Simungatumikire Ambuye Awiri
“Kapolo sangatumikire ambuye awiri . . . Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”—MAT. 6:24.
1-3. (a) Kodi mabanja ambiri amakumana ndi mavuto ati? (b) Nanga ena amatani pofuna kuthana ndi mavutowo? (Onani chithunzi pamwambapa.) (c) Kodi ndi mavuto ati amene amakhalapo pa nkhani yolera ana ngati makolo atapita kunja?
MLONGO wina dzina lake Marilyna anati: “Amuna anga ankabwera kuntchito atatoperatu koma ndalama zimene ankalandira zinali zochepa. Ndiye ndinkafuna kuwathandiza komanso kugulira mwana wanga Jimmy zinthu zimene anzake akusukulu anali nazo.” Mlongoyu ankafunanso kuti azithandiza abale ake komanso asunge ndalama zina kuti adzagwiritse ntchito m’tsogolo. Anzake ambiri anali atapita kumayiko akunja kukasaka ndalama. Koma pamene iye ankaganiza zopita kunjako, ankakayikakayika. N’chifukwa chiyani ankakayika?
2 Marilyn ankada nkhawa akaganiza zoti asiyane ndi banja lake komanso zoti asiye kuchitira limodzi zinthu zokhudza kulambira. Koma ankaona kuti pali anthu ena amene anachoka ndipo mabanja awo akuchita bwino mumpingo. Iye ankadzifunsanso kuti, ‘Koma ndikapita kunja Jimmy akula bwino?’ Ankaona kuti n’zovuta kulera mwana wakeyo ‘m’malangizo a Yehova ndi kumuphunzitsa kaganizidwe kake’ kudzera pa Intaneti.—Aef. 6:4.
3 Marilyn anayamba kufufuza malangizo. Mwamuna wake ananena kuti sangakonde kuti apite kunja koma sangamuletse kupita. Akulu, komanso abale ndi alongo ena, anamuuza kuti asapite koma panali alongo ena angapo amene ankamulimbikitsa kuti apite. Alongowo ankati: “Ngati umakondadi banja lako upite basi. Sikuti usiya kutumikira Yehova.” Ngakhale kuti ankakayikakayika, Marilyn anatsanzika mwamuna wake ndi mwana wakeyo n’kupita kunja kukagwira ntchito. Ponyamukapo anati: “Ndibwerera posachedwa.”
TSATIRANI MFUNDO ZA M’BAIBULO POSAMALIRA BANJA LANU
4. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena amapita kunja? (b) Kodi ndi ndani amene amakhala ndi udindo wosamalira ana awo?
4 Yehova samafuna kuti atumiki ake akhale pa umphawi wadzaoneni, ndipo kuyambira kale anthu akhala akusamukira kwina chifukwa cha umphawi. (Sal. 37:25; Miy. 30:8) Pa nthawi ya njala, Yakobo anatuma ana ake kuti apite ku Iguputo kukagula chakudya.b (Gen. 42:1, 2) Masiku ano, anthu ambiri amene amapita m’mayiko ena, samapita chifukwa cha njala. Ena amapita kuti abweze ngongole. Komanso ena amangofuna kukhala ndi moyo wapamwamba. Pofuna kukwaniritsa zolinga zimenezi, anthu ena amasiya mabanja awo n’kupita kudziko lina kapena m’dera lina m’dziko lawo lomwelo. Nthawi zambiri anthuwa amasiya udindo wosamalira ana m’manja mwa kholo limodzi, mwana wamkulu, agogo, achibale kapena anzawo. Ngakhale kuti anthuwa amamva chisoni kusiya mabanja awo, amadzikhululukira n’kumati sangachitire mwina koma kupita basi.
5, 6. (a) Kodi Yesu anati anthu angapeze bwanji chimwemwe? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene Yesu anauza otsatira ake kuti azipempha? (c) Kodi Yehova amatidalitsa bwanji?
5 M’nthawi ya Yesu, anthu ambiri analinso osauka, ndipo ayenera kuti ankaganiza kuti angakhale osangalala ngati akanakhala ndi ndalama zambiri. (Maliko 14:7) Koma Yesu ankafuna kuti anthuwo azidalira Yehova yemwe amapereka chuma chosatha. Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anafotokoza kuti chimwemwe chenicheni sichimapezeka chifukwa chokhala ndi chuma kapena zimene ifeyo tingachite koma chifukwa chokhala pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba.
