Kodi Mumalola Kuti Yehova Akuthandizeni?
“Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzawopa.”—AHEBRI 13:6.
1, 2. N’chifukwa chiyani tikufunika kulola Yehova kutithandiza ndi kutitsogolera m’moyo?
YEREKEZANI kuti mukuyenda m’njira ya m’phiri. Koma sikuti muli nokha ayi, popeza kuti munthu wina wadzipereka kuti ayende nanu ndi kukuonetsa malowo, ndipo palibenso wina amene angakuyendetseni bwino kuposa iyeyo. Iye akuwadziwa bwino kwambiri malowo komanso ndi wamphamvu kuposa inuyo, koma akuleza mtima ndipo akuyenda nanu limodzi. Kenaka akuona kuti inuyo mukupunthwa kawirikawiri. Poopa kuti mungavulale, iye akutambasula dzanja lake kuti akuthandizeni kudutsa malo enaake oopsa kwambiri. Kodi mungakane thandizo lakelo? N’zodziwikiratu kuti simungakane, chifukwa chakuti mungathe kuvulala kwambiri ngati simuthandizidwa.
2 Popeza kuti ndife Akristu, tikuyenda m’njira yovuta kwambiri kuyendamo. Kodi tikufunika kuyenda tokha m’njira yochepetsetsayi? (Mateyu 7:14) Ayi. Baibulo limasonyeza kuti Yehova Mulungu, yemwe angayende nafe bwino kwambiri, amalola kuyenda ndi anthu. (Genesis 5:24; 6:9) Kodi Yehova amathandiza atumiki ake akamayenda m’njirayi? Iye anati: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usawope ndidzakuthandiza iwe.” (Yesaya 41:13) Mofanana ndi munthu woyendetsa mnzake tam’tchula m’fanizo uja, Yehova mokoma mtima amafuna kuthandiza komanso kukhala paubwenzi ndi anthu ofuna kuyenda naye. Kunena zoona palibe aliyense pakati pathupa amene angakane thandizo lake.
3. Kodi pamene tikukambirana nkhani ino tiyankha mafunso ati?
3 M’nkhani yapitayi, takambirana njira zinayi zomwe Yehova ankathandizira anthu ake m’nthawi zakale. Kodi masiku ano amathandizanso anthu ake m’njira zomwezo? Ndipo nanga kodi tingatani poonetsetsa kuti tikulola kulandira thandizo loterolo lomwe tikufunikira? Tiyeni tiyankhe mafunso amenewa. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova ndiyedi Mthandizi wathu.—Ahebri 13:6.
Amatithandiza Kudzera mwa Angelo
4. N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu masiku ano angakhale ndi chikhulupiriro chakuti angelo amawathandiza?
4 Kodi angelo amathandiza atumiki a Yehova a masiku ano? Inde, amawathandiza. Ndi zoona kuti masiku ano angelo sachita kubwera pamaso m’pamaso kuti apulumutse olambira oona akakhala m’mavuto. Ngakhalenso m’nthawi za m’Baibulo, sikawirikawiri pamene angelo ankathandiza anthu motero. Anthu sankaona zambiri zomwe iwo ankachita, monganso mmene zilili masiku ano. Komabe atumiki a Mulungu amene ankadziwa kuti pali angelo oti awathandize ankalimbikitsidwa kwambiri. (2 Mafumu 6:14-17) Nafenso tili ndi zifukwa zomveka zoganizirira chimodzimodzi.
5. Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti angelo akugwira nawo ntchito yolalikira masiku ano?
