Kodi Muli ndi Mphamvu Iliyonse pa Tsogolo Lanu?
KODI tsogolo lathu linakonzedwa kale? Kodi zinthu zimene timasankha kuchita pamoyo wathu sizikhudza tsogolo lathu?
Tatiyeni tingoyerekezera kuti n’zoonadi munthu ali ndi mphamvu yokonza yekha zinthu zonse zochitika pamoyo wake. Kodi ngati n’choncho, pangapezeke munthu aliyense amene Mulungu anamuikiratu kuti adzagwire ntchito inayake kapena kuti adzakhale ndi udindo winawake? Komanso kodi Mulungu angadzakwaniritse bwanji cholinga chake chokhudza dziko lapansi ngati anthu ali ndi ufulu wokonza okha tsogolo lawo? Mafunso amenewa Baibulo limawayankha mogwira mtima kwambiri.
Kodi Chiphunzitso cha Chikonzero Chimagwirizana ndi Ufulu Wosankha?
Taganizirani mmene Yehova Mulungu anatilengera. Baibulo limati: “M’chifanizo cha Mulungu adam’lenga [munthu]; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” (Genesis 1:27) Pakuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, timatha kusonyeza makhalidwe ake monga chikondi, chilungamo, nzeru, ndi mphamvu. Mulungu anatipatsanso mphatso yokhala ndi ufulu wosankha zochita. Ufulu umenewu tili nawo ndife tokha pa zolengedwa zonse za padziko pano. Anthufe tingathe kusankha kumvera malangizo a Mulungu pankhani ya makhalidwe kapena ayi. N’chifukwa chake mneneri Mose ananena kuti: “Ndichititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira iye.”—Deuteronomo 30:19, 20.
Komabe mphatso yokhala ndi ufulu wosankha zochita, siitanthauza kuti tili ndi ufulu wochita chilichonse chimene tikufuna. Mphatso imeneyi siitipatsa ufulu wophwanya malamulo a m’chilengedwe ndiponso a makhalidwe abwino amene Mulungu anapereka pofuna kuti m’chilengedwe chonse mukhale bata ndiponso mtendere. Mulungu anakhazikitsa malamulo amenewa n’cholinga choti atipindulitse ndipo ngati titawaphwanya m’njira ina iliyonse tingathe kulowa nazo m’mavuto adzaoneni. Mwachitsanzo, dziko lapansili lili ndi mphamvu yachilengedwe yokoka zinthu, ndiyeno tangoganizirani zimene zingachitike ngati titanyalanyaza mphamvuyi n’kudumpha dala kuchokera padenga la nyumba yaitali kwambiri.—Agalatiya 6:7.
Ufulu wosankha zochita umatipatsanso udindo wina umene zolengedwa zina zopanda ufuluwu zilibe. Pankhaniyi, wolemba mabuku wina, Corliss Lamont anafunsa kuti: “Kodi bwenzi anthu akuimbidwa mlandu pa zolakwa zawo kukanakhala kuti . . . zochita zawo zonse n’zokonzedweratu ndi Mulungu?” Inde, sibwenzi anthu akuimbidwa mlandu. Zinyama zimangochita zinthu monga mwa chilengedwe chawo motero siziimbidwa mlandu pochita khalidwe linalake loipa. Makompyuta nawo saimbidwa mlandu akamachita ntchito zimene anawakonzera. Motero ufulu wosankha umatipatsa udindo waukulu kwambiri ndipo umatipatsa mlandu tikachita zinthu zolakwika.
Zolakwa zathuzi zikanakhala zochita kukonzedweratu ndi Yehova Mulungu ifeyo tisanabadwe, bwenzi tikuti iyeyo ndi Mulungu wopanda chikondi ndiponso chilungamo chifukwa amatiimba mlandu tikamachita zoipa. Komatu Mulungu sanakonzeretu zochita zathu chifukwa choti “Mulungu ndiye chikondi” ndiponso “njira zake zonse ndi chiweruzo,” kapena kuti chilungamo. (1 Yohane 4:8; Deuteronomo 32:4) Iye anatipatsa ufulu wosankha, ndipo atatero ‘sanakonzeretu pachiyambi pomwe kuti adzapulumutsa auje ndi auje ndi kuwononga auje ndi auje,’ monga mmene anthu okhulupirira chiphunzitso cha chikonzero amanenera. Chiphunzitsochi n’chosamveka tikaganizira za ufulu umene Mulungu anatipatsa, wosankha tokha zochita.
