Mmene Tingapangire ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso
1 Chonulirapo chokhumbidwa ndi Akristu onse ndicho kuphunzitsa ena choonadi ndi kupanga ophunzira kwa awo amene “ali oyenerera moyo wosatha.” (Mac. 13:48; Mat. 28:19, 20) Gulu la Yehova latipatsa chiŵiya chabwino kwambiri chochitira zimenezi—buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Mutu wake umasonyeza kufunika kwakukulu kwa maphunziro a Baibulo, pakuti moyo wosatha ukudalira pa kudziŵa Yehova, Mulungu woona yekha, ndi Mwana wake, Yesu Kristu.—Yoh. 17:3.
2 Buku la Chidziŵitso tsopano ndilo chofalitsa chachikulu cha Sosaite chochititsira maphunziro a Baibulo apanyumba. Ngati tiligwiritsira ntchito, tidzaphunzitsa ena choonadi mosavuta, momveka, ndiponso mwachidule. Zimenezi zidzatithandiza kufika mitima ya amene akuphunzitsidwa. (Luka 24:32) Zoonadi, pali kufunika kwakuti wochititsa phunziro agwiritsire ntchito maluso abwino. Chifukwa cha chimenecho, mphatika ino yalinganizidwa kuti ipereke malingaliro ndi zikumbutso za njira zophunzitsira zimene zapezedwa kukhala zogwira mtima. Mozindikira, ndipo malingana ndi mikhalidwe ya munthu, mukhoza kugwiritsira ntchito mopita patsogolo ena kapena malingaliro onse amene aperekedwa muno. Sungani mphatika ino, ndi kuiŵerenga nthaŵi ndi nthaŵi. Mfundo zosiyanasiyana za mmenemu zingakuthandizeni kukhala wogwira mtima kwambiri kugwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso popanga ophunzira.
3 Chititsani Phunziro la Baibulo la Panyumba Lopita Patsogolo: Khalani ndi chidwi chenicheni mwa wophunzirayo monga wothekera kukhala Mkristu wophunzira ndi mbale kapena mlongo wauzimu. Khalani waubwenzi, ndi wotenthedwa maganizo. Mwa kukhala womvetsera wabwino, mungathe kudziŵa munthu winayo—kukula kwake ndi mkhalidwe m’moyo—zimene zidzakuthandizani kuzindikira mmene mungamthandizire bwino koposa mwauzimu. Khalani wofunitsitsa kudzipereka pa kuthandiza wophunzirayo.—1 Ates. 2:8.
4 Phunziro litayambidwa, ndi bwino kuti muphunzire mitu ya m’buku la Chidziŵitso mwa dongosolo lake la manambala. Zimenezi zidzaloleza wophunzira kupeza chidziŵitso chopita patsogolo cha choonadi, popeza bukulo limafotokoza nkhani za Baibulo mwatsatanetsatane bwino kwambiri. Chititsani phunzirolo kukhala losavuta ndi lokondweretsa kuti likhale laumoyo ndi lopita patsogolo. (Aroma 12:11) Zingakhale zotheka kwa inu kuphunzira mitu yochuluka umodzi panthaŵi imodzi ya ola kapena kuposa pamenepo, zikumadalira pa mikhalidwe ndi luso la wophunzirayo, popanda kungothamanga ndi phunzirolo. Ophunzira adzapita bwino patsogolo pamene mphunzitsi ndi wophunzira yemwe asunga lonjezo lawo la phunziro mlungu uliwonse. Motero, kwa anthu ochuluka, kungakhale kotheka kumaliza mitu yonse 19 m’miyezi isanu ndi umodzi yokha kapena kuposerapo.
