“Dziwani Kuti Ine Ndili Pamodzi ndi Inu Masiku Onse”
“Dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.”—MAT. 28:20.
1. (a) Fotokozani mwachidule fanizo la tirigu ndi namsongole. (b) Kodi Yesu anati fanizoli likutanthauza chiyani?
FANIZO lina la Yesu lofotokoza za Ufumu wa Mulungu limanena za munthu amene anafesa mbewu zabwino za tirigu m’munda wake koma kenako mdani wake anafesamo namsongole. Namsongoleyo anachuluka kwambiri m’mundamo koma munthuyo anauza akapolo ake kuti: “Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola.” Nthawi yokolola itafika, namsongoleyo anawonongedwa ndipo tirigu anasonkhanitsidwa m’nkhokwe. Ndiyeno Yesu anafotokoza tanthauzo la fanizoli. (Werengani Mateyu 13:24-30, 37-43.) Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo limeneli? (Onani bokosi lakuti “Tirigu ndi Namsongole.”)
2. (a) Kodi zimene zinachitika m’munda wa tirigu zikuimira chiyani? (b) Kodi m’nkhani ino tikambirana za chiyani?
2 Zimene zinachitika m’mundawu zikutithandiza kudziwa nthawi yosonkhanitsa tirigu ndiponso mmene Yesu akuchitira zimenezi. Tiriguyu akuimira Akhristu odzozedwa amene adzalamulire limodzi ndi Khristu mu Ufumu wake. Ntchito yofesa inayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. Koma Yesu adzamaliza kusonkhanitsa tirigu pamene odzozedwa omwe adzakhale moyo pamapeto a dzikoli adzadindidwa chidindo chomaliza kenako n’kupita kumwamba. (Mat. 24:31; Chiv. 7:1-4) Fanizoli limafotokoza zinthu zimene ziyenera kuchitika pa zaka pafupifupi 2,000. Munthu amene wamvetsa fanizoli amakhala ngati wakwera paphiri ndipo akuona bwinobwino dera lonse lozungulira. Kodi fanizoli lingatithandize kumvetsa zinthu ziti zokhudza Ufumu? Fanizoli limanena za nthawi yofesa mbewu, nthawi imene zikukula ndiponso nthawi yokolola. Koma m’nkhani ino tikambirana kwambiri za nthawi yokolola.a
YESU WAKHALA AKUWATETEZA
3. (a) N’chiyani chinachitika atumwi onse atamwalira? (b) Kodi pa lemba la Mateyu 13:28 pali funso lotani ndipo ndani analifunsa? (Onaninso mawu akumapeto.)
3 Patangopita zaka zingapo atumwi onse atamwalira, ‘namsongole anaonekera’ m’munda. Izi zinachitika Akhristu onyenga atayamba kuonekera padzikoli. (Mat. 13:26) Patapita zaka pafupifupi 200 atumwi onse atamwalira, Akhristu okhala ngati namsongole anali atachuluka kwambiri kuposa Akhristu odzozedwa. Kumbukirani kuti m’fanizo lija, akapolo anafunsa mbuye wawo ngati akufuna kuti akazule namsongoleyo.b (Mat. 13:28) Kodi mbuyeyo anawayankha bwanji?
4. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa yankho la Yesu? (b) Kodi Akhristu okhala ngati tirigu anayamba liti kuonekera?
4 Ponena za tirigu ndi namsongole, Yesu anati: “Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola.” Mawu amenewa akusonyeza kuti kuyambira m’nthawi ya atumwi mpaka masiku ano, nthawi zonse padzikoli pakhala Akhristu odzozedwa omwe ali ngati tirigu. Yesu anatsimikizira zimenezi pamene anauza ophunzira ake kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Choncho Yesu wakhala akuteteza Akhristu odzozedwa masiku onse mpaka nthawi ya mapeto. Koma popeza kuti Akhristu okhala ngati namsongole anali atachuluka kwambiri, sitikudziwa bwinobwino anthu amene anali m’gulu la tirigu pa nthawiyo. Koma kutatsala zaka zochepa kuti nthawi yokolola ifike, tirigu anayamba kuonekera. Kodi zimenezi zinachitika bwanji?