Baibulo limasonyeza mosapita m’mbali kuti zimene timasankha zimakhudza tsogolo lathu. Mwachitsanzo, Mulungu amadandaulira ochita zoipa powauza kuti: “Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, ndi zoipa za ntchito zanu . . . ndingachitire inu choipa.” (Yeremiya 25:5, 6) Mulungu akanakhala kuti amakonzeratu tsogolo la munthu wina aliyense sibwenzi akuchonderera anthu chonchi. Chinanso n’chakuti Mawu a Mulungu amati: “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye.” (Machitidwe 3:19) Kodi Yehova angawauzirenji anthu kuti alape ndi kubwerera ngati akudziwa kale kuti palibe chilichonse chimene iwo angachite kuti asinthe tsogolo lawo?
Malemba amanenapo za anthu ena amene anaitanidwa ndi Mulungu kuti akakhale mafumu ndi Yesu Kristu kumwamba. (Mateyu 22:14; Luka 12:32) Komabe Baibulo limati iwowa angathe kulandidwa mwayi umenewo akapanda kupirira mpaka mapeto. (Chivumbulutso 2:10) Kodi Mulungu angawaitanirenji anthuwa ngati anakonza kale zoti pamapeto pake sadzawasankha? Taganiziraninso zimene mtumwi Paulo analembera okhulupirira anzake. Iye anati: “Tikachimwa ife eniake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo.” (Ahebri 10:26) Chenjezo limeneli silingakhale ndi phindu lililonse ngati Mulungu anakonza kale tsogolo la anthuwa. Komano kodi Mulungu sanakonzeretu zoti anthu enaake adzalamulire ndi Yesu Kristu?
Kodi Anasankhiratu Anthu Pawokhapawokha Kapena Anasankhiratu Gulu?
Mtumwi Paulo analemba kuti: “[Mulungu] anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m’zakumwamba mwa Kristu; monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi . . . Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Kristu.” (Aefeso 1:3-5) Kodi Mulungu anakonzeratu chiyani, ndipo kodi mawu akuti anawasankha “lisanakhazikike dziko lapansi” amatanthauza chiyani?
Mavesi amenewa amalongosola kuti Mulungu anasankha mbadwa zina za munthu woyambirira Adamu, kuti zikalamulire ndi Kristu kumwamba. (Aroma 8:14-17, 28-30; Chivumbulutso 5:9, 10) Komabe, zoti Yehova Mulungu anakonzeratu kuti anthu enaake adzalandire mwayi umenewu ndipo anachita izi zaka masauzande ambirimbiri anthuwo asanabadwe n’komwe, n’zotsutsana ndi mfundo yakuti anthu ali ndi ufulu wosankha zochita. Inde, Mulungu anakonzeratu gulu, la anthu koma osati anthu pawokhapawokha.
Mwachitsanzo: Ingoyerekezerani kuti boma linalake laganiza zokhazikitsa bungwe. Bomalo likukonzeratu zonse zomwe bungwelo liyenera kudzachita, mphamvu zimene lidzakhale nazo, ndiponso kukula kwake. Kenaka patatha nthawi ndithu chilikhazikitsireni, bungwelo likuyamba kugwira ntchito ndipo anthu a m’bungwelo akutulutsa chikalata chonena kuti: “Boma linakonza kalekale ntchito yoti tizichita. Tsopano tikuyamba ntchito yathu.” Kodi pamenepa inuyo mungaganize kuti bomalo linakonza kalekale kuti auje ndi auje ndi amene adzakhale m’bungwe limeneli? Ayi ndithu simungatero. Moteronso, Yehova anakonzeratu zoti adzakhazikitsa bungwe lapadera lodzathetsa mavuto obwera chifukwa cha uchimo wa Adamu. Iye anakonzeratu gulu la anthu oti adzatumikire m’bungwe limenelo koma sanakonzeretu zoti m’bungwemo mudzakhala auje ndi auje. Anthuwa amawasankha bungwelo atalikonza kale, ndipo amawavomereza kukhala m’bungwemo pamapeto penipeni pa moyo wawo, malingana ndi zimene akhala akuchita pa moyo wawo.
Kodi Paulo ankanena za dziko liti pamene anati: “[Mulungu] anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi?” Dziko limene Paulo anali kunena apa si dziko limene Mulungu anayambitsa pamene analenga Adamu ndi Hava. Dziko limenelo ‘linali labwino,’ chifukwa linali lopanda uchimo ndiponso zoipa zilizonse. (Genesis 1:31) Motero silimafunikira kuti ‘liwomboledwe’ kuuchimo.—Aefeso 1:7.
