Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi kubatizidwa chifukwa cha akufa n’kutani?
Polemba za kuukitsidwira kumwamba, mtumwi Paulo analemba ndime ina yochititsa chidwi kwambiri. M’Baibulo la Chichewa la Revised Nyanja (Union) Version timaŵerenga kuti: “Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?” Ndipo Baibulo la Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono linamasulira ndime imeneyi kuti: “Ngati Yesu sanauke kwa akufa, nanga adzatani iwo amene amabatizidwa m’malo mwa anthu amene anafa? Ngati akufa sauka konse, nanga bwanji amabatizidwa m’malo mwawo?”—1 Akorinto 15:29.
Kodi Paulo pa ndime imeneyi anali kutanthauza kuti anthu amoyo ayenera kubatizidwa m’malo mwa anthu amene anamwalira asanabatizidwe? Zingaoneke choncho malinga ndi mmene anamasulira m’mabaibulo ameneŵa pamodzinso ndi mabaibulo ena. Komabe, kupenda mosamala Malemba ndi mawu oyambirira Achigiriki amene Paulo anagwiritsa ntchito kukusonyeza kuti tanthauzo lake si limenelo. Paulo anali kutanthauza kuti Akristu odzozedwa amabatizidwa, kapena kuti kumizidwa, n’kuyamba moyo woti adzafikira kumwalira akadali okhulupirika monga mmene anachitira Kristu. Kenako, adzaukitsidwa n’kudzakhala ndi moyo wauzimu monga mmene Kristuyo anachitira.
Malemba amatsimikizira mfundo imeneyi. Paulo powalembera Aroma anati: “Kodi simudziŵa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake?” (Aroma 6:3) M’kalata imene analembera Afilipi, Paulo ananena za iye mwini kuti: ‘Ndinayanjana ndi zoŵaŵa [za Kristu], pofanizidwa ndi imfa yake; ngati n’kotheka ndikafikire kuuka kwa akufa.’ (Afilipi 3:10, 11) Paulo anali kufotokoza kuti moyo wa wotsatira wodzozedwa wa Kristu umafuna kukhulupirikabe poyesedwa, kuyembekezera imfa tsiku lililonse, ndipo kenako kumwalira ali wokhulupirika, n’kudzaukitsidwira kumwamba.
N’zochititsa chidwi kuti malemba ameneŵa ndiponso malemba ena amene amatchula mwachindunji imfa moigwirizanitsa ndi anthu obatizidwa, amanena za anthu amoyo amene anabatizidwa kale osati anthu amene anamwalira. Paulo anauzanso Akristu anzake odzozedwa kuti: “Munaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m’chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.”—Akolose 2:12.
Liwu la Chigiriki lakuti hy·perʹ, limene analimasulira kuti “chifukwa cha” kapena “m’malo mwa,” m’mabaibulo osiyanasiyana pa 1 Akorinto 15:29, lingatanthauzenso kuti “n’cholinga choti.” Choncho, mogwirizana ndi malemba ena a m’Baibulo, Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures molondola linamasulira vesi limeneli kuti: “Kodi adzachita chiyani amene akubatizidwa n’cholinga choti adzakhale akufa? Ngati akufa sadzaukitsidwa, n’chifukwa chiyani akubatizidwanso n’cholinga choti akhale otero?”