Oyenerera Kutsogoleredwa ku Akasupe a Madzi a Moyo
“Mwanawankhosa . . . adzawaweta ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.”—CHIV. 7:17.
1. Kodi Mawu a Mulungu amati Akhristu odzozedwa ndani, ndipo Yesu anawapatsa udindo wotani?
MAWU A MULUNGU amati Akhristu odzozedwa amene akusamalira zinthu za Khristu padziko lapansi pano ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Khristu atayendera “kapolo” ameneyo mu 1918, anapeza odzozedwawo padziko lapansi ali okhulupirika popereka ‘chakudya chauzimu panthawi yoyenera.’ N’chifukwa chake pambuyo pake Yesu, Mbuye wawo, anawaika ndi mtima wonse kukhala ‘oyang’anira zinthu zake zonse.’ (Werengani Mateyo 24:45-47.) Choncho, odzozedwawo asanalandire cholowa chawo cha kumwamba, amatumikira anthu olambira Yehova pano padziko lapansi.
2. Kodi zinthu za Yesu ndi chiyani?
2 Mbuye amakhala ndi mphamvu pa zinthu zake kapena chuma chake, ndipo amazigwiritsa ntchito mmene akufunira. Zinthu za Yesu Khristu, Mfumu yoikidwa ndi Yehova, ndi zinthu zonse za Ufumu padziko lapansi. Zimenezo zikuphatikizapo “khamu lalikulu” limene mtumwi Yohane anaona m’masomphenya. Pofotokoza khamu lalikululo, Yohane anati: “Ndinaona khamu lalikulu limene munthu sanathe kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse, fuko, mtundu, ndi lilime lililonse, ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera, nthambi za kanjedza zili m’manja mwawo.”—Chiv. 7:9.
3, 4. N’chifukwa chiyani a khamu lalikulu ali ndi mwayi waukulu?
3 Anthu a khamu lalikulu ali m’gulu la anthu amene Yesu anawatchula kuti “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Iwo ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Ali ndi chikhulupiriro chonse kuti Yesu ‘adzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo.’ Chifukwa cha chiyembekezo chimenechi, iwo“achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:14, 17) Iwo amakhulupirira nsembe ya Yesu ndipo n’chifukwa chake Mulungu amawaona kuti ‘ayeretsa mikanjo’ yawo. Amayesedwa olungama monga mabwenzi a Mulungu mofanana ndi Abulahamu.
4 Ndiponso a khamu lalikulu akuyembekeza kudzapulumuka pamene dongosolo lino la zinthu lidzawonongedwa pa chisautso chachikulu chifukwa chakuti Mulungu amawaona kuti ndi olungama. (Yak. 2:23-26) Iwo amayandikira Yehova, ndipo monga gulu, ali ndi chiyembekezo chosangalatsa chopulumuka Aramagedo. (Yak. 4:8; Chiv. 7:15) Sachita zinthu paokha koma modzipereka amatumikira motsogoleredwa ndi Mfumu ya kumwamba limodzi ndi abale ake odzozedwa amene ali pa dziko lapansi.
5. Kodi a khamu lalikulu akuthandiza bwanji abale odzozedwa a Khristu?
5 Akhristu odzozedwa akhala akutsutsidwa koopsa ndi dziko la Satana ndipo zimenezi zipitirirabe. Ngakhale zili choncho, iwo amadalira thandizo la anzawo a khamu lalikulu. Pamene chiwerengero cha Akhristu odzozedwa chili chochepa tsopano, khamu lalikulu likuwonjezeka ndi anthu zikwizikwi chaka chilichonse. Odzozedwa sangakwanitse kukhala mu uliwonse wa mipingo yachikhristu yokwanira pafupifupi 100,000 padziko lonse lapansi ndi kuuyang’anira. Motero, thandizo lina limene odzozedwa amalandira kwa nkhosa zina ndi lakuti amuna oyenerera a khamu lalikulu ndi akulu mumpingo. Akulu amenewa amathandiza kusamalira Akhristu mamiliyoni amene anawaikiza m’manja mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”
