Muzidalira Yehova Pamene Mapeto Akuyandikira
“Anthu inu muzidalira Yehova nthawi zonse.”—YES. 26:4.
1. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa atumiki a Mulungu ndi anthu a m’dzikoli?
M’DZIKOLI anthu ambiri sadziwa munthu kapena zinthu zoyenera kudalira chifukwa chakuti akhumudwitsidwapo kambirimbiri. Koma izi n’zosiyana kwambiri ndi atumiki a Yehova. Chifukwa chotsogoleredwa ndi nzeru yochokera kwa Mulungu, iwo amadziwa kuti si bwino kukhulupirira dzikoli kapena ‘anthu ake olemekezeka.’ (Sal. 146:3) M’malomwake, iwo amaika moyo wawo ndi chiyembekezo chawo m’manja mwa Yehova ndipo amadziwa kuti iye amawakonda komanso amakwaniritsa Mawu ake nthawi zonse.—Aroma 3:4; 8:38, 39.
2. Kodi Yoswa anatsimikizira bwanji kuti Mulungu ndi wodalirika?
2 M’mbuyomu, Yoswa anatsimikizira kuti Mulungu ndi wodalirika. Chakumapeto kwa moyo wake, iye anauza Aisiraeli anzake kuti: “Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu.”—Yos. 23:14.
3. Kodi dzina la Mulungu limatiuza chiyani za iye?
3 Yehova samangokwaniritsa malonjezo ake chifukwa chokonda atumiki ake koma makamaka chifukwa cha dzina lake. (Eks. 3:14; 1 Sam. 12:22) Ponena za dzina la Mulungu, mawu oyamba a Baibulo limene linamasuliridwa ndi J. B. Rotherham amati: “[Dzinali] ndi lonjezo losonyeza kukoma mtima; limasonyeza kuti Mulungu akhoza kusintha mogwirizana ndi mmene zinthu zilili, vuto lililonse kapena ngati pali chifukwa chilichonse . . . [Dzinali] ndi lonjezo, . . . limatiuzanso zambiri za Mulungu ndipo limatithandiza kumukumbukira. Nthawi zonse Mulungu adzachita zinthu mogwirizana ndi Dzinali ndipo sadzachita nalo manyazi.”–The Emphasized Bible.
4. (a) Kodi lemba la Yesaya 26:4 likutilimbikitsa kuchita chiyani? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?
4 Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimamudziwa bwino Yehova moti nditha kumudalira pa chilichonse? Kodi sindiopa za m’tsogolo podziwa kuti Mulungu akuona zonse ndipo akudziwa zoyenera kuchita?’ Lemba la Yesaya 26:4 limati: “Anthu inu muzidalira Yehova nthawi zonse, pakuti Ya Yehova ndiye Thanthwe mpaka kalekale.” N’zoona kuti masiku ano Mulungu salowerera m’njira yozizwitsa pa zochitika za pamoyo wa anthu ngati mmene ankachitira nthawi zina kalelo. Koma popeza iye ndi “Thanthwe mpaka kalekale,” tingamudalire “nthawi zonse.” Kodi Mulungu wathu wodalirikayu amathandiza bwanji atumiki ake okhulupirika masiku ano? Tiyeni tione njira zitatu zimene iye amachitira zimenezi. Choyamba, iye amatipatsa mphamvu tikamamupempha kuti atithandize pamene tikuyesedwa kuti tichite zoipa. Chachiwiri, amatithandiza tikakumana ndi anthu opanda chidwi kapena otsutsa. Ndipo chachitatu, iye amatilimbikitsa tikapanikizika ndi nkhawa. Pamene tikukambirana mfundo zitatu zimenezi, ganizirani zimene mungachite kuti muzidalira kwambiri Yehova.