6 M’pemphero la chitsanzo, Yesu sanatiphunzitse kuti tizipempha chuma koma anati tizipempha “chakudya chathu chalero,” kutanthauza zofunika za tsiku ndi tsiku. Iye anapereka malangizo osapita m’mbali akuti: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi . . . Koma unjikani chuma chanu kumwamba.” (Mat. 6:9, 11, 19, 20) Tizikhulupirira kuti Yehova adzatidalitsa monga mmene amalonjezera. Sikuti iye amangosangalala mumtima mwake akaona tikumumvera koma amatipatsa zimene timafuna. Choncho kuti tipeze chimwemwe chenicheni tiyenera kudalira Atate wathu wachikondi osati ndalama.—Werengani Mateyu 6:24, 25, 31-34.
7. (a) Kodi Yehova wapereka kwa ndani udindo wolera ana? (b) N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuthandizana kulera ana awo?
7 Munthu amene ‘amafunafuna choyamba chilungamo cha Mulungu,’ amaona udindo wake m’banja mmene Mulungu amauonera. Mu Chilamulo cha Mose muli mfundo imene Akhristu ayenera kuitsatira. Mfundo yake ndi yakuti makolo ayenera kuphunzitsa ana awo za Yehova. (Werengani Deuteronomo 6:6, 7.) Mulungu anapereka udindo umenewu kwa makolo osati kwa agogo kapena wina aliyense. Mfumu Solomo ananena kuti: “Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.” (Miy. 1:8) Apa Yehova ankatanthauza kuti makolo onse awiri ayenera kuthandizana kuphunzitsa ana awo. (Miy. 31:10, 27, 28) Nthawi zambiri ana amaphunzira za Yehova akamamva makolo awo akukambirana kapena akamaona zochita zawo.
MAVUTO AMENE AMAKHALAPO
8, 9. (a) Kodi chimachitika n’chiyani ngati makolo apita kukagwira ntchito kunja? (b) Kodi ndi mavuto ena ati amene amabwera ngati munthu wasiyana ndi banja lake?
8 Anthu ambiri asanapite kunja amaganizira ubwino ndi kuipa kwake koma pali mavuto ena amene sawaganizira. (Miy. 22:3)c Marilyn amene tamutchula uja atangopita kunja, anayamba kulisowa banja lake koopsa. Nayenso mwamuna wake ndi mwana wake ankamusowa kwambiri. Jimmy ankangokhalira kumufunsa kuti, “Amayi, n’chifukwa chiyani mwandithawa?” Poyamba ankaganiza kuti akhala miyezi yochepa koma anakhala zaka zingapo. Kenako anadabwa kuona kuti zinthu zayamba kusintha. Anaona kuti Jimmy wasintha kwambiri moti sankakondanso mayi akewo kapena kuwauza maganizo ake ngati poyamba. Marilyn ananena modandaula kuti, “Mwana wanga sandikondanso.”
9 Makolo akasiyana ndi ana awo, chikondi chimayamba kuchepa ndipo makhalidwe a anawo amasokonekera.d Ana akasiyidwa ali aang’ono, makolowo n’kukhala kwina kwa nthawi yaitali mavuto amene amakhalapo amakhalanso aakulu kwambiri. Marilyn ankauza Jimmy kuti wapita kunjako n’cholinga choti amuthandize, koma Jimmy ankaona kuti mayi akewo amuthawa. Jimmy ankadandaula kwambiri chifukwa cha kuchoka kwa mayi akewo. Koma akabwera kudzamuona sankasangalala nawonso. Jimmy ankaona kuti zimene mayi akewo akuchita si zabwino ndipo si oyenera kuwamvera kapena kuwakonda. Umutu ndi mmene ana ambiri amene asiyidwa amamvera.—Werengani Miyambo 29:15.
10. (a) Kodi ana amavutika bwanji ngati makolo ali kwina n’kumangotumiza mphatso? (b) Kodi makolo amene ali kutali sangathe kuchitira ana awo zinthu ziti?
10 Marilyn ankayesa kutumiza ndalama komanso mphatso koma anazindikira kuti zimenezi zinali zosakwanira kwa mwana wakeyo. Iye mosazindikira ankaphunzitsa mwanayo kuti aziona chuma kukhala chofunika kwambiri kuposa ubwenzi ndi Mulungu komanso ndi anthu a m’banja lake. (Miy. 22:6) Nthawi zina, Jimmy ankanena kuti: “Mayi, olo musadzabwerenso. Muzingotumiza mphatsozo basi.” Marilyn anazindikira kuti n’zosatheka kulera bwinobwino mwana wake kudzera pa Intaneti, makalata kapena mafoni. Iye anati: “N’zosatheka kukumbatira mwana wako pa Intaneti.”
