Pitirizani Kukhala Monga “Anthu Osakhalitsa M’dzikoli”
“Popeza ndinu alendo ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikoli, ndikukudandaulirani kuti muzipewa zilakolako za thupi.”—1 PET. 2:11.
1, 2. Kodi Petulo ankanena za ndani pamene anati “osankhidwa”? N’chifukwa chiyani ananena kuti iwo ndi “anthu osakhalitsa m’dzikoli”?
ZAKA pafupifupi 30 kuchokera pamene Yesu anapita kumwamba, mtumwi Petulo analemba kalata yopita kwa Akhristu ‘osankhidwa ndi Mulungu, amene anali alendo osakhalitsa, omwe anamwazikana ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asia, ndi ku Bituniya.’ (1 Pet. 1:1) Potchula “osankhidwa,” Petulo ankanena za anthu, ngati iyeyo, amene anadzozedwa ndi mzimu woyera. Mulungu ‘anawabereka mwatsopano kuti akhale ndi chiyembekezo cha moyo’ chodzalamulira ndi Khristu kumwamba. (Werengani 1 Petulo 1:3, 4.) Koma n’chifukwa chiyani pambuyo pake ananena kuti iwo ndi “alendo ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikoli”? (1 Pet. 2:11) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife masiku ano? Tikufunsa choncho chifukwa ndi Mboni zochepa zokha padziko lonse zimene zimanena kuti ndi odzozedwa, kapena kuti osankhidwa.
2 M’nthawi ya Petulo, mawu oti “anthu osakhalitsa m’dzikoli” anali oyenerera kwa Akhristu odzozedwa. Tikutero chifukwa chakuti iwo analidi osakhalitsa m’dzikoli, mofanana ndi mmene zilili ndi odzozedwa amene ali ndi moyo masiku ano. Mtumwi Paulo, yemwenso anali wodzozedwa wa ‘m’kagulu ka nkhosa,’ anafotokoza kuti: “Koma ife, ndife nzika zakumwamba, kumenekonso tikuyembekezera mwachidwi mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu.” (Luka 12:32; Afil. 3:20) Popeza kuti odzozedwa ndi “nzika zakumwamba,” akamwalira amachoka padzikoli n’kukakhala ndi moyo wabwino kwambiri kumwamba. Kumeneko, iwo amakalandira moyo wosafa. (Werengani Afilipi 1:21-23.) Choncho n’zomveka kutchedwa kuti “anthu osakhalitsa m’dzikoli,” lomwe Satana akulilamulira.
3. Kodi ndi funso liti lomwe tingafunse lokhudza “nkhosa zina”?
3 Koma nanga bwanji za “nkhosa zina”? (Yoh. 10:16) Kodi si zoona kuti iwo ali ndi chiyembekezo cha m’Malemba chodzakhala padzikoli kwamuyaya? Inde, adzakhaladi padzikoli mpaka kalekale. Koma panopa tinganene kuti iwonso ndi “anthu osakhalitsa m’dzikoli.” N’chifukwa chiyani tikutero?
“CHILENGEDWE CHONSE CHIKUBUULA”
4. Kodi atsogoleri a dziko sangakwanitse kuchita chiyani?
4 Pamene dziko loipa la Satanali likupitiriza kukhalapo, anthu onse, ngakhalenso Akhristu, adzapitirizabe kuvutika chifukwa cha mavuto amene anayamba pamene Satana anapandukira Yehova. Lemba la Aroma 8:22 limati: “Tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” Atsogoleri a dzikoli, asayansi ndiponso anthu ena ofuna kuthandiza anzawo alibe mphamvu zothetsa mavuto amenewa.
5. Kodi anthu ambiri asankha kuchita chiyani kuyambira mu 1914? Nanga n’chifukwa chiyani achita zimenezi?
5 M’pake kuti kuyambira mu 1914, anthu mamiliyoni asankha kumvera Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, yomwe ndi Khristu Yesu. Iwo sakufuna n’komwe kukhala mbali ya dziko la Satana loipali ndipo amakaniratu kulowerera m’zochitika zake. M’malomwake, amagwiritsa ntchito mphamvu zawo ndiponso chuma chawo kuti agwire ntchito za Ufumu wa Mulungu.—Aroma 14:7, 8.