Muzidalira Mulungu Mukamayesedwa Kuti Muchite Zoipa
5. Kodi kukhulupirira Mulungu kungakhale kovuta pa nkhani iti?
5 Kudalira Yehova kuti adzakwaniritsa malonjezo ake okhudza Paradaiso ndi kuukitsidwa kwa akufa n’kosavuta chifukwa izi ndi zinthu zimene timazilakalaka. Koma nthawi zina si chinthu chapafupi kumudalira pa nkhani ya makhalidwe abwino. Zingakhale zovuta kukhulupirira ndi mtima wonse kuti tiyenera kutsatira mfundo zake komanso kuti tingasangalale kwambiri ngati titamazitsatira. Mfumu Solomo inalemba malangizo akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” (Miy. 3:5, 6) Onani kuti palembali anatchula mawu akuti “njira.” Izi zikusonyeza kuti tiyenera kukhulupirira Mulungu pa njira zathu zonse, kapena kuti pa moyo wathu wonse, osati pa nkhani ya chiyembekezo chathu chachikhristu chokha ayi. Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Mulungu tikamayesedwa kuti tichite zoipa?
6. Kodi tingatani kuti tisamavutike kukana maganizo oipa?
6 Kukana zoipa kumayambira m’maganizo. (Werengani Aroma 8:5; Aefeso 2:3.) Kodi mungatani kuti musamavutike kukana maganizo oipa? Taganizirani njira zisanu izi: 1. Muzipemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni. (Mat. 6:9, 13) 2. Muzisinkhasinkha zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene sanamvere Yehova ndiponso amene anamumvera, n’kuona zotsatira zake.a (1 Akor. 10:8-11) 3. Muziganizira mmene inuyo ndiponso anthu amene mumawakonda angavutikire maganizo ngati mutachita tchimo. 4. Muziganiziranso mmene Mulungu angamvere ngati mmodzi mwa atumiki ake atachita tchimo lalikulu. (Werengani Salimo 78:40, 41.) 5. Ndiyeno ganiziraninso mmene Yehova angasangalalire mumtima mwake akaona mtumiki wake wokhulupirika akukana kuchita zoipa n’kuchita zabwino, kaya pa maso pa anthu ena kapena ali payekha. (Sal. 15:1, 2; Miy. 27:11) Inunso mungasonyeze kuti mumadalira Yehova.
Muzidalira Mulungu Mukamakumana ndi Anthu Opanda Chidwi Ndiponso Otsutsa
7. Kodi Yeremiya anakumana ndi mavuto ati ndipo kodi nthawi zina ankamva bwanji?
7 Abale athu ambiri amatumikira m’madera amene amafunika kupirira kwambiri. Mneneri Yeremiya anatumikiranso m’dera lotereli. Iye ankalalikira mu ufumu wa Yuda utatsala pang’ono kuwonongedwa ndipo iyi inali nthawi yovuta kwambiri. Tsiku lililonse chikhulupiriro cha Yeremiya chinkayesedwa chifukwa chomvera Mulungu pogwira ntchito yolalikira uthenga wa chiweruzo Chake. Pa nthawi ina ngakhale Baruki, yemwe anali mlembi wake wokhulupirika, anadandaula chifukwa chotopa. (Yer. 45:2, 3) Kodi Yeremiya anagwa ulesi chifukwa cha zimenezi? Pa nthawi zina iye ankavutika kwambiri maganizo mpaka anafika ponena kuti: “Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!” Ananenanso kuti: “N’chifukwa chiyani ndinabadwa? Kodi ndinabadwa kuti ndidzagwire ntchito yakalavulagaga ndi kukhala wachisoni, ndi kuti moyo wanga ufike kumapeto kwake ndili wamanyazi?”—Yer. 20:14, 15, 18.
8, 9. Malinga ndi Yeremiya 17:7, 8 ndi Salimo 1:1-3, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisasiye kubala zipatso zabwino?
