Kodi Mungaphunzire Chiyani kwa Ana?
“UKUNGOCHITA zinthu ngati mwana!” Ngati munthu wina atatilankhula choncho, mosakayikira tingakhumudwe kwambiri. Ngakhale kuti ana aang’ono amakhala osangalatsa kuwaona, iwo amakhala osakhwima maganizo, osadziwa zambiri, ndiponso a nzeru zachibwana.—Yobu 12:12.
Komabe, panthawi ina Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Mukapanda kutembenuka ndi kukhala ngati ana aang’ono, simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba.” (Mateyo 18:3) Kodi Yesu ankatanthauzanji? Ndi makhalidwe otani omwe ana aang’ono ali nawo amene akuluakulu ayenera kutsanzira?
Khalani Odzichepetsa Ngati Ana
Taganizani zimene zinachititsa kuti Yesu anene mawu amenewo. Atayenda ulendo wautali n’kufika ku Kaperenao, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Munali kukangana chiyani m’njira?” Ophunzirawo anachita manyazi n’kukhala chete, chifukwa ankakangana zoti ndani anali wamkulu pakati pawo. Kenako, analimba mtima n’kumufunsa Yesu kuti: “Ndani kwenikweni amene adzakhala wamkulu koposa mu ufumu wa kumwamba?”—Maliko 9:33, 34; Mateyo 18:1.
N’zodabwitsa kuti pambuyo pokhala ndi Yesu kwa zaka pafupifupi zitatu, ophunzirawo anali kukanganiranabe udindo. Koma chifukwa chake n’choti, iwo anakulira mu chipembedzo chachiyuda chomwe chinkalimbikitsa kwambiri nkhani zoterezi. Mosakayikira, zimene anaphunzitsidwa ndi chipembedzo chimenecho kuphatikizapo kupanda ungwiro, ndi zimene zinachititsa kuti ophunzirawo akhale ndi maganizo amenewo.
Yesu anakhala pansi ndipo anaitana ophunzirawo, n’kunena kuti: “Ngati aliyense akufuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza pa onse, ndi mtumiki wa onse.” (Maliko 9:35) Mosakayikira mawu amenewa anawadabwitsa chifukwa maganizo a Yesu anali osiyana kwambiri ndi mfundo zachiyuda pa nkhani ya ukulu. Kenako Yesu anaitana kamwana n’kukaika pambali pake. Atakakupatira mwachikondi, ananena motsindika mfundo yake yakuti: “Ndithu ndikukuuzani, Mukapanda kutembenuka ndi kukhala ngati ana aang’ono, simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba. Chotero, aliyense amene adzichepetsa ngati mwana wamng’ono uyu ndi amene adzakhala wamkulu koposa mu ufumu wa kumwamba.”—Mateyo 18:3, 4.
Anawapatsadi phunziro labwino kwambiri pa nkhani ya kudzichepetsa. M’maganizo mwanu, tayerekezerani zimene zinachitika. Gulu la anthu akuluakulu omwe anali chetechete, linazungulira kamwana kamodzi kakang’ono, maso awo ali dwi pa kamwanako. Kamwanako kayenera kuti kanali kololera ndiponso kokhulupirira ena. Kanalinso kopanda kupikisana ndi dumbo, kogonjera, ndiponso kosadzikuza. Zoonadi, kamwana kameneko kanasonyeza bwino kwambiri khalidwe la Mulungu la kudzichepetsa.
Mfundo ya Yesu ndi yomveka bwino. Kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu, tonsefe tiyenera kudzichepetsa ngati mmene amachitira ana. M’gulu la Yehova, lomwe lili ngati banja, n’zosaloleka kuti munthu akhale wampikisano ndiponso wonyada. (Agalatiya 5:26) Ndipotu, makhalidwe amenewa ndi amene anachititsa Satana Mdyerekezi kuukira Mulungu. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yehova amadana nawo.—Miyambo 8:13.