5 Angelo a Yehova ali ndi chidwi chachikulu ndi ntchito yapadera yomwe ife tikugwira. Kodi ntchito yake ndi yotani? Tingapeze yankho la funsoli pa Chivumbulutso 14:6. Lembali limati: “Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” “Uthenga Wabwino wosatha” umenewu n’ngogwirizana kwambiri ndi ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ Malinga ndi zomwe Yesu ananeneratu, uthenga wabwinowu “udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse” mapeto a dongosolo ili la zinthu asanafike. (Mateyu 24:14) N’zoona kuti angelo salalikira mwachindunji. Yesu anapereka kwa anthu ntchito yofunika kwambiri imeneyi. (Mateyu 28:19, 20) Kodi sizolimbikitsa kudziwa kuti pamene tikugwira ntchitoyi, timathandizidwa ndi angelo oyera, omwe ndi anthu auzimu, anzeru ndiponso amphamvu kwambiri?
6, 7. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti angelo akuthandiza nawo pantchito yathu yolalikira? (b) Kodi tingatani kuti tikhale otsimikiza kuti tilandira thandizo la angelo a Yehova?
6 Pali umboni wochuluka wosonyeza kuti angelo akutithandiza pantchito yathu. Mwachitsanzo, timamva nthawi zambiri kuti pamene Mboni za Yehova zili mu utumiki wawo, zimapeza anthu oti angopemphera kumene kuti Mulungu awathandize kupeza choonadi. Nkhani ngati izi zimachitika kawirikawiri zedi moti sitinganene kuti zimangochitika mwangozi. Chifukwa cha thandizo la angelo limeneli, anthu ambiri akuphunzira kuchita zimene ‘mngelo wouluka pakati pa mlengalenga’ analengeza, zakuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero.”—Chivumbulutso 14:7.
7 Kodi mumalakalaka angelo amphamvu a Yehova atakuthandizani? Ndiyetu khalani wakhama mu utumiki wanu. (1 Akorinto 15:58) Tikadzipereka mosangalala pantchito yapadera imene Yehova watipatsayi, tingakhale otsimikiza kuti angelo ake atithandiza.
Amatithandiza Kudzera mwa Mkulu wa Angelo
8. Kodi Yesu ali ndi udindo waukulu uti kumwamba, ndipo n’chifukwa chiyani izi zimatilimbikitsa?
8 Yehova amatipatsa thandizo la mtundu winanso lodzera mwa angelo. Lemba la Chivumbulutso 10:1 limafotokoza za ‘mngelo wolimba’ kwambiri ndipo ‘nkhope yake ndi yangati dzuwa.’ Mngelo amene anaoneka m’masomphenyayu mwachionekere akuimira Yesu Kristu atapatsidwa ulemerero komanso ali ndi mphamvu zake zakumwamba. (Chivumbulutso 1:13, 16) Kodi Yesu ndi mngelodi? Tinganene kuti inde, chifukwa chakuti iye ndi mngelo wamkulu. (1 Atesalonika 4:16) Pa ana onse auzimu a Yehova, Yesu ndiye wamphamvu kwambiri. Yehova anaika Yesu kukhala mkulu wa magulu Ake onse a angelo. Popeza kuti Yesu ndi mkulu wa angelo, iye amatithandiza kwambiri. Kodi amachita zimenezi motani?
9, 10. (a) Tikachimwa, kodi Yesu amakhala ngati “mthandizi” wathu motani? (b) Kodi tingathandizidwe motani ndi chitsanzo cha Yesu?
9 Mtumwi Yohane yemwe anali atakalamba analemba kuti: “Akachimwa wina, Nkhoswe [“mthandizi,” NW] tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama.” (1 Yohane 2:1) N’chifukwa chiyani Yohane ananena kuti Yesu ndi “mthandizi” wathu makamaka ‘tikachimwa’? Timachimwa tsiku ndi tsiku, ndipo tchimo limadzetsa imfa. (Mlaliki 7:20; Aroma 6:23) Koma, Yesu anapereka moyo wake monga nsembe ya machimo athu. Ndipo panopa ali limodzi ndi Atate wathu wachifundo kuti azitipembedzera. Tonsefe timafunika thandizo lotereli. Kodi tingalole motani kulandira thandizoli? Tikufunika kulapa machimo athu ndi kupempha kuti atikhululukire pogwiritsira ntchito nsembe ya Yesu. Tiyeneranso kupewa kubwereza machimo athuwo.