‘MTHENGA ANAKONZA NJIRA’
5. Kodi ulosi wa Malaki unakwaniritsidwa bwanji pamene Yesu anali padzikoli?
5 Zaka zambiri Yesu asananene fanizo la tirigu ndi namsongole, Yehova anauza mneneri Malaki kuti alosere zinthu zina zimene zikugwirizananso ndi fanizoli. (Werengani Malaki 3:1-4.) Yohane M’batizi anali ‘mthenga amene anakonza njira.’ (Mat. 11:10, 11) Pamene iye ankayamba ntchito yake mu 29 C.E., mtundu wa Isiraeli unali utatsala pang’ono kuweruzidwa. Yesu anali mthenga wachiwiri. Iye anayeretsa kawiri kachisi ku Yerusalemu. Anachita zimenezi atangoyamba utumiki wake komanso chakumapeto kwa utumikiwo. (Mat. 21:12, 13; Yoh. 2:14-17) Choncho Yesu anagwira ntchito yoyeretsayi kwa nthawi ndithu.
6. (a) Kodi ulosi wa Malaki unakwaniritsidwa m’njira yaikulu iti? (b) Kodi Yesu anayendera kachisi wauzimu pa nthawi iti? (Onaninso mawu akumapeto.)
6 Koma ulosi wa Malaki unakwaniritsidwanso m’njira yaikulu. Kwa zaka zambiri chaka cha 1914 chisanafike, C. T. Russell ndi anzake anagwira ntchito yofanana ndi ya Yohane M’batizi. Iwo anayamba kuphunzitsanso mfundo zoona za m’Baibulo. Ophunzira Baibulo amenewa ankaphunzitsa tanthauzo lenileni la nsembe ya dipo ya Khristu, ankasonyeza kuti anthu sakawotchedwa kumoto ndiponso ankalengeza kuti nthawi za anthu amitundu ina zatsala pang’ono kutha. Komabe pa nthawiyo, panali magulu ambiri azipembedzo amene ankati ndi otsatira a Khristu. Choncho funso lofunika kwambiri linali lakuti: Pamagulu amenewo, kodi ndi ndani amene anali tirigu? Kuti tirigu adziwike, Yesu anayamba kuyendera kachisi wauzimu mu 1914. Ntchito yoyendera ndi kuyeretsayi inatenga nthawi ndithu chifukwa inayamba mu 1914 n’kutha chakumayambiriro kwa 1919.c
ZAKA ZIMENE ANAYENDERA NDIPONSO KUYERETSA
7. Kodi Yesu atayamba kuyendera kachisi wauzimu mu 1914, anapeza zotani?
7 Kodi Yesu atayamba kuyendera kachisi wauzimu, anapeza zotani? Anapeza kagulu ka Ophunzira Baibulo amene ankalalikira mwakhama ndipo ankagwiritsa ntchito zinthu zawo pa ntchitoyi. Kaguluka kanali katachita zimenezi kwa zaka zoposa 30.d Yesu ndi angelo ayenera kuti anasangalala kwambiri atapeza kagulu kamene kanali ngati tirigu wamphamvu yemwe sanafe chifukwa chopanikizidwa ndi namsongole amene Satana anafesa. Komabe panafunika ‘kuyeretsa ana a Levi’ omwe akuimira Akhristu odzozedwa. (Mal. 3:2, 3; 1 Pet. 4:17) N’chifukwa chiyani zimenezi zinali zofunika?
