Anthu Amene Amakhulupirira Yehova Amakhala Olimba Mtima
“Yehova adzamva ndikaitana.”—SAL. 4:3.
1, 2. (a) Kodi Davide anakumana ndi mavuto aakulu ati? (b) Kodi tikambirana masalimo ati?
MFUMU DAVIDE atalamulira Isiraeli zaka zambiri anakumana ndi mavuto aakulu. Mwana wake Abisalomu anamupandukira ndipo analengeza kuti iye ndi mfumu. Izi zinachititsa kuti Davide athawe ku Yerusalemu. Mnzake wapamtima anamupandukiranso ndipo Davide anadutsa m’phiri la Maolivi akulira komanso asanavale nsapato. Iye ankayenda pamodzi ndi anzake ochepa okhulupirika. Kenako munthu wa m’banja la Mfumu Sauli dzina lake Simeyi anali kumugenda, kumuwaza fumbi ndiponso kumutukwana.—2 Sam. 15:30, 31; 16:5-14.
2 Kodi mavuto amenewa akanachititsa Davide kuti afe ali ndi chisoni komanso manyazi? Ayi ndithu, chifukwa chakuti ankakhulupirira Yehova. Umboni wa zimenezi uli m’Salimo lachitatu limene Davide anapeka. Salimoli limanena za nthawi imene Davide ankathawa. Iye analembanso Salimo lachinayi ndipo masalimo onsewa amasonyeza kuti Davide ankakhulupirira zoti Mulungu amamva ndiponso kuyankha mapemphero. (Sal. 3:4; 4:3) Masalimowa amatitsimikizira kuti Yehova amakhala ndi atumiki ake okhulupirika usana ndi usiku. Iye amawadalitsa powathandiza kukhala ndi mtendere mumtima ndiponso kukhala otetezeka. (Sal. 3:5; 4:8) Tiyeni tikambirane masalimo amenewa n’kuona mmene angatithandizire kukhala olimba mtima ndiponso kukhulupirira Mulungu.
‘Anthu Otiukira Akachuluka’
3. Malinga ndi Salimo 3:1, 2, kodi zinthu zinali bwanji pa moyo wa Davide?
3 Munthu wina anauza Davide kuti: “Mitima ya anthu a mu Isiraeli yatsatira Abisalomu.” (2 Sam. 15:13) Davide anadabwa kuti anthu ambiri ali ku mbali ya Abisalomu ndipo anafunsa kuti: “Inu Yehova, n’chifukwa chiyani adani anga achuluka chotere? N’chifukwa chiyani anthu ondiukira achuluka? Ponena za moyo wanga, ambiri akuti: ‘Mulungu sam’pulumutsa ameneyu.’” (Sal. 3:1, 2) Aisiraeli ambiri ankaganiza kuti Yehova sapulumutsa Davide m’manja mwa Abisalomu ndi gulu lake.
4, 5. (a) Kodi Davide sankakayikira za chiyani? (b) Kodi mawu akuti “Wonditukula mutu” akutanthauza chiyani?
4 Koma Davide anali wolimba mtima chifukwa chokhulupirira Mulungu. Iye anaimba kuti: “Koma inu Yehova ndinu chishango changa, ulemerero wanga ndiponso Wonditukula mutu.” (Sal. 3:3) Davide sankakayika kuti Yehova amuteteza ngati mmene chishango chimatetezera msilikali. Mfumu yokalambayi inaphimba kumutu n’kumathawa chowerama chifukwa chochititsidwa manyazi. Koma Wam’mwambamwamba anali wokonzeka kusintha zinthu kuti Davide akhalenso wolemekezeka. Yehova anadzamuweramutsa n’kutukula mutu wake ndiponso kumuchotsera manyazi. Davide anafuula kwa Mulungu ali ndi chikhulupiriro chakuti amuyankha. Kodi inunso mumakhulupirira kuti Yehova adzakuyankhani?