10 Kuwonjezera pa kutifera, Yesu anatisiyira chitsanzo chabwino kwambiri. (1 Petro 2:21) Chitsanzo chake chimatitsogolera, chimatithandiza kulinganiza moyo wathu kuti tipewe machimo aakulu ndiponso kuti tizikondweretsa Yehova Mulungu pamoyo wathu. Kodi sitiyamikira kulandira thandizo loterolo? Yesu analonjeza anthu om’tsatira kuti adzalandira thandizo linanso.
Amatithandiza Kudzera mwa Mzimu Woyera
11, 12. Kodi mzimu wa Yehova n’chiyani, uli ndi mphamvu zotani, ndipo n’chifukwa chiyani timafunikira mzimuwu masiku ano?
11 Yesu analonjeza kuti: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina [kapena kuti mthandizi wina], kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kum’landira.” (Yohane 14:16, 17) “Mzimu wa choonadi” umenewu, kapena kuti mzimu woyera, si munthu ayi, koma mphamvu yomwe Yehova amagwiritsira ntchito. Mphamvu imeneyi ilibe malire. Ndi mphamvu yomwe Yehova anaigwiritsira ntchito polenga chilengedwe chonse, pochita zozizwitsa, ndiponso podziwitsa anthu zolinga zake kudzera m’masomphenya. Popeza kuti masiku ano Yehova sagwiritsira ntchito mzimu wake mwanjira zimenezi, kodi zikutanthauza kuti ife sitifunika thandizo limeneli?
12 Ayi. ‘M’nthawi zowawitsa’ zino, timafunika mzimu wa Yehova kwambiri kusiyana ndi mmene zinalili m’mbuyomu. (2 Timoteo 3:1) Mzimuwu umatilimbikitsa kupirira mayesero. Umatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino kwambiri amene amapangitsa kuti tikhale paubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso abale ndi alongo athu auzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Motero, kodi tingapindule motani ndi thandizo labwino limeneli la Yehova?
13, 14. (a) Kodi n’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova amapatsa anthu ake mzimu wake woyera? (b) Kodi ndi zinthu zotani zimene zingasonyeze kuti sitilola kwenikweni mphatso ya mzimu woyera?
13 Choyamba, tiyenera kupempha mzimu woyera. Yesu anati: “Ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye?” (Luka 11:13) Inde, sitingaganizirenso Atate wina wabwino kwambiri kuposa Yehova. Ngati tim’pempha ndi chikhulupiriro ndiponso moona mtima kuti atipatse mzimu woyera, n’zosatheka ngakhale pang’ono kuti iye akane kutipatsa mzimuwu. Motero, funso n’lakuti, Kodi timapempha mzimu woyera? Ndithu, tiyenera kumapempha mzimu woyera tsiku ndi tsiku.
14 Chachiwiri, timalandira mphatso imeneyi mwa kuchita zinthu zimene sizitsutsana ndi mzimuwo. Taonani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti Mkristu akulimbana ndi chizolowezi chokonda kuona zinthu zolaula. Wapempha mzimu woyera kuti um’thandize kulimbana ndi khalidwe loipali. Wapemphanso malangizo kwa akulu achikristu, ndipo iwo amuuza kuti achite zinthu zomwe zingathetseretu vutolo, mwa kusayandikira n’komwe zinthu zoipazo. (Mateyu 5:29) Bwanji ngati atanyalanyaza malangizo a akuluwo n’kumapitiriza kuona zinthu zoterozo? Kodi akuchita zinthu zogwirizana ndi pemphero lake lopempha mzimu woyera kuti um’thandize? Kapena iye kwenikweni, akudziika pangozi yoti angathe kumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu, n’kutaya mwayi wolandira mphatsoyi? (Aefeso 4:30) Kunena zoona, tonsefe tiyenera kuchita khama kuonetsetsa kuti tikupitiriza kulandira thandizo labwinoli la Yehova.