6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mboni za Yehova ndi alendo m’dzikoli?
6 Mboni za Yehova zili m’mayiko oposa 200 ndipo ndi nzika zomvera malamulo. Koma kaya amakhala m’dziko lanji, iwo amakhala ngati alendo. Salowerera ndale kapena zinthu zina zofuna kusintha dziko la Satanali. Ngakhale panopa, iwo amaona kuti ndi nzika za dziko latsopano la Mulungu. Amasangalala kudziwa kuti nthawi yawo yokhala “anthu osakhalitsa m’dzikoli” itha posachedwapa.
7. Kodi atumiki a Mulungu adzakhala nzika za chiyani? Nanga izi zidzachitika liti?
7 Posachedwapa, Khristu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake kuwononga dziko loipa la Satanali. Boma langwiro la Khristu lidzathetseratu uchimo ndiponso kuvutika padzikoli. Lidzachotsanso aliyense wopandukira ulamuliro wa Yehova. Kenako atumiki okhulupirika a Mulungu adzatha kukhala nzika za m’Paradaiso. (Werengani Chivumbulutso 21:1-5.) Pa nthawiyi, chilengedwe chidzakhala chitamasulidwa “ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.
ZIMENE AKHRISTU OONA AYENERA KUCHITA
8, 9. Fotokozani tanthauzo la mawu a Petulo akuti “muzipewa zilakolako za thupi.”
8 Petulo anafotokoza zimene Akhristu ayenera kuchita. Iye anati: “Okondedwa, popeza ndinu alendo ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikoli, ndikukudandaulirani kuti muzipewa zilakolako za thupi zimene zili pa nkhondo yolimbana ndi moyo.” (1 Pet. 2:11) Iye anali kupereka malangizowa kwa Akhristu odzozedwa koma ndi ofunikanso kwa nkhosa zina za Yesu.
9 Zilakolako zina si zolakwika ngati timazikwaniritsa mogwirizana ndi malamulo a Mlengi wathu. Zingatithandize kusangalala ndi moyo. Mwachitsanzo, timalakalaka zakudya zabwino, zakumwa, zosangalatsa zimene zimatitsitsimula komanso kucheza ndi anthu abwino. Ngakhale chilakolako chathu cha kugonana ndi mwamuna kapena mkazi wathu ndi choyenera. (1 Akor. 7:3-5) Koma Petulo anali kulankhula za “zilakolako za thupi” zimene “zili pa nkhondo yolimbana ndi moyo.” Mabaibulo ena amasonyeza bwino zimene iye ankatanthauza. Mwachitsanzo, Baibulo la Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero limamasulira mawuwa kuti “zilakolako za uchimo.” Choncho n’zoonekeratu kuti tiyenera kusamala kwambiri ndi zilakolako zimene zimawombana ndi cholinga cha Yehova ndiponso zomwe zingasokoneze ubwenzi wathu ndi iye. Ngati sitisamala, tikhoza kuika moyo wathu pa ngozi.
10. Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira ziti kuti akope Akhristu kukhala mbali ya dzikoli?
10 Satana ali ndi cholinga cholepheretsa Akhristu oona kudzionabe monga “anthu osakhalitsa m’dzikoli.” Amafuna kuti tizikopeka ndi kufunafuna chuma, chiwerewere, kufuna kutchuka, kudzikonda kapena mzimu wokonda dziko lathu ndiponso fuko lathu. Koma tiyenera kukumbukira kuti zinthu zonsezi ndi misampha ya Satana. Tikamayesetsa kwambiri kupewa zilakolako zoipa zimenezi, timasonyeza ndi mtima wonse kuti sitikufuna kukhala mbali ya dziko loipa la Satanali. Timapereka umboni woti ndife osakhalitsa m’dzikoli. Timachita zimenezi chifukwa ndife ofunitsitsa kudzakhala nzika za dziko latsopano la Mulungu. Ndipo tikuyesetsa kwambiri kuti zimenezi zidzatheke.
KHALIDWE LABWINO
11, 12. Kodi nthawi zina anthu amaona bwanji alendo? Nanga anthu amaona bwanji Mboni za Yehova?