6. Kodi ulosi unati chiyani za thandizo limene a nkhosa zina amapereka kwa Akhristu odzozedwa?
6 Mneneri Yesaya analosera kuti Akhristu odzozedwa adzathandizidwa ndi anzawo a nkhosa zina amene adzadzipereka ndi mtima wonse. Iye analemba kuti: “Atero Yehova, ntchito ya [antchito yosalipidwa a, NW] Aigupto, ndi malonda a Kusi, ndi a Sabea, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo.” (Yes. 45:14) Mophiphiritsa, Akhristu amene chiyembekezo chawo ndi chokhala padziko lapansi, masiku ano akutsatira pambuyo pa gulu la kapolo la odzozedwa ndi Bungwe Lolamulira la kapoloyo. Zimenezi zikutanthauza kuti amatsatira utsogoleri wawo. Monga “antchito yosalipidwa,” a nkhosa zina amadzipereka ndi mtima wonse kugwiritsa ntchito mphamvu ndi chuma chawo kuti achirikize ntchito yolalikira padziko lonse lapansi imene Khristu anapatsa otsatira ake odzozedwa.—Mac. 1:8; Chiv. 12:17.
7. Kodi a khamu lalikulu akuphunzitsidwa pokonzekera chiyani?
7 Pothandiza abale awo odzozedwa, akhamu lalikulu akuphunzitsidwa monga maziko a mtundu watsopano wa anthu umene udzakhalapo pambuyo pa Aramagedo. Maziko amenewo ndi olimba, ndipo anthu ake afunika kutsatira ndi mtima wonse malangizo a Mbuye wawo. Mkhristu aliyense akupatsidwa mpata wosonyeza kuti Mfumu Khristu Yesu, akhoza kumugwiritsa ntchito. Mwa kusonyeza chikhulupiriro ndi kukhala wokhulupirika panopa, iye amasonyeza kuti adzalabadira mosavuta Mfumu ikamamupatsa malangizo m’dziko latsopano.
Khamu Lalikulu Likusonyeza Chikhulupiriro Chawo
8, 9. Kodi a khamu lalikulu akusonyeza chikhulupiriro chawo m’njira zotani?
8 A nkhosa zina omwe ndi anzawo a mpingo wa Akhristu odzozedwa amasonyeza kukhulupirika kwawo m’njira zosiyanasiyana. Choyamba, iwo amathandiza odzozedwa polengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Chachiwiri, iwo amagonjera ndi mtima wonse malangizo operekedwa ndi Bungwe Lolamulira.—Aheb. 13:17; werengani Zekariya 8:23.
9 Chachitatu, a khamu lalikulu amathandiza abale awo odzozedwa mwa kutsatira mfundo zolungama za Yehova. Amayesetsa kukhala ndi makhalidwe monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa, kudziletsa.” (Agal. 5:22, 23) Masiku ano, anthu ambiri amakonda “ntchito zathupi” m’malo mokhala ndi makhalidwe amenewa. Ngakhale zili choncho, a khamu lalikulu amayesetsa kupewa “dama, chonyansa, khalidwe lotayirira, kupembedza mafano, kukhulupirira mizimu, maudani, ndewu, nsanje, kumapsa mtima, mikangano, magawano, magulu a mpatuko, kaduka, kumamwa mwauchidakwa, maphwando aphokoso, ndi zina zotero.”—Agal. 5:19-21.
10. Kodi a khamu lalikulu amayesetsa kuchita chiyani?
10 Popeza ndife opanda ungwiro, zingakhale zovuta kuti tikhale ndi zipatso za mzimu, tipewe ntchito zathupi, ndiponso kuti tilimbane ndi mavuto a m’dziko la Satanali. Komabe, timayesetsa kupewa kugwa ulesi chifukwa cha kufooka kwathu, zophophonya zathu, kapena matenda ndi ukalamba. Sitifuna kuti zimenezi ziwononge chikhulupiriro chathu ndi chikondi chathu pa Yehova. Timadziwa kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake lopulumutsa khamu lalikulu pa chisautso chachikulu.
