Mzimu Umachitira Umboni Limodzi ndi Mzimu Wathu
“Mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.”—AROMA 8:16.
1-3. (a) Kodi ndi zinthu zapadera ziti zimene zinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E.? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi zimene zinachitikazo zinakwaniritsa bwanji ulosi wa m’Baibulo?
M’CHAKA cha 33 C.E., anthu ambiri anasonkhana ku Yerusalemu kuti achite mwambo wa Pentekosite. Mwambowu unali wapadera kwambiri ndipo unkachitika pa nthawi imene anthu akuyamba kukolola tirigu. M’chaka chimenechi, tsiku la Pentekosite linali Lamlungu ndipo pa tsikuli m’mawa, mkulu wa ansembe anapereka nsembe kukachisi monga mwa nthawi zonse. Kenako cha m’ma 9 koloko, anapereka nsembe ya mitanda iwiri ya mkate yokhala ndi chofufumitsa ndiponso yopangidwa ndi ufa watirigu woyambirira. Popereka nsembeyo kwa Yehova, anaitenga n’kuiweyulira uku ndi uku.—Lev. 23:15-20.
2 Koma pamene izi zinkachitika, n’kuti zinthu zinanso zofunika kwambiri zitatsala pang’ono kuchitika. Zinthuzi sizinachitikire kukachisiko koma m’chipinda cham’mwamba m’nyumba inayake. Ophunzira a Khristu pafupifupi 120 anali atasonkhana m’chipindamo ndipo ‘ankapemphera.’ (Mac. 1:13-15) Zimene wansembe ankachita pa Pentekosite chaka chilichonse zinali zogwirizana kwambiri ndi zomwe zinali zitatsala pang’ono kuchitikira ophunzirawa. Komanso zomwe zinawachitikirazo zinakwaniritsa ulosi wa Yoweli womwe unali utalembedwa zaka 800 m’mbuyomo. (Yow. 2:28-32; Mac. 2:16-21) Koma kodi chinachitika n’chiyani?
3 Werengani Machitidwe 2:2-4. Pa tsikuli ophunzira a Khristuwo analandira mzimu woyera wa Mulungu ndipo anadzozedwa. (Mac. 1:8) Kenako gulu la anthu linafika pamalopo ndipo ophunzirawo anayamba kuwauza zinthu zodabwitsa za Mulungu zimene anaona komanso kumva. Ndiyeno Petulo anawafotokozera kufunika kwa zimene zinachitikazo. Kenako anawauza kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Mukatero mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera.” Atanena zimenezi anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa n’kulandira mzimu woyera.—Mac. 2:37, 38, 41.
4. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene zinachitika pa Pentekosite n’zofunika kwa ife? (b) M’nthawi ya Mose, kodi ndi zinthu ziti zimene mwina zinachitika pa tsiku lofanana ndi la Pentekosite? (Onani mawu akumapeto.)
4 Kodi zimene zinachitika pamwambo wa Pentekosite mu 33 C.E. n’zofunika kwa ife? Inde. Osati chifukwa cha zimene wansembe uja anachita kukachisi. Koma chifukwa choti zimene Yesu Khristu, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe wapamwamba anachita pa nthawiyi, zinakwaniritsa zimene zinkachitika pakachisi pamwambo wa Pentekosite.[1] Pamwambowu, mkulu wa ansembe ankapereka kwa Yehova mitanda iwiri ya mkate yokhala ndi chofufumitsa. Mitandayi inkaimira ophunzira odzozedwa amene anasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ochimwa kuti akhale ana a Mulungu. Choncho mwayi unatseguka woti odzozedwawa, omwe ndi “zipatso zoyambirira,” adzapite kumwamba kukalamulira mu Ufumu wa Mulungu. (Yak. 1:18) Yehova adzadalitsa anthu onse omvera pogwiritsa ntchito Ufumuwo. (1 Pet. 2:9) Choncho kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, zimene zinachitika pa Pentekosite wa mu 33 C.E. ndi zofunika kwa ife.
KODI MUNTHU AMADZOZEDWA BWANJI?
