“Kuika Maganizo pa Zinthu za Mzimu Kumabweretsa Moyo ndi Mtendere”
“Otsatira za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.”—AROMA 8:5.
1, 2. N’chifukwa chiyani chaputala 8 cha Aroma ndi chofunika kwambiri kwa Akhristu odzozedwa?
MWINA mwawerenga lemba la Aroma 8:15-17 pokonzekera mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Mavesi amenewa amafotokoza zimene zimathandiza Akhristu kudziwa kuti adzozedwa. Amasonyeza kuti mzimu woyera umachitira umboni limodzi ndi mzimu wawo. Vesi loyamba m’chaputalachi limatchula za anthu “amene ali ogwirizana ndi Khristu Yesu.” Koma kodi mfundo za mu Aroma chaputala 8 n’zothandiza kwa odzozedwa okha? Kapena n’zothandizanso kwa Akhristu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli?
2 N’zoona kuti mfundo za mu chaputalachi kwenikweni zimanena za odzozedwa. Iwo amalandira “mzimu” monga amene ‘akudikira ndi mtima wonse kuti atengedwe kukhala ana a Mulungu n’kumasulidwa ndi dipo kuti atuluke m’matupi awo.’ (Aroma 8:23) Akhristu amenewa amayembekezera kukakhala ana a Mulungu kumwamba. Zimenezi zimatheka chifukwa Mulungu anawakhululukira machimo awo ndipo amawaona kuti ndi olungama komanso ndi ana ake.—Aroma 3:23-26; 4:25; 8:30.
3. N’chifukwa chiyani tingati mfundo za mu Aroma chaputala 8 ndi zothandizanso kwa Akhristu amene adzakhale padziloli?
3 Komabe chaputala 8 cha Aroma n’chothandizanso kwa amene adzakhale padzikoli chifukwa nawonso Mulungu amawaona kuti ndi olungama. Umboni wa zimenezi ndi zomwe Paulo analemba asanalembe chaputalachi. Mwachitsanzo, m’chaputala 4 anafotokoza za Abulahamu. Abulahamu anali ndi chikhulupiriro ndipo anakhala ndi moyo Yesu asanatifere komanso Yehova asanapereke Chilamulo kwa Aisiraeli. Komabe Yehova anaona chikhulupiriro chake ndipo ankamuona kuti ndi wolungama. (Werengani Aroma 4:20-22.) Masiku anonso Yehova amaona kuti Akhristu okhulupirika amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli ndi olungama. Choncho mfundo za mu Aroma chaputala 8 ndi zothandizanso kwa iwo.
4. Tikawerenga lemba la Aroma 8:21, kodi tiyenera kudzifunsa funso liti?
4 Pa Aroma 8:21 timapeza mfundo yotitsimikizira kuti Mulungu adzatipatsa dziko latsopano. Vesili limanena kuti: “Chilengedwecho chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” Ndiyeno funso n’kumati, kodi ifeyo tidzakhala m’dziko limeneli n’kulandira nawo madalitsowa? Chaputala 8 cha buku la Aroma chingatithandize kudziwa zoyenera kuchita.
“KUIKA MAGANIZO PA ZINTHU ZA THUPI”
5. Palemba la Aroma 8:4-13, kodi Paulo anatchula nkhani yofunika kwambiri iti?
5 Werengani Aroma 8:4-13. Chaputala 8 cha Aroma chimafotokoza kusiyana pakati pa anthu amene amayenda “motsatira zofuna za thupi” ndi amene amayenda “motsatira za mzimu.” Ena angaganize kuti apa akusiyanitsa Akhristu ndi anthu amene si Akhristu. Komatu musaiwale kuti kalata ya Pauloyi inkapita kwa ‘amene anali ku Roma monga okondedwa a Mulungu, oitanidwa kukhala oyera.’ (Aroma 1:7) Choncho apa Paulo ankafotokoza kusiyana pakati pa Akhristu amene ankayenda motsatira thupi, ndi Akhristu amene ankayenda motsatira za mzimu. Kodi kusiyana kwake kunali kotani?
