Kodi Mulungu Amakumvetsani?
ZIMENE CHILENGEDWE CHIMATIPHUNZITSA PA NKHANIYI
Taganizirani za mgwirizano waukulu umene umakhalapo pakati pa ana amapasa. Ana amapasa amakondana kwambiri. Mayi wina dzina lake Nancy Segal yemwe ndi mkulu wa gulu lofufuza za ana amapasa, amene nayenso anabadwa mapasa, ananena kuti ana ena amapasa “amatha kumvetsa mmene mnzawo akumvera ngakhale atapanda kuwafotokozera chilichonse.” Mayi winanso yemwe anabadwa mapasa, ananena zofanana ndi zimenezi kuti: “Timadziwa chilichonse chokhudza mnzathuyo.”
N’chifukwa chiyani ana amapasawa amatha kumumvetsa bwino mnzawo? Kafukufuku amasonyeza kuti zina zimene zimachititsa zimenezi ndi kumene anawo akulira komanso mmene aleredwera. Koma chinanso chomwe chimachititsa zimenezi ndi choti amakhala ndi majini ofanana.
TAGANIZIRANI MFUNDO IYI: Mlengi yemwe anapanga majini amenewa, ayenera kuti amatimvetsa kwambiri chifukwa amadziwa mmene tinapangidwira. N’chifukwa chake Davide ananena kuti: “Munali kunditchinga m’mimba mwa mayi anga. Mafupa anga sanali obisika kwa inu pamene munali kundipanga m’malo obisika, . . . Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.” (Salimo 139:13, 15, 16) Choncho Mulungu amadziwa mavuto amene takumana nawo ndiponso zimene zachititsa kuti tikhale ndi khalidwe linalake. Popeza amadziwa zonsezi ayenera kuti amatidziwa bwino kwambiri.
BAIBULO LIMASONYEZA KUTI MULUNGU AMATIMVETSA
Davide anapemphera kuti: “Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa. Inu mumadziwa ndikakhala pansi kapena ndikaimirira. Mumadziwa maganizo anga muli kutali. Ndisananene kanthu, inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.” (Salimo 139:1, 2, 4) Kuwonjezera pamenepa, Yehova amadziwa mmene tikumvera komanso “amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.” (1 Mbiri 28:9; 1 Samueli 16:6, 7) Kodi mavesiwa akutithandiza kudziwa zotani zokhudza Yehova?
Ngakhale zitakhala kuti sitinamuuze m’pemphero chilichonse chimene tikufuna, Mlengi wathu amadziwa zonse ndipo samangoona zimene tikuchita koma amadziwa chifukwa chake tikuchita zinthuzo. Kuwonjezera apo, amadziwanso zabwino zimene timafuna titachita ngakhale zitakhala kuti talephera kuchita zinthuzo chifukwa cha mavuto ena. Ndiye popeza Yehova anatilenga ndi mtima wachikondi, amafunitsitsa kuona tikuchita zabwino ndipo amamvetsa kuti timafuna kuchita zabwinozo ngakhale titalephera.—1 Yohane 4:7-10.
Mulungu amaona chilichonse chimene chimachitika pa moyo wathu. Amaona mavuto onse amene tikukumana nawo ngakhale zitakhala kuti anthu ena sakuona kapena kumvetsa mmene tikumvera
Malemba awa amatitsimikizira mfundo imeneyi
“Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo.”—1 PETULO 3:12.
Mulungu akulonjeza kuti: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.”—SALIMO 32:8.
MULUNGU NDI WACHIFUNDO KWAMBIRI
Kodi kudziwa kuti Mulungu amamvetsa mmene zinthu zilili pa moyo wathu komanso kuti amamvetsa mmene tikumvera kungatithandize bwanji kupirira mavuto amene tikukumana nawo? Taganizirani zimene zinachitikira Anna wa ku Nigeria. Iye anati: “Mavuto amene ndinkakumana nawo anachititsa kuti ndisamaonenso chifukwa chokhalira moyo. Mwamuna wanga anali atamwalira ndipo ndinkadwazika mwana wanga yemwe anali ndi vuto la madzi muubongo. Pa nthawiyi anandipezanso ndi khansa ya m’mawere moti ndinkafunika kuchitidwa opaleshoni komanso kulandira chithandizo champhamvu kwambiri cha mankhwala. Zinali zovuta kwambiri kugonekedwa m’chipatala pa nthawi yomwenso mwana wanga ankadwala.”
Kodi n’chiyani chinathandiza Anna kupirira vuto limeneli? Iye anati: “Ndinkakonda kuganizira malemba monga Afilipi 4:6, 7, lomwe limanena kuti ‘mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.’ Ndikayamba kuganizira lemba limeneli, ndinkaona kuti Yehova amandikonda kwambiri komanso amandidziwa bwino kuposa mmene ndimadzidziwira. Abale ndi alongo a mumpingo wathu anandilimbikitsanso kwambiri.”
“Ngakhale kuti panopa ndikuvutikabe ndi matendawa, ndikuona kuti zikusintha ndithu ndipo nayenso mwana wanga uja akupezako bwino. Popeza Yehova ali kumbali yathu, taphunzira kuti tisamangoganizira mavuto athu. Lemba la Yakobo 5:11 limatilimbikitsa kuti: ‘Anthu amene anapirira timawatcha odala. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa, mwaona kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.’” Yehova ankamvetsa mavuto amene Yobu ankakumana nawo. Choncho nafenso sitikayikira kuti amadziwa bwino zimene zikuchitika pa moyo wathu.