Akhristu oona amafuna kutumikira, osati kulamulira. Kaya ntchitoyo ikhale yosasangalatsa kapena munthu amene tikumutumikirayo akhale wonyozeka, mtima wodzichepetsadi umatichititsa kutumikira ena. Kutumikira modzichepetsa koteroko kumabweretsa madalitso ambiri. Yesu anati: “Aliyense wolandira mmodzi wa ana aang’ono oterewa m’dzina langa, walandira ine; ndipo aliyense wolandira ine, salandira ine ndekha, komanso iye amene anandituma ine.” (Maliko 9:37) Kukhala ndi mtima wopatsa, wodzichepetsa, ndiponso wangati wa ana, kumatigwirizanitsa ndi Munthu wamkulu zedi m’chilengedwe chonse ndiponso Mwana wake. (Yohane 17:20, 21; 1 Petulo 5:5) Ndipo tidzapeza chimwemwe chimene chimadza chifukwa chopatsa. (Machitidwe 20:35) Ndipo timasangalala podziwa kuti tikuthandiza nawo kudzetsa mtendere ndi mgwirizano womwe uli pakati pa anthu a Mulungu.—Aefeso 4:1-3.
Ophunzitsika Ndiponso Okhulupirira Ena
Kenako Yesu anatchulanso mfundo ina yomwe akuluakulu angaphunzire kwa ana: “Aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowa konse mu ufumuwo.” (Maliko 10:15) Kuwonjezera pa kudzichepetsa, ana ndi ophunzitsika. Mayi wina anati: “Ana amayamwa zimene amva monga mmene imachitira siponji.”
Choncho, kuti tidzalowe mu Ufumu wa Mulungu, tiyenera kulandira ndi kumvera uthenga wa Ufumu. (1 Atesalonika 2:13) Monga makanda amene angobadwa kumene, tiyenera kulakalaka ‘mkaka wosasukuluka wa mawu, kuti mwa kumwa mkakawo, tikule ndi kukhala oyenera chipulumutso.’ (1 Petulo 2:2) Nanga bwanji ngati mfundo inayake imene Baibulo limaphunzitsa ikuoneka yovuta kumvetsa? Mayi wina yemwe amagwira ntchito yosamalira ana anati: “Ana amafunsabe kuti ‘N’chifukwa chiyani?’ mpaka atapeza mayankho ogwira mtima a mafunso awo.” Tingachite bwino kutsatira chitsanzo chawo. Choncho pitirizani kuphunzira. Lankhulani ndi Akhristu okhwima mwauzimu, ndipo pemphani nzeru kwa Yehova. (Yakobe 1:5) Mosakayikira, kupemphera kwanu mwakhama kudzafupidwa m’kupita kwa nthawi.—Mateyo 7:7-11.
Komabe, ena angafunse kuti, ‘Kodi anthu osavuta kuwaphunzitsa sangasocheretsedwe mosavuta?’ Sangasocheretsedwe ngati amene akuwatsogolera ali wodalirika. Mwachitsanzo, ana mwachibadwa amadalira makolo awo kuti awatsogolere. Tate wina anati: “Makolo amasonyezadi kuti ndi odalirika mwa kuteteza ndiponso kupezera ana awo zosowa za tsiku ndi tsiku.” Ndithudi, tili ndi zifukwa zofanana ndi zimenezi zokhulupirira Atate wathu wakumwamba, Yehova. (Yakobe 1:17; 1 Yohane 4:9, 10) Yehova mosalephera amatitsogolera kupyolera m’Mawu ake olembedwa. Amatitonthoza ndiponso kutithandiza kupyolera mwa mzimu woyera ndiponso gulu lake. (Mateyo 24:45-47; Yohane 14:26) Tikamagwiritsa ntchito zinthu zimenezi tidzapewa kuvulala mwauzimu.—Salmo 91:1-16.
Kudalira Mulungu ngati ana kumatipatsanso ufulu wa m’maganizo. Katswiri wina wa Baibulo anati: “Tikakhala ana, timangonyamuka ulendo tilibe ndalama yolipirira, ndiponso popanda kudziwa kuti tikafika bwanji kumene tikupitako, koma sitikayika ngakhale pang’ono kuti makolo athu akatifikitsa bwinobwino kumeneko.” Kodi tili ndi chikhulupiriro ngati chimenechi mwa Yehova pamene tikuyenda pamoyo wathu?—Yesaya 41:10.