5 Yambani phunziro lililonse ndi ndemanga zachidule zimene zili zosonkhezera munthu mu nkhaniyo. Mudzaona kuti mutu uliwonse ndiwo mfundo yaikulu ya nkhaniyo, imene iyenera kugogomezeredwa. Mutu waung’ono uliwonse ukusonyeza mfundo yaikulu, ukumakuthandizani kutsatira nkhani ya mutuwo. Peŵani kulankhula kwambiri. M’malo mwake, yesani kuchititsa wophunzira kukambapo. Kufunsa mafunso apadera otsogolera a wophunzira, ozikidwa pa zimene akudziŵa kale, kudzamthandiza kulingalira ndi kufika pa kuzindikira zinthu moyenera. (Mat. 17:24-26; Luka 10:25-37; onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 51, ndime 10.) Mamatirani pa mawu osindikizidwa a m’buku la Chidziŵitso. Kuloŵetsa mfundo zina zatsopano kungapatutse kapena kusokoneza mfundo zazikulu ndi kuchititsa phunzirolo kutalika. (Yoh. 16:12) Ngati pabuka funso limene lili losakhala la nkhani imene mukuphunzira, kaŵirikaŵiri ndi bwino kukambitsirana funsolo mutamaliza phunziro. Zimenezi zidzakulolezani kuphunzira phunziro la mlunguwo popanda kupambutsidwa. Fotokozani kwa wophunzirayo kuti mafunso ake ambiri adzayankhidwa m’kupita kwanthaŵi pamene phunzirolo likupita patsogolo.—Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 94, ndime 14.
6 Ngati wophunzirayo akuumirira zolimba pa Utatu, kusafa kwa sou [soul], helo wa moto, ndi ziphunzitso zina zonyenga, ndipo zimene zikufotokozedwa m’buku la Chidziŵitso sizikumkhutiritsa, mungampatse buku la Kukambitsirana kapena chofalitsa china chimene chikufotokoza nkhaniyo. Muuzeni kuti mudzakambitsirana naye nkhaniyo atasinkhasinkha pa zimene waŵerenga.
7 Kuyamba ndi kumaliza phunziro ndi pemphero kaamba ka chitsogozo cha Yehova ndi dalitso lake kumalemekeza chochitikacho, kumachititsa munthu kukhala ndi maganizo aulemu, ndipo kumachititsa maganizo kusumikidwa pa Yehova monga Mphunzitsi woona. (Yoh. 6:45) Ngati wophunzirayo akali kusuta fodya, mwina m’kupita kwa nthaŵi mungampemphe kuleka kusutako mkati mwa phunzirolo.—Mac. 24:16; Yak. 4:3.
8 Phunzitsani Mogwira Mtima ndi Malemba, Mafanizo, ndi Mafunso Openda: Zilibe kanthu kuti waphunzira kangati nkhaniyo, mphunzitsi waluso amapendanso phunziro lililonse polingalira za wophunzira winawake. Zimenezi zimathandizira kukonzekera mafunso ena amene angafunsidwe ndi wophunzira. Kuti muphunzitse mogwira mtima, mvetsetsani mfundo zazikulu m’mutuwo. Ŵerengani malemba kuti muone mmene akugwirira ntchito mu nkhaniyo, ndipo sankhani amene muyenera kukaŵerenga m’phunzirolo. Sinkhasinkhani mmene mungaphunzitsire mwa kumagwiritsira ntchito mafanizo ndi mafunso openda kumapeto a mutu uliwonse.