6, 7. (a) Kodi m’Baibulo mawu akuti “thupi” amatanthauza chiyani? (b) Kodi mawu akuti “thupi” amene Paulo anatchula pa Aroma 8:4-13, ankatanthauza chiyani?
6 Kodi palembali Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti “thupi”? M’Baibulo mawu akuti thupi angatanthauze zinthu zosiyanasiyana. Nthawi zina amanena za thupi lathu lenilenili kapena mnofu. (Aroma 2:28; 1 Akor. 15:39, 50) Mawuwa angatanthauzenso chibale. Mwachitsanzo, Yesu anali “wa mbewu ya Davide, monga mwa thupi.” Komanso Paulo ankaona kuti Ayuda ndi ‘abale ake, monga mwa thupi.’—Aroma 1:3; 9:3, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
7 Komabe zimene Paulo analemba m’chaputala 7 zingatithandize kudziwa zimene mawu akuti “thupi” a pa Aroma 8:4-13 akutanthauza. Iye analemba kuti: “Pamene tinali kukhala mogwirizana ndi thupi, zilakolako za uchimo zimene zinaonekera chifukwa cha Chilamulo zinali kugwira ntchito m’ziwalo zathu.” (Aroma 7:5) Choncho ponena kuti anthu amene amakhala “mogwirizana ndi thupi” Paulo ankanena za anthu amene amangotsatira zilakolako za uchimo n’kumachita chilichonse chimene akufuna.
8. N’chifukwa chiyani Paulo anachenjeza Akhristu onse pa nkhani ya kuyenda “mogwirizana ndi thupi”?
8 Koma mwina mungadabwe kuti, n’chifukwa chiyani Paulo anachenjeza Akhristu odzozedwa kuopsa koyenda “mogwirizana ndi thupi”? Chenjezo limeneli ndi lofunikanso kwa Akhristu onse. Tikutero chifukwa Mkhristu aliyense atapanda kusamala angayambe kuyenda mongotsatira zilakolako za thupi. Mwachitsanzo, Paulo analemba kuti Akhristu ena a ku Roma anali akapolo a chiwerewere, kudya, kumwa ndi zinthu zina. Ena ankapusitsa “anthu oona mtima.” (Aroma 16:17, 18; Afil. 3:18, 19; Yuda 4, 8, 12) Komanso paja munthu wina wa ku Korinto anatengana ndi “mkazi wa bambo ake.” (1 Akor. 5:1) Ndiye m’pake kuti Mulungu anauzira Paulo kuti achenjeze Akhristu pa nkhani ya “kuika maganizo pa zinthu za thupi.”—Aroma 8:5, 6.
9. Kodi chenjezo la Paulo pa Aroma 8:6 silitanthauza chiyani?
9 Chenjezo limeneli ndi lofunika kwambiri masiku ano. Mkhristu amene watumikira kwa nthawi yaitali angayambe kuika maganizo ake pa zinthu za thupi. Koma izi sizikutanthauza kuti n’kulakwa kuganizira nthawi zina za chakudya, ntchito, zosangalatsa komanso kukondana m’banja. Mtumiki wa Yehova aliyense akhoza kuganizira zimenezi. Paja nayenso Yesu ankadya komanso kudyetsa anthu. Iye ankadziwanso kuti kupeza nthawi yosangalala n’kofunika. Ndipo mtumwi Paulo anasonyezanso kufunika kosonyezana chikondi m’banja.
10. Kodi mawu oti “kuika maganizo” amene ali pa Aroma 8:5, 6 amatanthauza chiyani?
10 Ndiyeno kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “kuika maganizo pa zinthu za thupi”? Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti kuika maganizo amasonyeza kuti maganizo onse, mapulani onse komanso mtima wonse uli pa chinthu chinachake. Anthu amene amatsatira zofuna za thupi nthawi zonse amangochita zimene thupi lochimwali limalakalaka. Katswiri wina ananena kuti mawu oti “kuika maganizo” omwe ali pa Aroma 8:5 amanena za munthu amene amakonda kwambiri zimene thupi lake limalakalaka. Munthuyo amalankhulalankhula za zinthu zimenezo ndipo amasangalala akamazichita.