8. Kodi ndi zinthu zotani zimene zinachitika chaka cha 1914 chitadutsa?
8 Chakumapeto kwa 1914, Ophunzira Baibulo ena anakhumudwa chifukwa chakuti sanapite kumwamba. Ndiyeno mu 1915 ndi 1916 anthu omwe ankatsutsa Ophunzira Baibulo anachititsa kuti ntchito yolalikira isamayende bwino. Kenako zinthu zinavuta kwambiri M’bale Russell atamwalira mu October 1916. Abale ena anayambitsa mavuto m’gululi. Abale 4, amene anali m’gulu la abale 7 omwe ankayendetsa bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society, sanagwirizane ndi zoti M’bale Rutherford alowe m’malo mwa M’bale Russell. Iwo anayesetsa kuti agawanitse abale. Koma mu August 1917, anthu amenewa anachoka pa Beteli. Apatu gulu linayeretsedwadi. Komanso, Ophunzira Baibulo ena anafooka chifukwa choopa anthu. Komabe, abale ambiri anavomereza kuti Yesu awayeretse ndipo anasintha zina ndi zina zomwe zinali zofunikira. Choncho Yesu poweruza, ananena kuti iwo ndi Akhristu oona omwe ali ngati tirigu. Koma anakana anthu onse amene ankanamizira kuti ndi Akhristu, kuphatikizapo onse a m’matchalitchi onyenga. (Mal. 3:5; 2 Tim. 2:19) Ndiyeno n’chiyani chinachitika? Kuti tipeze yankho, tiyeni tionenso fanizo la tirigu ndi namsongole lija.
ZIMENE ZIYENERA KUCHITIKA M’NYENGO YOKOLOLA
9, 10. (a) Kodi tikambirana zinthu ziti zokhudza nyengo yokolola? (b) N’chiyani chinachitika kumayambiriro kwa nyengo yokolola?
9 Yesu ananena kuti “nthawi yokolola ikuimira mapeto a nthawi ino.” (Mat. 13:39) Nthawi yokololayi inayamba mu 1914. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zisanu zimene Yesu analosera kuti zichitika m’nthawi yokololayi.
10 Choyamba ndi kusonkhanitsa namsongole. Yesu anati: “M’nyengo yokolola ndidzauza okololawo kuti, Choyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga m’mitolo.” Chaka cha 1914 chitadutsa, angelo anayamba ‘kusonkhanitsa’ Akhristu omwe anali ngati namsongole powasiyanitsa ndi Akhristu odzozedwa, omwe ndi “ana a ufumu.”—Mat. 13:30, 38, 41.
11. N’chiyani chimasiyanitsa Akhristu oona ndi Akhristu onyenga?
11 Pamene ntchito yosonkhanitsa inkapitirira, kusiyana kwa magulu awiriwa kunayamba kuonekera bwino. (Chiv. 18:1, 4) Pofika mu 1919, zinali zoonekeratu kuti Babulo Wamkulu wagwa. Koma kodi n’chiyani chimene chinasiyanitsa kwambiri Akhristu oona ndi onyenga? Inali ntchito yolalikira. Abale amene ankatsogolera m’gulu la Ophunzira Baibulo anayamba kutsindika kwambiri zoti aliyense ayenera kugwira nawo ntchitoyi. Mwachitsanzo, mu 1919 panatuluka kabuku kolimbikitsa Akhristu onse odzozedwa kuti azilalikira kunyumba ndi nyumba. M’kabukuka munali mawu akuti: “Ntchitoyi ikuoneka kuti ndi yaikulu kwambiri. Komabe mwiniwake ndi Ambuye ndipo atithandiza kuti tiikwanitse. Inuyo muli ndi mwayi wogwira nawo ntchitoyi.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Nsanja ya Olonda ya 1922 inanena kuti kungoyambira nthawi imeneyo, Ophunzira Baibulo anayamba kugwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri. Pasanapite nthawi, Akhristu okhulupirikawo ankadziwika ndi ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba, ndipo zili choncho mpaka masiku ano.
12. Kodi ntchito yosonkhanitsa tirigu inayamba liti?
12 Chachiwiri ndi kusonkhanitsa tirigu. Yesu analamula angelo ake kuti: “Mupite kukasonkhanitsa tirigu ndi kumuika m’nkhokwe yanga.” (Mat. 13:30) Kuyambira mu 1919, odzozedwa akhala akusonkhanitsidwa mumpingo wachikhristu womwe unayeretsedwa. Akhristu odzozedwa amene adzakhalebe ndi moyo pamapeto a dzikoli, adzasonkhanitsidwa komaliza pamene adzalandire mphoto yawo kumwamba.—Dan. 7:18, 22, 27.
13. Kodi lemba la Chivumbulutso 18:7 likusonyeza kuti panopa hule, kapena kuti Babulo Wamkulu, kuphatikizapo matchalitchi amene amati ndi achikhristu, akutani?
