Kodi Inuyo Mumamvera Ndani—Mulungu Kapena Anthu?
“Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—MACHITIDWE 5:29.
1. (a) Kodi ndi lemba lanji limene pachokera nkhani ino? (b) N’chifukwa chiyani atumwi anawagwira?
OWERUZA a khoti lapamwamba la Ayuda ayenera kuti anapsa mtima kwambiri. Akaidi anali atasowa. Ndipo akaidi akewo anali atumwi a Yesu Kristu, munthu amene khoti lalikulu linali litamuweruza kuti aphedwe milungu ingapo m’mbuyomo. Tsopano, khotilo linali litakonzeka kuthana ndi otsatira ake amene iye anali kuwakonda kwambiri. Koma pamene alonda anapita kukawatenga, anapeza kuti m’ndende muja mulibe, ngakhale kuti zitseko zinali zotseka. Sipanapite nthawi, alondawo anamva kuti atumwiwo ali m’kachisi ku Yerusalemu, ndipo akuphunzitsa anthu mopanda mantha za Yesu Kristu. Inde, anali kuchita ntchito yomwe ija imene anawamangirapo! Nthawi yomweyo alonda aja anapita kukachisi, kugwira atumwiwo, n’kuwabweretsa kukhoti.—Machitidwe 5:17-27.
2. Kodi mngelo analamula atumwi kuchita chiyani?
2 Mngelo anali atatulutsa atumwiwo m’ndende. Koma kodi iye anawatulutsa kuti iwo asazunzikenso? Iyayi. M’malo mwake, anafuna kuti anthu a mu Yerusalemu amve uthenga wabwino wa Yesu Kristu. Mngeloyo anauza atumwi kuti ‘akalankhule m’kachisi kwa anthu onse mawu a moyo umenewo.’ (Machitidwe 5:19, 20) Ndipo iwo anatero kumene. N’chifukwa chake pamene alonda a pakachisi anafika kumeneko, anapeza atumwiwo akuchita zimene anauzidwazo, kusonyeza kumvera.
3, 4. (a) Kodi Petro ndi Yohane anayankha kuti chiyani atalamulidwa kusiya kulalikira? (b) Nanga atumwi enawo anayankha kuti chiyani?
3 Mtumwi Petro ndi Yohane, awiri mwa alaliki olimbikira amenewa, anali atalowapo kale m’khotimo. N’chifukwa chake Joseph Kayafa, amene anali woweruza wamkulu, analankhula mwaukali powakumbutsa zimenezo. Iye anati: “Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina [la Yesu]; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu.” (Machitidwe 5:28) Kayafa sanayenere kudabwa ataonanso Petro ndi Yohane m’khotimo chifukwa choti ulendo woyamba umene analamulidwa kuti asiye kulalikira, atumwi awiriwa anayankha kuti: ‘Weruzani, ngati n’kwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu; pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.’ Monga Yeremiya mneneri wakale, Petro ndi Yohane sakanasiya ntchito yolalikira imene analamulidwa kuchita.—Machitidwe 4:18-20; Yeremiya 20:9.
4 Apa, sikuti ndi Petro ndi Yohane okha amene anafunika kunena maganizo awo pa zimene akhotiwo analamula. Atumwi onse, kuphatikizapo Matiya amene anali atangom’sankha kumene, anafunika kutero. (Machitidwe 1:21-26) Atawalamula kusiya kulalikira, iwonso anayankha molimba mtima kuti: ‘Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.’—Machitidwe 5:29.
Kodi Tiyenera Kumvera Mulungu Kapena Munthu?
5, 6. Kodi n’chifukwa chiyani atumwi sanamvere zimene khoti linalamula?
5 Atumwi anali anthu omvera lamulo ndipo sichinali chizolowezi chawo kusamvera zimene akhoti alamula. Ndipo munthu wina aliyense, kaya akhale ndi mphamvu zotani, alibe ufulu wolamula mnzake kuti aphwanye limodzi la malamulo a Mulungu. Yehova ndiye “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Sikuti iye wangokhala “Woweruza wa dziko lonse lapansi” chabe, komanso ndi Wopereka Malamulo Wamkulu, ndiponso Mfumu yosatha. Choncho, ngati khoti lina lililonse likhazikitsa lamulo lotsutsa limodzi la malamulo a Mulungu, lamulo la khotilo siligwira ntchito kwa Mulungu.—Genesis 18:25; Yesaya 33:22.