11. Kodi ena amangokhalira kuchita chiyani pa moyo wawo?
11 Choncho Akhristu a ku Roma anafunika kuonanso zimene amakonda. Izi zikanawathandiza kudziwa ngati maganizo awo onse anali pa “zinthu za thupi.” Nafenso masiku ano tiyenera kudzifufuza. Kodi timakonda kwambiri chiyani nanga timalankhulalankhula za chiyani? Kodi tsiku lililonse timakonda kuganizira kapena kuchita chiyani? Ena akhoza kuzindikira kuti amangokhalira kulawa mitundu yosiyanasiyana ya vinyo, kukongoletsa nyumba yawo, kufufuza masitayilo a zovala, kusunga ndalama, kupita kokasangalala ndi zina. N’zoona kuti zinthuzi pazokha si zolakwika. Mwachitsanzo, Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo ndipo Paulo anauza Timoteyo kuti azimwa “vinyo pang’ono.” (1 Tim. 5:23; Yoh. 2:3-11) Koma kodi Yesu ndi Paulo ankangokhalira kulankhula za vinyo kapena kumwa vinyoyo? Ayi. Nanga bwanji ifeyo? Kodi timaona kuti chofunika kwambiri pa moyo wathu n’chiyani?
12, 13. N’chifukwa chiyani tiyenera kusintha ngati tayamba kuika maganizo pa zinthu za thupi?
12 N’chifukwa chiyani tiyenera kudzifufuza pa nkhaniyi? Paulo analemba kuti: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa.” (Aroma 8:6) Izitu n’zoopsa chifukwa munthu angafe pawiri. Panopa angafe mwauzimu ndipo m’tsogolomu sadzapeza moyo wosatha. Koma mawu a Paulowa sakutanthauza kuti munthu akangoyamba “kuika maganizo pa zinthu za thupi” ndiye kuti afa basi. N’zotheka kusintha. Chitsanzo ndi munthu wa ku Korinto amene ankatsatira zofuna za thupi mpaka kufika pochotsedwa mumpingo. Mwayi wosintha unalipo ndipo anasinthadi. Iye anasiya kutsatira zofuna za thupi ndipo anayamba kuchita zabwino.—2 Akor. 2:6-8.
13 Ngati munthu wa ku Korintoyu anali ndi mwayi wosintha, ndiye kuti masiku ano mwayiwu uliponso. N’zotheka ndithu kuti Mkhristu amene wayamba kutsatira zofuna za thupi asinthe. Choncho mfundo yoti “kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa” iyenera kulimbikitsa Mkhristu aliyense kusintha moyo wake.
“KUIKA MAGANIZO PA ZINTHU ZA MZIMU”
14, 15. (a) Kodi Paulo anati tiziika maganizo athu pa zinthu ziti? (b) Kodi “kuika maganizo pa zinthu za mzimu” sikutanthauza chiyani?
14 Mtumwi Paulo atachenjeza za kuopsa kwa “kuika maganizo pa zinthu za thupi,” anafotokoza mfundo yolimbikitsa yakuti: “Kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.” Amenewatu ndi madalitso aakulu. Koma kodi tingatani kuti tipeze madalitsowa?
15 Komatu “kuika maganizo pa zinthu za mzimu” sikutanthauza kuti munthu azingokhalira kuchita zinthu zokhudza kulambira. Sizitanthauza kuti munthu azingolankhula ndi kuganiza zokhudza Baibulo, Yehova ndi dziko latsopano basi. Tizikumbukira kuti Paulo ndi Akhristu ena okhulupirika ankachitanso zinthu zina. Iwo ankadya komanso kumwa. Ndipo ambiri anali ndi mabanja komanso ankagwira ntchito.—Maliko 6:3; 1 Ates. 2:9.
