“Ali Wosangalala Munthu Wopirira Mayesero”
1 Akhristu onse amakumana ndi mayesero. (2 Tim. 3:12) Angakumane ndi mayesero osiyanasiyana monga matenda, mavuto a zachuma, kapena zizunzo. Satana amatiyesa n’cholinga choti tifooke pa utumiki wathu, tisiye kulalikira, kapena kutumikira Mulungu. (Yobu 1:9-11) Kodi kupirira mayesero kumabweretsa motani chisangalalo?—2 Pet. 2:9.
2 Konzekerani Kukumana ndi Mayesero: Yehova watipatsa Mawu ake a choonadi, omwe amafotokoza za moyo wa Yesu ndi zimene anaphunzitsa. Tikamamvera zimene Yesu ananena ndi kuzichita, timayala maziko olimba, mwa kutero timakhala okonzeka kukumana ndi mayesero. (Luka 6:47-49) Ndiponso timalimbikitsidwa ndi abale athu auzimu, misonkhano ya mpingo, ndiponso mabuku ofotokoza za m’Baibulo omwe gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru limatipatsa. Komanso timagwiritsa ntchito kwambiri mphatso ya pemphero imene Mulungu watipatsa.—Mat. 6:13.
3 Yehova watipatsanso chiyembekezo. Tikakhala ndi chikhulupiriro cholimba pa malonjezo a Yehova, chiyembekezo chathu chimakhala monga ‘nangula wa miyoyo yathu. N’chotsimikizika, ndiponso chokhazikika.’ (Aheb. 6:19) M’nthawi za m’Baibulo, ngalawa sinkanyamuka yopanda nangula, ngakhale pamene mphepo inali bwino. Ngati mphepo yamkuntho itayamba mwadzidzidzi, kuponya nangula m’madzi kunali kuteteza ngalawa kuti isawombe miyala ya kugombe. N’chimodzimodzinso ifeyo, tikakhala ndi chikhulupiriro cholimba pa malonjezo a Mulungu panopa, chikhulupirirocho chidzatithandiza pamene takumana ndi mavuto. Mavuto angayambe mwadzidzidzi. Mwachitsanzo, poyamba anthu ankamvetsera zimene Paulo ndi Baranaba ankalalikira ku Lusitara, koma zinthu zinadzasintha mwadzidzidzi pamene Ayuda otsutsa anafika kumeneko.—Mac. 14:8-19.
4 Kupirira Kumabweretsa Chimwemwe: Tikamapitiriza kulalikira ngakhale anthu akutitsutsa, timakhala ndi mtendere wa mumtima. Ndipo timasangalala tikamayesedwa ndi kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha Khristu. (Mac. 5:40, 41) Kupirira mayesero kumatithandiza kuti tisonyeze kwambiri makhalidwe monga kudzichepetsa, kumvera, ndi kupirira. (Deut. 8:16; Aheb. 5:8; Yak. 1:2, 3) Kumatiphunzitsanso kudalira Yehova ndi kukhulupirira malonjezo ake.—Miy. 18:10.
5 N’zoona kuti mayesero n’ngakanthawi. (2 Akor. 4:17, 18) Mayesero amatipatsa mwayi wosonyeza mmene timakondera Yehova. Tikamapirira mayesero, timapereka yankho ku zitonzo za Satana. Choncho, timapitirizabe kupirira popeza “ali wosangalala munthu wopirira mayesero, chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira kolona wa moyo.”—Yak. 1:12.
(Yapitirizidwa pa tsa. 7, danga 3)
Kupirira Mayesero (Yapitirizidwa)