9 Mwa kugwiritsira ntchito malemba mogwira mtima, mudzathandiza wophunzira kudziŵa kuti iye akuphunziradi Baibulo. (Mac. 17:11) Kugwiritsira ntchito bokosi lakuti “Lidziŵeni Bwino Baibulo Lanu,” patsamba 14 la buku la Chidziŵitso, mphunzitseni mmene angapezere malemba. Msonyezeni mmene angadziŵire mavesi ogwidwa mawu m’phunzirolo. Ngati nthaŵi ilola, tsegulani ndi kuŵerenga malemba osonyezedwa amene sanagŵidwe mawu. Pemphani wophunzirayo kufotokoza mmene malembawo akuchirikizira kapena kumveketsa bwino zimene zanenedwa m’ndime. Gogomezerani mbali zazikulu za mavesi kuti azindikire zifukwa za mfundo zazikulu za phunzirolo. (Neh. 8:8) Kaŵirikaŵiri, mphunzitsi safunikira kuwonjezera malemba ena m’kukambitsiranako pa amene ali m’bukumo. Fotokozani za kufunika kwa kudziŵa maina a malemba ndi dongosolo lake m’Baibulo. Kungakhale kothandiza kwa wophunzira kuŵerenga masamba 27-30 a Nsanja ya Olonda ya June 15, 1991. Pamene kuli koyenera, mlimbikitseni kugwiritsira ntchito New World Translation. Mungathe kumsonyeza pang’onopang’ono mmene angagwiritsirire ntchito mbali zake zosiyanasiyana, monga ngati malifalensi am’mphepete ndi indekisi ya mawu a m’Baibulo.
10 Phunziro 34 la Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki limafotokoza kuti mafanizo amasonkhezera maganizo a munthu ndi kuchititsa kuzindikira malingaliro atsopano kukhala kosavuta. Amagwirizanitsa pamodzi mphamvu ya maganizo ndi ya mtima, kotero kuti uthenga wake umaperekedwa ndi mphamvu imene simatulutsidwa ndi mawu okha. (Mat. 13:34) Buku la Chidziŵitso lili ndi mafanizo ambiri ophunzitsa amene ali okhweka komanso amphamvu. Mwachitsanzo, fanizo limene lagwiritsiridwa ntchito m’mutu 17 limachititsa kuzindikira bwino mmene Yehova m’lingaliro lauzimu amaperekera chakudya, zovala, ndi pokhala kupyolera mumpingo wachikristu. Zithunzithunzi zokongola za buku la Chidziŵitso zingagwiritsiridwe ntchito kusonkhezera mtima. Pa mutu waung’ono wakuti “Chiukiriro Chokondweretsa,” patsamba 185, mphamvu ya ndime 18 idzalimbitsidwa mwa kupempha wophunzira kuyang’ananso chithunzi cha patsamba 86. Zimenezi zingamsonkhezere kuona chiukiriro kukhala chenicheni mu Ufumu wa Mulungu.
11 Ophunzira Baibulo afunikira kupita patsogolo mwauzimu pa phunziro lililonse. Chifukwa chake, musalephere kufunsa mafunso openda a m’bokosi lakuti “Yesani Chidziŵitso Chanu” limene lili kumapeto kwa mutu uliwonse. Mvetserani zoposa yankho lolondola la zimene mwaphunzira. Angapo a mafunso ameneŵa alinganizidwa kuchititsa munthu kudziyankhira kuchokera mumtima. Mwachitsanzo, onani tsamba 31, pamene wophunzira akufunsidwa kuti: “Kodi ndi mikhalidwe ya Yehova iti imene imakukondweretsani makamaka?”—2 Akor. 13:5.
12 Phunzitsani Ophunzira Kukonzekera Phunziro: Wophunzira amene amaŵerenga za m’phunziro pasadakhale, kuchonga mayankho, ndi kuganiza za mmene angawafotokozere m’mawu akeake amapita patsogolo mwauzimu mwamsanga. Mwa chitsanzo chanu ndi chilimbikitso, mungamphunzitse kukonzekera phunziro. Msonyezeni buku lanu, mmene mwalembamo kapena kuchongamo mfundo zazikulu kapena mawu. Fotokozani mmene angapezere mayankho achindunji a mafunso osindikizidwa. Kukonzekera naye pamodzi mutu wina kungakhale kothandiza kwa wophunzira. Mlimbikitseni kufotokoza zinthu m’mawu akeake. Ndi pokhapo pamene mudzadziŵa ngati akumvetsa nkhaniyo. Ngati akuŵerenga mayankho ake m’buku, mungasonkhezere maganizo ake mwa kumfunsa mmene angafotokozere mfundoyo munthu wina m’mawu ake.
