Anthu Amene Amatumikira “Mulungu Wachimwemwe” Amakhala Osangalala
“Odala [kapena kuti osangalala] ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—SAL. 144:15.
1. N’chifukwa chiyani anthu a Yehova amakhala osangalala? (Onani chithunzi choyambirira.)
A MBONI ZA YEHOVA amakhala osangalala kwambiri. Nthawi zonse akakumana pamisonkhano yampingo ndi ikuluikulu komanso akamacheza amakhala osangalala ndipo amakonda kuseka. Kodi zimatheka bwanji? Chifukwa chachikulu n’chakuti amadziwa ndiponso kutumikira Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe,” ndipo amayesetsa kumutsanzira. (1 Tim. 1:11; Sal. 16:11) Popeza ndi Mulungu wachimwemwe, Yehova amafuna kuti nafenso tizisangalala ndipo amatipatsa zinthu zambiri zotithandiza kuti tikhale osangalala.—Deut. 12:7; Mlal. 3:12, 13.
2, 3. (a) Kodi munthu wosangalala amatani? (b) Kodi ndi mavuto ati amene amachititsa kuti anthu asamasangalale?
2 Nanga bwanji inuyo panokha? Kodi mumasangalala? Nanga mungatani kuti muzisangalala kwambiri? Munthu wosangalala amamva bwino mumtima mwake. Nthawi zambiri amakhala alibe nkhawa ndipo nthawi zina amakhala wansangala kwambiri. Baibulo limasonyeza kuti anthu amene ali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi amene amakhala osangalala kwambiri. Koma masiku ano zingakhale zovuta kuti munthu akhale wosangalala. N’chifukwa chiyani tikutero?
3 Mavuto monga kuferedwa, kutha kwa banja, kusowa ntchito komanso kuchotsedwa kwa mnzathu angapangitse kuti tisamasangalale. Mavuto a m’banja komanso kusemphana maganizo zimachititsanso kuti tizikhala ndi nkhawa. Ena amasowa mtendere chifukwa chotsutsidwa ndi anzawo kuntchito kapena kusukulu ndipo ena amazunzidwa kapena kumangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Anthu angalepherenso kusangalala chifukwa cha matenda osiyanasiyana. Koma tizikumbukira kuti, Yesu Khristu yemwe amatchedwa “wachimwemwe ndi Wamphamvu yekhayo” ankakonda kuthandiza anthu kuti azisangalala. (1 Tim. 6:15; Mat. 11:28-30) Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anatchula zinthu zingapo zimene zingatithandize kukhala osangalala ngakhale kuti timakumana ndi mavuto m’dziko la Satanali.
TIYENERA KUKHALA PA UBWENZI WOLIMBA NDI MULUNGU KUTI TIZISANGALALA
4, 5. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhala osangalala?
4 Yesu anayamba ndi kutchula chinthu chofunika kwambiri. Iye anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.” (Mat. 5:3) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timazindikira zosowa zathu zauzimu? Timachita zimenezi tikamaphunzira Mawu a Mulungu, kuyamikira mfundo zochokera kwa Yehova komanso kuika kutumikira Mulungu wachimwemwe pamalo oyamba. Tikamachita zonsezi tidzakhala osangalala kwambiri. Tidzayambanso kukhulupirira kwambiri kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Komanso tidzalimbikitsidwa ndi “chiyembekezo chosangalatsa” chimene Baibulo limalonjeza anthu amene amalambira Yehova.—Tito 2:13.
5 Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale wosangalala. Pa nkhani imeneyi, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye [Yehova]. Ndibwerezanso, Kondwerani.” (Afil. 4:4) Kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova tiyenera kukhala ndi nzeru yochokera kwa Mulungu. Paja Mawu a Mulungu amati: “Wodala ndi munthu amene wapeza nzeru, ndiponso munthu amene wapeza kuzindikira, munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye, ndipo ozigwiritsitsa adzatchedwa odala.”—Miy. 3:13, 18.
6. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhalebe osangalala?