16. Ngakhale kuti Paulo ankachita zinthu zina, kodi ankaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani?
16 Komabe Paulo ndi Akhristu enawo sanalole kuti zinthu za tsiku ndi tsiku zikhale zofunika kwambiri pa moyo wawo. Mwachitsanzo, tikudziwa kuti Paulo ankagwira ntchito yopanga matenti. Koma Baibulo limasonyeza kuti iye ankaona kuti chofunika kwambiri ndi ntchito yolalikira ndiponso kuphunzitsa. Choncho iye ankatanganidwa kwambiri kugwira ntchito imeneyi ndipo analimbikitsanso Akhristu a ku Roma kuti azichita zomwezo. (Werengani Machitidwe 18:2-4; 20:20, 21, 34, 35.) Paulo ankaona kuti kutumikira Mulungu n’kofunika kwambiri ndipo Akhristu a ku Roma ankafunika kumutsanzira. Ifenso masiku ano tiyenera kuchita chimodzimodzi.—Aroma 15:15, 16.
17. Kodi tidzadalitsidwa bwanji ‘tikamaika maganizo athu pa zinthu za mzimu’?
17 Kodi timapeza madalitso ati ‘tikamaika maganizo pa zinthu za mzimu’? Lemba la Aroma 8:6 limati: “kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.” Kuti tiziika maganizo athu pa zinthu za mzimu tiyenera kulola kuti mzimu woyera uzititsogolera komanso tiziyesetsa kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Tikamachita zimenezi tidzakhala osangalala panopa ndipo m’tsogolo tidzapeza moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padzikoli.
18. Kodi “kuika maganizo pa zinthu za mzimu” kumathandiza bwanji kuti tizikhala mwamtendere?
18 Koma kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti ‘kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa mtendere’? Anthu ambiri masiku ano alibe mtendere koma ife tili nawo. Timakhala ndi mtenderewu chifukwa choti timayesetsa kukhala bwino ndi anthu mumpingo komanso m’banja. Timadziwa kuti tonsefe ndi ochimwa choncho mavuto sangalephere. Koma zoterezi zikachitika, timatsatira malangizo a Yesu akuti: “Pita ukayanjane ndi m’bale wako.” (Mat. 5:24) Sizivuta kuthetsa mavuto tikamakumbukira kuti m’bale kapena mlongo wathuyo nayenso akutumikira “Mulungu amene amapatsa mtendere.”—Aroma 15:33; 16:20.
19. Kodi kuika maganizo pa zinthu za mzimu kungatithandize kukhalanso ndi mtendere uti?
19 Koma palinso mtendere wina wamtengo wapatali kwambiri umene tili nawo. ‘Tikamaika maganizo pa zinthu za mzimu’ timakhala pa mtendere ndi Mulungu. Pa nkhani imeneyi, mawu amene Yesaya ananena akukwaniritsidwa masiku ano. Ponena za Yehova, iye analemba kuti: ‘Anthu amene ali ndi mtima wosagwedezeka mudzawateteza powapatsa mtendere wosatha, chifukwa amadalira inu.’—Yes. 26:3; werengani Aroma 5:1.
20. Kodi chingachitike n’chiyani tikatsatira malangizo opezeka mu Aroma chaputala 8?
20 M’nkhaniyi taona kuti kaya ndife odzozedwa kapena ayi, malangizo opezeka mu Aroma chaputala 8 angatithandize. Tikuyamikira kwambiri kuti Mawu a Mulungu amatiuza kuti tiziika maganizo athu onse pa kutumikira Yehova osati kuchita zofuna za thupi lathu. Taonanso kuti “kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.” Tikamayesetsa kutsatira malangizowa tidzapeza madalitso amuyaya. Paja Paulo analemba kuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 6:23.