Tsanzirani Yesu Lambirani Mulungu Moyenera
Mulungu amaitana anthu mwachikondi ‘ochokera m’dziko lililonse, fuko, mtundu, ndi lilime lililonse’ kuti amulambire. (Chiv. 7:9, 10; 15:3, 4) Anthu amene amamvera zimenezi ‘angapenye kukongola kwake kwa Yehova.’ (Sal. 27:4; 90:17) Mofanana ndi wamasalmo, iwo amatamanda Mulungu mwa kunena kuti: “Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.”—Sal. 95:6.
Kulambira Kumene Mulungu Amasangalala Nako
Monga Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, Yesu anali ndi mwayi wodziwa maganizo, mfundo ndi malamulo a Atate ake. Choncho, Yesu anatha kuuza anthu njira yoyenera yolambirira Mulungu. Iye anati: “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yoh. 1:14; 14:6.
Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino zedi pankhani yodzichepetsa ndi kugonjera Atate ake. Iye anati: “Sindichita kanthu mongoganiza ndekha; koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.” Ndipo anawonjezeranso kuti: “Ndimachita zinthu zom’kondweretsa nthawi zonse.” (Yoh. 8:28, 29) Kodi Yesu anasangalatsa Atate ake motani?
Yesu anali wodzipereka ndi mtima wonse kwa Atate ake, ndipo imeneyi ndi mfundo yofunika kwambiri pankhani yolambira Mulungu. Iye anasonyeza kuti ankakonda kwambiri Atate ake mwa kuwamvera ndi kuchita zofuna zawo, ngakhale nthawi imene zimenezi zinali zovuta kwambiri. (Afil. 2:7, 8) Chinthu chofunika kwambiri chimene Yesu ankachita polambira chinali kugwira ntchito yopanga ophunzira. Ntchitoyi ankaigwira kawirikawiri moti anthu okhulupirira ndi osakhulupirira omwe ankamutchula kuti Mphunzitsi. (Mat. 22:23, 24; Yoh. 3:2) Yesu ankadziperekanso kwambiri pothandiza ena. Mtima umenewu unkapangitsa kuti asakhale ndi nthawi yambiri yochitira zinthu zake, komabe ankasangalala kutumikira ena. (Mat. 14:13, 14; 20:28) Ngakhale kuti ankatanganidwa kwambiri, Yesu nthawi zonse ankapeza nthawi yopemphera kwa Atate ake wakumwamba. (Luka 6:12) Ndithudi, Mulungu ankasangalala kwambiri ndi kulambira kwa Yesu.
Tiziyesetsa Kusangalatsa Mulungu
Yehova anaona khalidwe labwino la Mwana wake ndipo linam’sangalatsa. (Mat. 17:5) Satana Mdyerekezi nayenso anaona kuti Yesu anali wokhulupirika. Choncho Satana anayamba kumulondalonda. Chifukwa chiyani? Chifukwa panalibe munthu amene anamvera Mulungu m’zinthu zonse ndiponso amene anamulambira mu njira imene Iye amafuna ngati mmene Yesu amachitira. Mdyerekezi ankafuna kusiyitsa Yesu kulambira Yehova, yemwe ndi woyenera kulambiridwa.—Chiv. 4:11.
Pofuna kusokoneza Yesu, Satana anamunyengerera ndi chinthu chokopa. Iye anapita ndi Yesu “pa phiri lalitali kwambiri, ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo.” Ndiyeno anamuuza kuti: “Zinthu zonsezi ndikupatsani ngati mugwada pansi ndi kundilambirako ine.” Kodi Yesu anatani? Iye anayankha kuti: “Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo utumiki wako wopatulika uyenera kupita kwa iye yekha basi.” (Mat. 4:8-10) Yesu anadziwa kuti kugwadira Satana n’chimodzimodzi ndi kulambira fano ngakhale kutakhala ndi phindu linalake. Iye sanafune ndi pang’ono pomwe kulambira wina aliyense kupatulapo Yehova.
Masiku ano, Satana sangatilonjeze kuti atipatsa maufumu a dzikoli ndi ulemerero wake pofuna kuti tisiye kulambira Mulungu. Komabe akuyesetsa kusokoneza Akhristu oona polambira Mulungu. Mdyerekezi amangofuna kuti tizilambira munthu winawake kapena chinachake.—2 Akor. 4:4.