5 Mawu amene Davide ananena akuti “Wonditukula mutu,” amasonyeza zimene anali kuyembekezera kuti Yehova amuchitire. Baibulo lina linamasulira lembali kuti: “Koma inu AMBUYE ndinu chishango chonditeteza ku zinthu zoopsa, mumandithandiza kupambana ndiponso kulimba mtima.” (Today’s English Version) Ponena za mawu akuti “Wonditukula mutu,” buku lina limanena kuti: “Mulungu akatukula . . . ‘mutu’ wa munthu, Amam’patsa munthuyo chiyembekezo ndiponso kumulimbitsa mtima.” Davide anali ndi chifukwa chokhala wokhumudwa kwambiri popeza anachotsedwa pa mpando wachifumu wa Isiraeli. Koma ‘kutukula mutu wake’ kunachititsa kuti akhalenso wolimba mtima ndiponso kuti azikhulupirira kwambiri Mulungu.
‘Yehova Adzandiyankha’
6. N’chifukwa chiyani Davide ananena kuti pemphero lake lidzayankhidwa kuchokera kuphiri loyera la Yehova?
6 Chifukwa chokhulupirira Yehova ndiponso kukhala wolimba mtima, Davide anapitiriza kuti: “Ndidzafuulira Yehova mokweza, ndipo iye adzandiyankha m’phiri lake loyera.” (Sal. 3:4) Davide analamula kuti likasa la pangano limene linali kuimira Mulungu likaikidwe kuphiri la Ziyoni, ndipo pa nthawiyi linali kumeneko. (Werengani 2 Samueli 15:23-25.) N’chifukwa chake Davide ananena kuti pemphero lake lidzayankhidwa kuchokera kuphiri loyera la Yehova.
7. N’chifukwa chiyani Davide sankaopa chilichonse?
7 Chifukwa chokhulupirira kuti Mulungu adzayankha pemphero lake, Davide sankaopa chilichonse. M’malomwake anaimba kuti: “Koma ine ndidzagona pansi ndi kupeza tulo. Ndidzadzuka ndithu, pakuti Yehova amandithandiza.” (Sal. 3:5) Ngakhale usiku, pamene munthu angaukiridwe mosavuta, Davide ankagona mtima uli m’malo. Iye sankakayikira kuti akagona adzukanso. Chifukwa cha zimene zinamuchitikira m’mbuyomu, Davide ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu amuthandiza. Choncho ifenso tingakhale ndi chikhulupiriro choterechi ngati timatsatira “njira za Yehova” ndiponso ngati sitichoka kwa iye.—Werengani 2 Samueli 22:21, 22.
8. Kodi Salimo 27:1-4 likusonyeza bwanji kuti Davide ankakhulupirira Mulungu?
8 Mu salimo lina Davide anasonyezanso kuti anali wolimba mtima ndiponso ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Iye anauziridwa kulemba kuti: “Yehova ndiye kuwala kwanga ndi chipulumutso changa. Ndingaopenso ndani? Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga. Ndingachitenso mantha ndi ndani? . . . Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire, mtima wanga sudzachita mantha. . . . Chinthu chimodzi chimene ndapempha kwa Yehova, chimenecho ndi chimene ndimachikhumba, n’chakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kuti ndione ubwino wa Yehova, komanso kuti ndiyang’ane kachisi wake moyamikira.” (Sal. 27:1-4) Ngati mumamva mmene Davide ankamvera, mudzayesetsa mmene mungathere kusonkhana nthawi zonse limodzi ndi olambira Yehova anzanu.—Aheb. 10:23-25.
9, 10. Ngakhale kuti Davide analemba Salimo 3:6, 7, kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti iye analibe mtima wobwezera?
9 Ngakhale kuti Abisalomu anamupandukira Davide ndiponso anthu ena anali osakhulupirika kwa iye, Davide anaimba kuti: “Sindidzaopa anthu masauzande makumimakumi amene andiukira ndi kundizungulira. Nyamukani, inu Yehova! Ndipulumutseni inu Mulungu wanga! Pakuti mudzakantha adani anga onse pachibwano. Mano a anthu oipa mudzawaphwanyaphwanya.”—Sal. 3:6, 7.