6 Koma kuti tizisangalalabe sitiyenera kungowerenga Mawu a Mulungu koma tizitsatira zimene taphunzirazo. Potsindika kufunika kotsatira zimene taphunzira, Yesu ananena kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.” (Yoh. 13:17; werengani Yakobo 1:25.) Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri kuti munthu apeze zinthu zimene akusowa mwauzimu komanso kuti akhale wosangalala. Koma kodi tingakhale bwanji osangalala ngakhale kuti pali zinthu zambiri zimene zingatilepheretse kusangalala? Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene Yesu ananena pa ulaliki wake wapaphiri.
MAKHALIDWE AMENE AMATITHANDIZA KUKHALA OSANGALALA
7. Kodi zingatheke bwanji kuti anthu amene akumva chisoni akhale osangalala?
7 “Odala ndi anthu amene akumva chisoni, chifukwa adzasangalatsidwa.” (Mat. 5:4) Ena akhoza kudabwa kuti, ‘Zingatheke bwanji kuti munthu amene akumva chisoni akhale wosangalala?’ Sikuti Yesu ankanena za munthu aliyense amene angamve chisoni pa zifukwa zosiyanasiyana. Ngakhale anthu oipa amamva chisoni ndi mavuto amene timakumana nawo ‘m’masiku otsirizawa.’ (2 Tim. 3:1) Koma chisoni chimene amakhala nacho sichiwathandiza kuti alimbitse ubwenzi wawo ndi Yehova choncho sichingachititse kuti akhale osangalala. Yesu ankanena za anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu ndipo amamva chisoni chifukwa cha zochita za anthu osaopa Mulungu zimene zafala. Iwo amazindikira kuti ndi ochimwa ndipo amaona mavuto amene abwera m’dzikoli chifukwa cha uchimo. Yehova amaona anthu amene akumva chisoni chifukwa cha zimenezi ndipo amawalimbikitsa, kuwadalitsa, kuwathandiza kukhala osangalala komanso kuwalonjeza moyo wosatha.—Werengani Ezekieli 5:11; 9:4.
8. Kodi kukhala wofatsa kumathandiza bwanji kuti munthu akhale wosangalala?
8 “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mat. 5:5) Kodi kukhala wofatsa kungathandize bwanji kuti munthu akhale wosangalala? Munthu akaphunzira choonadi amasintha makhalidwe ake. Pali anthu ena amene m’mbuyomu anali ankhanza, okonda kukangana komanso aukali. Koma panopa anavala umunthu watsopano ndipo amasonyeza “chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akol. 3:9-12) Izi zimawathandiza kuti azikhala mwamtendere, azikondana ndi anthu komanso azikhala osangalala. Mawu a Mulungu amalonjeza kuti anthu oterewa “adzalandira dziko lapansi.”—Sal. 37:8-10, 29.
9. (a) Kodi anthu ofatsa adzalandira bwanji dziko lapansi? (b) Kodi anthu amene “akumva njala ndi ludzu lachilungamo” angakhale bwanji osangalala?
9 Kodi mawu akuti ofatsa “adzalandira dziko lapansi” amatanthauza chiyani? Odzozedwa adzalandira dziko lapansi akadzayamba kulilamulira ngati mafumu ndi ansembe. (Chiv. 20:6) Koma anthu mamiliyoni ambiri amene sakupita kumwamba adzalandira dzikoli akadzaloledwa kukhalamo kwamuyaya. Pa nthawiyo adzakhala angwiro ndipo azidzakhala mwamtendere komanso mosangalala. Anthu amenewa amakhalanso osangalala chifukwa choti amamva “njala ndi ludzu la chilungamo.” (Mat. 5:6) Koma njala ndi ludzu la chilungamo zimene amamva panopa zidzatheratu m’dziko latsopano. (2 Pet. 3:13) Yehova akadzachotsa anthu onse oipa, anthu olungama adzakhala osangalala chifukwa sadzasokonezedwanso ndi anthu osamvera malamulo komanso opanda chilungamo.—Sal. 37:17.
