Kodi Ndinu Wokonzeka Kuchita Ulaliki Wamwamwayi?
1. Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti ulaliki wamwamwayi ungakhale wothandiza?
1 Ulaliki wamwamwayi ungakhale wothandiza kwambiri. Baibulo lili ndi zitsanzo zambiri za ulaliki wamwamwayi umene unali ndi zotsatirapo zabwino. (Yoh. 4:7-15) Kodi tingatani kuti tikhale okonzeka kuchita ulaliki umenewu?
2. Kodi kuvala ndi kudzikongoletsa moyenera kungatithandize bwanji kulalikira?
2 Kuvala ndi Kudzikongoletsa: Ngati nthawi zonse tizikongoletsa ndiponso kuvala bwino, tidzakhala omasuka kuuza ena zimene timakhulupirira. (1 Tim. 2:9, 10) Nthawi zambiri zingativute kulalikira ngati tiona kuti sitinavale bwino. Koma ngati zovala zathu zili zoyera ndiponso tikuoneka bwino, anthu ena angafune kudziwa chifukwa chake timavala bwino. Mwachitsanzo, banja lina la Mboni linali pa ulendo ndipo linavala bwino kwambiri. Pa ulendowu linakumana ndi bambo wina wachisilamu. Bamboyu ataona mmene banjalo limaonekera, anafunsa ngati iwo anali Akhristu. Zimenezi zinachititsa kuti akambirane nkhani za m’Baibulo kwa maola atatu.
3. Potsatira chitsanzo cha Yesu, kodi munatani kuti muyambe kukambirana ndi anthu?
3 Mmene Tingayambire Kukambirana: Yesu atakumana ndi mayi wachisamariya pachitsime cha Yakobo, anayamba kukambirana naye mwa kungom’pempha madzi akumwa. Ifenso tingathe kuyamba kukambirana ndi anthu mwa kungonena mawu ena achidule kapena kufunsa funso losavuta kuyankha. Mwina nthawi zina tingachite mantha, koma mwa kudalira Yehova tingathe ‘kulimba mtima’ n’kuyamba kukambirana ndi anthu.—1 Ates. 2:2.
4. Kodi tingatani kuti tikhale okonzeka kulalikira mwamwayi?
4 Funani Mipata Yolalikira Mwamwayi: Ofalitsa ambiri apeza njira zochitira ulaliki wamwamwayi. Nanunso onani mmene zinthu zilili pa moyo wanu ndipo ganizirani anthu amene mungakumane nawo tsiku ndi tsiku. Muzinyamula mabuku ndi magazini oyenera komanso Baibulo. Khalani tcheru ndipo muzichita chidwi ndi anthu amene mwayandikana nawo. Mukaganizira mipata yolalikira mwamwayi imene mungakhale nayo pa tsiku, mungathe kukhala wokonzeka kulalikira mogwira mtima.—Afil. 1:12-14; 1 Pet. 3:15.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera ulaliki wamwamwayi?
5 Tili ndi zifukwa zabwino ziwiri zogwiritsira ntchito mipata imene ingakhalepo kuti tilalikire mwamwayi. Zifukwa zake ndi kukonda Mulungu ndiponso kukonda anthu anzathu. (Mat. 22:37-39) Poganizira kuti ntchito yolalikira ikufunika kuchitika mwamsanga, tiyenera kumakonzekera kuchita ulaliki wamwamwayi. Tiyenera kukhala okonzeka kugwiritsa ntchito mpata uliwonse umene ungakhalepo kuti tiuze ena uthenga wabwino wa Ufumu nthawi isanathe.—Aroma 10:13, 14; 2 Tim. 4:2.