6 Ndipotu akatswiri ambiri a zamalamulo amaivomereza mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, William Blackstone, amene anali woweruza wotchuka wa ku England zaka za m’ma 1700 analemba kuti n’zosaloleka kuti lamulo la anthu lina lililonse litsutse “lamulo loperekedwa [ndi Mulungu]” limene lili m’Baibulo. Choncho, Sanihedirini inadutsa malire ake pamene inalamula kuti atumwi asiye kulalikira. Atumwiwo sakanayerekeza m’pang’ono pomwe kumvera lamulolo.
7. Kodi n’chifukwa chiyani ntchito yolalikira inawakwiyitsa ansembe aakulu?
7 Atumwi atatsimikiza kuti sasiya kulalikira, ansembe aakulu anakwiya. Ena mwa ansembewo, ndi Kayafa yemwe, anali Asaduki, ndipo sanali kukhulupirira kuti akufa adzauka. (Machitidwe 4:1, 2; 5:17) Koma atumwiwo analimbikira kunena kuti Yesu anauka kwa akufa. Chinanso, ena mwa ansembe aakulu anali atayesetsa kuchita zotheka kuti akuluakulu a Roma awakonde. Atapatsidwa mpata wosankha Yesu kukhala mfumu yawo pozenga mlandu wa Yesuyo, ansembe aakulu anafika mpaka pofuula kuti: “Tilibe Mfumu koma Kaisara.” (Yohane 19:15)a Sikuti atumwiwo anali kungonena motsimikiza kuti Yesu anauka kwa akufa, komanso anali kuphunzitsa kuti kupatulapo dzina la Yesu, “palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 2:36; 4:12) Ansembe anali kuopa kuti ngati anthu ayamba kuyang’ana kwa Yesu amene anauka kwa akufa kukhala Mtsogoleri wawo, ndiye kuti Aroma adzabwera ndipo atsogoleri a Chiyudawo angataye ‘malo awo ndi mtundu wawo.’—Yohane 11:48.
8. Kodi Gamaliyeli anauza bwalo la Sanihedirini uphungu wanzeru woti chiyani?
8 Zinthu zinaoneka ngati siziwayendera bwino atumwi a Yesu Kristu. Oweruza a Sanihedirini anafuna kuti awaphe basi. (Machitidwe 5:33) Koma zinthu zinatembenuka mwadzidzidzi. Gamaliyeli, katswiri pa Chilamulo, anaimirira ndipo anachenjeza anzake kuti asachite zinthu mopupuluma. Iye mwanzeru ananena kuti: “Ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka; koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula.” Kenako, Gamaliyeli anatchula mfundo yofunika kwambiri ndipo anati: “Kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.”—Machitidwe 5:34, 38, 39.
9. Kodi umboni wakuti ntchito ya atumwi inachokera kwa Mulungu n’chiyani?
9 Kenako zimene zinachitika, ndi zinthu zoti aliyense sakanayembekeza. Khotilo linamvera uphungu wa Gamaliyeli. A m’bwalo la Sanihedirini “adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.” Atumwiwo sanachite mantha. M’malo mwake, anatsimikiza mtima kumvera zimene mngelo anawauza kuti alalikire. Ndiye atawamasula, “masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, [atumwiwo] sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.” (Machitidwe 5:40, 42) Yehova anawadalitsa chifukwa cha khama lawo. Motani? “Mawu a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu.” Ndipotu “khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.” (Machitidwe 6:7) Koma ndiye zimenezo zinawasokoneza kwambiri ansembe aakulu aja! Umboni wakuti ntchito ya atumwi inali yochokeradi kwa Mulungu unali kuchulukirachulukira.
Otsutsana ndi Mulungu Sapambana
10. Kutengera maganizo aumunthu, n’chifukwa chiyani Kayafa angakhale ataona ngati kuti zonse zinali kum’yendera bwino ali pa udindo wake, nanga n’chifukwa chiyani analakwitsa kudalira zimenezo?
