Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 2
YESAYA akukwaniritsa mokhulupirika ntchito yake monga mneneri. Uthenga umene analengeza wotsutsa Ufumu wa mafuko khumi a Isiraeli unali utakwaniritsidwa kale. Tsopano ali ndi uthenga wina wokhudza tsogolo la Yerusalemu.
Mzinda wa Yerusalemu udzawonongedwa ndipo anthu okhalamo adzatengedwa ku ukapolo. Koma chiwonongeko chake sichidzakhalitsa. M’kupita kwa nthawi, kulambira koona kudzabwezeretsedwa. Umenewu ndi uthenga waukulu wa Yesaya 36:1–66:24.a Tingapindule mwa kuganizira zimene zalembedwa m’machaputala amenewa chifukwa ulosi wambiri womwe walembedwa m’machaputalawa uli ndi kukwaniritsidwa kwakukulu, kapena kuti komaliza, m’masiku athu ano ndipo wina ukwaniritsidwa kutsogoloku. Ndiponso, chigawo chimenechi cha buku la Yesaya chili ndi ulosi wochititsa chidwi wokhudza Mesiya.
“TAONA, MASIKU AFIKA”
M’chaka cha 14 cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya (732 B.C.E.), Asuri anabwera kudzamenya nkhondo ndi Yuda. Yehova analonjeza kuti adzateteza Yerusalemu. Nkhondoyo inatha pamene mngelo wa Yehova anapha yekha asilikali 185,000 a Asuri.
Hezekiya anadwala. Yehova anayankha pemphero lake n’kumuchiritsa, ndipo anawonjezera zaka 15 pa moyo wake. Pamene mfumu ya Babulo inatumiza nthumwi kuti zikamuone atachira, Hezekiya mosaganiza bwino anazisonyeza chuma chake chonse. Yesaya anauza Hezekiya uthenga wa Yehova ponena kuti: “Taona, masiku afika, kuti zonse za m’nyumba mwako, ndi zimene atate ako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babulo.” (Yesaya 39:5, 6) Ulosi umenewu unakwaniritsidwa patatha zaka 100.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
38:8—Kodi “makwerero” omwe mthunzi unabwererapo anali chiyani? Pofika m’zaka za m’ma 700 B.C.E, anthu a ku Iguputo ndi ku Babulo akafuna kudziwa nthawi ankagwiritsa ntchito chipangizo chinachake chokhala ndi magawo oimira maola. Akafuna kudziwa kuti nthawi ili bwanji, ankayang’ana pamene mthunzi wafika pa magawo a chipangizocho. Choncho, n’zotheka kuti makwererowo akunena za magawo a chipangizocho, chomwe mwina bambo wa Hezekiya, Ahazi, anali nacho. Kapenanso m’nyumba yachifumu mwina munali masitepe ndipo pafupi ndi masitepewo panali chipilala chomwe chinkachititsa mthunzi kukwera pang’onopang’ono pa masitepewo. Akanathanso kugwiritsa ntchito zimenezi kuti adziwe nthawi.
Zimene Tikuphunzirapo:
36:2, 3, 22. Ngakhale kuti Sebina anachotsedwa pa ntchito yake yoyang’anira nyumba, analoledwa kupitiriza kutumikira mfumu monga mlembi wa munthu yemwe analowa ntchito yake yakaleyo. (Yesaya 22:15, 19) Ifeyo tikachotsedwa paudindo m’gulu la Yehova pa chifukwa chinachake, kodi si bwino kuti tipitirizebe kutumikira Mulungu m’njira iliyonse yomwe angalole?
37: 1, 14, 15; 38:1, 2. Tikakhala pa mavuto, n’chinthu chanzeru kupemphera kwa Yehova ndi kum’dalira pa zonse.
