Mmene Ndinadziwira Kuti Mulungu ‘Amachita Zinthu Zazikulu’
Yosimbidwa ndi Maurice Raj
Banja lathu, pamodzi ndi anthu enanso masauzande ambiri ochokera m’mayiko ena, tinathawa kumenyana koopsa kwambiri kumene kunachitika pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Kwa masiku ambiri tinayenda m’nkhalango yowirira kwambiri ya ku Burma ndipo nthawi zambiri tinkagona pansi pamtengo. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 9. Zinthu zanga zonse zinali m’kachikwama komwe ndinabereka kumsana. Koma chimenechi chinali chiyambi chabe cha mavuto.
ZIMENEZI zinachitika mu 1942. Dziko lonse lapansi linali pa nkhondo, ndipo tinali kuthawa asilikali a ku Japan amene anali atangoyamba kumene kumenyana ndi dziko la Burma, limene masiku ano limatchedwa kuti Myanmar. Asilikali amenewa anali atalanda zitsime za mafuta za ku mumzinda wa Yenangyaung. Koma tisanakafike kumalire ndi dziko la India, asilikali a ku Japan aja anatipeza ndipo anatilamula kuti tibwerere.
Ndili mwana, tinkakhala ku Yenangyaung kumene bambo anga ankagwira ntchito pakampani ya mafuta yotchedwa Burmah Oil Company. Asilikali a ku Japan atalanda dziko la Burma, ndege zankhondo za ku Britain zinayamba kuponya mabomba pafupipafupi m’dera la migodi ya mafuta ku Yenangyaung. Nthawi ina, banja lathu linabisala m’dzenje kwa masiku atatu, mabomba akuphulika pena paliponse. Kenako tinathawa pa boti kupita ku Sale, yomwe ndi tauni yaing’ono imene ili m’mphepete mwa mtsinje wa Ayeyarwady, kapena kuti Irrawaddy. Tinasangalala kwambiri kuti tinapulumuka ndipo nkhondo yonse inatha tili kumeneko.
Mavuto Aakulu Anachititsa Kuti Tidziwe Choonadi
Mng’ono wanga anabadwa mu 1945, chaka chimene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inatha. Bambo, amene panthawiyi anali achikulire, anasangalala kwambiri ndi kubadwa kwa mwanayo. Koma chisangalalo chimenechi chinali cha kanthawi kochepa chifukwa mwanayo anamwalira patangotha miyezi itatu. Posakhalitsa nawonso bambo anamwalira chifukwa cha chisoni ndi imfa ya mwanayo.
Pofuna kunditonthoza, anzanga ankandiuza kuti Mulungu anatenga bambo ndi mng’ono wangayo kuti akakhale nawo kumwamba. Inenso ndinkafunitsitsa nditapita kumwambako kuti ndikakhale ndi bambo ndi mng’ono wanga. Banja lathu linali lachikatolika ndipo ndi kumene ndinaphunzira zinthu zambiri zachipembedzo. Anandiphunzitsa kuti ansembe ndiponso masisitere akamwalira amapita kumwamba nthawi yomweyo, koma ena onse amapita kaye ku purigatoliyo kumene amakazunzidwa kwa kanthawi kuti machimo awo ayeretsedwe. Chifukwa chofunitsitsa kukaonananso ndi bambo ndiponso mng’ono wanga, ndinkafunitsitsa kudzalowa seminale ya Akatolika kuti ndidzakhale wansembe. Seminale imeneyi inali mumzinda wa Maymyo, umene masiku ano umatchedwa Pyin Oo Lwin ndipo unali pamtunda wa makilomita 210 kuchokera kumene tinkakhala.
Kuti ulowe seminale imeneyi unkafunika kukhala wophunzira. Koma chifukwa chosamukasamuka ndinali nditangophunzira sukulu zaka ziwiri zokha. Kenako sukulu zinatsekedwa pa nthawi yonse ya nkhondo. Ngakhale kuti nkhondo itatha sukulu anazitsekulanso, sindinathe kupitiriza chifukwa banja lathu linali pa umphawi wadzaoneni. Mayi anga ankalera ineyo, azikulu anga awiri komanso ana atatu amasiye a ang’ono awo. Choncho sakanakwanitsa kutilipirira anyamatafe sukulu.