10 Nthawi ya atumwi, amene anali kusankha akulu a ansembe achiyuda anali akuluakulu a boma la Roma. Amene anasankha Joseph Kayafa wachumayo kukhala mkulu wa ansembe anali Valerius Gratus, ndipo anakhala wansembe zaka zambiri kuposa anzake amene analipo m’mbuyomo. N’kutheka kuti Kayafa anaganiza kuti zimenezi zinatheka chifukwa cha luso lake lodziwa kulankhula ndi anthu ndiponso ubwenzi wake ndi Pilato, osati chifukwa cha Mulungu. Kaya anaganiza zotani, mfundo n’njakuti analakwitsa kudalira anthu. Patangodutsa zaka zitatu kuchokera pamene atumwi anaonekera pamaso pa Sanihedirini, akuluakulu a boma la Roma anasiya kum’konda Kayafa ndipo anam’chotsa pa udindo wake kuti asakhale mkulu wa ansembe.
11. Kodi Pontiyo Pilato ndi dongosolo la Chiyuda zinthu zinawathera bwanji, ndipo mukutipo bwanji pa zimenezi?
11 Amene analamula kuti Kayafa am’chotse pa udindo anali Lucius Vitellius, amene anali ndi mphamvu kuposa Pilato. Ameneyu anali bwanamkubwa wa Suriya. Ngakhale kuti Pilato anali bwenzi la Kayafa lapamtima, sanathe kuletsa zimene zinachitikazo. Ndipotu, patangodutsa chaka kuchokera pamene Kayafa anachotsedwa pa udindo wake, nayenso Pilato anam’chotsa pa udindo wake ndipo anamuitana kuti abwerere ku Roma kukayankha milandu ikuluikulu. Nanga bwanji za atsogoleri a Chiyuda amene anakhulupirira Kaisara? Aroma anawalanda ‘malo awo ndi mtundu wawo’ womwe. Zimenezi zinachitika chaka cha 70 C.E. pamene asilikali a Roma anawonongeratu mzinda wa Yerusalemu, ngakhale kachisi ndi nyumba ya Sanihedirini yomwe. Apatu, mawu a wamasalmo anakwaniritsidwa akuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”—Yohane 11:48; Salmo 146:3.
12. Kodi nkhani ya Yesu ikutsimikiza bwanji kuti kumvera Mulungu ndiyo njira yanzeru?
12 Kusiyana ndi zimene zinawachitikirazo, Mulungu anasankha Yesu Kristu amene anauka kwa akufa kukhala Mkulu wa Ansembe pakachisi wamkulu wauzimu. Palibe munthu amene angasinthe zimenezo. Inde, Yesu “ali nawo unsembe wosasinthika.” (Ahebri 2:9; 7:17, 24; 9:11) Mulungu anasankhanso Yesu kukhala Woweruza amoyo ndi akufa. (1 Petro 4:5) Ndi udindo umenewo, Yesu adzaona ngati Joseph Kayafa ndi Pontiyo Pilato ali ndi mwawi wokhala ndi moyo m’tsogolo.—Mateyu 23:33; Machitidwe 24:15.
Olalikira Ufumu Amakono Opanda Mantha
13. M’nthawi zamakono, kodi ndi ntchito iti imene inachokera kwa anthu, nanga ndi ntchito iti imene inachokera kwa Mulungu? Mwadziwa bwanji zimenezo?