8 Koma Yeremiya sanasiye ntchito yake. Iye anapitiriza kudalira Yehova. Zotsatira zake zinali zakuti mneneriyu anaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yehova olembedwa pa Yeremiya 17:7, 8 akuti: “Wodala ndi munthu aliyense amene amakhulupirira Yehova, amene amadalira Yehova. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi. Kutentha kukadzafika iye sadzadziwa, koma masamba ake adzachuluka ndi kukhala obiriwira. Pa nthawi ya chilala sadzada nkhawa kapena kusiya kubala zipatso.”
9 Mofanana ndi mtengo wa zipatso wobiriwira “wobzalidwa m’mphepete mwa madzi” kapena m’munda wa zipatso wothiriridwa bwino, Yeremiya ‘sanasiye kubala zipatso.’ Iye sanalole kufooketsedwa ndi anthu oipa amene ankamunyoza. M’malomwake, iye nthawi zonse ankadalira Kasupe wa “madzi” opatsa moyo ndipo ankatsatira zonse zimene Yehova anamuuza. (Werengani Salimo 1:1-3; Yer. 20:9) Apatu Yeremiya anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri makamaka ngati tikutumikira Mulungu m’madera ovuta. Ngati mukutumikira m’dera lovuta, pitirizani kudalira kwambiri Yehova amene angakuthandizeni kupirira “polengeza dzina lake kwa anthu ena.”—Aheb. 13:15.
10. Kodi tili ndi madalitso otani ndipo tiyenera kudzifunsa funso liti?
10 Yehova watipatsa paradaiso wauzimu wokhala ndi zinthu zambiri pofuna kutithandiza kuti tipirire mavuto a pa moyo wathu masiku otsiriza ano. Zina mwa zinthu zimene watipatsa ndi Baibulo lonse, lomwe ndi Mawu ake, ndipo likumasuliridwa molondola m’zinenero zambirimbiri. Iye wapereka chakudya chauzimu chambiri ndiponso pa nthawi yake kudzera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Iye watipatsanso abale ndi alongo amene amatilimbikitsa tikamacheza nawo pa misonkhano yampingo ndi ikuluikulu. Kodi mumagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimene watipatsazi? Anthu onse amene amagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimenezi “adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.” Koma amene samvera Mulungu ‘adzalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo adzafuula chifukwa chosweka mtima.’—Yes. 65:13, 14.
Muzidalira Mulungu Mukamalimbana ndi Nkhawa
11, 12. Poona mavuto amene ali m’dzikoli, kodi chinthu cha nzeru chimene tingachite n’chiyani?
11 Mogwirizana ndi ulosi, mavuto amene anthu akukumana nawo akuwonjezekawonjezeka. (Mat. 24:6-8; Chiv. 12:12) Madzi akasefukira, anthu amathawira padenga la nyumba kapena pamalo ena alionse okwera. Mofanana ndi zimenezi, pamene mavuto a m’dzikoli akuwonjezeka anthu ambiri amafufuza chitetezo m’zinthu zimene amaona kuti ndi zapamwamba monga mabungwe azachuma, andale, zipembedzo kapena zipangizo zamakono. Komatu zonsezi sizipereka chitetezo chenicheni. (Yer. 17:5, 6) Mosiyana ndi anthu amenewa, atumiki a Yehova amapeza chitetezo chenicheni kwa Yehova, yemwe ndi “Thanthwe mpaka kalekale.” (Yes. 26:4) Wamasalimo ananena kuti: “[Yehova] ndi thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.” (Werengani Salimo 62:6-9.) Kodi tingatani kuti tipeze chitetezo m’Thanthwe limeneli?
12 Timamamatira Yehova ngati tikumvera Mawu ake amene nthawi zambiri amatsutsana ndi nzeru za anthu. (Sal. 73:23, 24) Mwachitsanzo, anthu amene amayendera nzeru za anthu angatiuze kuti: ‘Moyotu ndi waufupi.’ ‘Mupeze ntchito yabwino.’ ‘Muzipeza ndalama zambiri.’ ‘Mugule zakutizakuti.’ Kapena anganene kuti, ‘Muziyenda kuti muone dziko n’kumasangalala.’ Koma nzeru yochokera kwa Mulungu imagwirizana ndi malangizo akuti: “Amene amagwiritsira ntchito dzikoli azikhala ngati amene sakuligwiritsira ntchito mokwanira, pakuti zochitika za padzikoli zikusintha.” (1 Akor. 7:31) Yesu nayenso akutilimbikitsa kuti nthawi zonse tiziika zinthu za Ufumu patsogolo ndipo tikatero ndiye kuti tikusunga ‘chuma kumwamba,’ malo amene ndi otetezeka kwambiri.—Mat. 6:19, 20.