5. Kodi anthu onse amadzozedwa mofanana? Fotokozani.
5 Ophunzira a Yesu amene anali m’chipinda chapamwamba chija sakanaiwala zimene zinachitikazo. Paja aliyense anali ndi mzimu woyera wooneka ngati lawi lamoto pamutu pake. Yehova anawathandizanso kuti athe kulankhula zilankhulo zina. Choncho iwo sanakayikire ngakhale pang’ono zoti adzozedwa ndi mzimu woyera. (Mac. 2:6-12) Koma kodi anthu onse amadzozedwa mofanana ndi mmene ophunzira 120 aja anadzozedwera? Ayi. Anthu ena amene anadzozedwa pa tsikulo, anadzozedwa pamene ankabatizidwa ndipo sanalandire mzimu woyera wooneka ngati malawi amoto. (Mac. 2:38) Asamariya anadzozedwa patapita nthawi kuchokera pamene anabatizidwa. (Mac. 8:14-17) Pomwe pa zifukwa zina, Koneliyo ndi anthu a m’banja lake anadzozedwa asanabatizidwe n’komwe.—Mac. 10:44-48.
6. Kodi odzozedwa onse amalandira chiyani, ndipo zimenezi zimawathandiza bwanji?
6 Choncho Akhristu amadzozedwa m’njira zosiyanasiyana. Ena amadziwa nthawi yomweyo kuti adzozedwa, pomwe ena amazindikira pang’onopang’ono. Koma zimene mtumwi Paulo ananena zimachitikira aliyense amene wadzozedwa. Iye anati: “Mutakhulupirira munaikidwa chidindo cha mzimu woyera wolonjezedwawo, umene ndi chikole cha cholowa chathu cham’tsogolo.” (Aef. 1:13, 14) Yehova amapatsa odzozedwa mzimu woyera ngati chizindikiro kapena chidindo chowatsimikizira kuti asankhidwa kudzapita kumwamba ndipo zimakhala ngati alandira chikole.—Werengani 2 Akorinto 1:21, 22; 5:5.
7. Kodi wodzozedwa aliyense ayenera kuchita chiyani kuti adzalandire mphoto yake?
7 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mkhristu akadzozedwa ndiye kuti basi adzapita kumwamba? Ayi. N’zoona kuti munthuyo amadziwa kuti wasankhidwa kuti adzapita kumwamba. Koma adzapita pokhapokha akakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Petulo anati: “Pa chifukwa chimenechi abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, n’cholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha, pakuti mukapitiriza kuchita zinthu zimenezi simudzalephera ngakhale pang’ono. Ndipo mukatero, adzakutsegulirani khomo kuti mulowe mwaulemerero mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.” (2 Pet. 1:10, 11) Choncho wodzozedwa aliyense ayenera kuyesetsa kukhalabe wokhulupirika chifukwa kupanda kutero, sadzalandira mphoto yake.—Aheb. 3:1; Chiv. 2:10.
KODI MUNTHU AMADZIWA BWANJI KUTI WADZOZEDWA?
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano amavutika kumvetsa bwino zimene zimachitika munthu akadzozedwa? (b) Kodi munthu amadziwa bwanji kuti wadzozedwa?
8 Popeza atumiki a Yehova ambiri masiku ano si odzozedwa, amavutika kumvetsa zimene zimachitika munthu akadzozedwa. Paja Mulungu analenga anthu ndi cholinga choti akhale padziko lapansi osati kumwamba. (Gen. 1:28; Sal. 37:29) Koma Yehova wasankha anthu ena kuti apite kumwamba kukakhala mafumu ndi ansembe. Choncho munthu akadzozedwa amasintha mmene amaganizira, mmene amaonera zinthu ndipo chiyembekezo chake chimasinthanso.—Werengani Aefeso 1:18.
9 Koma kodi munthu amadziwa bwanji kuti wadzozedwa? Zimene Paulo anauza Akhristu a ku Roma, omwe anali “oitanidwa kukhala oyera,” zingatithandize kuyankha funsoli. Iye anawauza kuti: “Simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: ‘Abba, Atate!’ Pakuti mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.” (Aroma 1:7; 8:15, 16) Choncho mwachidule tingati Mulungu akadzoza munthu, amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera n’kumuthandiza kuti atsimikize zoti wasankhidwa kudzalamulira nawo mu Ufumu.—1 Ates. 2:12.
10. Kodi lemba la 1 Yohane 2:27 limatanthauza chiyani ponena kuti Akhristu odzozedwa safunikira wina aliyense kuti aziwaphunzitsa?