13 Monga masiku a atumwi, masiku anonso pakhala anthu ambiri “otsutsana ndi Mulungu.” (Machitidwe 5:39) Mwachitsanzo, pamene Mboni za Yehova ku Germany zinakana kuvomereza kuti Adolf Hitler ndiye Mtsogoleri wawo, Hitler analumbira kuti athana nazo. (Mateyu 23:10) Chiwembu chambanda chimene iye anakonza chinaoneka ngati kuti a Mboni sangapulumuke. Achipani cha Nazi anatha kugwira Mboni zikwizikwi ndi kuzitumiza ku ndende zawo zozunzirako anthu. Mpaka anapha Mboni zina. Koma achipani cha Naziwo analephera kuthetsa mtima wa Mboni wofuna kupembedza Mulungu yekha, ndipo analephera kuwonongeratu gulu la atumiki a Mulungu limeneli. Ntchito ya Akristu amenewa inachokera kwa Mulungu, osati kwa munthu, ndipo palibe amene angapasule ntchito ya Mulungu. Papita zaka 60 tsopano, ndipo anthu okhulupirika amene anapulumuka kundende za Hitler zozunzirako anthu akutumikirabe Yehova ‘ndi mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi nzeru zawo zonse.’ Koma Hitler ndi chipani chake cha Nazi kulibe, ndipo anthu amangowakumbukira chifukwa cha nkhanza zawo.—Mateyu 22:37.
14. (a) Kodi otsutsa ayesetsa kuchita chiyani pofuna kuipitsa mbiri ya atumiki a Mulungu, ndipo chachitika n’chiyani? (b) Kodi zimenezi zidzapweteka anthu a Mulungu kosatha? (Ahebri 13:5, 6)
14 Kuchokera pamene chipani cha Nazi chinayamba kuvutitsa mpaka pano, enanso ailowa nkhondo imene sangapambane, yolimbana ndi Yehova ndi anthu ake. M’mayiko ambiri ku Ulaya, atsogoleri a zipembedzo ndi andale ongwala amalimbikira kunena kuti Mboni za Yehova ndi kagulu ‘kampatuko koopsa,’ mlandu womwenso anaimba Akristu oyambirira. (Machitidwe 28:22) Zoona zake n’zakuti, khoti la ku Ulaya loona za ufulu wachibadwidwe (European Court of Human Rights) lanena kuti Mboni za Yehova ndi chipembedzo, osati kagulu kampatuko ayi. Otsutsawo akudziwa zimenezi. Koma ngakhale akudziwa, sasiya kuipitsa mbiri ya Mbonizo. Chifukwa chowaipitsira mbiri moteremu, ena mwa Akristu amenewa achotsedwa ntchito. Ana a Mboni akhala akuwavutitsa kusukulu. Eni malo amene Mboni zakhala zikugwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali kuchitirapo misonkhano, athetsa mapangano awowo chifukwa cha mantha. Nthawi zina mpaka mabungwe a boma aletsa anthu ena kuti akhale nzika, chabe chifukwa chakuti anthuwo ndi Mboni za Yehova! Koma Mboni sizileka.
15, 16. Kodi Mboni za Yehova ku France zachita chiyani chifukwa cha ntchito yawo yachikristu imene ena akuitsutsa, ndipo n’chifukwa chiyani sizisiya kulalikira?
15 Mwachitsanzo, anthu ku France n’ngabwino kwambiri. Koma anthu angapo otsutsa alimbikitsa kuti akhazikitse malamulo oletsa ntchito ya Ufumu. Nanga kodi Mboni za Yehova kumeneko zachitapo chiyani? Zachita changu pa ntchito yolalikira, changu chimene sizinachitepo m’mbuyo monsemo, ndipo zotsatira zake zakhala zosangalatsa kwambiri. (Yakobo 4:7) Panthawi ina, m’miyezi isanu ndi umodzi yokha, maphunziro a Baibulo apanyumba anawonjezeka ndi 33 peresenti m’dziko lonselo! Ndiyetu Mdyerekezi ayenera kuti amakwiya akamaona anthu oona mtima ku France akulabadira uthenga wabwino. (Chivumbulutso 12:17) Akristu anzathu ku France ali n’chikhulupiriro chakuti mawu amene mneneri Yesaya ananena adzakwaniritsidwa pa iwo. Iye anati: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa.”—Yesaya 54:17.
16 Mboni za Yehova sizisangalala zikamazunzidwa. Koma pofuna kumvera lamulo la Mulungu kwa Akristu onse, sizingasiye ndipo sizidzasiya kulankhula zinthu zimene zamva. Zimayesetsa kukhala nzika zomvera malamulo. Koma pamene lamulo la Mulungu lisemphana ndi lamulo la anthu, izo zimamvera Mulungu monga wolamulira.