13 Limbikitsani wophunzira kuŵerenga malemba osagwidwa mawu pakukonzekera kwake mlungu ndi mlungu, popeza sipangakhale nthaŵi ya kuŵerenga onse mkati mwa phunziro. Muyamikireni chifukwa cha kuyesayesa kumene akusonyeza m’maphunziro. (2 Pet. 1:5; onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1993, masamba 13-14, kaamba ka malingaliro ena owonjezereka pa zimene mphunzitsi ndi wophunzira yemwe angachite kuti awonjezere kuphunzira pa phunziro la Baibulo.) Mwa njira imeneyi, wophunzira amaphunzitsidwa kukonzekera ndi kupereka ndemanga zatanthauzo pamisonkhano ya mpingo. Adzakhala akuphunzira mmene angakulitsire zizoloŵezi zabwino za phunziro la Baibulo laumwini zimene zidzamtheketsa kupitabe patsogolo m’choonadi atamaliza phunziro lake m’buku la Chidziŵitso.—1 Tim. 4:15; 1 Pet. 2:2.
14 Tsogolerani Ophunzira ku Gulu la Yehova: Ndi thayo la wopanga wophunzira kutsogolera wophunzira wachidwi ku gulu la Yehova. Wophunzira adzapita patsogolo mofulumira ku uchikulire wauzimu ngati azindikira ndi kuyamikira gulu ndi kudziŵa za kufunika kwa kukhala wogwirizana nalo. Tikufuna kuti apeze chisangalalo cha kuyanjana ndi anthu a Mulungu ndi kuyembekezera kukhala nafe pa Nyumba ya Ufumu, pamene angalandire chichirikizo chauzimu ndi chamtima chimene mpingo wachikristu umapereka.—1 Tim. 3:15.
15 Brosha lakuti Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana Padziko Lonse latulutsidwa kuti lidziŵitse munthu aliyense za gulu lokha looneka limene Yehova akugwiritsira ntchito lerolino kuchitira chifuniro chake. Bwanji osapatsa wophunzirayo kope lake, mutakhazikitsa phunzirolo? Kuyambira pachiyambi penipeni, pitirizani kuitanira wophunzirayo ku misonkhano. Fotokozani mmene imachitidwira. Mungamuuze mutu wa nkhani yapoyera imene ikudza kapena msonyezeni nkhani imene idzakambitsiridwa pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Mwina mungamke naye kuti akaone Nyumba ya Ufumu pamene kulibe msonkhano kuti muchepetse nkhaŵa imene angakhale nayo ya kupita ku malo atsopano kwa nthaŵi yoyamba. Mwina mukhoza kumtenga pa galimoto kumka naye ku misonkhano. Pamene afikapo, mchititseni kukhala wolandiridwa ndi womasuka. (Mat. 7:12) Mdziŵikitseni kwa Mboni zina, kuphatikizapo akulu. Tikhulupirira kuti adzayamba kuona mpingo monga banja lake lauzimu. (Mat. 12:49, 50; Marko 10:29, 30) Mungamuikire chonulirapo, monga ngati kufika pa msonkhano umodzi mlungu uliwonse, ndi kupitiriza kuwonjezera chonulirapocho.—Aheb. 10:24, 25.
16 Pamene phunziro la Baibulo la panyumba likupitiriza m’buku la Chidziŵitso, gogomezerani zigawo zimene zikusonyeza kufunika kwa kuyanjana nthaŵi zonse ndi mpingo pamisonkhano. Onani makamaka pamasamba 52, 115, 137-9, 159, ndiponso mutu 17. Sonyezani malingaliro a inu mwini a chiyamikiro chachikulu pa gulu la Yehova. (Mat. 24:45-47) Lankhulani momangirira ponena za mpingo wa kumaloko ndi zimene mumaphunzira pamisonkhano. (Sal. 84:10; 133:1-3) Kungakhale bwino ngati wophunzira angathe kuonerera vidiyo iliyonse ya Sosaite, kuyambira ndi yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. Kuti mupeze malingaliro ena onena za mmene mungatsogolere munthu ku gulu, onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1985, masamba 14-18, ndi mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa April 1993.