11. Kodi Satana wagwiritsa ntchito njira ziti kuti afooketse chikhulupiriro cha Akhristu?
11 Komabe, timakhala tcheru nthawi zonse chifukwa timadziwa kuti mdani wathu weniweni ndi Mdyerekezi, ndipo satopa. (Werengani 1 Petulo 5:8 ) Iye wayesa kugwiritsa ntchito anthu ampatuko ndi enanso kutikopa kuti tiziona ngati tikuphunzira zinthu zabodza. Koma njira imeneyo yalephera. Ngakhale kuti nthawi zina chizunzo chimasokoneza ntchito yolalikira, nthawi zambiri chimalimbitsa chikhulupiriro cha anthu amene akuzunzidwawo. Choncho, Satana akuyesetsa kwambiri kugwiritsa ntchito njira imene akudziwa kuti singalephere kufooketsa chikhulupiriro chathu. Iye amapezerapo mwayi munthu akalefuka kapena kukhumudwa. Akhristu oyambirira anachenjezedwa za vuto limeneli pamene anauzidwa kuti: “Lingalirani mozama za munthu [Khristu] amene wapirira malankhulidwe onyoza ngati amenewo a ochimwa, amene anadzichimwitsa nawo iwo okha.” Pofotokoza chifukwa chimene anawachenjezera, iye anati: “Kuti musatope, ndi kuti moyo wanu usalefuke.”—Aheb. 12:3.
12. Kodi uphungu wa m’Baibulo umawalimbitsa motani anthu amene alefuka kapena kukhumudwa?
12 Kodi munayamba mwaganizapo zongosiya zimene mukuchita potumikira Yehova? Kodi nthawi zina mumaona kuti ndinu munthu wolephera? Ngati ndi choncho, musalole Satana kupezerapo mwayi wokulepheretsani kutumikira Yehova. Kuphunzira Baibulo mozama, kupemphera mochokera pansi pa mtima, kupezeka pa misonkhano nthawi zonse ndiponso kucheza ndi okhulupirira anzanu, kudzakulimbitsani ndi kukutetezani kuti “moyo wanu usalefuke.” Yehova walonjeza kuthandiza atumiki ake kupezanso mphamvu ndipo lonjezo lakelo ndi lodalirika. (Werengani Yesaya 40:30, 31.) Ikani mtima wanu pautumiki wa Ufumu. Pewani kuchita zinthu zimene zingakudyereni nthawi, ndipo limbikirani kuthandiza ena. Mukatero, mudzakhala ndi mphamvu yopirira ngakhale pamene mwalefuka kapena kukhumudwa.—Agal. 6:1, 2.
Kupulumuka Chisautso ndi Kulowa M’dziko Latsopano
13. Kodi anthu opulumuka Aramagedo adzakhala ndi ntchito yotani?
13 Aramagedo itadutsa, anthu ambirimbiri osalungama amene adzauka, adzafunikira kuphunzitsidwa njira za Yehova. (Mac. 24:15) Adzafunikira kuphunzira za nsembe ya dipo ya Yesu. Komanso adzaphunzitsidwa kukhulupirira nsembeyo kuti apindule nayo. Adzafunikiranso kusiya zikhulupiriro zawo zonse zonyenga zakale zachipembedzo ndi moyo wawo wakale. Adzayenera kuphunzira kuvala umunthu watsopano umene umadziwikitsa Akhristu oona. (Aef. 4:22-24; Akol. 3:9, 10) A nkhosa zina amene adzapulumuka adzakhala ndi ntchito yaikulu. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kugwira ntchito ya Yehova imeneyo popanda mavuto ndi zododometsa zimene zilipo m’dziko loipali.
14, 15. Kodi padzakhala kukambirana zotani pakati pa anthu opulumuka chisautso chachikulu ndi anthu olungama amene adzaukitsidwa?
14 Atumiki okhulupirika a Yehova amene anamwalira Yesu asanayambe utumiki wake wa padziko lapansi, adzaphunziranso zambiri. Adzadziwa kuti Mesiya, amene anali kumuyembekezera mwachidwi koma sanamuone, anali ndani. Ali moyo, iwo anali ndi mtima wofuna kuphunzitsidwa ndi Yehova. Tangoganizani mmene zidzakhalira zosangalatsa kuthandiza anthu amenewo. Mwachitsanzo, tingadzakhale ndi mwayi wofotokozera Danieli mmene maulosi amene iye analemba koma osawamvetsa, anakwaniritsidwira.—Dan. 12:8, 9.