37:15-20; 38:2, 3. Pamene Asuri anali kuukira Yerusalemu, nkhawa ya Hezekiya inali pa mmene kuwonongedwa kwa Yerusalemu kudzaipitsira dzina la Yehova. Atadziwa kuti amwalira ndi matenda akewo, Hezekiya anada nkhawa chifukwa cha zinthu zambiri osati chifukwa chongoganizira za iyeyo. Anada nkhawa kwambiri chifukwa chodziwa kuti akamwalira popanda mwana amene angalowe ufumu wake, mzere wa Davide wa mafumu udzasokonekera. Anadanso nkhawa kuti ndani adzatsogolera nkhondo yomenyana ndi Asuri iyeyo akamwalira. Mofanana ndi Hezekiya, timaona kuyeretsa dzina la Yehova ndi kukwaniritsa chifuniro chake monga zinthu zofunika kwambiri kuposa chipulumutso chathu.
38:9-20. Nyimbo ya Hezekiya imeneyi imatiphunzitsa kuti palibe chofunika kwambiri pamoyo kuposa kutamanda Yehova.
“ADZAMANGIDWA”
Atangomaliza kumene kuneneratu kuti Yerusalemu adzawonongedwa ndipo anthu ake adzatengedwa ku ukapolo ku Babulo, Yesaya analoseranso za kubwezeretsedwa kwa kulambira koona. (Yesaya 40:1, 2) Lemba la Yesaya 44:28 limati: “[Yerusalemu] adzamangidwa.” Mafano a milungu ya ku Babulo adzachotsedwa ngati “mtolo.” (Yesaya 46:1) Babulo adzawonongedwa. Zonsezi zinakwaniritsidwa patapita zaka 200.
Yehova adzapereka atumiki ake kuti akhale “kuunika kwa amitundu.” (Yesaya 49:6) “Kumwamba” kwa Babulo, kapena kuti anthu ake olamulira, “kudzachoka ngati utsi,” ndipo anthu okhala m’menemo “adzafa chimodzimodzi”; koma ‘mwana wamkazi wam’nsinga wa Ziyoni adzadzimasulira maunyolo a pakhosi pake.’ (Yesaya 51:6; 52:2) Kwa anthu obwera kwa iye kuti adzamvetsere, Yehova anati: “Ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.” (Yesaya 55:3) Anthu akamakhala moyo wogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna ‘amakondwa mwa Yehova.’ (Yesaya 58:14) Koma zoipa za anthu ‘zimawalekanitsa ndi Mulungu wawo.’—Yesaya 59:2.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
40:27, 28—Kodi Aisiraeli ananeneranji kuti: “Njira yanga yabisika kwa Yehova; ndipo chiweruzo cha Mulungu wanga chandipitirira”? Ayuda ena ku Babulo mwina ankamva kuti zinthu zopanda chilungamo zimene anali kupirira zinali zobisika kwa Yehova kapena zosaoneka kwa iye. Anakumbutsidwa kuti Mlengi wa dziko lapansi, yemwe salefuka kapena kulema, sangalephere kuwafikira ku Babulo.
43:18-21—Kodi anthu obwerera kwawo anauzidwa kuti ‘asakumbukire zinthu zakale’ chifukwa chiyani? Zimenezi sizinatanthauze kuti aiwale zimene Yehova anachita m’mbuyo populumutsa anthu ake ayi. Koma Yehova anafuna kuti iwowo am’tamande chifukwa cha “chinthu chatsopano” chomwe chidzawachitikira iwowo, monga ngati kuyenda bwinobwino pa ulendo wawo wobwerera ku Yerusalemu, mwinamwake kudzera njira yachidule ya m’chipululu. Anthu a “khamu lalikulu” limene lidzatuluka “m’chisautso chachikulu” aliyense payekha adzakhalanso ndi zifukwa zatsopano zotamandira Yehova.—Chivumbulutso 7:9, 14.
49:6—Kodi Mesiya ndi “kuunika kwa amitundu” m’njira yotani popeza anangochita utumiki wake padziko lapansi kwa ana a Isiraeli? Zimenezi zili choncho chifukwa cha zimene zinachitika Yesu ataphedwa. Baibulo limasonyeza kuti lemba la Yesaya 49:6 likunena za ophunzira a Yesu. (Machitidwe 13:46, 47) Masiku ano, Akhristu odzozedwa, omwe amathandizidwa ndi khamu lalikulu la anthu opembedza, amatumikira monga “kuunika kwa amitundu,” pamene akuunikira anthu “ku malekezero a dziko lapansi.”—Mateyo 24:14; 28:19, 20.