Mkulu wanga anayamba ntchito koma ineyo ndinali ndi zaka 13 zokha, choncho palibe chimene ndikanachita. Bambo anga aang’ono dzina lawo a Manuel Nathan ankakhala m’tauni ya Chauk yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Sale. Ndinaganiza zochoka panyumba ndi cholinga choti anthu oti aziwadyetsa achepeko. Choncho ndinapita kukakhala ndi bambo anga aang’ono ku Chauk.
Sindinadziwe kuti bambowo anali atayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova ndipo ankafunitsitsa kundiuza zimene anali kuphunzira m’Baibulo. Iwo anayamba kundiphunzitsa Baibulo pang’onopang’ono ndipo anayamba ndi kundifotokozera tanthauzo la pemphero la Atate Wathu Wakumwamba. Pemphero limeneli limayamba ndi mawu akuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”—Mateyu 6:9, 10.
Ndiyeno iwo ananena kuti: “Waona, ndiye kutitu Mulungu ali ndi dzina. Dzina lake ndi Yehova.” Kenako anandionetsa m’Baibulo dzina la Mulungu. Ndinachita chidwi ndi zimenezi ndipo ndinafuna kudziwa zambiri. Koma vuto linali loti sindinkatha kuwerenga bwinobwino ngakhale m’chilankhulo changa cha Chitamiwu. Komanso Baibulo ndi mabuku ophunzitsa Baibulo amene bambo angawo anali nawo anali achingelezi chimenenso sindinkachidziwa bwinobwino. Koma ngakhale kuti ndinali wosaphunzira kwenikweni, pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa. (Mateyu 11:25, 26) Ndinayamba kumvetsa kuti ziphunzitso zambiri zimene ndinaphunzira sizinali zochokera m’Baibulo. Tsiku lina ndinawauza kuti: “Bambo, ichi ndiye choonadi.”
Ndili ndi zaka 16, ndinayamba kuuza anthu ena zimene ndinkaphunzira. Nthawi imeneyo, ku Myanmar kunali Mboni za Yehova 77 zokha basi. Pasanapite nthawi, mmishonale wina wa Mboni za Yehova dzina lake Robert Kirk anabwera ku Chauk kudzachezera bambo anga aang’ono. Mmishonaleyu anali wochokera mumzinda wa Rangoon, umene masiku ano umatchedwa Yangon ndipo unali likulu la dziko la Myanmar. Ndinauza Robert kuti ndinadzipereka kwa Yehova kuti ndimutumikire. Kenako posonyeza kudziperekako ndinabatizidwa mumtsinje wa Ayeyarwady pa December 24, 1949.
Kupirira Mavuto
Pasanapite nthawi ndinasamukira mumzinda wa Mandalay kuti ndikapeze ntchito yabwino. Koma kwenikweni cholinga changa chinali choti ndizidzagwira ntchito yolalikira nthawi zonse imene a Mboni za Yehova amaitchula kuti upainiya. Koma tsiku lina ndikuonera mpira ndinakomoka. Kumeneko kunali kuyambika kwa matenda a khunyu. Choncho ndinabwerera kwathu kuti achibale anga akandisamalire.
Matenda angawa anapitirizabe kwa zaka 8. Kenako nditapezako bwino ndinapeza ntchito ina. Ngakhale kuti mayi anga sankafuna kuti ndiyambe upainiya chifukwa cha matenda angawo, tsiku lina ndinawauza kuti: “Ndatsimikiza kuti ndikufuna kuyamba upainiya basi. Yehova azindisamalira.”
Choncho mu 1957 ndinasamukira ku Yangon ndipo ndinayamba upainiya. N’zodabwitsa kuti panapita zaka 50 ndisanadwalenso matenda akhunyu mpaka mu 2007 pamene anayambiranso. Panopo ndimamwa mankhwala a matenda amenewa. Mu 1958 anandisankha kuti ndikhale mpainiya wapadera ndipo mwezi uliwonse ndinkalalikira kwa maola 150.
Dera langa loyambirira kugwirako ntchito imeneyi unali mudzi wa Kyonsha womwe uli pamtunda wa makilomita 110 kumpoto cha kumadzulo kwa Yangon. Kumeneko kunali kagulu ka anthu amene anawerenga mabuku athu ophunzitsa Baibulo ndipo ankafuna kudziwa zambiri. Ineyo ndi Robert titafika kumeneko, anthu ambiri anasonkhana. Tinayankha mafunso awo ambiri okhudza Baibulo kenako tinawaphunzitsa mmene angachitire misonkhano yophunzira Baibulo. Pasanapite nthawi, ena mwa anthu amenewa anayamba kugwira nafe ntchito yolalikira. Ineyo ndinapemphedwa kuti nditsale m’mudzi umenewu. Patangotha miyezi yochepa, kagulu ka anthu kaja kanakula n’kukhala mpingo waukulu. Masiku ano kudera limeneli kuli Mboni za Yehova zoposa 150.