Musawaope
17. (a) N’chifukwa chiyani adani athu sitiyenera kuwaopa? (b) Kodi tiziwaona bwanji anthu amene akutizunza?
17 Adani athu ali poopsa kwambiri. Pajatu akutsutsana ndi Mulungu. Ndiye, mogwirizana ndi lamulo la Yesu, ife timapempherera amene akutizunzawo m’malo mowaopa. (Mateyu 5:44) Timapemphera kuti ngati ena a iwo akutsutsana ndi Mulungu mosadziwa, muja anachitira Saulo wa ku Tariso, Yehova mokoma mtima awatsegule maso kuti azindikire choonadi. (2 Akorinto 4:4) Saulo anakhala Mkristu komanso mtumwi Paulo, ndipo anavutika kwambiri chifukwa cha akuluakulu a boma masiku akewo. Ngakhale anavutika, sanasiye kukumbutsa okhulupirira anzake kuti “agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino; asachitire mwano munthu aliyense [ngakhale anthu amene ankakonda kuwazunza], asakhale andewu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.” (Tito 3:1, 2) Mboni za Yehova ku France ndi kwina kulikonse zikuchita zotheka kutsatira uphungu umenewu.
18. (a) Kodi Yehova angalanditse anthu ake m’njira zotani? (b) Kodi chimene chimachitika n’chiyani potsirizira pake?
18 Mulungu anauza mneneri Yeremiya kuti: “Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe.” (Yeremiya 1:8) Kodi Yehova angatilanditse bwanji ku chizunzo masiku ano? Angaonetsetse kuti pakhala woweruza wosakondera ngati Gamaliyeli. Kapena angaonetsetse kuti, mwadzidzidzi, mkulu wina wa boma amene sachita zinthu mwachilungamo kapena wotsutsa alowedwa m’malo ndi wina wabwino. Koma nthawi zina, Yehova angalole anthu ake kumazunzika. (2 Timoteo 3:12) Ngati Mulungu walola kuti tizunzike, amatipatsa mphamvu kuti tipirire chizunzo. (1 Akorinto 10:13) Ndipo kaya Mulungu alole zotani, tikudziwa zimene zimachitika potsirizira pake: Otsutsana ndi anthu a Mulungu, akutsutsana ndi Mulungu, ndipo otsutsana ndi Mulungu sapambana.
19. Kodi lemba la chaka cha 2006 ndi lemba lanji, ndipo n’loyenera chifukwa chiyani?
19 Yesu anauza ophunzira ake kuti adzakumana ndi mazunzo. (Yohane 16:33) Ndi zimene ananenazo, mawu olembedwa pa Machitidwe 5:29 ndi apanthawi yake kuposa kalelonse. Mawuwo amati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” N’chifukwa chake mawu osangalatsa amenewa asankhidwa kukhala lemba la Mboni za Yehova la chaka cha 2006. Tiyeni, chaka chino mpaka muyaya, titsimikize ndi mtima wonse kumvera Mulungu monga Wolamulira, zivute zitani!
[Mawu a M’munsi]
a “Kaisara” amene ansembe aakulu anavomereza pamaso pa anthu nthawi imeneyo anali Tiberiyo, Mfumu ya Roma imene anthu anaida kwambiri, ndipo iye anali mthira kuwiri ndi wambanda. Tiberiyo anali kudziwikanso monga munthu wokonda zachiwerewere zonyansa.—Danieli 11:15, 21.
Kodi Mungayankhe?
• Kodi atumwi anatiikira chitsanzo cholimbikitsa chotani malinga ndi mmene anachitira ndi chitsutso?
• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Mulungu nthawi zonse monga wolamulira koposa anthu?
• Kodi amene amatsutsana nafe amakhala akutsutsana ndi ndani kwenikweni?
• Kodi amene amapirira chizunzo zidzawathera bwanji?
[Mawu Otsindika patsamba 23]
Lemba la chaka cha 2006 ndi lakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29
[Chithunzi patsamba 19]
“Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu”
[Chithunzi patsamba 21]
M’malo mokhulupirira Mulungu, Kayafa anakhulupirira anthu