13 Chachitatu ndi kulira ndi kukukuta mano. Kodi anthu okhala ngati namsongole akadzamangidwa m’mitolo chidzawachitikire n’chiyani? Yesu ananena kuti: “Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.” (Mat. 13:42) Kodi zimenezi zikuchitika panopa? Ayi. Matchalitchi amene amati ndi achikhristu, omwe ndi mbali ya hule, akunenabe kuti: “Ine ndine mfumukazi. Sindine mkazi wamasiye, ndipo sindidzalira ngakhale pang’ono.” (Chiv. 18:7) N’zoona kuti matchalitchi amenewa akudziona kuti ndi amphamvu ndipo ali ngati mfumukazi yolamulira atsogoleri andale. Masiku ano, anthu amene ali ngati namsongole sakulira koma akudzitama. Komabe zinthu zisintha posachedwapa.
14. (a) Kodi mawu akuti Akhristu onyenga ‘adzakukuta mano awo’ akutanthauza chiyani, ndipo zidzachitika liti? (b) Kodi zimene tafotokoza zokhudza lemba la Mateyu 13:42 zikugwirizana bwanji ndi mfundo ya pa Salimo 112:10? (Onani mawu akumapeto.)
14 Pa chisautso chachikulu, zipembedzo zonse zonyenga zikadzawonongedwa, anthu onse amene ankagwirizana nazo adzayesa kubisala koma sadzapeza malo. (Luka 23:30; Chiv. 6:15-17) Iwo adzazindikira kuti awonongedwa basi chifukwa sangathe kuthawa. Pa nthawi imeneyi, adzalira chifukwa chosowa mtengo wogwira ndipo ‘adzakukuta mano’ chifukwa chokwiya. Mu ulosi wake wonena za chisautso chachikulu, Yesu ananena kuti zinthu zikadzawathina chonchi, “adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni.”e—Mat. 24:30; Chiv. 1:7.
15. Kodi n’chiyani chidzachitikire namsongole, ndipo zidzachitika liti?
15 Chachinayi ndi kuponyedwa m’ng’anjo yamoto. Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu omwe ali ngati mitolo ya namsongole? Angelo “adzawaponya m’ng’anjo yamoto.” (Mat. 13:42) Zimenezi zikutanthauza kuti adzawonongedweratu. Choncho, anthu onse amene ankagwirizana ndi zipembedzo zonyenga adzawonongedwa pa Aramagedo, yomwe ndi mbali yomaliza ya chisautso chachikulu.—Mal. 4:1.
16, 17. (a) Kodi Yesu anamaliza fanizo lake ndi mawu ati? (b) N’chifukwa chiyani tikunena kuti mawu amenewo adzakwaniritsidwa m’tsogolo?
16 Chachisanu ndi kuwala kwambiri. Yesu anamaliza ulosi wake ndi mawu akuti: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambiri ngati dzuwa mu ufumu wa Atate wawo.” (Mat. 13:43) Kodi iwo adzawala liti ndiponso kuti? Ulosi umenewu udzakwaniritsidwa m’tsogolo muno. Apa Yesu analosera zinthu zimene zidzachitike kumwamba osati zimene zikuchitika masiku ano padziko lapansi.f Tikutero pa zifukwa ziwiri.
17 Chifukwa choyamba chikukhudza nthawi. Yesu anati: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambiri.” Mawu a Yesu akuti “pa nthawi imeneyo,” ayenera kuti akunena za nthawi ya zinthu zimene anali atangotchula kumene. Iye anali atangonena kumene za ‘kuponya namsongole m’ng’anjo yamoto.’ Zimenezi zidzachitika kumapeto kwa chisautso chachikulu. Choncho odzozedwa “adzawala kwambiri” pa nthawi imeneyo. Chifukwa chachiwiri chikukhudza malo. Yesu ananena kuti olungama ‘adzawala kwambiri mu ufumu.’ Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Akhristu onse odzozedwa amene adzakhalebe padzikoli mbali yoyamba ya chisautso chachikulu itatha adzakhala atadindidwa kale chidindo chomaliza. Kenako, malinga ndi ulosi wa Yesu wonena za chisautso chachikulu, iwo adzasonkhanitsidwa kumwamba. (Mat. 24:31) Kumwambako n’kumene adzawale “mu ufumu wa Atate wawo.” Ndiyeno nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, iwo adzasangalala kwambiri kukhala m’gulu la mkwatibwi pa “ukwati wa Mwanawankhosa.”—Chiv. 19:6-9.