10 Akhristu amene asankhidwa ndi Mulungu safunikira umboni wina wowatsimikizira kuti adzozedwa. Yehova amawathandiza kuti asamakayikire ngakhale pang’ono za zimenezi. Mtumwi Yohane anauza Akhristu odzozedwa kuti: “Munadzozedwa ndi woyerayo, ndipo nonsenu ndinu odziwa choonadi.” Anawonjezeranso kuti: “Mulungu anakudzozani ndi mzimu ndipo mzimu umenewo udakali mwa inu. Chotero simukufunikira wina aliyense kuti azikuphunzitsani, koma popeza kuti munadzozedwadi moona osati monama, chifukwa cha kudzozedwako, mukuphunzitsidwa zinthu zonse. Monga mmene mwaphunzitsidwira, pitirizani kukhala ogwirizana naye.” (1 Yoh. 2:20, 27) N’zoona kuti odzozedwa amafunikira kuphunzitsidwa mfundo za m’Baibulo ngati mmene zilili ndi Akhristu ena onse. Koma safunikira kuti munthu wina awatsimikizire zoti adzozedwa. Zili choncho chifukwa mzimu wa Mulungu umawathandiza kudziwa zimenezi.
ZIMENE ZIMACHITIKA AKABADWA MWATSOPANO
11, 12. Kodi Mkhristu wodzozedwa angamadzifunse funso liti, koma sakayikira za chiyani?
11 Mkhristu akadzozedwa, amasintha kwambiri mmene amaganizira moti Yesu ananena kuti zimakhala ngati ‘wabadwanso’ kapena kuti wabadwa kuchokera kumwamba.[2] (Yoh. 3:3, 5) Yesu ananenanso kuti: “Usadabwe chifukwa ndakuuza kuti, Anthu inu muyenera kubadwanso. Mphepo imawombera kumene ikufuna, ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita. N’chimodzimodzinso aliyense wobadwa mwa mzimu.” (Yoh. 3:7, 8) Apa n’zoonekeratu kuti n’zosatheka kufotokozera munthu amene sanadzozedwe zonse zimene zimachitika, munthuyo n’kumvetsa bwinobwino.
12 Munthu akadzozedwa angamadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu wasankha ineyo?’ Mwinanso angamadzione kuti ndi wosayenera kupatsidwa udindo wodzalamulira ndi Yesu. Komabe sikuti amakayikira zoti wadzozedwa. Amasangalala komanso amayamikira Yehova chifukwa chomupatsa mwayiwu. Amamva ngati mmene Petulo ankamvera pamene anati: “Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, pakuti mwachifundo chake chachikulu, anatibereka mwatsopano kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu. Anatibereka kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka. Cholowa chimenechi anasungira inuyo kumwamba.” (1 Pet. 1:3, 4) Mkhristu aliyense wodzozedwa akawerenga mawu amenewa amadziwiratu kuti Atate wake wakumwamba akulankhula ndi iyeyo.
13. Kodi zinthu zimasintha bwanji munthu akadzozedwa ndipo n’chifukwa chiyani?
13 Mkhristu asanadzozedwe, amasangalala kuti adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Amalakalaka kudzaona Yehova atakonza dzikoli n’kuchotsapo zinthu zonse zoipa. Komanso amaganizira mmene adzasangalalire akamadzalandira achibale ake omwe anamwalira. Mwina amaganiziranso kuti adzamanga nyumba yabwino n’kumakhalamo komanso azidzadya zipatso zomwe adzabzale. (Yes. 65:21-23) Koma akadzozedwa zonsezi zimasintha. Sizisintha chifukwa chakuti sakusangalalanso kukhala ndi moyo padziko lapansi kapena pongofuna kuthawa mavuto padzikoli. Si chifukwanso chakuti amayamba kuona kuti moyo wosatha padziko lapansili udzakhala wotopetsa kapena chifukwa chongofuna kukaona zina kumwamba. Koma amasintha chifukwa chakuti Mulungu akamudzoza ndi mzimu wake, mzimuwo umamuthandiza kusintha chiyembekezo chake ndiponso mmene amaganizira.
14. Kodi odzozedwa amafuna kuti afe n’cholinga choti apite kumwamba? Fotokozani.
14 Kodi tinganene kuti odzozedwa amafuna kuti afe n’cholinga choti apite kumwamba? Ayi. Paulo anafotokoza mmene odzozedwa amamvera ponena kuti: “Ife amene tili mumsasa uno tikubuula chifukwa cholemedwa. Kwenikweni si chifukwa chofuna kuuvula, koma kuti tivale nyumba inayo, kuti chokhoza kufachi chilowedwe m’malo ndi moyo.” (2 Akor. 5:4) Choncho sitinganene kuti moyo umawatopetsa ndipo amafuna kuti afe msanga. Iwo amasangalala kwambiri akamatumikira Yehova limodzi ndi achibale ndiponso anzawo. Komabe nthawi zonse amaganizira zinthu zabwino zimene akuyembekezera m’tsogolo.—1 Akor. 15:53; 2 Pet. 1:4; 1 Yoh. 3:2, 3; Chiv. 20:6.
