Kukhala Okoma Mtima M’dziko Losaganiziranali
“Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake.”—MIYAMBO 19:22.
1. N’chifukwa chiyani kungakhale kovuta kusonyeza kukoma mtima?
KODI mumaona kuti ndinu munthu wokoma mtima? Ngati ndi choncho, kukhala m’dziko la masiku anoli kungakhale kovuta kwambiri. Inde, Baibulo limafotokoza kuti kukoma mtima ndi mbali ya “chipatso cha mzimu,” komano n’chifukwa chiyani n’kovuta kwambiri kusonyeza kukoma mtima ngakhale m’mayiko amene amatchedwa kuti ndi achikristu? (Agalatiya 5:22) Monga mmene taonera m’nkhani yapitayo, mbali ina ya yankho la funso limeneli ndi zimene mtumwi Yohane analemba, kuti dziko lonse lapansi lili m’manja mwa munthu wauzimu wosakoma mtima, Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Yesu Kristu ananena kuti Satana ndi “mkulu wa dziko lapansi.” (Yohane 14:30) Motero, dzikoli limatsanzira wolamulira wake wopanduka, amene maganizo ake ndi odzala ndi makhalidwe oipa.—Aefeso 2:2.
2. Kodi ndi mavuto otani amene angakhudze kusonyeza kwathu kukoma mtima?
2 Zimatipweteka kwambiri ngati anthu ena atichitira zinthu mosakoma mtima. Kusakoma mtima kungasonyezedwe ndi anthu okhala nawo pafupi osafunira anzawo zabwino, alendo osachezeka, ngakhale anzathu ndi anthu a m’banja lathu amene nthaŵi zina angachite zinthu mosaganizira. Nthaŵi zambiri kuchita zinthu ndi anthu amwano amene amakalipirana kapena kutukwanana kumatichititsa kuvutika mumtima. Kusakoma mtima kwa anthu enawo kungatichititsenso ife kusaganizira ena, ndipo tingaganize zobwezera kusakoma mtimako. Zimenezo zikhoza kuyambitsa mavuto auzimu pamoyo wa munthu kapena kumuwonongera thanzi lake.—Aroma 12:17.
3. Kodi ndi mavuto aakulu ati amene anthu amakumana nawo amene amachititsa kuti avutike kusonyeza kukoma mtima?
3 Mavuto amene tikukumana nawo m’dzikoli angatichititsenso kuvutika kuti tisonyeza kukoma mtima. Mwachitsanzo, anthu ambiri amavutika maganizo chifukwa chodera nkhaŵa za uchigaŵenga ndiponso kuti mayiko akhoza kugwiritsa ntchito zida zofalitsa tizilombo toyambitsa matenda kapena zida za nyukiliya. Kuwonjezera pamenepo, anthu ambirimbiri ali paumphaŵi wadzaoneni, alibe chakudya chokwanira, malo ogona abwino, zovala zokwanira, ndi chithandizo chokwanira chamankhwala. Kusonyeza kukoma mtima kumakhala kovuta ngati zinthu zikuoneka kuti sizikupereka chiyembekezo chilichonse.—Mlaliki 7:7.
4. Kodi anthu ena angaganize zinthu zolakwika ziti akamalingalira zosonyeza kukoma mtima kwa ena?
4 M’posavuta kuti munthu aganize kuti kusonyeza kukoma mtima si kofunika kwambiri ndipo mwina kungakhale chizindikiro cha kufooka. Angaone ngati akudyeredwa masuku pamutu, makamaka ngati anthu ena samuchitira zinthu momuganizira. (Salmo 73:2-9) Komabe, Baibulo limatipatsa malangizo abwino pamene limanena kuti: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu oŵaŵitsa aputa msunamo.” (Miyambo 15:1) Kufatsa ndi kukoma mtima ndi mbali ziŵiri za chipatso cha mzimu zomwe ndi zogwirizana kwambiri ndipo zimathandiza kwambiri zinthu zikavuta.