Dziko limene Paulo ankanena apa ndi dziko limene linadzakhalapo Adamu ndi Hava ataukira Mulungu mu Edene ndipo limeneli ndi dziko losiyana kwambiri ndi dziko limene Mulungu ankafuna pachiyambi. Ndi dziko limene linayamba ana a Adamu ndi Hava atabadwa. Dziko limenelo ndi dziko la anthu amene anatalikirana kwambiri ndi Mulungu omwenso ali akapolo a uchimo ndi zoipa. Ndi dziko la anthu osachimwa mwadala monga Adamu ndi Hava chifukwa iwowa angathe kuwomboledwa.—Aroma 5:12; 8:18-21.
Yehova Mulungu anapezeratu njira yokonzera vuto limene linabuka chifukwa cha anthu awiri amene anaukira mu Edene aja. Atangoona kuti pakufunika bungwe lapadera, nthawi yomweyo iye anakonza zoti kudzakhale Ufumu wa Mesiya ndipo anauika m’manja mwa Yesu Kristu, komanso anakonza zoti adzagwiritsira ntchito Ufumuwu powombola anthu ku uchimo wa Adamu. (Mateyu 6:10) Mulungu anachita zimenezi “lisanakhazikike dziko lapansi” la anthu otha kuwomboledwa, kutanthauza kuti anachita zimenezi Adamu ndi Hava asanabale ana.
Nthawi zambiri, anthu asanachite zinazake, amafunika kukonzekera bwinobwino zimene akufuna kuchitazo. Chiphunzitso cha chikonzero chimagwirizana ndi mfundo yakuti Mulungu ayenera kuti anakonzeratu mwatsatanetsatane zochitika zonse zokhudza chilengedwe chonse. Roy Weatherford analemba kuti: “Akatswiri ambiri a maphunziro oganiza kwambiri akhala akuona kuti popeza kuti Mulungu ndi Wamphamvuyonse ayenera kuti anakonzeratu zochitika zonse m’chilengedwe.” Kodi Mulungu amafunikiradi kukonzeratu chilichonse chimene chidzachitike m’tsogolo?
Pakuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire ndiponso nzeru zosaneneka, iye angathe kuthana ndi vuto lililonse kapena chilichonse chimene chingabuke mwadzidzidzi chifukwa cha mmene anthu akugwiritsira ntchito ufulu wawo. (Yesaya 40:25, 26; Aroma 11:33) Iye angathe kuchita zimenezi nthawi yomweyo ndiponso popanda kuchita kukonzekera kaye. Mulungu Wamphamvuyonse sali ngati anthu opanda ungwiro, omwe amalephera kuchita zinthu zina, motero Iye safunika kukonzeratu mwatsatanetsatane zinthu zonse zoti zidzachitikire munthu aliyense padziko pano. (Miyambo 19:21) Choncho, pomasulira lemba la Aefeso 3:11 mabaibulo angapo amati Mulungu ali ndi “chifuniro cha nthawi zonse,” osati chikonzero chosasinthika.
Mmene Mungakonzere Tsogolo Lanu
Mulungu analenga dziko lapansi ndi cholinga, ndipo cholinga chimenechi anachikonza kalekale. Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limati: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Inde, dziko lapansi lino lidzasanduka paradaiso, monga mmene Yehova anafunira pachiyambi. (Genesis 1:27, 28) Komano funso n’lakuti, Kodi inuyo mudzakhalamo m’paradaisomu? Mungadzakhalemo ngati panopo mutamachita zinthu zoyenerera. Yehova sanakonzeretu tsogolo lanu ayi.
Nsembe ya dipo imene Yesu Kristu, mwana wa Mulungu anapereka imathandiza kuti zitheke kuti aliyense womukhulupirira adzalandire moyo wosatha. (Yohane 3:16, 17; Machitidwe 10:34, 35) Baibulo limati: “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo.” (Yohane 3:36) Mungathe kusankha moyo pophunzira m’Baibulo za Mulungu, za Mwana wake, ndi za cholinga Chake komanso potsatira zimene mukuphunzirazo. Munthu aliyense amene amachita zinthu zogwirizanadi ndi nzeru zenizeni zosonyezedwa m’Mawu a Mulungu asakayike n’komwe kuti “adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.”—Miyambo 1:20, 33.
[Zithunzi patsamba 5]
Anthu sali ngati nyama, chifukwa choti zochita zawo zonse n’zoti amachita kuziganizira
[Mawu a Chithunzi]
Eagle: Foto: Cortesía de GREFA