11. (a) Kodi banja limakumana ndi mavuto ati ngati wina wapita kunja kukagwira ntchito? (b) Kodi n’chiyani chinathandiza mlongo wina kuzindikira kuti ayenera kubwerera kwawo?
11 Ubwenzi wa Marilyn ndi Yehova komanso ndi mwamuna wake unayamba kusokonekeranso. Mipata yopita ku misonkhano komanso mu utumiki inayamba kuchepa ndipo abwana ake ankamuvutitsa kuti agone naye. Marilyn ndi mwamuna wake analibe munthu woti azimufotokozera zakukhosi akakumana ndi mavuto. Choncho anayamba kucheza ndi anthu olakwika moti anangotsala pang’ono kuchita chigololo. Marilyn anazindikira kuti ngakhale kuti sanachite chigololo, iwo analephera kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti azilimbikitsana komanso kupatsana mangawa. Zinali zosatheka kuti akaona zosangalatsa aziuzana nthawi yomweyo, kapena kusekererana komanso kusonyezana chikondi m’njira zosiyanasiyana. (Nyimbo 1:2; 1 Akor. 7:3, 5) Sakanathanso kulambira Yehova limodzi ndi mwana wawo. Marilyn anati: “Nditamva pa msonkhano wachigawo kuti Kulambira kwa Pabanja n’kofunika kwambiri kuti tidzapulumuke, ndinaona kuti ndi bwino kubwerera. Ndinafunika kukonzanso ubwenzi wanga ndi Yehova komanso ndi banja langa.”
MALANGIZO ENA NDI ABWINO KOMA ENA NDI OIPA
12. Kodi ndi malangizo ati a m’Malemba omwe angathandize anthu amene asiya mabanja awo chifukwa cha ntchito?
12 Marilyn ataganiza zobwerera kwawo anthu ena sanasangalale nazo. Akulu a mumpingo umene ankasonkhana anamuyamikira chifukwa cha chikhulupiriro komanso kulimba mtima kwake. Koma abale ndi alongo ena amene nawonso anasiya mabanja awo, sanasangalale ndi zomwe Marilyn anasankhazi. M’malo motengera chitsanzo chakechi iwo anayamba kulankhula zomufooketsa. Iwo anamuuza kuti: “Iwetu tikuona ukubweranso posachedwapa. Ukuganiza kuti uzikapeza bwanji ndalama kumudziko?” M’malo molankhula mawu ofooketsa ngati amenewa, Akhristu ayenera kulimbikitsa “akazi achitsikana kukonda amuna awo, kukonda ana awo, kukhala . . . ogwira ntchito zapakhomo,” kutanthauza panyumba pawo, “kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.”—Werengani Tito 2:3-5.
13, 14. N’chifukwa chiyani pamafunika chikhulupiriro cholimba kuti munthu amvere Mulungu osati anthu? Perekani chitsanzo.
13 Anthu ambiri amene amapita kukagwira ntchito m’mayiko ena amakhala m’madera amene anthu amaona kuti kupezera banja komanso makolo zinthu n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse. Choncho kuti Mkhristu asatengere zimenezi, n’kuchita zimene zingasangalatse Yehova, amafunika kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.
14 Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Carin. Iye anati: “Pamene mwana wathu Don ankabadwa, ine ndi mwamuna wanga tinkagwira ntchito kunja. Ndipo ndinali nditangoyamba kumene kuphunzira Baibulo. Achibale anga onse ankafuna kuti ndim’tumize Don kumudzi kukakhala ndi makolo anga mpaka titapeza ndalama zokwanira.” Koma Carin atakana kuchita zimenezi achibale akewo, kuphatikizapo mwamuna wake, anamuseka kwambiri ndipo ankamunena kuti ndi waulesi. Carin anati: “Kunena zoona, pa nthawiyo sindinkadziwa bwinobwino mavuto amene angakhalepo chifukwa cholola kuti Don akakhale ndi makolo anga kwa zaka zochepa. Koma zomwe ndinkadziwa n’zakuti Yehova anapereka udindo wolera ana kwa makolo.” Carin atakhalanso woyembekezera, mwamuna wake yemwe sanali Mboni anamulimbikitsa kuti achotse mimbayo. Zomwe Carin anachita poyamba paja, zinalimbitsa chikhulupiriro chake moti pa nkhaniyi anamveranso Yehova. Panopa iye amakhala mosangalala ndi mwamuna wake komanso ana awo awiri. Akanakhala kuti anatumiza anawo kuti azikakhala ndi anthu ena si bwenzi zili chonchi.