Kenako anandisankha kuti ndizigwira ntchito yoyendera mipingo ya Mboni za Yehova komanso timagulu takutali m’dziko lonse la Myanmar. Nthawi zambiri ndinkayenda maulendo ataliatali nditakwera pamwamba pa lole yodzaza ndi katundu. Ndinkadutsa m’nkhalango, kuwoloka mitsinje komanso kukwera mapiri. Ngakhale kuti mwachibadwa ndinalibe mphamvu kwambiri, ndinkaona kuti Yehova akundipatsa mphamvu.—Afilipi 4:13.
“Yehova Adzakuthandiza”
Mu 1962 ndinasamukira ku ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ku Yangon ndipo Robert anandiphunzitsa ntchito. Koma posakhalitsa, boma linalamula kuti amishonale onse ochokera kumayiko ena achoke ku Myanmar ndipo anachokadi patangotha milungu yochepa. Chifukwa cha zimenezi anandisankha kuti ndiziyang’anira ntchito zonse pa ofesi yanthambi.
Ndinadzifunsa kuti, ‘popeza ndine wosaphunzira komanso ndangofika kumene pa ofesi yanthambi, kodi ndikwanitsa bwanji kugwira ntchito imeneyi?’ Pozindikira nkhawa yangayi, abale achikulire anandiuza kuti: “Maurice, usadandaule. Yehova akuthandiza ndipo tonsefe tikuthandiza.” Mawu amenewa anandilimbikitsa kwambiri. Patangopita miyezi yochepa ndinafunika kulemba lipoti lapachaka lonena za ntchito yathu yolalikira ku Myanmar loti liikidwe mu Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 1967. Kuyambira nthawi imeneyo, kwa zaka 38 zotsatira ndinkalemba lipoti lonena za ntchito yathu m’dzikoli chaka chilichonse. Nthawi zambiri ndinkaona umboni wosonyeza kuti Yehova akutsogoleradi ntchito yathu.
Mwachitsanzo nthawi ina nditasaina mafomu opempha kuti ndikhale nzika ya dziko la Myanmar, pankafunika ndalama zolipirira chiphaso zokwana 450 kyats.a Koma chifukwa choti ndinalibe ndalamazo ndinaganiza zodikira kaye. Ndiyeno tsiku lina ndikudutsa pakampani ina yomwe kale ndinkagwirapo ntchito, munthu wina amene poyamba anali bwana wanga anandiona. Ndiyeno anakuwa kuti: “Raj, bwera udzatenge ndalama zako. Sitinakupatse ndalama zako mmene unkachoka.” Ndalamazi zinali zokwanira 450 kyats.
Mmene ndinkachoka mu ofesi ya bwanayo, ndinkangoganiza zimene ndingachite ndi ndalama zimenezi. Koma popeza ndalamayi inali ndendende ndalama zimene zinkafunika zija kuti ndipeze chiphaso chija, ndinaganiza kuti Yehova akufuna kuti ndizigwiritse ntchito kuchitira zimenezo. Zinaoneka kuti zimene ndinasankha pamenepa zinathandiza kwambiri. Popeza ndinali nzika ya dzikoli, ndinatha kupitirizabe kukhala m’dzikoli, kuyenda momasuka, kuitanitsa mabuku kuchokera m’mayiko ena ndiponso kugwira ntchito zina zofunika zokhudza ntchito yathu m’dzikoli.
Msonkhano Waukulu Umene Unachitikira Kumpoto
Mu 1969, ntchito yathu inapita patsogolo kambiri m’tauni ya Myitkyina, imene ili kumpoto kwa Myanmar. Choncho tinasankha kuti msonkhano wathu waukulu uchitikire pafupi ndi mzinda umenewu. Koma vuto lalikulu linali kupezera thiransipoti abale a kum’mwera kuti adzapezeke pamsonkhanowu. Tinapemphera za nkhaniyi ndipo tinapempha akuluakulu a kampani ya Myanmar Railways kuti atisungire mabogi 6 a sitima ya pamtunda kuti mudzakwere abalewo. Tinasangalala kwambiri atativomera kuti asungadi mabogiwo.