15 Ngakhale kuti anthu oukitsidwa adzaphunzira zinthu zambiri kwa ife, ifenso tidzakhala ndi mafunso ambiri owafunsa. Iwo adzatifotokozera mwatsatanetsatane nkhani zimene Baibulo limafotokoza mwachidule. Taganizani mmene zidzakhalira zosangalatsa kuphunzira za moyo wa Yesu kuchokera kwa m’bale wake Yohane Mbatizi. Mosakayikira zinthu zimene tidzaphunzira kwa mboni zokhulupirika zimenezo, zidzatithandiza kumvetsetsa Mawu a Mulungu kuposa panopa. Atumiki a Yehova okhulupirika amene anamwalira, kuphatikizapo a khamu lalikulu amene akumwalira m’nthawi ino ya mapeto, adzapeza “kuuka kwabwino koposa.” Iwo anayamba kutumikira Yehova m’dziko lolamuliridwa ndi Satana. Koma adzakhala osangalala kwambiri kupitiriza utumiki wawo zinthu zili bwino kwambiri m’dziko latsopano.—Aheb. 11:35; 1 Yoh. 5:19.
16. Malinga ndi ulosi, kodi Tsiku la Chiweruzo lidzayenda bwanji?
16 Nthawi ina pa Tsiku la Chiweruzo, mipukutu idzafunyululidwa. Mipukutu imeneyi, pamodzi ndi Baibulo, idzakhala maziko oweruzira anthu onse amoyo ngati ali oyenerera moyo wosatha. (Werengani Chivumbulutso 20:12, 13.) Tsiku la Chiweruzo likamafika ku mapeto, munthu aliyense adzakhala atapatsidwa mpata wokwanira wosonyeza kuti ali mbali iti pankhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse. Kodi iye adzachirikiza Ufumuwo ndi kulola Mwanawankhosa kumutsogolera ku “akasupe a madzi a moyo”? Kapena kodi adzalimbalimba ndi kukana kugonjera Ufumu wa Mulungu? (Chiv. 7:17; Yes. 65:20) Panthawi imeneyo, anthu onse padziko lapansi adzakhala atapatsidwa mpata wodzisankhira okha, mosasokonezedwa ndi uchimo wobadwa nawo kapena dziko loipa. Palibe amene adzakayikira kuti chiweruzo chomaliza cha Yehova ndi cholungama. Anthu oipa okha ndi amene adzawonongedwa kotheratu.—Chiv. 20:14, 15.
17, 18. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu odzozedwa ndi a nkhosa zina amasangalala akamayembekezera Tsiku la Chiweruzo?
17 Akhristu odzozedwa masiku ano, pokhala oyenerera kulandira Ufumu, amadikira mwachidwi kulamulira Tsiku la Chiweruzo. Iwo adzakhala ndi mwayi waukulu kwambiri. Chiyembekezo chimenechi chimawalimbikitsa kutsatira uphungu umene Petulo anapereka kwa abale awo kalelo, kuti: “Chitani chilichonse chotheka kuti kuitanidwa ndi kusankhidwa kwanu kukhale kotsimikizika mu mtima mwanu; pakuti mukapitiriza kuchita zinthu zimenezi simudzalephera konse. Ndipo mukatero, adzakutsegulirani khomo lonse lolowera mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.”—2 Pet. 1:10, 11.
18 A nkhosa zina amasangalala ndi chiyembekezo cha abale awo odzozedwa. Iwo safuna kusiya kuwathandiza. Popeza kuti iwo ndi mabwenzi a Mulungu, akuyesetsa kuchita chilichonse chotheka potumikira Mulungu. Pa Tsiku la Chiweruzo, adzasangalala kuchirikiza ndi mtima wonse makonzedwe a Mulungu pamene Yesu akuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo. Ndipo pomaliza, adzayenerera kukhala atumiki a Yehova a padziko lapansi kosatha.—Aroma 8:20, 21; Chiv. 21:1-7.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi zinthu za Yesu ndi chiyani?
• Kodi a khamu lalikulu amathandiza bwanji abale awo odzozedwa?
• Kodi a khamu lalikulu amasangalala ndi utumiki ndiponso chiyembekezo chotani?
• Kodi Tsiku la Chiweruzo mumaliona bwanji?
[Chithunzi patsamba 25]
A khamu lalikulu achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa
[Chithunzi patsamba 27]
Kodi inu mukuyembekezera kuphunzira chiyani kwa anthu okhulupirika amene adzaukitsidwa?