11 Petulo anapitiriza kufotokoza zimene Akhristu “osakhalitsa m’dzikoli” ayenera kuchita. Pa vesi 12, iye anati: “Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli, kuti pamene akukunenerani monga anthu ochita zoipa, pa mapeto pake iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zochita zanu zabwino, adzatamande Mulungu m’tsiku lake loyendera.” Nthawi zina, anthu amanenera zoipa alendo amene afika m’dziko lawo. Eni dzikolo akhoza kumaona alendowo ngati anthu oipa chifukwa chakuti amasiyana nawo. Mwachitsanzo akhoza kusiyana kalankhulidwe, kachitidwe ka zinthu, kavalidwe ngakhalenso maonekedwe. Koma alendowo akamakhala ndi khalidwe labwino, anthu amatha kuzindikira kuti iwo si anthu oipa.
12 Nawonso Akhristu amasiyana ndi anthu ena m’dzikoli. Mwachitsanzo, akhoza kusiyana nawo pa nkhani ya zolankhula kapena zosangalatsa zimene amasankha. Komanso nthawi zambiri, amaoneka osiyana ndi anzawo chifukwa cha mmene amavalira ndi kudzikongoletsera. Chifukwa cha zimenezi, anthu ena amawaona ngati oipa. Koma ena amawayamikira chifukwa cha mmene amachitira zinthu.
13, 14. Kodi mawu akuti “nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake” amatanthauza chiyani? Perekani chitsanzo.
13 N’zoona kuti khalidwe labwino lingathandize anthu kuzindikira kuti si ife anthu oipa. Ngakhale Yesu, yemwe anali wangwiro ndiponso wokhulupirika kwa Mulungu, ankaimbidwa mlandu. Anthu ena ankanena kuti iye ndi “munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa.” Koma khalidwe lake labwino potumikira Mulungu linasonyeza kuti mlanduwu unali wabodza. Yesu anati: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mat. 11:19) N’chimodzimodzinso masiku ano. Mwachitsanzo, anthu ena amaona kuti moyo wa abale ndi alongo amene amatumikira ku Beteli ku Selters m’dziko la Germany si wabwino. Koma meya wa kumeneko anaikira kumbuyo Mboni ponena kuti: “N’zoona kuti a Mboni amene amatumikira kumeneko amachita zinthu mosiyana ndi anthu ena m’derali koma sasokoneza anthu m’njira iliyonse.”
14 Chitsanzo china ndi zimene zinachitikira Mboni za Yehova mumzinda wa Moscow m’dziko la Russia. Iwo anaimbidwa milandu yabodza ingapo. Koma mu June 2010, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, limene lili mumzinda wa Strasbourg m’dziko la France, linagamula kuti: “Khotili likuona kuti [a ku Moscow] analibe mphamvu zophwanya ufulu wolambira ndiponso wosonkhana pamodzi wa [Mboni za Yehova]. Makhoti [a ku Russia] sanapereke ‘zifukwa zomveka ndiponso zokwanira’” zoti Mboni za Yehova zinali ndi mlandu wochita zinthu monga kusokoneza mabanja, kuchititsa anthu kudzipha kapena kukana chithandizo cha kuchipatala. Choncho “makhotiwa anagwiritsa ntchito malamulo awo okhwima kuti apereke chilango chopitirira malire. Komanso chilangocho chinali chosayenera chifukwa sanapeze umboni wa milandu imene anasumiridwa.”
KUGONJERA KOYENERA
15. Kodi Akhristu oona padziko lonse amatsatira mfundo iti ya m’Baibulo?
15 Petulo anafotokozanso mfundo ina yofunika kwa Akhristu yomwe Mboni za Yehova ku Moscow ndiponso padziko lonse zimatsatira. Iye analemba kuti: “Chifukwa cha Ambuye, gonjerani dongosolo lililonse lopangidwa ndi anthu: kaya mfumu chifukwa ili ndi udindo waukulu, kapena nduna.” (1 Pet. 2:13, 14) N’zoona kuti Akhristu oona sali mbali ya dziko loipali. Koma amatsatira ndi mtima wonse malangizo a Paulo akuti azigonjera maboma pamene malamulo awo sakusemphana ndi a Mulungu.—Werengani Aroma 13:1, 5-7.