10. Kodi munthu wachifundo amatani?
10 “Odala ndi anthu achifundo, chifukwa adzachitiridwa chifundo.” (Mat. 5:7) Mawu achiheberi amene amagwirizana ndi mawu akuti chifundo amatanthauza ‘kukonda anthu ena komanso kuwamvera chisoni mumtima mwathu.’ Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti chifundo amanenanso za kumvera munthu wina chisoni. Koma mawu a m’Baibulo akuti chifundo amanena za munthu amene amamvera anthu ena chisoni komanso kuchita zinthu zowathandiza.
11. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Msamariya wachifundo?
11 Werengani Luka 10:30-37. Kuti timvetse tanthauzo la chifundo, tiyeni tikambirane fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo. Mtima wachifundo ndi umene unalimbikitsa Msamariyayu kuti achite zinthu zothandiza munthu amene anavulazidwa. Yesu atamaliza kufotokoza fanizoli anauza munthu amene ankalankhula naye kuti: “Pita, iwenso uzikachita zomwezo.” Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimachita zimenezi? Kodi ndimachita zinthu ngati mmene anachitira Msamariya wachifundo uja? Kodi pali zinthu zinanso zimene ndingachite pothandiza anthu amene akuvutika? Nanga ndingathandize bwanji Akhristu achikulire, amasiye komanso amene makolo awo si Mboni? Kodi ndingamayesetse kulankhula “molimbikitsa kwa amtima wachisoni”?’—1 Ates. 5:14; Yak. 1:27.
12. Kodi kukhala achifundo kungatithandize bwanji kukhala osangalala?
12 Kodi n’chifukwa chiyani anthu achifundo amakhala osangalala? Tikamachitira anthu chifundo timapeza chimwemwe chomwe chimabwera chifukwa chopatsa. Komanso timadziwa kuti zimene tikuchitazo zimasangalatsa Yehova. (Mac. 20:35; werengani Aheberi 13:16.) Ponena za munthu amene amaganizira anzake, Mfumu Davide ananena kuti: “Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo. Adzatchedwa wodala padziko lapansi.” (Sal. 41:1, 2) Tikamachitira anthu chifundo, Yehova adzatichitiranso chifundo ndipo zimenezi zidzatithandiza kukhala osangalala mpaka muyaya.—Yak. 2:13.
ANTHU “OYERA MTIMA” AMAKHALA OSANGALALA
13, 14. N’chifukwa chiyani anthu oyera mtima amakhala osangalala?
13 Yesu ananena kuti: “Odala ndi anthu oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.” (Mat. 5:8) Kuti tikhale oyera mtima tiyenera kuganizira komanso kulakalaka zinthu zabwino. Kukhala ndi maganizo oyera kumatithandiza kuti tizitumikira Yehova m’njira yoyenera.—Werengani 2 Akorinto 4:2; 1 Tim. 1:5.
14 Anthu oyera mtima amakhala osangalala komanso amasangalatsa Yehova yemwe ananena kuti: “Odala ndiwo amene achapa mikanjo yawo.” (Chiv. 22:14) Kodi ‘amachapa mikanjo yawo’ m’njira yotani? Tinganene kuti Akhristu odzozedwa ‘amachapa mikanjo yawo’ chifukwa chakuti amakhala oyera pamaso pa Yehova ndipo adzapatsidwa moyo wosafa komanso adzasangalala kumwamba mpaka kalekale. A khamu lalikulu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli akhoza kukhala anzake a Mulungu ndipo amawaonanso kuti ndi oyera. Baibulo limanena kuti “achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.”—Chiv. 7:9, 13, 14.
15, 16. Kodi oyera mtima ‘amaona’ bwanji Mulungu?
15 Popeza ‘palibe munthu angaone Mulungu n’kukhalabe ndi moyo,’ kodi anthu oyera mtima ‘amaona’ bwanji Mulungu? (Eks. 33:20) Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti ‘kuona’ amatanthauzanso ‘kuona m’maganizo, kuzindikira komanso kudziwa.’ Anthu amene amaona Mulungu mumtima mwawo ndi amene amamudziwa bwino komanso kudziwa makhalidwe ake. (Aef. 1:18) Yesu ankasonyeza makhalidwe a Mulungu kwambiri moti anati: “Amene waona ine waonanso Atate.”—Yoh. 14:7-9.