13. Mogwirizana ndi lemba la 1 Yohane 2:15-17, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
13 Kodi mmene mumaonera “dziko” ndiponso “zinthu za m’dziko” zimasonyeza kuti mumadalira Mulungu ndi mtima wanu wonse? (1 Yoh. 2:15-17) Kodi mumaona kuti chuma chauzimu ndiponso kuchita zambiri pa ntchito ya Ufumu ndi zofunika kwambiri kwa inu kuposa zinthu zimene dzikoli limapereka? (Afil. 3:8) Kodi mumayesetsa kukhala ndi ‘diso lolunjika pa chinthu chimodzi’? (Mat. 6:22) Koma sikuti Mulungu akufuna kuti muzinyalanyaza maudindo ena amene muli nawo makamaka ngati muli ndi banja limene muyenera kulisamalira. (1 Tim. 5:8) Iye amafuna kuti atumiki ake azimukhulupirira ndi mtima wonse osati kukhulupirira dziko la Satana limene likupitali.—Aheb. 13:5.
14-16. Kodi ena apindula bwanji chifukwa chokhala ndi ‘diso lolunjika pa chinthu chimodzi’ ndiponso kupitiriza kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba?
14 Taganizirani za Richard ndi Ruth omwe ali ndi ana atatu. Richard anati: “Mumtimamu ndinkaona kuti ndingathe kuchita zambiri potumikira Yehova. Sindinkasowa zinthu zakuthupi koma ndinkaona kuti ndikuchita zinthu zochepa potumikira Mulungu. Titapempherera nkhaniyi n’kuionanso bwinobwino, ine ndi Ruth tinagwirizana zoti ndikapemphe bwana wanga kuti ndizingogwira ntchito masiku anayi pa mlungu ngakhale kuti m’dziko lathu munali mavuto a zachuma. Bwanayo anavomera ndipo pasanathe mwezi umodzi ndinayamba kugwira ntchito masiku anayi pa mlungu.” Kodi panopa Richard amamva bwanji?
15 Iye anati: “Malipiro anga atsika ndi 20 peresenti koma ndili ndi masiku ena 50 pa chaka amene ndimakhala limodzi ndi banja langa n’kumaphunzitsa ana anga. Ndawonjezera nthawi imene ndimalalikira kuwirikiza kawiri, maphunziro anga a Baibulo awirikizanso katatu ndipo ndikutumikira mokwanira pa udindo wanga mu mpingo. Popeza ndili ndi nthawi yokhala pakhomo n’kumathandiza kusamalira ana, Ruth amakwanitsa kuchita upainiya wothandiza nthawi ndi nthawi. Panopa ndatsimikiza mtima kuti ndizichita zimenezi basi.”
16 Roy ndi Petina amakhala ndi mwana wamkazi mmodzi pakhomo ndipo achepetsa nthawi imene amagwira ntchito n’cholinga choti azichita utumiki wa nthawi zonse. Roy anati: “Ine ndimagwira ntchito masiku atatu pa mlungu ndipo Petina amagwira masiku awiri. Tinasamukanso m’nyumba yomwe tinkakhala n’kupita m’nyumba yaing’ono yosavuta kuisamalira. Tinkachita upainiya tisanabereke mwana wathu wamwamuna ndi wamkazi ndipo sitinasiye mtima wofuna kuchita upainiya. Ana athu atakula tinayambiranso kuchita utumiki wa nthawi zonse. Madalitso amene tapeza sangafanane ndi ndalama, ngakhale zitakhala zochuluka bwanji?”