Khristu Yesu anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa. Mwa kuchita zimenezi, Yesu analemekeza Yehova kuposa mmene munthu wina aliyense anachitira. Masiku ano, Akhristu oona timayesetsa kutsatira moyo wokhulupirika wa Yesu mwa kuona kulambira Mlengi kukhala kofunika kuposa china chilichonse. Inde, chinthu chofunika kwambiri chimene tili nacho ndi ubwenzi wathu ndi Mulungu.
Madalitso Amene Amabwera Chifukwa Cholambira Mulungu Moyenera
“Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa” pamaso pa Mulungu, kumabweretsa madalitso ambiri. (Yak. 1:27) Mwachitsanzo, tikukhala m’nthawi imene anthu ambiri ndi “odzikonda, okonda ndalama, odzimva” ndiponso “osakonda zabwino.” (2 Tim. 3:1-5) Koma m’nyumba ya Mulungu, tili ndi mwayi wocheza ndi anthu oyera ndiponso abwino amene amayesetsa kutsatira zimene Mulungu amafuna pomulambira. Kodi zimenezi sizolimbikitsa?
Chifukwa chosadetsedwa ndi dzikoli, timakhala ndi chikumbumtima chabwino. Limenelinso ndi dalitso. Timakhalabe ndi chikumbumtima chabwino mwa kutsatira mfundo zolungama za Mulungu ndiponso kumvera malamulo a Kaisara amene satsutsana ndi malamulo a Mulungu.—Maliko 12:17; Mac. 5:27-29.
Kulambira Mulungu ndi mtima wonse kumabweretsanso madalitso ena. Mtima wathu ukakhala pa kuchita zimene Mulungu amafuna osati zofuna zathu, moyo wathu umakhala ndi cholinga komanso umakhala wosangalatsa. M’malo monena kuti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, popeza mawa tifa,” tili ndi chiyembekezo chodalirika chodzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lino lapansi.—1 Akor. 15:32.
Buku la Chivumbulutso limanena kuti anthu amene Yehova amawaona kuti ndi oyera, ‘adzatuluka m’chisautso chachikulu.’ Nkhani imeneyi imanena kuti: “Iye wokhala pampando wachifumuyo adzafunyulula hema wake pa iwo.” (Chiv. 7:13-15) Wokhala pampandoyo ndi Yehova Mulungu, munthu wolemekezeka kwambiri m’chilengedwe chonse. Tangoganizirani mmene mudzasangalalire akadzakulandirani mu hema wake monga mlendo ndi kukutetezani kuti musavulazidwe. Ndipo ngakhale panopo akhoza kutiteteza ndi kutisamalira.
Komanso, anthu onse amene amalambira Mulungu moyenera amanenedwa kuti akutsogoleredwa “ku akasupe a madzi a moyo.” Akasupe otsitsimula amenewa akuimira zinthu zonse zimene Yehova wapereka zotithandiza kupeza moyo wosatha. Ndithudi, kudzera mwa dipo la Khristu, “Mulungu adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo.” (Chiv. 7:17) Anthu adzakhalanso ndi moyo wangwiro. Ndipo zimenezi zidzakhala zosangalatsa kwambiri kwa anthu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo kosatha padziko lino lapansi. Ngakhale panopo, olambira Mulungu amafuula mosangalala, poyamikira Yehova mochokera pansi pamtima. Ndipo iwo amamulambira pamodzi ndi amene ali kumwamba omwe amaimba kuti: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njira zanu ndi zolungama ndi zoona, Mfumu ya muyaya inu. Uyo amene sadzakuopani ndani, inu Yehova, ndani sadzalemekeza dzina lanu? Pakuti inu nokha ndinu wokhulupirika! Pakuti mitundu yonse idzabwera kudzalambira pamaso panu, chifukwa malamulo anu olungama aonekera.”—Chiv. 15:3, 4.
[Chithunzi patsamba 27]
Kodi Satana akutipatsa chiyani pofuna kuti tisiye kulambira Mulungu?