NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUCHITA ZINTHU MOONA MTIMA?
Kodi Ubwino Wopewa Chinyengo Ndi Wotani?
“Tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.
M’Baibulo mawu achigiriki amene nthawi zina amamasuliridwa kuti “kuona mtima,” amatanthauza “chinthu chabwino kwambiri.” Mawuwa angatanthauzenso munthu amene amaonedwa kuti ndi wokongola chifukwa choti ali ndi khalidwe labwino.
Akhristu amayesetsa kutsatira mawu a Paulo akuti: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” Komatu kuchita zimenezi si nkhani yamasewera.
KUPEWA CHINYENGO SI KOPHWEKA
Anthu ambiri amakonda kudziyang’anira pagalasi tsiku lililonse. Akaona kuti penapake sipali bwino, amadzikonzakonza kuti aoneke bwino. Komabe kukhala ndi khalidwe labwino n’kofunika kwambiri kuposa kuoneka bwino kapena kutchena. Munthu akhoza kukhala wooneka bwino koma ngati alibe khalidwe, kukongolako kumakhala kopanda ntchito.
Mawu a Mulungu amanena kuti nthawi zambiri anthufe timakhala ndi maganizo ofuna kuchita zinthu zoipa. Lemba la Genesis 8:21 limati: “Maganizo a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.” Choncho kuti tisamachite zinthu zachinyengo, timafunika kulimbana ndi kamtima kameneka. Zimenezi ndi zimenenso mtumwi Paulo ankachita ndipo anafotokoza kuti: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu, koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo chimene chili m’ziwalo zanga.”—Aroma 7:22, 23.
Mwachitsanzo, mtima wathu ukamafuna kuchita zoipa, m’pamene maganizo ofuna kuchita zinthu mwachinyengo amakula. Zikatero tisamachite zimene mtima ukufuna koma tizilimbana ndi maganizo oipawo. Ngati munthu atamachita zimenezi akhoza kupewa kuchita zachinyengo ngakhale kuti n’zimene anthu ena amachita.
N’ZOTHEKA KUPEWA CHINYENGO
Kuti tipewe kuchita zachinyengo timafunika kukhala ndi malangizo abwino oti tizitsatira. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amatha nthawi yaitali akuganizira za mmene akuonekera m’malo moganizira za khalidwe lawo. Ndiye anthu amenewa akamafuna kuchita zinazake, saona vuto kuchita zachinyengo. Buku lina linati: “Nthawi zambiri anthufe timanama n’cholinga choti ena azingotiona ngati abwino.” (The (Honest) Truth About Dishonesty) Kodi pali malangizo alionse amene angatithandize kuti tisamachite zachinyengo? Inde alipo, ndipo amapezeka m’Baibulo.
Anthu mamiliyoni ambiri padzikoli amaona kuti Baibulo limawathandiza kuti asamachite zachinyengo. Baibulo lili ndi malangizo abwino kwambiri amene angatithandize kukhala ndi khalidwe labwino. (Salimo 19:7) Lilinso ndi malangizo omwe angatithandize m’banja, pantchito komanso popembedza Mulungu. Malangizowa satha ntchito ngakhale kuti analembedwa kalekale ndipo amathandiza anthu a mitundu yonse. Choncho kuphunzira Baibulo komanso kugwiritsa ntchito zomwe taphunzirazo kungatithandize kuti tiziyesetsa kupewa kuchita zinthu mwachinyengo.
Komabe pali zinthu zinanso zomwe timafunika kuchita. Popeza tikukhala m’dziko limene anthu ambiri amachita zinthu zoipa, nthawi zina zimakhala zovuta kuchita zinthu zabwino. Choncho tiyenera kumapemphera kwa Yehova kuti azitithandiza. (Afilipi 4:6, 7, 13) Zimenezi zingatithandize kuti tizichita zinthu molimba mtima n’kumapewa kuchita zachinyengo.