5. Kodi ndi mbali zina ziti za moyo zimene timafunika kusonyeza kukoma mtima?
5 Popeza kusonyeza chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu n’kofunika kwambiri kwa ife Akristu, tiyenera kuona mmene tingasonyezere khalidwe la kukoma mtima lomwe ndi limodzi mwa makhalidwe amenewo. Kodi n’zotheka kukhala wokoma mtima m’dziko losaganiziranali? Ngati ndi choncho, ndi mbali zina ziti zimene tingapereke umboni wakuti sitikulola kuti Satana agonjetse kukoma mtima kwathu, makamaka tikakumana ndi mavuto? Tiyeni tikambirane mmene tingasonyezere kukoma mtima m’banja, kuntchito, kusukulu, kwa anthu amene timakhala nawo pafupi, muutumiki, ndiponso kwa okhulupirira anzathu.
Kukoma Mtima M’banja
6. N’chifukwa chiyani kukoma mtima n’kofunika kwambiri m’banja, ndipo kungasonyezedwe bwanji?
6 Kuti Yehova atidalitse ndi kutitsogolera, chipatso cha mzimu n’chofunika kwambiri ndipo tifunika kuchikulitsa kwambiri. (Aefeso 4:32) Tiyeni tikambirane kufunika koti anthu a m’banja azikomerana mtima. Pochitirana zinthu tsiku ndi tsiku, mwamuna ndi mkazi wake ayenera kukomerana mtima ndi kuganizirana ndipo ayenera kuchitanso zimenezi ndi ana awo. (Aefeso 5:28-33; 6:1, 2) Kukoma mtima kumeneku kuyenera kuonekera pa mmene anthu a m’banjamo amalankhulirana, ana ayenera kulemekeza makolo awo ndipo makolo ayenera kuwachitira zinthu ana awo moyenera. Muyamikireni nthaŵi yomweyo munthu wa m’banja lanu akachita zinthu zabwino, koma musamafulumire kudzudzula.
7, 8. (a) Kodi ndi makhalidwe ati amene tifunika kupeŵa kuti tisonyeze kukoma mtima kwenikweni m’banja? (b) Kodi kulankhulana kwabwino kumathandiza bwanji kuti banja likhale lolimba? (c) Kodi mungasonyeze bwanji kukoma mtima m’banja lanu?
7 Kukomera mtima anthu a m’banja lathu kumafuna kutsatira langizo la mtumwi Paulo lakuti: “Tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka mkamwa mwanu.” Tsiku lililonse, mabanja achikristu ayenera kulankhulana mwaulemu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kulankhulana kwabwino ndi chinthu chofunika kwambiri kuti banja likhale labwino komanso lolimba. Pofuna kuchepetsa mkangano pakakhala kusagwirizana, yesetsani kuthetsa vutolo osati kufuna kupambana mkanganowo. Anthu a m’banja limodzi achimwemwe amayesetsa kulimbikitsa kukoma mtima ndi kuganizirana pakati pawo.—Akolose 3:8, 12-14.
8 Kukoma mtima ndi kwabwino ndipo kumatipangitsa kufuna kuchitira zabwino anthu ena. Motero, timayesetsa kukhala wodalirika, woganizira ena, ndiponso wothandiza pogwirizana ndi ena m’banjamo. Pamafunika munthu aliyense payekha ndiponso onse m’banjamo kuchita zinthu zoti asonyeze kukoma mtima kumene kungachititse banjalo kukhala ndi mbiri yabwino. Zotsatira zake n’zakuti Mulungu adzawadalitsa komanso adzachititsa kuti Yehova, Mulungu wokoma mtima, alemekezedwe mumpingo ndi m’dera limene banjalo likukhala.—1 Petro 2:12.
Kukoma Mtima Kuntchito
9, 10. Fotokozani mavuto ena amene angabuke kuntchito, ndipo fotokozani mmene munthu angachitire ndi mavuto amenewo mokoma mtima.