17 Limbikitsani Ophunzira Kuchitira Umboni kwa Ena: Cholinga chathu pophunzira ndi anthu ndicho kupanga ophunzira amene amachitira umboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Zimenezo zikutanthauza kuti mphunzitsi ayenera kulimbikitsa wophunzira kulankhula kwa ena zimene akuphunzira m’Baibulo. Zimenezi zingachitidwe mwa kungofunsa kuti: “Kodi mungafotokoze motani choonadi chimenechi ku banja lanu?” kapena “Kodi ndi lemba liti limene mungagwiritsire ntchito kusonyeza zimenezi kwa bwenzi lanu?” Gogomezerani pa malo ofunika a m’buku la Chidziŵitso pamene kuchitira umboni kukulimbikitsidwa, monga ngati pamasamba 22, 93-5, 105-6, ndiponso mutu 18. Pamene kuli koyenera, wophunzira angapatsidwe matrakiti pang’ono oti akagaŵire ena mu ulaliki wamwamwaŵi. Pemphani kuti aitane a m’banja lake kudzakhala nawo pa phunziro lake. Kodi ali ndi mabwenzi amenenso angakonde kuphunzira? Mpempheni kukuuzani awo amene akufuna.
18 Mwa kufika pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi pa Msonkhano Wautumiki, woyembekezeredwa kukhala wophunzira angathe kulandira maphunziro owonjezereka ndi chisonkhezero chimene chidzamthandiza kukhala wofalitsa uthenga wabwino. Pamene afuna kulembetsa sukulu kapena kukhala wofalitsa wosabatizidwa, mapulinsipulo amene andandalikidwa pa masamba 98 ndi 99 m’buku la Uminisitala Wathu adzatsatiridwa. Ngati kanthu kena m’moyo wake kamlepheretsa kukwaniritsa, mungathe kufufuza zofalitsa za Sosaite kaamba ka mfundo ina yothandiza imene ikufotokoza nkhaniyo ndi kukambitsirana naye. Mwachitsanzo, wophunzira angakhale ndi vuto pa kugonjetsa kusuta fodya kapena mankhwala ena. Buku la Kukambitsirana limasonyeza zifukwa za m’Malemba zimene Akristu amapeŵera zizoloŵezi zovulaza zotero, ndipo pamasamba 253-4 limafotokoza mwatsatanetsatane njira zimene zakhaladi zopambana pothandiza ena kuwonjoka. Pempherani naye za nkhaniyo, mukumamphunzitsa kukulitsa chidaliro chake pa chithandizo cha Yehova.—Yak. 4:8.
19 Njira yofunikira kutsatiridwa kuti mudziŵe ngati munthu ali woyenerera kukhala ndi phande muutumiki wapoyera yafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996, tsamba 16, ndime 6. Pamene wophunzira ayenerera, kukakhala kothandiza kuyeseza naye kuti mumkonzekeretse tsiku lake loyamba muutumiki wakumunda. Kambitsiranani bwino za machitidwe a anthu ndi zitsutso zimene zili zofala m’gawo lanu. Muyambitseni ntchito ya kunyumba ndi nyumba choyamba ngati nkotheka, ndipo mphunzitseni pang’onopang’ono mbali zina za utumiki. Ngati ulaliki wanu ukhala waufupi ndi wosavuta, kudzakhala kosavuta kwa iye kutsanzira. Khalani womangirira ndi wolimbikitsa, mukumasonyeza chimwemwe mu ntchitoyo, kuti atengere mzimu wanu ndi kuusonyeza. (Mac. 18:25) Cholinga cha wophunzira watsopano chiyenera kukhala cha kukhala wofalitsa uthenga wabwino wachangu wokhazikika. Mwina mungamthandize kukonza mndandanda wothandiza wa utumiki. Kuti iye apite patsogolo m’luso lake la kuchitira umboni kwa ena, mungampatse lingaliro lakuti aŵerenge kope la Nsanja ya Olonda la February 1, 1985, masamba 15-25; July 15, 1988, masamba 9-20; January 15, 1991, masamba 15-20; ndi January 1, 1994, masamba 20-5.
