Pindulani ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996—Mbali 1
1 Kodi mwaŵerenga malangizo operekedwa mu “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996”? Kodi mwaona kusintha kwina? Kuyambira January mpaka April, Nkhani Na. 3 idzazikidwa pa buku la Kukambitsirana, ndipo kuyambira May mpaka December, idzazikidwa pa buku lotulutsidwa chatsopano la Chidziŵitso. Nkhani Na. 4 idzazikidwa pa buku la Munthu Wamkulu.
2 Nkhani za Ophunzira: Nkhani Na. 3 imapatsidwa kwa mlongo. Pamene izikidwa pa buku la Kukambitsirana, chochitikacho chiyenera kukhala cha kukhomo ndi khomo kapena umboni wamwamwaŵi. Pamene izikidwa pa buku la Chidziŵitso, iyenera kuperekedwa monga ulendo wobwereza kapena phunziro la Baibulo lapanyumba. Zimenezi zidzakhala zothandiza kwambiri popeza buku la Chidziŵitso lidzagwiritsiridwa ntchito kwambiri pochititsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
3 Ngati chochitikacho ndi phunziro la Baibulo lapanyumba, alongo onse aŵiri angathe kukhala pansi. Loŵani msanga m’phunzirolo mwa kukamba mawu oyamba achidule, ndiyeno kufunsa funso losindikizidwa. Amene achita mbali ya mwini nyumba ayenera kuchita zenizeni. Malemba osonyezedwa ayenera kutsegulidwa ndi kuŵerengedwa ngati nthaŵi ilola. Mlongo ayenera kugwiritsira ntchito luso la kuphunzitsa mwa kufunsa mwini nyumba mafunso omsonkhezera kulankhula momasuka ndi kulingalira naye malemba ogwiritsiridwa ntchito.
4 Kodi nchiyani chiyenera kuchitidwa ngati nkhaniyo ili ndi malemba ochuluka amene sangafotokozedwe onse m’mphindi zisanu? Sankhani malemba ofunika kwambiri amene akugogomezera mfundo zazikulu. Ngati ili ndi malemba oŵerengeka chabe, mfundo zazikulu za phunzirolo zingafotokozedwe kwambiri. Ndime kapena sentensi imodzi ingaŵerengedwe apa ndi apo m’bukulo ndiyeno kuikambitsirana ndi mwini nyumbayo.
5 Bokosi lakuti “Yesani Chidziŵitso Chanu,” limene lili kumapeto a mutu uliwonse wa buku la Chidziŵitso, lingapendedwe mwachidule ndi wofalitsa amene nkhani yake ikukhudza ndime yomaliza ya mutuwo. Nawonso mabokosi okhala ndi chidziŵitso chowonjezera a m’ndime za nkhaniyo angakambitsiridwe ngati nthaŵi ilola. Ngati bokosi lokhala ndi chidziŵitso chowonjezera lili pakati pa magawo a nkhani ziŵiri, mlongo wokamba nkhani yoyamba angalipende. Ndemanga ziyenera kuperekedwa pa zithunzithunzi za m’bukulo paliponse pamene zikhudza mfundo zimene akukambitsirana.
6 Nkhani Na. 4 iyenera kukhala yochititsa chidwi ndi yothandiza. Mlungu uliwonse, idzafotokoza chitsanzo chenicheni cha Yesu Kristu. Kambani nkhaniyo mogwirizana ndi mutu wake, ndipo sankhani malemba a Baibulo amene adzathandiza omvetsera kusumika maganizo pa moyo wa Yesu ndi umunthu wake, kuphatikizapo mikhalidwe, zizoloŵezi ndi ndingaliro zimene tifunikira kutsanzira kapena kupeŵa. Malemba osakhudza molunjika moyo wa Yesu angaphatikizidwe ngati akusonyeza mmene Yehova amaonera zizoloŵezi zina zabwino kapena zoipa kapena ngati akukhudza mutu wa nkhaniyo.
7 Ngati tigwiritsira ntchito bwino lomwe maphunziro operekedwa m’sukuluyo, tidzakhozadi ‘kulalikira mawu’ mwanjira imene imasonyeza “luso la kuphunzitsa” labwino.—2 Tim. 4:2, NW.