9 Kwa Mkristu, zochitika za kuntchito za tsiku ndi tsiku zingamuchititse kuvutika kuti asonyeze kukoma mtima kwa antchito anzake. Kusagwirizana pakati pa anthu olembedwa ntchito kungachititse Mkristu kukhala pa vuto loti ntchito ingamuthere. Zimenezi zingatero chifukwa cha wogwira naye ntchito yemwe amachita zachinyengo pofuna kuti mbiri ya Mkristuyo kwa abwana ake ikhale yoipa. (Mlaliki 4:4) Sizophweka kusonyeza kukoma mtima pa zochitika ngati zimenezo. Komabe, pokumbukira kuti nthaŵi zonse kukoma mtima n’kwabwino kwambiri, mtumiki wa Yehova ayenera kuyesetsa mmene angathere kuti afeŵetse mtima wa anthu osagwirizanika. Kuwasonyeza kuti mumawaganizira kungathandize kuchita zimenezi. Mwina mungasonyeze kuganizira munthu amene mukugwira naye ntchito ngati wadwala kapena ngati munthu wina m’banja lake wadwala. Ngakhale kungofunsa chabe kuti ali bwanji kungamuchititse munthuyo kukhala ndi maganizo abwinopo. Inde, Akristu ayenera kuyesetsa kulimbikitsa mgwirizano ndi mtendere monga momwe angathere. Nthaŵi zina mawu okoma mtima osonyeza kuganizira ena angathandize kuti zinthu zikhale bwino.
10 Nthaŵi zina, bwana angaumirize antchito ake kutsatira maganizo ake ndipo angafune kuti aliyense achite nawo zinthu zina zosonyeza kukonda kwambiri dziko limene munthu akukhala kapena kuchita nawo zikondwerero zotsutsana ndi malemba. Ngati chikumbumtima cha Mkristu sichikumulola kuchita nawo zoterozo, zimenezi zingayambitse kusagwirizana. Panthaŵi imeneyi, sikungakhale kwanzeru kufotokoza mwatsatanetsatane kuipa kotsatira zimene bwanayo akufuna. Ndipotu, anthu amene satsatira zikhulupiriro zachikristu angaone ngati ndi chinthu chabwino kuchita nawo zimenezo. (1 Petro 2:21-23) Mwina mungafotokoze mokoma mtima zifukwa zimene inuyo panokha simungachitire nawo zimenezo. Ngati akulankhulani mokhadzula inu musabwezere mawu okhadzula. Ndi bwino kuti Mkristu atsatire malangizo abwino kwambiri amene ali pa Aroma 12:18, akuti: “Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”
Kukoma Mtima Kusukulu
11. Kodi achinyamata amakumana ndi mavuto otani pankhani yosonyeza kukoma mtima kwa ana asukulu anzawo?
11 Kungakhale kovuta kwambiri kwa achinyamata kusonyeza kukoma mtima kwa ana asukulu anzawo. Achinyamata nthaŵi zambiri amafuna kuti ophunzira anzawo aziwakonda. Anyamata ambiri amakonda kuvutitsa kuti ophunzira anzawo aziwatama, moti mpaka amafika popezerera ena kusukuluko. (Mateyu 20:25) Achinyamata ena amakonda kudzionetsera kuti ndi anzeru kwambiri, ndi aluso pa zamaseŵera, kapena aluso pa zochitika zina. Pofuna kusonyeza luso lawolo, nthaŵi zambiri sakomera mtima anzawo a m’kalasi kapena ophunzira ena. Iwo amaganiza molakwika kuti kukhala ndi luso loterolo kumawachititsa kukhala apamwamba kuposa ena. Mkristu wachinyamata ayenera kusamala kuti asatsanzire anthu oterowo. (Mateyu 20:26, 27) Mtumwi Paulo ananena kuti “chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima” ndiponso kuti chikondi “sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.” Motero, Mkristu sayenera kutsatira chitsanzo choipa cha anthu amene sakomera mtima anzawo, m’malo mwake ayenera kutsatira malangizo a m’Malemba pochita zinthu ndi ana asukulu anzake.—1 Akorinto 13:4.
12. (a) N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kwa achinyamata kukhala okoma mtima kwa aphunzitsi awo? (b) Kodi achinyamata angadalire thandizo la ndani akakumana ndi chiyeso choti asakhale okoma mtima?