KODI MUKUGANIZA KUTI MWADZOZEDWA?
15. Kodi ndi zinthu ziti zomwe si umboni wakuti munthu wadzozedwa?
15 Mwina nthawi ina munadzifunsapo kuti, ‘Kodi kapena ndadzozedwa?’ Ngati nthawi zina mumaganiza kuti mwina mwadzozedwa, mafunso otsatirawa angakuthandizeni. Kodi mukuona kuti mumalalikira mwakhama? Nanga mumakonda kwambiri kuphunzira Baibulo kuti mudziwe “zinthu zozama za Mulungu”? (1 Akor. 2:10) Kodi mukuona kuti Yehova akukudalitsani kwambiri pa ntchito yolalikira? Kodi mumafunitsitsa kuchita zimene Yehova amafuna? Nanga kodi mumafunitsitsanso kuthandiza ena kuti ayambe kutumikira Yehova? Kodi nthawi zina mumaona kuti Yehova amakuthandizani m’njira yodabwitsa? Ngati yankho lanu pa mafunso onsewa ndi lakuti inde, kodi ndiye kuti ndinu wodzozedwa? Ayi. Tikutero chifukwa choti si odzozedwa okha amene angayankhe kuti inde pa mafunsowa. Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake kuthandiza Akhristu onse, kaya ndi opita kumwamba kapena odzakhala padzikoli. Ndipotu ngati mumakayikira zoti mwina ndinu wodzozedwa, ndiye kuti si inu wodzozedwa. Tikutero chifukwa munthu wodzozedwa sakayikira ngakhale pang’ono. Amadziwiratu kuti Yehova wamusankha.
16. Kodi tikudziwa bwanji kuti sikuti aliyense amene amathandizidwa ndi mzimu wa Mulungu adzapita kumwamba?
16 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambiri okhulupirika amene mzimu woyera unkawathandiza, koma sanapite kumwamba. Mmodzi wa anthu amenewa ndi Yohane M’batizi. Yesu anamuyamikira kwambiri komabe ananena kuti sali m’gulu la anthu opita kumwamba. (Mat. 11:10, 11) Nayenso Davide ankathandizidwa kwambiri ndi mzimu woyera. (1 Sam. 16:13) Iye anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo analemba nawo Baibulo. (Maliko 12:36) Komabe mtumwi Petulo ananena kuti: “Davide sanakwere kumwamba.” (Mac. 2:34) Ngakhale kuti mzimu woyera unathandiza anthuwa kuchita zinthu zambiri, sunawachititse kuona kuti asankhidwa kuti adzapita kumwamba. Komabe izi sizikutanthauza kuti anthuwa anali ndi vuto linalake. Yehova adzawaukitsa kuti adzakhale m’Paradaiso padziko lapansi.—Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15.
17, 18. (a) Kodi atumiki ambiri a Mulungu a masiku ano ali ndi chiyembekezo chotani? (b) Kodi tidzakambirana mafunso ati m’nkhani yotsatira?
17 Atumiki ambiri a Mulungu a masiku ano sadzapita kumwamba. Mofanana ndi anthu monga Abulahamu, Davide ndi Yohane M’batizi, iwo amayembekezera kudzakhala padziko lapansi n’kumadzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu. (Aheb. 11:10) Masiku ano padzikoli pangotsala anthu ochepa kwambiri amene adzapite kumwamba. (Chiv. 12:17) Izi zikusonyeza kuti anthu ambiri amene ali m’gulu la 144,000 anamwalira kale ndipo panopa ali kumwamba.
18 Ndiyeno kodi anthu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli aziwaona bwanji abale ndi alongo amene amati ndi odzozedwa? Munthu wina wamumpingo wanu akayamba kudya zizindikiro pa Chikumbutso, kodi muyenera kutani? Nanga kodi muyenera kudandaula ngati chiwerengero cha anthu amene anadya zizindikiro chakwera? Tidzakambirana mafunsowa m’nkhani yotsatira.
^ [1] (ndime 4) N’kutheka kuti mwambo wa Pentekosite unkachitika pa nthawi yofanana ndi imene Chilamulo chinaperekedwa m’chipululu cha Sinai. (Eks. 19:1) Ngati zili choncho, ndiye kuti Yesu Khristu anathandiza odzozedwa kuti alowe m’pangano latsopano pa tsiku lofanana ndi limene Mose anathandiza Aisiraeli kulowa m’pangano la Chilamulo.
^ [2] (ndime 11) Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya kubadwanso, werengani tsamba 3 mpaka 11 mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2009.