Tikamakhulupirira Mulungu ndi mtima wonse, zimatithandiza kupewa maganizo ndi zochita zomwe zingawononge moyo wathu wauzimu. M’malo mwake timakhulupirira mawu a Yesu onena kuti Atate wathu wakumwamba amadziwa zochita zathu ndipo ngati tifunafuna choyamba Ufumu ndi chilungamo cha Mulungu, Mulungu adzatisamalira. Zimenezi zidzatithandiza kupewa kuda nkhawa kwambiri ndi zinthu zakuthupi n’kunyalanyaza maudindo athu auzimu.—Mateyo 6:19-34.
“Tiana pa Zoipa”
Ngakhale kuti ana amabadwa opanda ungwiro, amakhala ndi maganizo ndi mtima wabwino. Pachifukwa chimenechi, Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti: “Khalani tiana pa zoipa.”—1 Akorinto 14:20.
Taganizani za Monique wa zaka zisanu, amene mwachimwemwe anauza amayi ake kuti: “Mnzanga watsopano, Sara, ali ndi tsitsi lopiringizana ngati langa!” Sanatchule zoti iyeyo ndi Sara ndi osiyana khungu ndiponso fuko. Kholo lina linati: “Ana ang’onoang’ono satha kusiyanitsa mtundu. Sasankhana mafuko.” Pankhani imeneyi, ana amaonetsa bwino maganizo a Mulungu wathu wopanda tsankho, amene amakonda anthu a mitundu yonse.—Machitidwe 10:34, 35.
Ana ndi odabwitsanso pa nkhani yokhululukirana. Kholo lina linati: “Jack ndi Levi akamenyana, timawauza kuti apepesane, ndipo posakhalitsa amayambanso kusewera limodzi. Akafuna kukhululuka saganizira zomwe zinachitikazo, kukumbutsa zakale kapena kukakamira kuti wina agonje. Amangoiwala n’kupitiriza kusewera.” Chimenechi ndi chitsanzo chabwino zedi kwa akuluakulu.—Akolose 3:13.
Kuwonjezera pamenepo, ana ang’onoang’ono amavomereza mwamsanga zoti kuli Mulungu. (Aheberi 11:6) Khalidwe lawo lolankhula zinthu moona mtima nthawi zambiri limawapangitsa kuchitira umboni molimba mtima kwa ena. (2 Mafumu 5:2, 3) Mapemphero awo achidule, ndiponso ochokera pansi pamtima akhoza kukhudza mtima ngakhale anthu ouma mtima kwambiri. Ndipo akamayesedwa, ana amatha kutsatirabe makhalidwe abwino. Inde, ana ndi mphatsodi zamtengo wapatali.—Salmo 127:3, 4.
Kukongola Kungabwezeretsedwe
Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi n’zotheka kuti anthu akuluakulu akhalenso ndi makhalidwe abwino amene anali nawo ali ana?’ Yankho lachidule ndiponso lotsimikiza ndi loti, inde! Ndipotu, lamulo la Yesu lakuti ‘tikhale ngati ana aang’ono’ limatitsimikizira kuti n’zotheka.—Mateyo 18:3.
Tiyerekezere motere: Gulu lokonza zithunzi zowonongeka lingakhale ndi ntchito yokonza chithunzi chamtengo wapatali. Pogwira ntchitoyo, lingachotse zinthu zonse zosafunikira, n’kukozanso mwina ndi mwina momwe simunakonzedwe bwino poyamba. Litatha kugwira ntchitoyo mwakhama ndiponso modekha, mitundu yosiyanasiyana ya chithunzi chija ingayambirenso kuwala bwino ndipo aliyense angathe kuona kukongola kwake kwakale. Mofanana ndi zimenezo, ngati tichita khama, ngati tithandizidwa ndi mzimu woyera wa Yehova, ndiponso ngati tithandizidwa mwachikondi ndi mpingo wachikhristu, tingathe kukhalanso ndi makhalidwe abwino amene tinali nawo tili ana.—Aefeso 5:1.
[Chithunzi patsamba 9]
Mwachibadwa ana amakhala odzichepetsa
[Chithunzi patsamba 10]
Ana aang’ono sakhala ndi tsankho ndipo amakhululuka ndi kuiwala mosavuta