16, 17. (a) N’chiyani chimasonyeza kuti sitilimbana ndi maboma? (b) Kodi atsogoleri ena andale avomereza za chiyani?
16 Mboni za Yehova zimakhala monga “anthu osakhalitsa m’dzikoli.” Koma sizichita zimenezi chifukwa chofuna kulimbana ndi boma kapena anthu ena. Iwo amalemekeza ufulu wa anthu ena wosankha zochita pa nkhani zandale kapena zinthu zina. Mosiyana ndi zipembedzo zina, Mboni za Yehova sizilowerera ndale. Iwo sayesa kukakamiza olamulira kuti asinthe mmene amalamulirira. Sangayerekeze n’komwe kupandukira boma kapena kulimbikitsa anthu ena kuchita zimenezi.
17 Akhristu amamvera atsogoleri a boma potsatira malangizo a Petulo akuti ‘azilemekeza mfumu.’ Choncho amapatsa atsogoleriwo ulemu wogwirizana ndi udindo wawo. (1 Pet. 2:17) Pali olamulira ena amene anenapo mawu osonyeza kuti amadziwa zoti Mboni za Yehova sizingasokoneze zinthu m’dziko. Mwachitsanzo, wandale wina wa ku Germany anati: “Makhalidwe a Mboni za Yehova pamene anali m’ndende anali abwino ndiponso ofunika kwambiri pa nthawiyo komanso masiku ano m’mayiko a demokalase ngati kuno. Iwo anali olimba mtima pokana kugonjera asilikali a chipani cha Nazi komanso ankachitira chifundo akaidi anzawo. Masiku ano, anthu ambiri amachitira nkhanza alendo ndiponso anthu ena amene amasiyana nawo maganizo pa nkhani monga zandale. Choncho makhalidwe amene a Mboniwo anasonyeza ndi ofunika kwambiri kwa nzika iliyonse m’dziko lathuli.”
KUKONDA ENA
18. (a) N’chifukwa chiyani timakonda gulu lonse la abale? (b) Kodi anthu ena anenapo chiyani zokhudza Mboni za Yehova?
18 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Kondani gulu lonse la abale, opani Mulungu.” (1 Pet. 2:17) Mboni za Yehova zimaopa kukhumudwitsa Mulungu choncho zimayesetsa kuchita zofuna zake. Iwo amasangalala kutumikira Yehova limodzi ndi abale ndi alongo ena padziko lonse omwe amafunanso kusangalatsa Mulungu. Choncho iwo amakonda “gulu lonse la abale.” Koma anthu ambiri m’dzikoli sakondana. Chotero, anthu ena akaona Mboni zikukondana, amadabwa. Mwachitsanzo, munthu wina wotsogolera alendo, yemwe ankagwira ntchito pa kampani ya ku America yokonza za maulendo, anadabwa ndi zimene anaona ku Germany mu 2009 pa nthawi ya msonkhano wamayiko. Iye anaona kuti Mboni za Yehova zinkalandira mwachikondi ndiponso kuthandiza alendo ochokera kumayiko ena omwe anabwera kudzakhala nawo pa msonkhanowo. Ananenanso kuti pa zaka zonse zimene wakhala akugwira ntchitoyi, sanaonepo chikondi ngati chimenechi. Pofotokoza za wotsogolera alendo uja, m’bale wina anati: “Zimene iye ananena zokhudza ifeyo zinasonyeza kuti iye ankasangalala ndiponso kugoma nafe.” Kodi inunso mwaonapo anthu pa msonkhano amene anadabwa ndi mmene Mboni zimachitira zinthu?
19. Kodi tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
19 Monga taonera, Mboni za Yehova zimasonyeza m’njira zambiri kuti ndi “anthu osakhalitsa m’dzikoli.” Iwo ndi osangalala ndiponso ofunitsitsa kupitirizabe kuchita zimenezi. Zili choncho chifukwa chakuti ali ndi chiyembekezo champhamvu komanso chotsimikizika kuti posachedwapa, adzakhala nzika za dziko latsopano la Mulungu. Kodi inunso mukuyembekezera zimenezi?