10 Davide analibe mtima wobwezera. Mulungu ndi amene anayenera ‘kukantha adani ake pachibwano.’ Mfumu Davide inali itakopera buku la Chilamulo ndipo inkadziwa kuti m’bukulo Yehova anati: “Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.” (Deut. 17:14, 15, 18; 32:35) Mulungu ndi amenenso ‘adzaphwanyaphwanya mano a anthu oipa.’ Kuphwanya mano awo kumatanthauza kuwafoola kuti asavulazenso anthu ena. Yehova amadziwa anthu amene ndi oipa chifukwa “amaona mmene mtima ulili.” (1 Sam. 16:7) Timayamikira kuti Mulungu amatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso amatipatsa mphamvu kuti tithe kulimbana ndi Satana, amene ndi woipitsitsa. Posachedwapa iye adzatsekeredwa m’phompho ngati mkango wopanda mano woyenera kuwonongedwa basi.—1 Pet. 5:8, 9; Chiv. 20:1, 2, 7-10.
“Chipulumutso Chimachokera kwa Yehova”
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempherera okhulupirira anzathu?
11 Davide ankadziwa kuti ndi Yehova yekha amene angamupulumutse pa nthawi imene anapanikizikayi. Koma sikuti wamasalimoyu ankangodziganizira yekha. Iye ankaganiziranso anthu onse a Yehova. N’chifukwa chake Davide anamaliza salimo louziridwa ndi Mulungu limeneli ndi mawu akuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso anu ali pa anthu anu.” (Sal. 3:8) Davide anali ndi mavuto aakulu kwambiri koma anali kuganizira anthu onse a Yehova ndipo ankakhulupirira kuti Mulungu awadalitsa. Kodi nafenso sitiyenera kuganizira okhulupirira anzathu? Tiyenera kuwatchula m’mapemphero athu, n’kumapempha Yehova kuti awapatse mzimu woyera n’cholinga choti azilalikira uthenga wabwino molimba mtima.—Aef. 6:17-20.
12, 13. N’chiyani chinachitikira Abisalomu, nanga Davide anatani izi zitachitika?
12 Pamene nkhondo inayambika, asilikali a nkhondo a Abisalomu anagonjetsedwa. Abisalomu anayamba kuthawa atakwera nyulu koma tsitsi lake lalitali linakodwa m’ziyangoyango za nthambi ya m’munsi mwa mtengo waukulu. Iye anali lendelende moti palibe chimene akanatha kuchita mpaka pamene Yowabu anamupha pomulasa pamtima ndi mikondo itatu. (2 Sam. 18:6-17) Abisalomu anafa mochititsa manyazi kwambiri. Limeneli ndi chenjezo kwa anthu onse amene amazunza anzawo, makamaka amene amazunza odzozedwa a Mulungu monga Davide.—Werengani Miyambo 3:31-35.
13 Kodi Davide anasangalala atamva zoti mwana wake waphedwa? Ayi. M’malomwake iye ankangoyendayenda kwinaku akulira n’kumafuula kuti: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga Abisalomu! Haa! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine m’malo mwa iwe, Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!” (2 Sam. 18:24-33) Ndi mawu a Yowabu okha amene anathandiza Davide kuti asiye kulira. Abisalomu anafa momvetsa chisoni chifukwa chodzikuza. Iye anaukira bambo ake, omwe anali wodzozedwa wa Yehova, ndipo anadzibweretsera tsoka.—2 Sam. 19:1-8; Miy. 12:21; 24:21, 22.
Davide Asonyezanso Kukhulupirira Mulungu
14. Kodi tikudziwa chiyani za Salimo lachinayi?
14 Nalonso Salimo lachinayi ndi pemphero la Davide lochokera pansi pa mtima losonyeza kuti iye ankakhulupirira Yehova ndi mtima wonse. (Sal. 3:4; 4:3) N’kutheka kuti Davide analemba nyimbo imeneyi pofuna kusonyeza kuti wapeza mpumulo ndiponso kuyamikira Mulungu kuti zolinga za Abisalomu zalephereka. Apo ayi, ndiye kuti mwina analemba akuganizira za Alevi omwe anali oimba. Kaya zinthu zinali bwanji pa nthawiyo, kusinkhasinkha salimo limeneli kungalimbitse chikhulupiriro chathu mwa Yehova.
15. Kodi n’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yehova atiyankha tikapemphera kwa iye kudzera mwa Mwana wake?