Amatithandiza Kudzera M’Mawu Ake
15. Kodi tingasonyeze motani kuti sitinyalanyaza Baibulo?
15 Kwa zaka mazana ambiri, Baibulo lakhala likuthandiza atumiki okhulupirika a Yehova. M’malo monyalanyaza Malemba Opatulika, tikufunika kumakumbukira kuti thandizo limene Malembawa amapereka n’losasimbika. Pamafunika khama kuti tilole kulandira thandizo limeneli. Pa zochita zathu zatsiku ndi tsiku tiyenera kukhala ndi nthawi yowerenga Baibulo.
16, 17. (a) Kodi lemba la Salmo 1:2, 3 limafotokoza motani phindu lowerenga malamulo a Mulungu? (b) Kodi lemba la Salmo 1:3 limasonyeza motani kuti tikufunika kukhala akhama?
16 Pofotokoza za munthu amene amakondweretsa Mulungu, lemba la Salmo 1:2, 3 limati: “M’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” Kodi mukuona mfundo yaikulu ya mavesiwa? N’zosavuta kuti munthu awerenge mawu amenewa ndi kuganiza kuti akungofotokoza za malo abata, okhala ndi mtengo wamthunzi womwe uli m’mphepete mwa mtsinje. Kungakhale kosangalatsa kwambiri kugona pamalo oterowo masana. Koma lembali sikuti likufuna kutiganiziritsa za kupumula. Likufotokoza za zinthu zina zosiyana kwambiri ndi zimenezi. Likunena za kukhala munthu wakhama. Motani?
17 Onani kuti mtengo ukufotokozedwawu sikuti ndi mtengo wongokhala ndi mthunzi, womera mwamwayi m’mphepete mwa mtsinje. Ndi mtengo wobala zipatso, womwe munthu wachita kusankha malo oti ‘auwokepo,’ pomwe ndi “pa mitsinje ya madzi.” Kodi zingatheke bwanji kuti mtengo umodzi ukhale pa mitsinje ingapo? M’munda wa mitengo ya zipatso, mwinimundawo angathe kukumba ngalande zoti zizipatsira madzi mitengo yake yomwe ili yofunika kwambiri. Mwaonatu, tsopano mfundo ya m’mavesiwa yayamba kuoneka bwino kwambiri. Ngati tikufanana ndi mtengo umenewu mwauzimu, ndi chifukwa chakuti enaake anachita khama kwambiri potithandiza. Tili m’gulu limene limatipatsa madzi abwino a choonadi, koma tikufunika kuchita mbali yathu. Tikufunika kutenga ndi kumwa madzi amtengo wapataliwa. Tizisinkhasinkha ndi kufufuza zinthu m’Mawu a Mulungu kuti choonadi chake chitifike m’maganizo ndi mumtima. Tikatero, nafenso tidzabala zipatso zabwino.
18. Kodi timafunika kutani kuti tipeze mayankho a m’Baibulo pa mafunso omwe tili nawo?
18 Sitingapindule chilichonse ndi Baibulo ngati sitiliwerenga. Komanso sikuti Baibulo lili ngati kachithumwa moti tingatsinzine, kutsegula paliponse mongolota, n’kumayembekezera kuti patsamba lomwe tatsegulalo tipezapo mayankho a funso lomwe tili nalo. Tikamaganiza zoti tichite, tingati tiyenera kukumba m’Baibulo ngati mmene timafufuzira chuma chokwiririka, kuti ‘tim’dziwedi Mulungu.’ (Miyambo 2:1-5) Nthawi zambiri pamafunika kufufuza mfundo mwakhama ndi mosamala kuti tipeze malangizo a m’Malemba okhudza vuto lomwe tili nalo. Tili ndi mabuku ambiri ofotokoza za m’Baibulo omwe angatithandize pa kufufuza kwathu. Tikamagwiritsira ntchito mabuku amenewa kuti tipeze nzeru zakuya za m’Mawu a Mulungu, ndiye kuti tikugwiritsadi ntchito thandizo la Yehova.