20 Sonkhezerani Ophunzira Kulinga ku Kudzipatulira ndi Ubatizo: Kuyenera kukhala kotheka kwa wophunzira woona mtima kuphunzira zokwanira m’phunziro la buku la Chidziŵitso kuti adzipatulire kwa Mulungu ndi kuyenerera ubatizo. (Yerekezerani ndi Machitidwe 8:27-39; 16:25-34.) Komabe, munthu asanasonkhezereke kudzipatulira, afunikira kukulitsa kudzipereka kwake kwa Yehova. (Sal. 73:25-28) Nthaŵi zonse pamene mukuphunzira, funafunani mipata yokulitsira chiyamikiro pa mikhalidwe ya Yehova. Nenani mawu osonyeza chiyamikiro cha inu mwini choona mtima kaamba ka Mulungu. Thandizani wophunzira kuganiza za kukulitsa unansi wake wachikondi ndi Yehova. Ngati afikadi pa kudziŵa ndi kukonda Mulungu, pamenepo adzamtumikira Iye mokhulupirika, pakuti kudzipereka kwaumulungu nkogwirizana ndi mmene timaonera Yehova monga munthu.—1 Tim. 4:7, 8; onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 76, ndime 11.
21 Yesetsani kufika mtima wa wophunzira. (Sal. 119:11; Mac. 16:14; Aroma 10:10) Afunikira kuona mmene choonadi chikumkhudzira iye mwini ndi kusankha zimene ayenera kuchita ndi zimene waphunzira. (Aroma 12:2) Kodi akukhulupiriradi choonadi chimene akupatsidwa mlungu ndi mlungu? (1 Ates. 2:13) Muli ndi cholinga chimenecho, mungathe kuchititsa wophunzirayo kufotokoza za mumtima mwa kumfunsa mafunso a kufuna kudziŵa za lingaliro lake, onga akuti: Kodi mukuganiza bwanji pa zimenezi? Kodi mungagwiritsire ntchito motani zimenezi m’moyo wanu? Mwa mawu ake mungathe kuzindikira pamene pali pofunikira thandizo lowonjezereka kuti mufike mtima wake. (Luka 8:15; onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 52, ndime 11.) Mawu ofotokoza zithunzi pamasamba 172 ndi 174 a buku la Chidziŵitso amafunsa kuti: “Kodi mwadzipatulira kwa Mulungu m’pemphero?” ndi “Kodi nchiyani chikuletsani kubatizidwa?” Ameneŵa angasonkhezere mogwira mtima wophunzirayo kuchitapo kanthu.
22 Njira yoti itsatiridwe pamene wofalitsa wosabatizidwa akufuna kukhala wobatizidwa yafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996, tsamba 17, ndime 9. Buku la Chidziŵitso linalembedwa ndi cholinga cha kukonzekeretsa munthu kuyankha “Mafunso Kaamba ka Awo Ofuna Kubatizidwa,” opezeka mu zowonjezeredwa za buku la Uminisitala Wathu, amene akulu adzapenda naye. Ngati mwagogomezera mayankho a mafunso osindikizidwa a m’buku la Chidziŵitso, wophunzirayo adzakhala wokonzekera bwino kufunsidwa ndi akulu pokonzekera ubatizo wake.