15 Davide anasonyezanso kukhulupirira Mulungu ndi mtima wonse ndiponso kuti amadziwa zoti Yehova amayankha mapemphero. Iye anaimba kuti: “Ndikaitana, mundiyankhe inu Mulungu wanga wolungama. M’masautso anga mundiimiritse pamalo otakasuka. Mundikomere mtima ndipo imvani pemphero langa.” (Sal. 4:1) Nafenso tingakhale ndi chikhulupiriro chotere ngati timachita zinthu mwachilungamo. Tikudziwa kuti Yehova, yemwe ndi ‘Mulungu wolungama,’ amadalitsa anthu oongoka mtima. Choncho sitingakayikire kuti atiyankha tikapemphera kwa iye kudzera mwa Mwana wake tili ndi chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Yesu. (Yoh. 3:16, 36) Zimenezitu zimatipatsa mtendere wa mumtima.
16. Kodi mwina Davide anakhumudwa ndi chiyani?
16 Nthawi zina tikhoza kukumana ndi mavuto amene angatifooketse. Mwina izi n’zimene zinachitikira Davide pa nthawi ina chifukwa anaimba kuti: “Inu ana a anthu, kodi mudzandinyoza chifukwa cha ulemerero wanga kufikira liti? Mudzakonda zinthu zopanda pake kufikira liti? Mudzafunafuna nkhani yoti mundinamizire kufikira liti?” (Sal. 4:2) Zikuoneka kuti palembali mawu akuti “ana a anthu” anawagwiritsa ntchito posonyeza kuti anthuwo si abwino. Adani a Davide ‘ankakonda zinthu zopanda pake.’ Baibulo lina linamasulira lembali kuti: “Mudzakonda zinthu zonama ndi kufunafuna milungu yonyenga mpaka liti?” (New International Version) Ngakhale pamene takhumudwa ndi zinthu zimene anthu ena achita, tiyenera kupitiriza kupemphera kuchokera pansi pa mtima n’kumasonyeza kuti timakhulupirira kwambiri Mulungu woona.
17. Fotokozani mmene tingachitire zinthu mogwirizana ndi Salimo 4:3.
17 Mawu ena amene Davide analemba akusonyeza kuti iye ankakhulupirira Mulungu. Davide analemba kuti: “Choncho dziwani kuti Yehova adzapatula wokhulupirika wake. Yehova adzamva ndikaitana.” (Sal. 4:3) Munthu ayenera kulimba mtima ndiponso kukhulupirira kwambiri Yehova kuti akhalebe wokhulupirika kwa iye. Mwachitsanzo, banja lachikhristu lingafunikire makhalidwe amenewa ngati wachibale wosalapa wachotsedwa. Mulungu amalemekeza anthu amene ndi okhulupirika kwa iye ndiponso amene amatsatira njira zake. Kukhulupirika ndiponso kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse kumathandizanso anthu ake kukhala osangalala.—Sal. 84:11, 12.
18. Malinga ndi Salimo 4:4, kodi tiyenera kuchita chiyani ngati munthu wina watinenera kapena kutichitira zinthu zokhumudwitsa?
18 Kodi tingatani ngati munthu wanena kapena kuchita zinthu zimene zatikhumudwitsa? Tingakhalebe osangalala ngati titsatira mawu a Davide akuti: “Ngati mwakwiya, musachimwe. Lankhulani mumtima mwanu, muli pabedi panu, ndipo mukhale chete.” (Sal. 4:4) Ngati wina watinenera zoipa kapena kutichitira zinthu zokhumudwitsa, tisabwezere chifukwa tikatero tichimwa. (Aroma 12:17-19) Tingalankhule mumtima mwathu pamene tili pabedi pathu. Tikapemphera za nkhaniyo, tikhoza kuyamba kuiona m’njira ina n’kungomukhululukira munthuyo chifukwa cha chikondi. (1 Pet. 4:8) Malangizo a Paulo, amene mwina anawatenga pa Salimo 4:4, ndi othandizanso pa nkhaniyi. Iye anati: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndipo musam’patse malo Mdyerekezi.”—Aef. 4:26, 27.
19. Kodi Salimo 4:5 lingatithandize bwanji pa nkhani yopereka nsembe zauzimu?
19 Potsindika kufunika kokhulupirira Mulungu, Davide anaimba kuti: “Perekani nsembe zachilungamo, ndipo khulupirirani Yehova.” (Sal. 4:5) Nsembe zimene Aisiraeli ankapereka zinkakhala zamtengo wapatali pokhapokha ngati anthu operekawo anali ndi zolinga zabwino. (Yes. 1:11-17) Nafenso ngati tikufuna kuti Mulungu alandire nsembe zathu zauzimu, tiyenera kuzipereka ndi zolinga zabwino ndiponso kukhulupirira Mulungu ndi mtima wonse.—Werengani Miyambo 3:5, 6; Aheberi 13:15, 16.