Amatithandiza Kudzera mwa Okhulupirira Anzathu
19. (a) N’chifukwa chiyani nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! tiyenera kuziona kuti ndi thandizo loperekedwa kudzera mwa okhulupirira anzathu? (b) Kodi inuyo munathandizidwapo motani ndi nkhani ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani!?
19 Anthu otumikira Yehova akhala akuthandizana m’mbuyo monsemu. Kodi Yehova anasintha masiku ano? Ayi, sanasinthe ngakhale pang’ono. Mosakayikira, tonsefe tingaganizire nthawi zina pamene tinalandira thandizo loyenerera panthawiyo kuchokera kwa okhulupirira anzathu. Mwachitsanzo, kodi mungakumbukire nkhani inayake ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! yomwe inakulimbikitsani pamene munkafunika kulimbikitsidwa, kapena yomwe inakuthandizani kuthetsa vuto linalake kapena kugonjetsa nkhani yolimbana ndi chikhulupiriro chanu? Yehova anakupatsani thandizo limenelo kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene anapatsidwa ntchito yopereka “zakudya panthawi yake.”—Mateyu 24:45-47.
20. Kodi akulu achikristu amasonyeza motani kuti iwo ndi “zaufulu kwa anthu”?
20 Komabe nthawi zambiri thandizo lochokera kwa okhulupirira anzathu limakhala lachindunji. Mkulu wachikristu amatha kukamba nkhani yotigwira mtima, kapena angapange ulendo waubusa wotithandiza m’nthawi yovuta, kapenanso mokoma mtima, iye angatipatse malangizo amene angatithandize kuona ndi kuthetsa vuto lathu. Mlongo wina anafotokoza izi poyamikira thandizo limene mkulu wina mumpingo anam’patsa: “Pamene tinali mu utumiki wakumunda, iye anandithandiza kukhala womasuka kunena zakukhosi kwanga. Usiku wa tsiku limenelo, ndinali nditapemphera kwa Yehova, kupempha munthu woti ndilankhule naye za vuto langa. Tsiku lotsatira ndiye limene mbaleyu analankhula nane mokoma mtima. Anandithandiza kuona mmene Yehova wakhala akundithandizira kwa zaka zambiri. Ndikuthokoza Yehova chifukwa chonditumizira mkulu ameneyu.” Pa zonse zomwe amachitazi, akulu achikristu amasonyeza kuti iwo ndi “zaufulu kwa anthu,” zomwe Yehova wapereka kudzera mwa Yesu Kristu kuti zitithandize kupirira pamene tikuyenda m’njira ya kumoyo.—Aefeso 4:8.
21, 22. (a) Kodi pamachitika zinthu zotani mpingo ukamatsatira malangizo a pa Afilipi 2:4? (b) Kodi n’chifukwa chiyani zinthu ngakhale zing’onozing’ono zimene ena amachita chifukwa chokoma mtima zili zofunika?
21 Kuwonjezera pa akulu, Mkristu aliyense wokhulupirika ayenera kutsatira lamulo louziridwa lakuti “asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:4) Anthu a mumpingo wachikristu akamatsatira malangizo amenewa, amachitirana zinthu zabwino kwambiri chifukwa chokoma mtima. Mwachitsanzo, banja lina linakumana mwadzidzidzi ndi vuto ladzaoneni. Bambo wa banjalo anapita kusitolo ndi mwana wake wamkazi. Pobwerera kunyumba, galimoto yawo inachita ngozi. Mtsikanayo anafa; ndipo bamboyo anavulala kwambiri. Atatuluka m’chipatala, poyamba sankatha kudzichitira yekha zinthu chifukwa choti ziwalo zake zinafa. Mkazi wake anasokonezeka maganizo kwambiri moti sakanatha kusamalira yekha mwamuna wakeyo. Motero, banja lina la mumpingo wawo linawatenga n’kumakhala nawo kunyumba kwawo ndi kumawasamalira kwa milungu ingapo.
