M’bale Watsopano M’bungwe Lolamulira
LACHITATU m’mawa pa 24 January 2018 banja la Beteli ku United States ndi ku Canada linasangalala litamva chilengezo chapadera chakuti M’bale Kenneth Cook Jr. waikidwa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.
M’bale Cook anabadwira ku Pennsylvania m’dziko la United States. M’baleyu anaphunzira choonadi kwa mnzake wa m’kalasi atangotsala pang’ono kumaliza maphunziro a kusekondale. Anabatizidwa pa 7 June 1980. Kenako anayamba upainiya wokhazikika pa 1 September 1982. Atachita upainiya kwa zaka ziwiri anaitanidwa ku Beteli ndipo utumiki umenewu anauyambira ku Wallkill ku New York pa 12 October 1984.
Zaka 25 zotsatira, m’baleyu anatumikira kudipatimenti yosindikiza mabuku ndi madipatimenti ena. Mu 1996, M’bale Cook anakwatira mlongo Jamie ndipo anayamba kutumikira limodzi ku Wallkill. Mu December 2009, m’bale ndi mlongoyu anatumizidwa ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson ndipo M’bale Cook ankagwira ku Dipatimenti Yoyankha Makalata. Mu April 2016, anapita kukatumikira ku Wallkill kwa nthawi yochepa kenako anatumizidwa ku Brooklyn. Patangopita miyezi 5, anapita kulikulu lathu ku Warwick. Mu January 2017, m’baleyu anasankhidwa kuti akhale wothandiza mu Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku ya Bungwe Lolamulira.