KODI KUMVETSA ZIMENEZI KWATITHANDIZA BWANJI?
18, 19. Kodi kumvetsa tanthauzo la fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole kwatithandiza bwanji?
18 Kodi kumvetsa tanthauzo la fanizo la Yesu limeneli kwatithandiza bwanji? Kwatithandiza m’njira zitatu. Choyamba, tawonjezera zimene timadziwa. Fanizoli likusonyeza chifukwa china chachikulu chimene Yehova walolera kuti zoipa zizichitika. Iye walekerera “ziwiya za mkwiyo” pofuna kukonza “ziwiya zachifundo” zomwe zikuimira tirigu.g (Aroma 9:22-24) Chachiwiri, kwatithandiza kuti chikhulupiriro chathu chilimbe. Pamene mapeto akuyandikira, adani athu adzalimbana nafe kwambiri “koma sadzapambana.” (Werengani Yeremiya 1:19.) Kwa zaka zambirimbiri, Yehova wakhala akuteteza Akhristu odzozedwa. Ifenso Atate wathu wakumwamba akugwiritsa ntchito Yesu pamodzi ndi angelo kuti akhale nafe “masiku onse.”—Mat. 28:20.
19 Chachitatu, fanizoli latithandiza kudziwa Akhristu omwe ali ngati tirigu. Kudziwa Akhristu amenewa n’kofunika kwambiri chifukwa kungatithandize kupeza yankho la funso limene Yesu anafunsa mu ulosi wake wonena za masiku otsiriza. Iye anafunsa kuti: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?” (Mat. 24:45) Nkhani ziwiri zotsatira zidzayankha bwinobwino funso limeneli.
a Ndime 2: Kuti mukumbukire tanthauzo la mbali zina za fanizoli, tikukulimbikitsani kuti muwerenge nkhani yakuti “Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2010.
b Ndime 3: Popeza atumwi a Yesu anali atamwalira ndipo odzozedwa amene anatsala padzikoli ankaimiridwa ndi tirigu, akapolo amenewa akuimira angelo. Komanso m’fanizo lomweli Yesu ananena kuti osonkhanitsa namsongole ndi angelo.—Mat. 13:39.
c Ndime 6: Zimenezi zikusintha zimene tinkakhulupirira m’mbuyomu. Poyamba tinkakhulupirira kuti Yesu anabwera kudzayendera mu 1918.
d Ndime 7: Kuyambira mu 1910 kufika mu 1914, Ophunzira Baibulo anagawira mabuku pafupifupi 4,000,000 ndi timapepala toposa 200,000,000.
e Ndime 14: Izi zikusintha zimene tinkakhulupirira pa lemba la Mateyu 13:42. Poyamba, tinkafotokoza m’mabuku athu kuti Akhristu onyenga akhala ‘akulira ndi kukukuta mano’ kwa zaka zambiri chifukwa chakuti “ana a ufumu” akuwaulula kuti ndi “ana a woipayo.” (Mat. 13:38) Komabe Baibulo limasonyeza kuti nthawi imene anthu adzakukute mano m’pamene adzawonongedwa.—Sal. 112:10.
f Ndime 16: Lemba la Danieli 12:3 limanena kuti “Anthu ozindikira [Akhristu odzozedwa] adzawala ngati kuwala kwa kuthambo.” Pamene iwo ali padziko lapansi, amawala akamagwira ntchito yolalikira. Komabe, lemba la Mateyu 13:43 limatchula nthawi imene adzawale kwambiri mu Ufumu wakumwamba. M’mbuyomu, tinkakhulupirira kuti malemba onse awiriwa akunena za ntchito yolalikira.
g Ndime 18: Onani buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, tsamba 288 ndi 289.