapadera, tinazindikira tanthauzo lenileni la mawu a Paulo a pa 1 Timoteo 6:8 akuti: “Pokhala nazo zakudya ndi zopfunda, zimenezi zitikwanire.” Tinkatsatira kwambiri bajeti pogula zofunika pa moyo wathu. Chotero tinkapatula ndalama za mafuta a chitofu chotenthetsa m’nyumba, za lendi, za magetsi ndi za chakudya. Tikathana ndi zimenezi, tinkatsala ndi masenti 25 oti tigwiritse ntchito momwe tikufunira mwezi umenewo.
Kusoŵa kwathu ndalama kunatipangitsa kuti tiziyatsa chitofucho m’nyumbamo usiku wokha kwa maola ochepa. Choncho m’chipinda chathu simunkatentha kuposa madigiri seshasi 15, chotero nthaŵi zambiri munkazizira. Ndiyeno tsiku lina mwana wa amene Ruby anali kuphunzira naye Baibulo anabwera kudzacheza. Ayenera kuti anakauza amayi ake kuti tinali kufa ndi kuzizira, chifukwa kuyambira pamenepo ankatitumizira mwezi uliwonse madola khumi kuti tizigulira mafuta achitofucho kuti nthaŵi zonse chizikhala choyatsa. Sitinkasoŵa kanthu kena kalikonse. Sitinali olemera, koma kuti nthaŵi zonse tinali ndi zinthu zofunika pamoyo. Tinkaona kuti chilichonse chowonjezera pamenepa chinali dalitso chabe. Mawu a pa Salmo 37:25 ndi oona zedi. Amati: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.”
Ngakhale tinali kukumana ndi chitsutso, ndinasangalala kuona anthu ambiri amene ndinaphunzira nawo Baibulo ataphunzira choonadi. Ena anayamba ntchito ya utumiki wanthaŵi zonse, zimene zimandisangalatsa kwambiri.
Ndathana ndi Mavuto
Mu 1970, anatitumiza kukatumikira ku dera latsopano la ku Cornwall, ku Ontario. Patatha pafupifupi chaka tili ku Cornwall, Amayi anayamba kudwala. Abambo anali atamwalira mu 1957, ndipo ine ndi akulu anga aŵiri tinkasinthana kusamalira amayi mpaka pamene anamwalira mu 1972. Anzathu amene tinali kuchita nawo upainiya wapadera Ella Lisitza ndi Ann Kowalenko anatilimbikitsa kwambiri ndi kutithandiza mwachikondi panthaŵi imeneyi. Anasamalira maphunziro athu a Baibulo ndiponso ntchito zina ife kulibe. Mawu a pa Miyambo 18:24 ndi oona kwambiri. Amati: “Lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.”
Moyo ndi wodzaza ndi mavuto. Koma ndi thandizo lachikondi la Yehova, ndalimbana nawo onse. Pano ndikuchitabe utumiki wanthaŵi zonse mosangalala. Bob yemwe anamwalira mu 1993, anatha zaka zoposa 20 akuchita upainiya, zaka 10 pa zaka zimenezi zinali zapadera kwambiri popeza anachita upainiya ndi mkazi wake Doll. Mkulu wanga Ella, yemwe anamwalira mu October 1998, anachita upainiya kwa zaka zoposa 30 ndipo nthaŵi zonse anali ndi mzimu wa upainiya. Mu 1991, mkulu wanga wina, Ruby, anam’peza ndi kansa. Komabe, anagwiritsa ntchito mphamvu zake zopereŵerazo kulalikira uthenga wabwino. Analinso wansangala mpaka m’mawa wa pa September 26, 1999 pamene anamwalira. Ngakhale kuti pano ndilibe akulu anga ndili ndi banja lauzimu la abale ndi alongo amene amandithandiza kukhalabe wosangalala.
Ndikayang’ana zimene ndachita pamoyo wanga, kodi ndingasinthe chiyani? Sindinakwatiwepo, koma ndinali ndi makolo achikondi, mchimwene ndi akulu anga amene anaika choonadi patsogolo m’moyo wawo. Ndikuyembekezera kuonana nawo onse posachedwapa akadzauka. Panopa ndikutha kuona abambo anga akundikupatira, amayi anga akulira titakupatirana kwambiri. Ella, Ruby, ndi Bob adzasangalala zedi.
Pakalipano, ndikufuna kupitirizabe kugwiritsa ntchito mphamvu zimene ndatsala nazo kutamanda ndi kulemekeza Yehova. Utumiki wa upainiya wanthaŵi zonse ndi wosangalatsa ndiponso wopindulitsa. Zili monga momwe wamasalmo ananenera zokhudza anthu amene amayenda m’njira ya Yehova, kuti: “Wodala iwe, ndipo kudzakukomera.”—Salmo 128:1, 2.
[Zithunzi patsamba 26]
Abambo ankakonda Baibulo. Anatiphunzitsa kuligwiritsa ntchito potsimikizira chikhulupiriro chathu
[Chithunzi patsamba 28]
Kuyambira kumanzere kupita kumanja: Ruby, ine, Bob, Ella, Amayi ndi Abambo mu 1947
[Chithunzi patsamba 28]
Mzere wa kutsogolo, kuyambira kumanzere kupita kumanja: Ine, Ruby, ndi Ella pa Msonkhano Wachigawo mu 1998