53:10—Kodi kunakomera motani Yehova kum’tundudza Mwana wake? Ziyenera kuti zinapweteka kwambiri Yehova, Mulungu wachikondi ndi wachifundo, kuona Mwana wake wokondedwa akuzunzidwa. Ngakhale zinali choncho, zinamukomera Yehova kuti Yesu anamvera modzipereka ndiponso zinthu zimene imfa ndi kuzunzidwa kwake zidzakwaniritsa zinamukomera.—Miyambo 27:11; Yesaya 63:9.
53:11—Kodi Mesiya “adzalungamitsa ambiri” ndi nzeru zotani? Nzeruzi ndi zimene Yesu anapeza mwa kubwera ku dziko lapansi, kukhala munthu, ndi kuzunzika mosalungama mpaka kuphedwa. (Aheberi 4:15) Mwa kuchita zimenezi, anapereka nsembe ya dipo yomwe inathandiza Akhristu odzozedwa ndi a khamu lalikulu kuti akhale olungama pamaso pa Mulungu.—Aroma 5:19; Yakobe 2:23, 25.
56:6—Kodi ‘alendo’ ndani ndipo ‘agwira zolimba chipangano cha Yehova’ m’njira yotani? ‘Alendo’ ndiwo “nkhosa zina” za Yesu. (Yohane 10:16) Agwira zolimba chipangano chatsopano mwa kumvera malamulo okhudza chipanganocho, kuchita mogwirizana ndi zonse zimene zakonzedwa kudzera m’chipanganocho, kudya chakudya chauzimu chofanana ndi Akhristu odzozedwa, ndi kuwathandiza m’ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira.
Zimene Tikuphunzirapo:
40:10-14, 26, 28. Yehova ndi wanyonga ndi wofatsa, wamphamvu yonse ndi wanzeru zonse, ndipo amatha kumvetsa zinthu kuposa mmene tingaganizire.
40:17, 23; 41:29; 44:9; 59:4. Mapangano andale ndi mafano ndi “opanda pake.” Kuwadalira n’kwachabe.
42:18, 19; 43:8. Tikatseka maso athu ku Mawu olembedwa a Mulungu ndipo tikatseka makutu athu ku malangizo ake ochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” timakhala akhungu ndi agonthi mwauzimu.—Mateyo 24:45.
43:25. Yehova amafafaniza zolakwa chifukwa cha dzina lake. Kumasulidwa kwathu ku ukapolo wa uchimo ndi imfa ndi kupulumuka kwathu si kofunika kwambiri poyerekezera ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova.
44:8. Tikuchirikizidwa ndi Yehova yemwe ali wokhazikika ndi wolimba ngati thanthwe. Tisaope n’komwe kupereka umboni woti iyeyo ndiye Mulungu.—2 Samueli 22:31, 32.
44:18-20. Kulambira mafano kumasonyeza kuti mtima wathu waipitsidwa. Palibe chimene chiyenera kutenga malo a Yehova m’mtima mwathu.
46:10, 11. Popeza Yehova angapangitse ‘uphungu wake kukhala,’ kapena kuti angakwaniritse cholinga chake, ndi umboni woonekeratu woti iye ndi Mulungu.
48:17, 18; 57:19-21. Tikayang’ana kwa Yehova kuti atipulumutse, kuyandikira kwa iye, ndi kumvera malamulo ake, tidzakhala ndi mtendere wochuluka kwambiri ngati madzi a mu mtsinje woyenda ndipo zochita zathu zolungama zidzakhala zochuluka ngati mafunde a nyanja. Anthu omwe amanyalanyaza Mawu a Mulungu ali ngati “nyanja yowinduka.” Alibe mtendere.
52:5, 6. Ababulo anaganiza molakwika kuti Mulungu woona n’ngofooka. Sanazindikire kuti Aisiraeli anali mu ukapolo chifukwa choti Yehova anawakwiyira. Mavuto akagwera anthu ena, n’chinthu chanzeru kusafulumira kuganiza kuti tikudziwa zimene zachititsa mavutowo.