Tinali titakonzekera zonse zokhudza msonkhanowu. Tsiku limene abale a kumpotowo amayembekezeka kufika, tinapita kukawachingamira masana kumalo okwerera sitima ndipo tinkayembekezera kuti sitimayo ifika nthawi ya 2:30 masanawo. Tili mkati modikira, woyang’anira malowo anatipatsa telegalamu imene inali ndi uthenga wakuti: “Mabogi 6 amene Watch Tower Society inachita hayala tawasiya.” Woyang’anirayo anafotokoza kuti sitimayo inalephera kukoka mabogiwa pamene inkakwera mtunda.
Kodi pamenepa tikanatani? Choyamba tinaganiza kuti mwina tingosintha masiku a msonkhanowo. Komabe zimenezi zinatanthauza kuti tinafunika kukasainanso mafomu ena opempha chilolezo chochitira msonkhano, amene akanatenga milungu yambiri kuti awavomereze. Nthawi yomweyo tinayamba kupemphera kwa Yehova. Kenako tinangoona sitima ija ikutulukira. Sitinakhulupirire zimene tinaona. M’mabogi 6 a sitimayo munadzaza a Mboni za Yehova okhaokha. Iwo anali osangalala kwambiri ndipo ankatimwetulira ndi kumatiimikira manja. Titawafunsa zimene zinachitika, mmodzi wa iwo anatiuza kuti: “Ndi zoona kuti mabogi okwanira 6 atsala, koma osati mabogi amene ife tinakwera.”
Pakati pa chaka cha 1967 ndi 1971, chiwerengero cha Mboni za Yehova ku Myanmar chinawonjezeka kwambiri mpaka kutsala pang’ono kufika 600. Kenako mu 1978 ofesi yanthambi inasamukira ku nyumba ina yosanjikiza. Ndipo patatha zaka 20 chichitikire zimenezi, chiwerengero cha Mboni za Yehova chinawonjezerekanso kupitirira 2,500. Choncho panafunika kuwonjezera nyumba za ofesi yanthambi ndipo pa January 22, 2000, M’bale John E. Barr wa mu Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anafika kuchokera ku United States kudzatsegulira ofesi yatsopano yosanjikiza katatu imenenso ili ndi nyumba zogona. Mpaka pano nyumba imeneyi ikugwiritsidwabe ntchito.
Yehova Wandidalitsa Kwambiri
Masiku ano pali anthu 52 amene akugwira ntchito yodzipereka panthambi imene ili ku Yangon ndipo m’dziko lonse la Myanmar muli Mboni pafupifupi 3,500 m’timagulu ndiponso mipingo yokwana 74. Ndikusangalala kuti mu 1969, mayi anga okondedwa anakhala a Mboni za Yehova koma anamwalira pasanapite nthawi.
Mtsikana wina dzina lake Doris Ba Aye, amene anali mpainiya, anayamba kugwira ntchito yomasulira pa ofesi yathu yanthambi cha m’ma 1960. Mu 1959 asanabwere ku ofesi yanthambi, anali atalowa m’kalasi ya nambala 32 ya Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo imene imaphunzitsa Mboni za Yehova ntchito ya umishonale. Iye ndi wokongola, wansangala komanso wokonda kwambiri zinthu zauzimu. Zimenezi zinandikopa kwambiri moti tinakwatirana mu 1970. Mpaka pano timakonda kwambiri Yehova ndipo awirife timakondananso kwambiri.
Kwa zaka zoposa 60 ndaona umboni woti Mulungu akuthandiza kuti ntchito yolalikira ipite patsogolo m’dziko lino. Zoonadi, Mulungu ndi wamkulu komanso woyeneradi kumutamanda. Iye ‘amachita zinthu zazikulu’ ndipo zimenezi ndi zimene ndaona pa moyo wanga wonse.—Salimo 106:21.
[Mawu a M’munsi]
a Nthawi imeneyo ndalama zimenezi zinali pafupifupi madola 95 a ku America ndipo zimenezi zinali ndalama zambiri ndithu.
[Chithunzi patsamba 27]
Ndikulalikira ku Rangoon m’dziko la Burma, cha mu 1957
[Chithunzi patsamba 28]
Ndili pa ulendo wopita ku msonkhano waukulu ku Kaleymo, m’dziko la Burma, cha m’ma 1970
[Chithunzi patsamba 29]
Ofesi yathu yanthambi yatsopano imene inatsegulidwa mu 2000
[Chithunzi patsamba 29]
Ndili ndi Doris masiku ano
[Chithunzi patsamba 29]
Ine ndi Doris, tikulalikira khomo ndi khomo