12 Achinyamata ayeneranso kukomera mtima aphunzitsi awo. Ophunzira ambiri amasangalala akamaputa aphunzitsi awo. Amaganiza kuti ndi ochenjera akachotsera ulemu aphunzitsi awowo mwa kuchita zinthu zakuswa malamulo a sukulu. Angachititse ana asukulu ena kuchita nawo zimenezo mwa kuwaopseza kuti atero. Mkristu wachinyamata akakana kuchita nawo zimenezo, angamamunyoze kapena kumuzunza. Kukumana ndi zimenezi m’chaka chonse cha sukulu kungachititse Mkristu kuvutika kusonyeza kukoma mtima. Koma kumbukirani kuti n’kofunika kwambiri kukhala mtumiki wa Yehova wokhulupirika. Khulupirirani kuti adzakuthandizani pogwiritsa ntchito mzimu wake panthaŵi zovuta kwambiri zimenezi.—Salmo 37:28.
Kukomera Mtima Anthu Amene Tikukhala Nawo Pafupi
13-15. Kodi n’chiyani chingalepheretse munthu kukomera mtima anthu amene akukhala nawo pafupi, ndipo angagonjetse bwanji vuto limeneli?
13 Kaya mukukhala m’nyumba yanuyanu, pa mdadada, m’nyumba yokokedwa ndi galimoto, kapena kwina kulikonse, mungaganizire njira zimene mungasonyezere kukoma mtima ndi kusonyeza kuwafunira zabwino anthu amene mukukhala nawo pafupi. Kuchitanso zimenezi sikophweka.
14 Bwanji ngati amene mwayandikana nawo nyumba amakusankhani chifukwa cha fuko lanu, mtundu wanu, kapena chipembedzo chanu? Bwanji ngati amachita mwano nthaŵi zina kapena sakuŵerengerani m’pang’ono pomwe? Monga mtumiki wa Yehova, kusonyeza kukoma mtima monga momwe mungathere kudzakhala kopindulitsa. Mudzaoneka kuti ndinu wosiyana, wotsitsimula ena, zimene zingachititse kuti Yehova, yemwe ndi chitsanzo cha kukoma mtima, alemekezedwe. Simukudziŵa kuti ndi liti pamene anthu omwe mukukhala nawo pafupiwo adzasintha maganizo awo chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mwina akhoza kukhala otamanda Yehova.—1 Petro 2:12.
15 Kodi mungawakomere mtima bwanji anthu amene mwayandikana nawo nyumba? Njira imodzi ndiyo mwa khalidwe labwino m’banja lanu pamene nonse mukusonyeza chipatso cha mzimu. Anthu amene mukukhala nawo pafupi angaone zimenezo. Nthaŵi zina mungachitire zabwino anthu amene mukukhala nawo pafupiwo. Kumbukirani kuti kukoma mtima kumatanthauza kufunira zabwino anthu ena.—1 Petro 3:8-12.
Kukoma Mtima Muutumiki
16, 17. (a) N’chifukwa chiyani kukoma mtima n’kofunika kwambiri mu utumiki umene timachita kwa anthu onse? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kukoma mtima pa mbali zosiyanasiyana za utumiki wakumunda?
16 Utumiki wathu wachikristu tiyenera kuuchita mokoma mtima pamene tikuyesetsa kulankhula ndi anthu m’nyumba zawo, kuntchito kwawo, ndiponso pamalo ena alionse pamene pali anthu. Tiyenera kukumbukira kuti tikuimira Yehova, yemwe ndi wokoma mtima nthaŵi zonse.—Eksodo 34:6.
17 Kodi ndi njira zina ziti zimene mungasonyezere kukoma mtima muutumiki? Mwachitsanzo, polalikira mumsewu, mungasonyeze kukoma mtima mwa kulankhula ndi anthu mwachidule komanso mowaganizira. M’njira za oyenda pansi m’mphepete mwa misewu nthaŵi zambiri mumakhala anthu ambiri, motero samalani kuti musatsekere ena njira. Ndiponso, mukamalalikira m’malo a bizinesi, sonyezani kukoma mtima mwa kulankhula mwachidule, pokumbukira kuti ogulitsa m’sitolo amafunika kusamala makasitomala.