52:7-9; 55:12, 13. Tili ndi zifukwa zosachepera zitatu zolalikirira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. Mapazi athu amakhala okongola kwa anthu odzichepetsa omwe ali ndi njala ya zinthu zauzimu. Timaona Yehova “maso ndi maso,” kapena kuti tili pa ubwenzi wabwino ndi iye. Timasangalalanso ndi zinthu zauzimu zochuluka.
52:11, 12. Kuti tikhale oyenerera kunyamula “zotengera za Yehova,” kapena kuti zinthu zokhudza utumiki wopatulika zomwe wakonza, tiyenera kukhala oyera mwauzimu ndi a makhalidwe abwino.
58:1-14. Kuchita zinthu mwachinyengo pofuna kuoneka wodzipereka kapena wolungama n’kopanda pake. Olambira enieni ayenera kuchita moona mtima zinthu zambiri zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu ndi chikondi chaubale.—Yohane 13:35; 2 Petulo 3:11.
59:15b-19. Yehova amayang’ana zochita za anthu ndipo adzachitapo kanthu pa nthawi yake.
ADZAKHALA “KORONA WOKONGOLA”
Ponena za kubwezeretsedwa kwa kulambira koona m’nthawi zakale ndiponso m’masiku athu, lemba la Yesaya 60:1 limati: “Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira.” Ziyoni ‘adzakhalanso korona wokongola m’dzanja la Yehova.’—Yesaya 62:3.
Yesaya anapemphera kwa Yehova za anthu a m’dziko lake omwe adzalape akadzakhala ku ukapolo ku Babulo. (Yesaya 63:15–64:12) Atayerekezera atumiki oona ndi onyenga, mneneriyo analengeza mmene Yehova adzadalitsire anthu om’tumikira.—Yesaya 65:1–66:24.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
61:8, 9—Kodi “pangano losatha” n’chiyani ndipo “ana” ndani? Panganoli ndi chipangano chatsopano chomwe Yehova wapangana ndi Akhristu odzozedwa. “Ana” ndiwo “nkhosa zina” zomwe zimamvera uthenga wa Akhristu odzozedwawo.—Yohane 10:16.
63:5—Kodi ukali wa Mulungu umamuchirikiza bwanji? Ukali umenewu Mulungu amaulamulira ndipo ndi mkwiyo wake wolungama. Ukali wakewo umamuthandiza ndi kumulimbikitsa kupereka ziweruzo zake.
Zimene Tikuphunzirapo:
64:6. Anthu opanda ungwiro sangathe kudzipulumutsa. Pa nkhani ya kuphimba machimo, zochita zawo zolungama zimakhala ngati zovala zodetsedwa basi.—Aroma 3:23, 24.
65:13, 14. Yehova amadalitsa atumiki ake okhulupirika mwa kuwakhutiritsa kwambiri mwauzimu.
66:3-5. Yehova amadana ndi chinyengo.
“Khalani Inu Okondwa”
Maulosi okhudza kubwezeretsa kulambira koona ayenera kuti analimbikitsadi Ayuda okhulupirika omwe anali mu ukapolo ku Babulo. Yehova anati: “Khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa.”—Yesaya 65:18.
Ifenso tikukhala m’nthawi imene mdima ukuphimba dziko lapansi ndipo anthu a mitundu yonse ali mu mdima waukulu. (Yesaya 60:2) Tili mu “nthawi yovuta yoikika.” (2 Timoteyo 3:1) Choncho, uthenga wa Yehova wa chipulumutso womwe uli m’buku la m’Baibulo la Yesaya ndi wolimbikitsa kwambiri kwa ife.—Aheberi 4:12.
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani ya “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 1” yofotokoza Yesaya 1:1–35:10 ikupezeka mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2006.
[Chithunzi patsamba 8]
Kodi mukudziwa chifukwa chachikulu chomwe Hezekiya anapempherera kuti apulumutsidwe kwa Asuri?
[Chithunzi patsamba 11]
“Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino”