“Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?”
1 Uthenga wosangalatsa, wochititsa chidwi, ndi wokhudza mtima udzalalikidwa padziko lonse m’zinenero 169. Kodi uthenga umenewu ngwachiyani? Ndipo udzaperekedwa bwanji?
2 Uthengawo ngwonena za chikondi cha pa mnansi. Ukupezeka mu Uthenga wa Ufumu Na. 35, wokhala ndi mutu wakuti “Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?” Uthenga wa Ufumu umenewu ukulongosola mwachidule mmene zinthu zakhalira lerolino padziko lonse, kusonyeza kuti muzu wa zopweteketsa mtima ndi zoŵaŵa zambiri ndiwo kupanda chikondi kwa anthu. Ukufotokoza chifukwa chake, makamaka m’tsiku lathu, chikondi cha pa mnansi chazirala mwa anthu ndi zotsatirapo zake za mtsogolo.
3 Panthaŵi imodzimodziyo, Uthenga wa Ufumu Na. 35 ukusonyeza kuti anthu mamiliyoni ambiri amene alipo lero ali nacho chikondi chenicheni cha pa mnansi. Ukudziŵikitsa anthu amene akuyambitsanso Chikristu chakale—kulambira kwa m’zaka za zana loyamba, komwe kunali kwa chikondi cha pa mnansi monga mmene Yesu Kristu anaphunzitsira.—Luka 10:25-37.
4 Uthenga wa Ufumu Na. 35 ukumaliza mwa kufotokoza mmene dziko lonse la anthu posachedwapa lidzakhalira ndi chikondi cha pa mnansi mu ulamuliro wa Kristu mu Ufumu wa Mulungu. Omwe akuuŵerenga uthengawu tikuwalimbikitsa kupeza brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kuti aphunzire mmene angapindulire ndi makonzedwe achikondi a padziko lonse omwe afotokozedwa momveka bwino m’Mawu a Mulungu.
5 Nanga Ndani Adzapereka Uthenga Umenewu? Mboni za Yehova padziko lonse zidzakhala zikunena uthenga umenewu wa chikondi cha pa mnansi kwa odziŵana nawo, anansi awo, ndi achibale awo m’miyezi ya October ndi November. Tikulimbikitsa onse amene ali oyenera kuti atenge mbali pakufalitsa Uthenga wa Ufumu Na. 35.
6 Cholinga chachikulu cha mkupitiwu nchodzutsa chidwi cha anthu kuti akhale ndi phunziro la Baibulo kaya m’brosha la Mulungu Amafunanji kapena m’buku la Chidziŵitso. Ndiponso, mtumiki aliyense wa Yehova atayesetsa ndi mtima wonse, adzachitira umboni wamphamvu Mulungu wachikondi, Yehova, ndi Mwana wake, Yesu Kristu.