23 Thandizani Awo Amene Amaliza Phunziro la Baibulo la Panyumba: Tiganiza kuti podzafika nthaŵi imene munthu akumaliza phunziro la buku la Chidziŵitso, kuona mtima kwake ndi kuya kwa chikondwerero m’kutumikira Mulungu kudzaoneka. (Mat. 13:23) Nchifukwa chake mutu waung’ono womaliza wa bukuli umafunsa kuti, “Kodi Mudzachitanji?” Ndime zomaliza zikusonkhezera wophunzira kuika mtima pa unansi umene ayenera kukulitsa ndi Mulungu, kufunikira kwa kugwiritsira ntchito chidziŵitso chimene waphunzira, ndi kufunikira kwa kuchitapo kanthu mofulumira kusonyeza chikondi chake pa Yehova. Palibe makonzedwe a kuphunzira zofalitsa zinanso ndi aja amene amamaliza buku la Chidziŵitso. Mokoma mtima ndi momveka fotokozani kwa wophunzira amene akulephera kuchitapo kanthu pa chidziŵitso cha Mulungu zimene ayenera kuchita kuti apite patsogolo mwauzimu. Mungamaonane naye pa nthaŵi ndi nthaŵi, mukumamsiyira khomo lotseguka la kutenga masitepe otsogolera ku moyo wosatha.—Mlal. 12:13.
24 Wophunzira amene amalandira choonadi ndi kubatizidwa adzafunikira kuchita zambiri kuti akulitse chidziŵitso ndi kumvetsa kwake zinthu kuti akhale wokhazikika mokwanira m’chikhulupiriro. (Akol. 2:6, 7) M’malo mwa kupitiriza phunziro lake la Baibulo lapanyumba mutatsiriza buku la Chidziŵitso, dzichititseni kukhala wopezeka kuti mupereke thandizo lililonse limene angafunikire kuti akule mwauzimu. (Agal. 6:10; Aheb. 6:1) Kumbali yake, angathe kuwonjezera kumvetsa kwake mwa kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kuphunzira Nsanja ya Olonda mwaumwini ndi zofalitsa zina za ‘kapolo wokhulupirika,’ kukonzekera ndi kufika pa misonkhano, ndi kukambitsirana choonadi ndi okhulupirira anzake. (Mat. 24:45-47; Sal. 1:2; Mac. 2:41, 42; Akol. 1:9, 10) Kuŵerenga kwake buku la Uminisitala Wathu ndi kugwiritsira ntchito zimene zilimo kudzamthandiza kwambiri kukhala wolinganizidwa mwateokrase kutsiriza utumiki wake mokwanira.—2 Tim. 2:2; 4:5.
25 Kulitsani Luso la Kuphunzitsa: Tapatsidwa ntchito ya “kupanga ophunzira . . . kuwaphunzitsa.” (Mat. 28:19, 20, NW) Popeza kuti luso la kuphunzitsa nlogwirizana kwambiri ndi kupanga ophunzira, tikufuna kuyesayesa kukulitsa maluso monga aphunzitsi. (1 Tim. 4:16; 2 Tim. 4:2) Kuti mupeze malingaliro enanso onena za mmene mungakulitsire luso la kuphunzitsa, mungaŵerenge mutu wakuti: “Kukulitsa Luso la Kuphunzitsa” ndi “Kufika Mtima wa Omvetsera Anu” mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, maphunziro 10 ndi 15; “Teacher, Teaching” mu Insight, Voliyumu 2; ndi nkhani za Nsanja ya Olonda yakuti “Kumanga Ndi Zomangira Zosanyeka ndi Moto” ndi yakuti “Pamene Muphunzitsa, Fikirani Mtima,” January 15, 1985; “Kodi Mumakambitsirana Mwachipambano za m’Malemba?” August 15, 1986; ndi yakuti “Mmene Mungapezere Chimwemwe Popanga Ophunzira,” February 15, 1996.
26 Pamene muyesayesa kupanga ophunzira, mogwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso, nthaŵi zonse pempherani kuti Yehova, amene “amakulitsa,” adzadalitsa zoyesayesa zanu za kufika mitima ya anthu ndi uthenga wabwino wa Ufumu. (1 Akor. 3:5-7) Mupezetu chimwemwe cha kuphunzitsa ena kumvetsa, kuzindikira, ndi kuchitapo kanthu pa chidziŵitso chotsogolera ku moyo wosatha!