16 Kuwonjezera pa kudziwa makhalidwe a Mulungu, anthu ake ‘amamuona’ akamaona mmene amawathandizira. (Yobu 42:5) Iwo amaonanso mumtima mwawo madalitso amene Mulungu walonjeza anthu amene amayesetsa kukhala oyera n’kumamutumikira mokhulupirika. Koma odzozedwa akadzaukitsidwa n’kupita kumwamba adzatha kuonadi Yehova.—1 Yoh. 3:2.
N’ZOTHEKA KUKHALA OSANGALALA NGAKHALE TIKUKUMANA NDI MAVUTO
17. Kodi mtendere umatithandiza bwanji kuti tikhale osangalala?
17 Kenako Yesu ananena kuti: “Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere.” (Mat. 5:9) Anthu amene amayesetsa kukhazikitsa mtendere amakhala osangalala. Paja Yakobo analemba kuti: “Chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.” (Yak. 3:18) Tikasemphana maganizo ndi munthu wina mumpingo kapena m’banja tiyenera kuchonderera Mulungu kuti atithandize kukhazikitsa mtendere. Zimenezi zingathandize kuti mzimu woyera uzigwira bwino ntchito, tizichita zinthu mwachilungamo komanso tikhale osangalala. Pofotokoza kufunika kokhazikitsa mtendere, Yesu ananena kuti: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.”—Mat. 5:23, 24.
18, 19. N’chiyani chimathandiza kuti Akhristu azisangalalabe ngakhale akukumana ndi mavuto?
18 “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine.” Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Iye anapitiriza kuti: “Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.” (Mat. 5:11, 12) Atumwi atamenyedwa komanso kulamulidwa kuti asiye kulalikira, “anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala.” N’zoona kuti kumenyedwa sikunawasangalatse. Koma anasangalala “chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.”—Mac. 5:41.
19 Masiku anonso anthu a Yehova amakhalabe osangalala akamazunzidwa chifukwa cha dzina la Yesu kapena akamakumana ndi mayesero aakulu kwambiri. (Werengani Yakobo 1:2-4.) Ifenso sikuti timasangalala ndi mavuto. Koma tikakhalabe okhulupirika kwa Mulungu pa nthawi ya mavuto, Yehova amatithandiza kuti tipirire mosangalala. Mwachitsanzo, mu August 1944 mu ulamuliro wankhanza wa m’dziko lina, M’bale Henryk Dornik ndi mchimwene wake anamangidwa. Anthu amene ankawatsutsawo anati: “Anthu amenewa sungawasinthe maganizo. Ngakhale aziphedwa amasangalalabe.” M’bale Dornik anati: “N’zoona kuti sindinkafuna kufa. Koma ndinkasangalala kuti ndalimba mtima n’kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. . . . Kupemphera kuchokera pansi pa mtima kunalimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova ndipo iye anandithandiza kwambiri.”
20. Kodi kutumikira “Mulungu wachimwemwe” kumatithandiza bwanji kukhala osangalala?
20 Tikamasangalatsa “Mulungu wachimwemwe,” timakhalabe osangalala ngakhale kuti tikudwala, ndife okalamba, tikuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chathu kapena kutsutsidwa ndi anthu a m’banja lathu. (1 Tim. 1:11) Timakhalanso osangalala chifukwa cha zimene talonjezedwa ndi “Mulungu amene sanganame.” (Tito 1:2) Madalitso amene Yehova watilonjeza ndi osangalatsa kwambiri moti akadzakwaniritsidwa, tidzaiwaliratu mavuto onse amene tikukumana nawo panopa. Zimene Yehova adzatichitire m’Paradaiso ndi zabwino kwambiri kuposa zilizonse zimene tingaganize. Pa nthawi imeneyo padzakhala chisangalalo chosaneneka moti tingati ‘tidzasangalala ndi mtendere wochuluka.’—Sal. 37:11.