22 Ndi zoona kuti si zinthu zonse zomwe Akristu amachita chifukwa cha kukoma mtima zomwe zimakhudza vuto ngati limeneli ndiponso zofuna kudzipereka kotereku. Chithandizo china chomwe timalandira chimakhala chochepa kwambiri. Koma timayamikirabe ngakhale munthu atasonyeza kukoma mtima kochepa motani. Kodi si choncho? Kodi zinakuchitikiranipo kuti mbale kapena mlongo, anakulimbikitsani kapena kukuchitirani zinazake mwa kukoma mtima kwake, ndipo zimene ananena kapena kuchitazo n’zimene munali kufunikiradi kwambiri panthawiyo? Nthawi zambiri Yehova amatisamalira m’njira zoterezi.—Miyambo 17:17; 18:24.
23. Kodi Yehova amaona motani zimene tikuyesetsa kuchita kuti tithandizane?
23 Kodi mukufuna kuti Yehova akugwiritsireni ntchito pothandizira ena? Mwayi wapadera umenewu ulipo. Ndipotu, Yehova amayamikira khama lanu pothandiza ena. Mawu Ake amati: “Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.” (Miyambo 19:17) Timapeza chimwemwe chachikulu tikadzipereka kuthandiza abale ndi alongo athu. (Machitidwe 20:35) Anthu amene amadzipatula mwadala sapeza chimwemwe chomwe chimadza chifukwa chothandiza ena m’njira imeneyi ndipo enanso sangathe kuwalimbikitsa iwowo. (Miyambo 18:1) Motero, tiyeni tiziyesetsa kufika pamisonkhano yachikristu nthawi zonse kuti tizilimbikitsana.—Ahebri 10:24, 25.
24. Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kuona ngati kuti tikumanidwa zinthu zina chifukwa choti sitinaone nawo zozizwitsa zomwe Yehova anachita m’mbuyomu?
24 Kodi sizosangalatsa kuona njira zimene Yehova amatithandizira? Ngakhale kuti m’nthawi yathu ino Yehova sachita zozizwitsa pofuna kukwaniritsa zolinga zake, sitiyenera kuona ngati kuti tikumanidwa zinthu zina. Chofunika kwambiri n’chakuti Yehova amatipatsa thandizo lonse lomwe timafuna kuti tipitirize kukhala okhulupirika. Ndipo ngati tipirira limodzi ndi abale athu m’chikhulupiriro, tidzaona zinthu zozizwitsa ndiponso zikuluzikulu kwambiri zimene Yehova sanachitepo n’kale lonse. Tiyeni titsimikize mtima kulola thandizo lomwe Yehova amapereka chifukwa cha chikondi chake ndi kuligwiritsira ntchito bwino kuti nafenso tithe kunena zomwe lemba lathu la chaka cha 2005 limanena, zakuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.”—Salmo 121:2.
Kodi Mukuganiza Bwanji?
Masiku ano, kodi Yehova amatipatsa motani thandizo lomwe tikulifuna—
• kudzera mwa angelo?
• kudzera mwa mzimu wake woyera?
• ndi Mawu ake ouziridwa?
• kudzera mwa okhulupirira anzathu?
[Chithunzi patsamba 18]
N’zolimbikitsa kudziwa kuti angelo akuthandiza nawo ntchito yolalikira
[Chithunzi patsamba 21]
Yehova angathe kugwiritsira ntchito wina mwa okhulupirira anzathu kuti atilimbikitse pamene tikufunikira kulimbikitsidwa