15, 16. (a) Fotokozani zimene zinachitikira mlongo wina makolo ake atamusiya kuti aleredwe ndi agogo ake. (b) N’chifukwa chiyani iye sanafune kuchita zimenezi ndi mwana wake?
15 Mlongo wina dzina lake Vicky ananena kuti: “Kwa zaka zingapo ndinaleredwa ndi agogo anga aakazi, pamene makolo anga ankakhala ndi mng’ono wanga. Atadzanditenga sindinkawaonanso ngati makolo anga. Mng’ono wanga ankamasuka nawo bwinobwino koma ine zinkandivuta mpaka pamene ndinakula. Ine ndi mng’ono wanga timauza makolo athu kuti tidzawasamalira akadzakalamba. Mng’ono wanga adzachita zimenezi chifukwa chowakonda koma ine ndidzangochita chifukwa choti ndi makolo anga.
16 Vicky anati: “Panopa mayi anga akufuna kuti ndikawasiyire mwana wanga wamkazi ngati mmene iwowo anachitira ndi ineyo. Koma ndinawakanira mwaulemu. Ine ndi mwamuna wanga tikufuna kuphunzitsa mwana wathu njira za Yehova. Ndiponso sindikufuna kusokoneza ubwenzi wanga ndi mwana wangayu.” Vicky anazindikira kuti chofunika kwambiri ndi kumvera Yehova osati kupeza chuma kapena kusangalatsa achibale. Yesu anafotokoza momveka bwino kuti: “Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”—Mat. 6:24; Eks. 23:2.
YEHOVA AMATITHANDIZA KUTI ZINTHU ZIZITIYENDERA BWINO
17, 18. (a) Kodi Mkhristu aliyense ayenera kusankha bwino pa nkhani iti? (b) Kodi nkhani yotsatira idzayankha mafunso ati?
17 Atate wathu wakumwamba ndi wokonzeka kutithandiza kupeza zofunika pa moyo wathu ngati tipitiriza kufunafuna Ufumu choyamba ndi chilungamo chake. (Mat. 6:33) Choncho Mkhristu aliyense ayenera kusankha bwino zochita nthawi zonse. Yehova walonjeza kuti adzapereka “njira yopulumukira” mavuto alionse popanda kuphwanya mfundo zake. (Werengani 1 Akorinto 10:13.) Tiyenera kuyembekezera Yehova ndi mtima wonse, kumudalira ndiponso kutsatira malamulo ndi mfundo zake. Tizimupempha kuti atipatse nzeru komanso azititsogolera. Tikatero “iye adzachitapo kanthu.” (Sal. 37:5, 7) Adzatidalitsa pamene tikuyesetsa kumutumikira podziwa kuti ndi Ambuye wabwino. Tikamayesetsa kumumvera pa chilichonse iye adzatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino.—Yerekezerani ndi Genesis 39:3.
18 Kodi munthu amene anasiyana ndi banja lake angatani kuti akonzenso ubwenzi wawo? Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite kuti tizisamalira banja lathu popanda kupita kwina kukagwira ntchito? Nanga tingathandize bwanji ena kuti asankhe bwino pa nkhani imeneyi? Mayankho a mafunso amenewa tidzawapeza m’nkhani yotsatira.
a Mayina asinthidwa.
b Ulendo uliwonse umene ana a Yakobo anayenda popita ku Iguputo sunkaposa milungu itatu. Ndipo pamene Yakobo ndi ana ake anasamukira ku Iguputo anatenga akazi ndi ana awo.—Gen. 46:6, 7.
c Onani nkhani yakuti, “Kodi Osamukira Kudziko Lina Amakapezadi Zimene Akufuna?” mu Galamukani! ya February 2013.
d Malipoti ochokera m’mayiko osiyanasiyana akusonyeza kuti munthu akasiyana ndi banja lake pamakhala mavuto ambiri. Ena amachita chigololo, amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo kapenanso ndi achibale awo.Ana amalowerera, sakhoza bwino kusukulu, amakhala olusa, ankhawa ndiponso mwina amafuna kudzipha.