Lalikiranibe!
1 Chifuniro cha Mulungu n’chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Tim. 2:4) Pachifukwa chimenechi, iye watigaŵira ntchito yolalikira uthenga wabwino. (Mat. 24:14) Ngati timvetsa chifukwa chake tiyenera kulalikirabe, sitidzalola chofooketsa kapena chopinga chilichonse kutiletsa.
2 Kodi n’kulimbikiriranji? M’dzikoli muli zochenjeneka zambiri zimene zimachititsa anthu kuiŵala kapena kupeputsa zimene timawauza. Choncho tiyenera kumawakumbutsabe za uthenga wa Mulungu wa chipulumutso. (Mat. 24:38, 39) Kuwonjezera apo, mikhalidwe m’miyoyo ya anthu imasintha nthaŵi zonse. Ngakhale mikhalidwe ya padziko imatha kusinthiratu nthaŵi imodzi. (1 Akor. 7:31) Maŵa, sabata yamaŵa, kapena mwezi wamaŵa, anthu amene timawalalikira angakumane ndi mavuto kapena nkhaŵa zatsopano zimene zingawachititse kuganizira mofatsa za uthenga wabwino umene timawabweretsera. Kodi inuyo simukuyamikira kuti Mboni imene inakubweretserani choonadi inali yolimbikira?
3 Kuti Titengere Chifundo cha Mulungu: Moleza mtima Yehova walola nthaŵi kupitapo asanapereke chiweruzo pa anthu oipa. Kudzera mwa ife iye wapitiriza kuchonderera anthu owongoka mitima kuti atembenukire kwa iye napulumutsidwe. (2 Pet. 3:9) Tidzakhala ndi mlandu wophetsa anthu ngati sitiuza anthu za uthenga wa chifundo cha Mulungu ndi kuwachenjeza za chiweruzo cha Mulungu chimene chikubwera pa anthu onse amene satembenuka kusiya njira zawo zoipa. (Ezek. 33:1-11) Ngakhale kuti si nthaŵi zonse pamene ulaliki wathu umalandiridwa, sitiyenera kugwa mphwayi pochita chilichonse chotheka kuti tithandize oona mtima kuzindikira chifundo chachikulu cha Mulungu.—Mac. 20:26, 27; Aroma 12:11.
4 Kuti Tionetse Chikondi Chathu: Yehova Mulungu, kudzera mwa Yesu Kristu, ndi amene analamula kuti uthenga wabwino ulalikidwe pa dziko lonse lapansi. (Mat. 28:19, 20) Ngakhale pamene anthu akana kumvetsera, umakhalabe mpata wathu wosonyeza chikondi ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu mwa kulimbikira pochita chabwino.—1 Yoh. 5:3.
5 Tiyenitu tikhale otsimikiza mtima kuti tidzalalikirabe! Tichitetu zimenezo mokangalika pamene lidakali “tsiku la chipulumutso” cha Yehova.—2 Akor. 6:2.