18. Kodi kuchita mwanzeru kumathandiza bwanji kusonyeza kukoma mtima muutumiki?
18 Pochita utumiki wa kunyumba ndi nyumba, chitani zinthu mwanzeru. Musakhale panyumbapo kwa nthaŵi yaitali, makamaka ngati nyengo siili bwino. Kodi mungazindikire munthu akafika poti saathanso kupirira kapena ngati sakusangalala ndi kubwera kwanu? Mwina m’dera limene mukukhala, Mboni za Yehova zimafika panyumba za anthu pafupipafupi. Ngati ndi choncho, sonyezani kuwaganizira mwapadera anthu, nthaŵi zonse khalani wokoma mtima ndiponso wabwino. (Miyambo 17:14) Ngati patsikulo mwininyumbayo sakufuna kumvetsera, vomerezani zifukwa zimene sakufunira. Kumbukirani kuti mbale kapena mlongo wanu wachikristu mosakayika adzafika panyumba imeneyo posachedwa. Ngati mwakumana ndi munthu wina wamwano, yesetsani kusonyeza kukoma mtima. Musakweze mawu anu kapena kukoka tsinya, m’malo mwake lankhulani mofatsa. Mkristu wokoma mtima safuna kuputa mwininyumba, zimene zingachititse kuti akangane. (Mateyu 10:11-14) Mwina tsiku lina munthu ameneyo adzamvetsera uthenga wabwino.
Kukoma Mtima pa Misonkhano ya Mpingo
19, 20. N’chifukwa chiyani kukoma mtima ndi kofunika mumpingo, ndipo tingakusonyeze bwanji?
19 N’kofunikanso kwambiri kukomera mtima Akristu anzathu. (Ahebri 13:1) Popeza ndife mbali ya ubale wa padziko lonse, kukoma mtima n’kofunika kwambiri pochitirana zinthu.
20 Ngati mpingo ukugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndi mpingo wina, kapena mipingo ina iŵiri kapena kuposerapo, n’kofunika kwambiri kukomera mtima a mipingo inayo, kuwachitira ulemu pamene mukuchita zinthu. Kusamvana sikungathandize kuti mugwirizane pa nkhani monga nthaŵi yochitira misonkhano ndi zinthu zina zofunika monga kuyeretsa ndi kukonzanso nyumbayo. Khalani okoma mtima ndi oganizira ena ngakhale kuti pangakhale kusiyana maganizo. Mwa kuchita zimenezi, kukoma mtima kudzapambana, ndipo Yehova adzakudalitsanidi chifukwa cha kuyesetsa kwanu kufunira ena zabwino.
Pitirizani Kusonyeza Kukoma Mtima
21, 22. Mogwirizana ndi Akolose 3:12, kodi titsimikize mtima kuchita chiyani?
21 Kukoma mtima ndi khalidwe limene limakhudza mbali iliyonse ya moyo wathu. Motero tiyenera kuyesetsa kuti khalidweli likhale mbali yofunika kwambiri ya moyo wathu wachikristu. Tiyenera kukhala ndi chizoloŵezi chokomera mtima anthu ena.
22 Tiyeni tonsefe tizikomera mtima anthu ena tsiku ndi tsiku ndipo motero tonse aliyense payekha tidzakhala tikutsatira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.”—Akolose 3:12.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani kumakhala kovuta kuti Mkristu asonyeze kukoma mtima?
• N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kusonyeza kukoma mtima m’banja?
• Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingachititse kukhala kovuta kusonyeza kukoma mtima kusukulu, kuntchito, ndi kwa anthu amene tikukhala nawo pafupi?
• Fotokozani mmene Akristu angasonyezere kukoma mtima muutumiki umene amachita kwa anthu onse.
[Chithunzi patsamba 18]
Anthu onse m’banja akamasonyeza kukoma mtima amakhala ogwirizana kwambiri
[Chithunzi patsamba 19]
Mungasonyeze kukoma mtima wantchito mnzanu kapena wa m’banja mwake akadwala
[Chithunzi patsamba 20]
Yehova amathandiza anthu amene amasonyeza kukoma mtima mokhulupirika ngakhale akunyozedwa
[Chithunzi patsamba 21]
Kuthandiza munthu amene mukukhala naye pafupi amene akufuna thandizo n’kumukomera mtima