Kodi Diso Lanu Limalunjika Pachinthu Chimodzi?
1. Kodi kukhala ndi ‘diso lolunjika chinthu chimodzi’ kumatanthauza chiyani?
1 Timachita zinthu mogwirizana ndi zimene timaziona kawirikawiri. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Ngati diso lako lili lolunjika chimodzi, thupi lako lonse lidzawala.” (Mat. 6:22) Diso lauzimu ‘limalunjika’ pachinthu chimodzi, chimene ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. Ngati tili ndi diso lolunjika pachinthu chimodzi, timaika Ufumu patsogolo ndipo sitilola kuti zinthu zosafunikira zakuthupi kapena zochita zina zizisokoneza utumiki wathu.
2. Kodi n’chiyani chingachititse kuti tisinthe n’kuyamba kuona zinthu zosafunika pa moyo ngati zofunika, ndipo tingapewe bwanji zimenezi?
2 Tiyenera Kudzifufuza: Tingayambe kuona zinthu zosafunika pa moyo ngati zofunika chifukwa cha zimene oitanira malonda amatisonyeza kapenanso chifukwa chosirira zinthu zimene anthu ena ali nazo. Ndi bwino “kuwerengera” mtengo tisanayambe kuchita chinachake kapena kugula chilichonse chofuna ndalama zambiri. N’chimodzimodzinso ndi zinthu zofuna nthawi yaitali kapena mphamvu zambiri pozisamalira. Tingawerengere mtengo mwa kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zindithandiza kutumikira bwino Yehova kapena zingondisokoneza?’ (Luka 14:28; Afil. 1:9-11) Kawirikawiri ndi bwino kumaganizira zimene tingasinthe pa moyo wathu kuti tiwonjezere nthawi yotumikira Mulungu.—2 Akor. 13:5; Aef. 5:10.
3. Kodi tikuphunzirapo chiyani kwa mlongo wina amene anasintha moyo wake kuti azikhala moyo wosafuna zambiri?
3 Mlongo wina atayamba upainiya wokhazikika, anasankha kuti asasiye ntchito yamalipiro ambiri imenenso inkamudyera nthawi yambiri, ngakhale kuti akanatha kumagwira maganyu n’kumapeza zimene amafunikira pa moyo. Koma pa mapeto pake, iye anati: “Palibe amene angatumikire ambuye awiri. Ndinaona kuti ndibwino kuti ndisamalimbane ndi zinthu zosafunikira kwenikweni, koma ndizingoyesetsa kupeza zinthu zofunikira. Ndinazindikira kuti zinthu zakuthupi sizikhalitsa ndipo kulimbikira kupeza zinthu zimenezi kumangotopetsa.” Malinga ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wake, iye anayamba kukhala moyo wosafuna zambiri komanso anasintha ntchito yake, zimene zinamuthandiza kuti apitirizebe kuchita upainiya.
4. N’chifukwa chiyani kukhalabe ndi diso lolunjika pachinthu chimodzi kuli kofunika kwambiri?
4 Kulunjikitsa diso lathu pachinthu chimodzi n‘kofunika kwambiri masiku ano chifukwa nthawi yatha. Tsiku lililonse tikuyandikira mapeto a dongosolo lino komanso kuyambika kwa dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. (1 Akor. 7:29, 31) Tikamakonda kwambiri ntchito yolalikira tidzadzipulumutsa tokha ndi anthu amene amamvetsera uthenga wathu.—1 Tim. 4:16.