“Mtendere wa Mulungu” Uziteteza Mtima Wanu
17. Ngakhale kuti moyo ndi wosadalirika, kodi Malemba amakulimbikitsani bwanji kuti musamade nkhawa?
17 Palibe munthu amene angadziwe kuti mawa zinthu zidzayenda bwanji, chifukwa “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka” zimagwera aliyense. (Mlal. 9:11) Komabe sikuti tizisowa mtendere poganiza kuti kodi mawa kugwa chiyani ngati mmene amachitira anthu amene sali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. (Mat. 6:34) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afil. 4:6, 7.
18, 19. Kodi Mulungu amatilimbikitsa m’njira ziti? Perekani chitsanzo.
18 Abale ndi alongo ambiri amene akukumana ndi mavuto odetsa nkhawa amapeza mtendere wochokera kwa Yehova ndipo mtima wawo umakhala m’malo. Mlongo wina anati: “Dokotala wina ankandiopseza mobwerezabwereza kuti ndilandire magazi. Nditangokumana naye anangofikira kunena kuti, ‘Sindikufuna magazi, sindikufuna magazi. Ndiye kuti chiyani?’ Ndiye pa nthawiyo komanso nthawi zina ndinkapemphera kwa Yehova chamumtima ndipo mtendere wake unkandikhazika mtima pansi. Zitatero ndinalimba mtima kwambiri. Ngakhale kuti ndinali wofooka chifukwa chokhala ndi magazi ochepa, ndinatha kufotokoza bwino zimene ndimakhulupirira pa nkhani ya magazi pogwiritsa ntchito Malemba.”
19 Nthawi zina Mulungu amatilimbikitsa kudzera mwa wokhulupirira mnzathu kapena kudzera m’chakudya chauzimu cha pa nthawi yoyenera. Mwina munamvapo m’bale kapena mlongo akunena kuti: “Nkhaniyi yafika pa nthawi yake. Zikungokhala ngati alembera ineyo.” Kaya tikumane ndi vuto lotani, Yehova adzatisonyeza chikondi chake ngati timudalira. Pajatu ndife “nkhosa” zake ndipo walola kuti tizidziwika ndi dzina lake.—Sal. 100:3; Yoh. 10:16; Mac. 15:14, 17.
20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti atumiki a Yehova adzakhala mwabata pamene dziko la Satanali likuwonongedwa?
20 Pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova,” limene lili pafupi kwambiri, zinthu zonse zimene anthu m’dziko la Satanali amaziona ngati zodalirika zidzawonongedwa. Golide, siliva ndi zinthu zonse zamtengo wapatali sizidzateteza anthu ngakhale pang’ono. (Zef. 1:18; Miy. 11:4) Chitetezo chidzapezeka kwa Yehova yekha yemwe ndi “Thanthwe mpaka kalekale.” (Yes. 26:4) Choncho tiyeni tisonyeze kuti timadalira Yehova ndi mtima wonse mwa kutsatira njira zake zolungama. Tizisonyezanso kuti timamudalira mwa kulalikira uthenga wake wa Ufumu, ngakhale kuti ena alibe nawo chidwi ndipo ena amatitsutsa, komanso tizimutulira nkhawa zathu zonse. Tikamachita zimenezi, tidzakhaladi ‘mwabata ndipo sitidzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.’—Miy. 1:33.
[Mawu a M’munsi]
a Onani buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu” tsamba 102 mpaka 106.
Kodi Mungafotokoze?
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadalira Mulungu
• tikamayesedwa kuti tichite zoipa?
• tikamakumana ndi anthu opanda chidwi kapena otsutsa?
• tikamalimbana ndi nkhawa?
[Chithunzi patsamba 13]
Munthu akamatsatira mfundo za Mulungu amakhala wosangalala
[Chithunzi patsamba 15]
“Yehova ndiye Thanthwe mpaka kalekale”