UBWINO WOPEWA CHINYENGO
A Hitoshi omwe tawatchula kumayambiriro aja, amadziwika kuti ndi munthu wokhulupirika chifukwa choti sachita zinthu zachinyengo. Panopo anapeza ntchito ina ndipo abwana awo amawakonda kwambiri. A Hitoshi ananena kuti: “Ndimasangalala chifukwa ndinapeza ntchito yabwino ndipo sindidziimba mlandu.”
Pali anthu enanso amene amasangalala chifukwa choti sachita zachinyengo. Tiyeni tione phindu limene apeza chifukwa chotsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti, “tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”
Sudziimba Mlandu
Mayi wina wa ku Ireland dzina lake Cheryl anati: “Ndili ndi zaka 13 ndinasiya sukulu n’kuyamba kuba ndi anzanga enaake moti ndalama zanga zambiri zinkakhala zakuba. Nditakwatiwa, ine ndi mwamuna wanga tinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Titaphunzira kuti Yehovaa amadana ndi kuchita zinthu zachinyengo, tinaganiza zosiya kuba. Ndiyeno mu 1990 tinabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.”—Miyambo 6:16-19.
A Cheryl anapitiriza kuti: “M’nyumba mwanga munkangodzaza ndi katundu wakuba yekhayekha, koma panopo ndimasangalala chifukwa ndilibe katundu aliyense wakuba. Ndimaona kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo kwambiri chifukwa anandilola kuti ndizimutumikira ngakhale kuti poyamba ndinkachita zinthu zoipa. Panopa ndimagona tulo tabwino chifukwa chodziwa kuti Yehova akusangalala ndi zimene ndikuchita.”
Bambo wina wa ku Hong Kong, dzina lake Sonny anati: “Abwana anga atadziwa kuti ndinakana kulandira ziphuphu anandiuza kuti, ‘Mulungu wanu ndi amene amakuthandizani kukhala wokhulupirika chonchi. Pakampani pano timafuna anthu ngati inuyo.’ Kupewa kuchita zachinyengo kumandithandiza kuti ndisamadziimbe mlandu. Ndimathandizanso anthu a m’banja langa komanso anthu ena kuti asamachite zachinyengo.”
Umakhala Ndi Mtendere Wamumtima
A Tom a ku United States anati: “Ndine wachiwiri kwa bwana wamkulu kubanki ina yaikulu. Anthu ambiri omwe amagwira ntchitoyi amaona kuti munthu sangalemere ngati sachita zachinyengo. Ena mpaka amafika ponena kuti, ‘Si vuto lalikulu kuchita zachinyengo kuti upeze chuma ndipo zimathandiza kuti chuma chadziko chiziyenda bwino.’ Koma ineyo ndimakhala ndi mtendere wa mumtima chifukwa ndimayesetsa kupewa zachinyengo. Ndinatsimikiza mtima kuti sindingachite zachinyengo ngakhale zinthu zitavuta bwanji. Mabwana anganso amadziwa zimenezi ndipo ngakhale iwowo sayerekeza n’komwe kundipempha kuti ndichite zachinyengo.”
Anthu Amakulemekeza
A Kaori a ku Japan anati: “Nthawi ina bwana wanga anandiuza kuti ndipereke lipoti labodza katundu wina atasowa, koma ine ndinamukanira. Anthu amene anaba katunduyo atadziwika, bwana wamkulu pakampani yathuyo anandithokoza kwambiri chifukwa chonena zoona. N’zoona kuti kupewa zachinyengo si kophweka. Koma anthu akadziwa kuti suchita zachinyengo, amakukhulupirira komanso kukulemekeza kwambiri.”
M’nkhaniyi taona kuti anthu amene sachita zachinyengo sadziimba mlandu, amakhala ndi mtendere wa mumtima ndiponso anthu ena amawalemekeza. Ndiyetu tiyeni tiziyesetsa kupewa kuchita zinthu zachinyengo.
a Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.