20. Kodi ‘kuwala kwa nkhope ya Yehova’ kumaimira chiyani?
20 Davide anapitiriza kuti: “Pali ambiri amene akunena kuti: ‘Ndani adzationetsa zinthu zabwino?’ Inu Yehova, tiunikeni ndi kuwala kwa nkhope yanu.” (Sal. 4:6) Kuunikidwa ndi ‘kuwala kwa nkhope ya Yehova’ kumaimira kukomeredwa mtima ndi Mulungu. (Sal. 89:15) Choncho pamene Davide anapemphera kuti: “Tiunikeni ndi kuwala kwa nkhope yanu,” anatanthauza kuti ‘tikomereni mtima.’ Chifukwa choti timakhulupirira Yehova, iye amatikomera mtima ndipo timasangalala kwambiri pomutumikira molimba mtima.
21. Kodi chidzachitike n’chiyani ngati tikuchita khama pa ntchito yokolola mwauzimu?
21 Poganizira zinthu zosangalatsa kwambiri kuposa za m’nyengo yokolola zimene Mulungu adzapereke, Davide anaimba kuti: “Mudzasangalatsadi mtima wanga, kuposanso mmene iwo amasangalalira, mbewu ndi vinyo wawo watsopano zikachuluka.” (Sal. 4:7) Ifenso tidzasangalala kwambiri ngati timagwira nawo mokwanira ntchito yokolola mwauzimu. (Luka 10:2) Panopa ‘mtundu wochuluka,’ womwe ndi Akhristu odzozedwa, ukutsogolera pa ntchitoyi ndipo tikusangalala pamene ‘antchito okolola’ akuwonjezeka. (Yes. 9:3) Kodi inuyo mukuchita zambiri mu ntchito yokololayi yomwe ndi yosangalatsa?
Pitirizani Kutumikira Mulungu Molimba Mtima Ndiponso Kumukhulupirira
22. Malinga ndi Salimo 4:8, kodi Aisiraeli zinkawayendera bwanji pamene anali kutsatira Chilamulo cha Mulungu?
22 Davide anamaliza salimo lakeli ndi mawu akuti: “Ndidzagona pansi ndi kupeza tulo mu mtendere, pakuti inu nokha Yehova mumandichititsa kukhala wotetezeka.” (Sal. 4:8) Pa nthawi imene Aisiraeli ankatsatira Chilamulo cha Yehova, iwo ankakhala naye pa mtendere ndiponso ankakhala otetezeka. Mwachitsanzo, kumayambiriro kwa ulamuliro wa Solomo, ‘Ayuda ndi Aisiraeli ankakhala mwabata.’ (1 Maf. 4:25) Anthu amene ankakhulupirira Mulungu ankakhala pa mtendere ngakhale pamene anthu a mitundu yoyandikana nayo ankadana nawo. Mofanana ndi Davide, timagona mtima uli m’malo chifukwa chakuti Mulungu amatichititsa kumva kuti ndife otetezeka.
23. Kodi chingachitike n’chiyani tikamakhulupirira kwambiri Mulungu?
23 Tiyeni tipitirize kutumikira Yehova molimba mtima. Tizipempheranso ndi chikhulupiriro kuti tikhale ndi “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afil. 4:6, 7) Zimenezitu zimatithandiza kukhala osangalala kwambiri. Tikamakhulupirira kwambiri Yehova tidzakhalabe olimba mtima zivute zitani.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Davide anakumana ndi mavuto otani chifukwa cha Abisalomu?
• Kodi Salimo lachitatu limatithandiza bwanji kukhala olimba mtima?
• Kodi Salimo lachinayi lingatithandize bwanji kukhulupirira kwambiri Yehova?
• Kodi tingapindule bwanji chifukwa chokhulupirira kwambiri Mulungu?
[Chithunzi patsamba 29]
Ngakhale pamene Davide ankathawa Abisalomu, ankadziwa kuti Yehova amuthandiza
[Zithunzi patsamba 32]
Kodi mumakhulupirira Yehova ndi mtima wonse?